Khalani ndi Moyo Wolinganizika, Wopepuka
“Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; . . . popeza masiku ali oipa.”—AEFESO 5:15, 16.
1, 2. Kodi nchiyani chomwe chiri chitokoso chenicheni lerolino, ndipo kodi chingayerekezedwe ndi chiyani?
CHIRI chitokoso kusanthula zoyambirira, kusamalira mathayo pa nthaŵi imodzi, ndi kupereka nthaŵi ndi nyonga ku mbali zofunika za moyo m’njira yolingalirika. Chirinso chitokoso kupeŵa kupambanitsa ndi kusungilira kukhazikika kwa maganizo ndi malingaliro.—Aefeso 5:17; 1 Timoteo 4:8; 1 Petro 1:13.
2 Chitokoso chimenechi chingayerekezedwe ku chija choyang’anizidwa ndi woseŵera woyesera kuyenda pa nsambo ya pamwamba yowonda. Kutaikiridwa kulinganizika kukakhala ngozi kwa iye. Mofananamo, kutaikiridwa kulinganizika kwauzimu kukakhala ngozi kwa ife. Munthu woyenda pa nsambo yapamwamba motsimikizirika samadzilemetsa iyemwini ndi zinthu zambiri. Iye amanyamula kokha zofunikira. Chotero, ndi cholinga chofuna kusungilira kulinganizika kwathu kwauzimu, tifunikira kukhala ndi moyo wopepuka, wosalemetsedwa.—Ahebri 12:1, 2.
3. Nchiyani chomwe tiyenera kuchita kuti tikhale ndi moyo wopepuka?
3 Ngati titi tikhale ndi moyo wopepuka, tiyenera kudziloŵetsa ife eni kokha m’zinthu zofunikira kusungilira kakhalidwe kolingalirika. M’kusiyanitsa ndi chimene ophunzira ake akayenera kufunafuna—Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo Chake—Yesu Kristu analankhula za “zinthu zimene amitundu akulondola mofunitsitsa.” (Mateyu 6:32, 33, NW) Chotero Yesu anatilangiza ife kupeŵa kukundika zochulukira za zinthu zimenezi. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti zingacholoŵanitse moyo wathu ndi kutisokeretsa. (Luka 12:16-21; 18:25) Uwu ndi uphungu wabwino, mosasamala kanthu kaya ndife olemera kapena osauka, ophunzira bwino kapena ayi.
Chifukwa Chimene Kuliri Kofunika Chotero Tsopano
4. Nchifukwa ninji kukhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka kuli kofunikira chotero tsopano?
4 Kukhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka kuli makamaka kofunika tsopano chifukwa chakuti Satana ndi ziwanda zake abindikiritsidwa ku dziko lapansi ndipo ali olakalaka kutithodwetsa ndi kupatutsa chisamaliro chathu kuchoka ku utumiki wa Mulungu. (Chibvumbulutso 12:7-12, 17) Chotero, kulibe ndi kale lonse pamene lamulo la Baibulo lakhala logwira ntchito koposa lakuti: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; [mukumadzipezera nthaŵi, NW], popeza masiku ali oipa.” (Aefeso 5:15, 16) Inde, tikukhala m’dziko loipa la Satana, osati dziko latsopano la Mulungu. Chotero, sitingakhoze kukhala osasamala.—2 Akorinto 4:4; 2 Petro 3:7, 13.
5. Ndimotani mmene atumiki a Mulungu a nthaŵi zakale anatikhazikitsira ife chitsanzo chabwino?
5 Atumiki a Mulungu omwe anakhala ndi moyo m’dziko lolamulidwa ndi Mdyerekezi limeneli m’nthaŵi zakale atikhazikitsira chitsanzo chabwino. Iwo “anavomereza kuti ali alendo ndi ogonera pa dziko.” Chotero, iwo anafunafuna “lina loposa, ndilo, la m’mwamba.” (Ahebri 11:13-16) Kugonjera kwawo kunali kwa Ufumu wa kumwamba wa Mulungu, mongadi mmene kwathu kuyenera kukhalira. Kaamba ka chifukwa chimenechi, mtumwi Petro anatcha Akristu kukhala “alendo ndi ogonera.” (1 Petro 2:11; Afilipi 3:20) M’chenicheni, Yesu ananena kuti otsatira ake owona “sali mbali ya dziko.” Ichi chimatanthauza, monga mmene mtumwi Paulo ananenera, kuti Akristu sayenera ‘kuchititsa nalo dziko lapansi.’—Yohane 17:16, NW; 1 Akorinto 7:31.
6. (a) Nchiyani chomwe tifunikira kukumbukira, ndipo ndi ku chiyani kumene mkhalidwe wathu ungayerekezedwe? (b) Ndi chitsanzo chochenjeza chotani chomwe tonsefe tiyenera kulabadira?
6 Chotero tifunikira nthaŵi zonse kukumbukira kuti dziko iri la Satana liri gawo lowopsya lokhalamo. Kusayenda bwino kungatanthauze tsoka. (1 Yohane 5:19; 1 Petro 5:8) Mkhalidwe wathu ungayerekezedwe ku uja wa munthu woyenda kupyola m’munda wodzalidwa mabomba. Akusonyeza chitsanzo cha chenjezo kaamba ka Akristu, mtumwi Paulo anasimba za Aisrayeli omwe anali okonzekera kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Ambiri anataya kulinganizika kwawo kwauzimu, anakhala oloŵetsedwa m’chisembwere, ndipo anaphedwa ndi Mulungu. “Chifukwa chake,” Paulo analemba tero, “iye wakuyesa kuti ali chiriri, ayang’anire kuti angagwe [kutayikiridwa kulinganizika kwake kwauzimu].”—1 Akorinto 10:12.
Chifukwa Chimene Kuliri Chinjirizo
7. Ndi kudzisanthula kwaumwini kotani komwe tiyenera kupanga mwanzeru?
7 Kukhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka kudzakuchinjirizani chifukwa chakuti kudzakupatsani inu nthaŵi yochulukira ndi nyonga kaamba ka zinthu zauzimu. Chotero mwanzeru dzifunseni inu mwini kuti: Kodi ndikupepukitsa moyo wanga, kapena kodi ndikuwupanga iwo kukhala wocholoŵanacholoŵana? Ndi zinthu zotani zomwe m’chenicheni zimakhala zoyamba m’moyo wanga? Ena amanena kuti ali ndi nthaŵi yochepera ya kuphunzira Baibulo kapena kugawana mu utumiki wa m’munda. Koma kodi chifukwa chake nchiyani? Mwachidziŵikire, kuli kulephera kwawo kwa kukhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka. Bwanji osayerekeza unyinji wa nthaŵi yomwe mumathera pa zosangulutsa, monga ngati kupenyerera wailesi ya kanema, ndi nthaŵi yomwe mumathera kutumikira Yehova m’mbali imodzi ya zochitachita Zachikristu kapena ina yake? Kodi kugwiritsira ntchito kwanu nthaŵi kuli kolinganizika? Kupeputsa moyo wanu kudzakupatsani inu nthaŵi kaamba ka zinthu zofunika kwenikweni, zomwe zimaphatikizapo kugawana ku mlingo wokulira mu kututa kwauzimu kofunika koposa.—Afilipi 1:9, 10; Mateyu 9:37.
8. Ndimotani mmene wina angalabadirire langizo la Yesu la kufunafuna choyamba Ufumu, ndipo nchiyani chomwe chimachitira fanizo kufunika kwa mphamvu yokankhira kutsogolo?
8 M’chenicheni, zochitachita zanu zauzimu ziri muyeso wa kaya mukukhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka. Akristu omwe akulabadira chenjezo la Yesu la kufunafuna Ufumu wa Mulungu choyamba akupita patsogolo pa liŵiro labwino m’phunziro lokhazikika la Baibulo, kupezeka pa misonkhano, ndi mu utumiki wa m’munda. Kupita patsogolo koteroko kuli chinjirizo lenileni lolimbana ndi kugwa. Lingayerekezedwe ku kupalasa njinga. Awo omwe ayesera kulinganiza njinga yomwe ikuyenda pang’onopang’ono kukaima amayamikira kufunika kwa mphamvu yokankhira kutsogolo. Mofananamo, malinga ngati inu mukupita patsogolo pa liŵiro labwino m’dongosolo lokhazikika la zochitachita zauzimu, inu mwachinjirizidwa ku kutayikiridwa kulinganizika kwanu ndi kugwa.—Afilipi 3:16.
9. (a) Nchiyani chomwe chiri chokumbutsa chabwino kaamba ka tonsefe? (b) Pamene tikulingalira kuyamba projekiti, ndi mafunso otani omwe tingadzifunse ife eni?
9 Komabe, pali kufunika kwa kukhala ogalamuka, kukumbukira kuti kudzichotsera ife eni zinthu zolemetsa kungatipatse ife nthaŵi yochulukira kaamba ka kuphunzira, kaamba ka kukonzekera msonkhano, ndi kaamba ka kuthandiza ena. “Nthaŵi zonse pamene ndayesedwa kugula chinachake chomwe sindikufuna, kapena kuyamba ntchito yomwe sindikufuna,” ananena tero mwamuna wina wa zamalonda Wachikristu, “ndimadziletsa inemwini ndi chokumbutsa cha kuchisunga icho kukhala chopepuka. Nthaŵi zina ndimafunikira kukhala wowona ndi inemwini.” Kodi chimenecho si chokumbutsa chabwino kaamba ka tonsefe? Pamene mukulingalira za kuyamba projekiti ina yake, mwinamwake kumanga kowonjezera ku nyumba yanu kapena chinachake, bwanji osadzifunsa inu mwini kuti: Kodi ichi chidzathandizira ku uzimu wanga ndi uja wa banja langa kapena kodi chidzatsekereza iwo? Kodi ndimafunikiradi zinthu zonsezi zomwe anthu a kudziko amazilondola mofunitsitsa, kapena kodi ndingachite popanda izo?
10. Ndimotani mmene mawonedwe a “munthu wachibadwidwe” amasiyanira ndi aja a “munthu wauzimu”?
10 Ngakhale kuli tero, winawake angatsutse kuti: ‘Kodi kudzipereka nsembe kwaumwini koteroko kulidi koyenerera? Kodi tikufunikira kukhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka?’ Chabwino, Paulo analankhula za “za munthu” ndi “za Mulungu” ndipo ananena kuti: “Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu. Koma iye amene ali wauzimu ayesa zonse, koma iye yekha sayesedwa ndi mmodzi yense.” (1 Akorinto 2:11, 14, 15) Inu mopepuka mungakhoze kukhala “munthu wachibadwidwe” mwa kufunafuna ndi kupeza zinthu zosayenerera za mkhalidwe wa chuma chakuthupi. Mu nkhani yoteroyo, kudzipereka nsembe kumawonekera kukhala kopambanitsa, ngakhale koseketsa. Koma kameneko ndiko kawonedwe ka “munthu wachibadwidwe,” osati kawonedwe ka “munthu wauzimu.”
11. Nchiyani chomwe chikanakhala njira yosalinganizika kaamba ka Nowa, ndipo ndimotani momwe timakhalira ndi moyo wolinganizika lerolino?
11 Munthu wauzimu ali uyo amene amawona zinthu kupyolera m’maso a chikhulupiriro. Iye amawona zinthu kuchokera ku kawonedwe ka Mulungu. Lingalirani Nowa. Kodi iye akanakhala wolinganizika ngati, pambuyo pa kuphunzira za chifuno cha Mulungu cha kuwononga dziko ndi chigumula, anawononga nthaŵi yake kumanga nyumba yaikulu ndi yabwinopo ndi kupeza chuma chakuthupi chochulukira? Ndithudi ayi! Chingalawa chinali chisungiko chake chowona. Kwa Nowa, kukhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka kunaphatikizapo kupereka chisamaliro chokwanira ku kumanga chingalawa ndi kukhala “mlaliki wa chilungamo,” mosasamala kanthu za kusekedwa ndi ‘anthu achibadwidwe’ opanda chikhulupiriro. (2 Petro 2:5; Mateyu 24:37-39) Mofananamo, popeza kuti tawunikiridwa ponena za kuyandikira kwa mapeto a dziko, njira yokha yolinganizika ya moyo kaamba ka ife iri kusumika chisamaliro chathu pa kuchita chifuniro cha Mulungu ndi kulengeza mbiri yabwino, ngakhale kuti chimenecho chingaphatikize chimene ambiri amawona kukhala kupereka nsembe yotchedwa njira yachibadwa ya moyo.—1 Yohane 2:17.
Yesu Anatiphunzitsa Ife Mmene Tingachitire
12. (a) Nchiyani chomwe Yesu ananena kuti tikayenera kuleka kuchita, ndipo nchiyani chomwe tiyenera kuchita m’malomwake? (b) Nchifukwa ninji kusintha kumeneku kwa chifuno kuli kofunikira?
12 Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anapereka uphungu wabwino wa kukhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka. Iye ananena kuti: “[Lekani, kudzikundikira, NW] nokha chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziwononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba.” Yesu anagwiritsira ntchito liwu lakuti “lekani” chifukwa chakuti anthu kaŵirikaŵiri amangopitirizabe “kukundika” zinthu zakuthupi kaamba ka iwo eni. Koma munthu yemwe wakhala wophunzira wa Yesu sangamachite tero mpang’ono pomwe. Moyo wake uyenera kukhala ndi chifuno chosiyana, monga momwe zasonyezedwera ndi lamulo lotsatira la Yesu lakuti: “Koma mudzikundikire nokha chuma m’mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba.” Akumapereka chifukwa chimene kusintha kumeneku kwa chifuno kuliri kufunika, Yesu ananena kuti: “Pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.”—Mateyu 6:19-21.
13. Ngati muti mukundike chuma m’mwamba, nchiyani chomwe muyenera kukhala okhutiritsidwa nacho?
13 Chuma chanu ndi chimene mumalingalira mowonadi kukhala chofunika. Kodi zinthu zakuthupi ziri chuma chanu? Kapena kodi kuli kuyeretsa kwa dzina la Yehova Mulungu ndi mphoto yake yolonjezedwa? Kuti muthere nthaŵi yanu kukundika chuma m’mwamba m’malo mwa pa dziko lapansi, inu muyenera kukhala wokhutiritsidwa kotheratu za chenicheni cha Ufumu. Dziko latsopano liyenera kukhala lenileni chotero kwa inu kotero kuti mungaliwone ilo m’diso lanu la m’malingaliro ndi kudziwona inu eni muli mmenemo kugwira ntchito kulinga ku kukwaniritsidwa kwa zifuno za Yehova kaamba ka dziko lapansi. Mofanana ndi Mose, inu muyenera ‘kuwona Uyo amene ali wosawoneka’ ndi kukhala wokhutiritsidwa mwamphamvu kuti ‘iye adzapereka mphoto kwa awo omufunafuna.’—Ahebri 11:6, 27.
14. Nchiyani chomwe chidzakhala chotulukapo ngati mitima yathu izikidwa pa zinthu zakuthupi?
14 Koma bwanji ngati mtima wanu, womwe umaphatikizapo zikhumbo zanu ndi chikondi, uli wozikika pa chuma chakuthupi? Baibulo limanena kuti: “Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.” Kulondola zinthu zakuthupi zimene ndalama zingagule sikumapereka konse chikhutiritso chowona chosatha. (1 Timoteo 6:10; Mlaliki 5:10) Koma changozi kwenikweni kuposa zonse, chikondi cha pa ndalama ndi zinthu zakuthupi chidzawononga unansi wanthu ndi Mulungu, yemwe amatiyembekezera ife kumutumikira iye ndi “mtima wangwiro.”—1 Mbiri 28:9.
15. (a) Ndi fanizo lotani limene Yesu anapereka ponena za diso? (b) Ponse paŵiri m’lingaliro lakuthupi ndi lauzimu, ndimotani mmene munthu amasungirira diso la kumodzi? (c) Ngati diso lathu liri la kumodzi, ndimotani mmene kawonedwe kathu kauzimu kadzakhalira konga kaja ka atumwi atatu a Yesu?
15 Kuti atithandize ife kupeŵa msampha wa kukondetsa zinthu zakuthupi, Yesu anapereka mafanizo aŵiri. Choyamba, iye ananena kuti: “Diso ndilo nyali ya thupi; chifukwa chake ngati diso lako liri la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowalitsidwa. Koma ngati diso lako liri loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa.” (Mateyu 6:22, 23) M’lingaliro lakuthupi, diso la “kumodzi” ndi limene liri m’kayang’anidwe, kupereka zithunzithunzi zowonekera bwino ku malingaliro. Diso losayang’ana bwino limapereka zithunzithunzi zosokonezeka ndi za chizimezime. Mofananamo, diso lauzimu uko ndiko kuti “la kumodzi,” kapena lokhala m’kayang’anidwe, limapereka chithunzithunzi chowonekera bwino cha Ufumu wa Mulungu, osati cha chizimezime, chithunzithunzi chosawoneka bwino chomwe chimapangitsa dziko latsopano kuwoneka ngati nthano chabe kapena nthanthi. Ngati diso lanu lauzimu liri m’kayang’anidwe, dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu lidzakhala lenileni kwa inu monga mmene Ufumu unaliri kwa atumwi atatu omwe anapatsidwa mwaŵi wa kuwona kawonekedwe kake m’masomphenya ozizwitsa a kusandulika kwa Yesu.—Mateyu 16:28–17:9; Yohane 1:14; 2 Petro 1:16-19.
16. M’fanizo lachiŵiri, ndimotani mmene Yesu anasonyezera kufunika kaamba ka umodzi wa chifuno?
16 Yesu anapereka fanizo lachiŵiri. “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye aŵiri,” iye anatero, “pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina.” Kubweretsa nsongayo m’lingaliro, iye anagogomezeranso kufunika kwa kusonyeza umodzi wa chifuno, akumanena kuti: “Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.” (Mateyu 6:24) Chimenecho mwa chokha sichingagwire ntchito. Chotero Yesu anapitirizabe kunena kuti: “Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhaŵa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzabvala, . . . Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa kumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo.”—Mateyu 6:25-32.
17. (a) Ndi nsonga yotani yomwe Yesu anali kupanga ndi malangizo ake okhudza zinthu zakuthupi? (b) Nchiyani chomwe Yesu pano anali kugogomezera, ndipo nchiyani chomwe kukhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka kumaphatikiza?
17 Yesu sanatanthauze kuti atsatiri ake alekere kupereka zofunikira zakuthupi ku mwaŵi kapena kuti iwo akayenera kukhala aulesi ndi kukana kugwira ntchito ndi cholinga chofuna kupereka zofunika kwa iwo eni ndi mabanja awo. (1 Timoteo 5:8) Ayi, koma nsonga iri yakuti zinthu zakuthupi zimenezi zolondoledwa mofunitsitsa ndi mitundu siziyenera kutenga malo oyamba. M’malomwake, monga momwe Yesu analangizira: “Pitirizani, kenaka, kufunafuna choyamba ufumu ndi chilungamo chake, ndipo zinthu zina zonsezi zidzawonjezeredwa kwa inu.” (Mateyu 6:33, NW) Chotero Yesu pano anali kulankhula ponena za zonulirapo m’moyo ndipo anali kugogomezera uchabe wa kulondola zinthu zakuthupi. Kukhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka kumaphatikizapo kulunjikitsa maso athu mwa umodzi pa zikondwerero za Ufumu, kupanga chinthu china chirichonse kukhala chachiŵiri.
Chitsanzo cha Yesu ndi Ena
18. Ndimotani mmeme Yesu anakhazikitsira chitsanzo kaamba ka ife?
18 Pamene anali kulimbikitsa Akristu “kutaya cholemetsa chirichonse ndi chimoli [la kusoweka kapena kutayikiridwa kwa chikhulupiriro] limangotizinga,” Paulo analimbikitsa kuti: “Tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera Woyambira ndi Womaliza wa Chikhulupiriro chathu, Yesu.” (Ahebri 12:1, 2) Yesu anali wodzipereka kotheratu chotero ku zikondwerero za Ufumu kotero kuti mkhalidwe wake unali monga momwe iye analongosolera kuti: “Ankhandwe ali nazo nkhwimba zawo, ndi mbalame za m’mlengalenga zisa zawo, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu wake.” (Mateyu 8:20) Pa nthaŵi imodzimodziyo, Yesu sanali wodzimana mopambanitsa. Malemba amasonyeza kuti iye anasangalala ndi zakudya zabwino ndi zovala, komabe chonulirapo chake chachikulu m’moyo chinali kukwaniritsa utumiki wake. Chotero Yesu anakhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka.—Luka 5:29; Yohane 19:23, 24.
19, 20. (a) Ndi chitsanzo chotani chimene Paulo anakhazikitsa ponena za zinthu zakuthupi? (b) Ndi phunziro lotani limene ambiri aphunzira lerolino, ndipo ndimotani mmene iwo amadzimverera ponena za njira yawo ya moyo?
19 Mtumwi Paulo nayenso anali ndi zoyambirira zake m’ndandanda yabwino. Iye analongosola kuti: “Sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni uthenga wabwino.” (Machitidwe 20:24) Inde, kuti akwaniritse utumiki wofunika koposawo, Paulo anali wokhutira ndi zofunikira zokha koma anali wosangalatsidwa kukondwera ndi zochulukira za kamodzikamodzi. Iye analemba kuti: “Konseko ndi m’zinthu zonse ndaloŵa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusoŵa.”—Afilipi 4:12.
20 M’chenicheni anthu makumi a zikwi aphunzira phunziro lofananalo lerolino. Ambiri a iwo ali atumiki a nthaŵi zonse a Mboni za Yehova, kuphatikizapo amishonale, apainiya, oyang’anira oyendayenda, ndi aja otumikira pa malikulu a mitundu yonse a gulu ndi maofesi a nthambi. Pambuyo pa zaka zingapo za utumiki wa nthaŵi zonse, ambiri amanena kuti: “Ngati ndikanafunikira kuzichitanso, sindikanachita china chirichonse chosiyanako.”
Madalitso Omwe Mungasangalale Nawo
21, 22. (a) Ndi mphoto zotani zomwe zikusangalalidwa ngakhale tsopano pomwe tikukhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka? (b) Ndi madalitso a mtsogolo otani omwe mungasangalale nawo?
21 Pamene kuli kwakuti kutsogoza moyo wolinganizika, wopepuka kumaloŵetsamo kudzipereka nsembe, madalitso ndi zisangalalo ziri zosayerekezeka. Inu mwakutero mudzakhala ndi nthaŵi yowonjezereka kupititsa patsogolo zikondwerero za Ufumu ndi mwaŵi wokulira m’kupeza okondwerera ndi kuwaphunzitsa iwo ponena za zifuno za Mulungu. Kukhutiritsa kowona ndi kukwanira kudzakhala kwanu, kuphatikizapo mtendere wa maganizo ndi chitsimikiziro chakuti mukukondweretsa Yehova Mulungu. Chimenecho chiri mphoto yomwe mungasangalale nayo ngakhale tsopano.—Afilipi 4:6, 7.
22 Koma madalitso a mtsogolo adzakhala okulira koposa, kupangitsa kudzipereka nsembe konse kwa tsopano lino komwe mungapange kukhala kutalitali m’kuyerekeza. Madalitso a Yehova amaphatikizapo “moyo womka muyaya.” Inde, amenewa angakhale madalitso anu—moyo wamuyaya m’chimwemwe m’dziko latsopano lolungama la Yehova. Khalani ndi moyo wolinganizika, wopepuka, kusalola zinthu za dziko lino kusakulinganizani inu. Kumbukirani kuti Mulungu adzapereka kwa inu zokhumba za mtima wanu.—Salmo 21:3, 4; 37:4; 133:3.
Mafunso kaamba ka Kubwereramo
◻ Ndi zitsanzo zotani ndi mafanizo zomwe mwawona kuti zingakuthandizeni kukhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka?
◻ Ndimotani mmene kukhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka kungatichinjirizire?
◻ Ngati diso lathu lauzimu liri lopepuka, kodi ichi chidzatanthauzanji kwa ife?
◻ Ndimotani mmene Yesu anatiphunzitsira kukhala ndi moyo wopepuka?
◻ Ndi ati omwe ali madalitso a kukhala ndi moyo wolinganizika, wopepuka?