Chitirani Ena Ulemu
“Mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.” —AROMA 12:10.
1, 2. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisonyeze kuti ndife odzichepetsa? (b) Kodi Baibulo kaŵirikaŵiri limawagwiritsa ntchito motani mawuwo “ulemu,” ndipo ndi anthu ati amene savutika kusonyeza ulemu?
NKHANI yathu yoyambayo inagogomeza uphungu wa m’Mawu a Mulungu wakuti: “Nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.” (1 Petro 5:5) Njira imodzi imene tingavalire kudzichepetsa ndiyo kuchitira ena ulemu.
2 Mawu akuti “ulemu” amatchulidwatchulidwa m’Baibulo pofuna kusonyeza kulemekeza, ndi kuganizirana kumene tiyenera kuchitira anthu ena. Timachitira ena ulemu mwa kuwasonyeza chifundo, kuwalemekeza monga anthu, kumvetsera malingaliro awo, kukhala wofunitsitsa kuchita zinthu zimene atipempha ngati tingathe kuzichita. Nthaŵi zambiri anthu odzichepetsa savutika kuchita zimenezi. Komabe, onyada angavutike kwambiri kuchitira ena ulemu weniweni ndipo m’malo mwake angamayese kupeza chiyanjo ndi mapindu mwa kusyasyalika.
Yehova Amachitira Anthu Ulemu
3, 4. Kodi Yehova anachitira ulemu Abrahamu motani, ndipo chifukwa chiyani?
3 Yehova iyemwini amapereka chitsanzo cha kuchitira ena ulemu. Analenga anthu ndi ufulu wakudzisankhira ndipo sawatenga ngati zinthu zosaganiza. (1 Petro 2:16) Mwachitsanzo, atauza Abrahamu kuti Sodomu adzawonongedwa chifukwa cha kuipa kwake, Abrahamu anafunsa kuti: “Kodi mudzawononga olungama pamodzi ndi oipa? Kapena alipo olungama makumi asanu mkati mwa mudzi; kodi mudzawononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo?” Yehova anayankha kuti sadzawononga mudziwo ngati muli anthu 50 olungama. Kenako Abrahamu anapitiriza kuchonderera modzichepetsa. Bwanji ngati mutakhala anthu 45 okha? 40 okha? 30 okha? 20 okha? 10 okha? Yehova anatsimikizira Abrahamu kuti sadzawononga Sodomu mutangopezeka anthu khumi okha olungama.—Genesis 18:20-33.
4 Yehova anadziŵa kuti m’Sodomu mulibe anthu khumi olungama, koma anapatsa Abrahamu ulemu mwa kumvetsera malingaliro ake ndi kuyankhula naye momulemekeza. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Abrahamu “anakhulupirira Yehova, ndipo kunayesedwa kwa iye chilungamo.” Abrahamu anatchedwa “bwenzi la Mulungu.” (Genesis 15:6; Yakobo 2:23) Ndiponso, Yehova anadziŵa kuti Abrahamu amachitira ena ulemu. Abusa a Abrahamuyo ndi a mphwake Loti atakanganirana malo odyetsera ziŵeto zawo, Abrahamu anapatsa ulemu Loti mwa kumuuza kuti ayambe ndiye kusankha dera limene akufuna. Loti anasankha dera limene analiona kukhala labwino koposa, ndipo Abrahamu anapita kwina.—Genesis 13:5-11.
5. Kodi Yehova anachitira Loti ulemu motani?
5 Yehova nayenso anachitira Loti wolungamayo ulemu. Asanawononge Sodomu, anauza Loti kuti athaŵire kumapiri. Koma Loti ananena kuti safuna kupita kumeneko; anasankha kuthaŵira ku Zoari, ngakhale kuti mudzi umenewo unali m’dera loyenera kuwonongedwalo. Yehova anauza Loti kuti: “Taona, ndikuvomereza iwe pamenepanso kuti sindidzawononga mudzi uwu umene wandiuza.” Yehova anachitira Loti wokhulupirikayo ulemu mwa kuchita zimene anapempha.—Genesis 19:15-22; 2 Petro 2:6-9.
6. Kodi Yehova anachitira Mose ulemu motani?
6 Yehova atatumizanso Mose ku Igupto kukatulutsa anthu Ake mu ukapolo ndi kuyankhula ndi Farao kuti alole anthu a Mulungu kupita, Mose anati: “Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosoŵa ponena.” Yehova anatsimikizira Mose kuti: “Ine ndidzakhala mkamwa mwako, ndi kukuphunzitsa chomwe ukalankhule.” Koma Mose anali wosafunitsitsabe. Pamenepo Yehova analimbikitsa Mose ndi kulinganiza kuti mbale wake, Aroni, apite naye monga wom’lankhulira.—Eksodo 4:10-16.
7. N’chifukwa chiyani Yehova anali wofunitsitsa kulemekeza ena?
7 Pazochitika zonsezi, Yehova anasonyeza kuti ndi wofunitsitsa kuchitira ena ulemu, makamaka atumiki ake. Ngakhale kuti zimene anthuwo anapempha mwina zinali zosiyana ndi zimene Yehova ankafuna kuchita poyamba, iye anamva zopempha zawo ndi kuwalola kuchita zimene apempha malinga ngati sizinali kutsutsana ndi chifuno chake.
Yesu Anachitira Ena Ulemu
8. Kodi Yesu anachitira motani ulemu mkazi yemwe ankadwala kwambiri?
8 Yesu anatsanzira Yehova pochitira ena ulemu. Nthaŵi inayake ali pakati pa namtindi wa anthu, panalinso mkazi wina amene anadwala nthenda ya kukha magazi kwa zaka 12. Madokotala analephera kum’chiritsa. Malinga ndi mwambo wa m’Chilamulo cha Mose, iye anali wodetsedwa ndipo sanayenere kupezeka pamalo amenewo. Anapita kumbuyo kwa Yesu nagwira chovala chake, ndi kuchiritsidwa. Yesu sanangotsatira Chilamulo mopanda chifundo ndi kum’dzudzula pa zimene anachita. M’malo mwake, podziŵa vuto lake, anam’patsa ulemu, nati: “Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wochira chivutiko chako.”—Marko 5:25-34; Levitiko 15:25-27.
9. Kodi Yesu anachitira motani ulemu munthu Wakunja?
9 Panthaŵi inayake, mkazi wa ku Kanani anati kwa Yesu: “Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiŵanda.” Podziŵa kuti anatumizidwa ku mtundu wa Israyeli ndipo osati kwa Akunja, Yesu anati: “Sichabwino kutenga mkate wa ana [a Israyeli], ndi kuuponyera tiagalu [Akunja].” Mkaziyo anayankha kuti: “Pakutinso tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye awo.” Kenako Yesu anati: “Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira.” Mwana wake wamkazi anachira. Yesu anachitira ulemu Wakunja ameneyu chifukwa cha chikhulupiriro chake. Ngakhale pamene anagwiritsa ntchito mawu akuti “tiagalu,” m’malo motchula mimbulu, anafeŵetsa nkhaniyo ndipo anasonyeza chifundo chake.—Mateyu 15:21-28.
10. Kodi Yesu anaphunzitsa ophunzira ake phunziro lalikulu lotani, ndipo n’chifukwa chiyani linali lofunika?
10 Yesu anapitirizabe kuphunzitsa ophunzira ake za kufunika kwa kudzichepetsa ndi kuchitira ena ulemu chifukwa chakuti iwo anali adakali ndi vuto lofuna kukhala patsogolo pa onse. Panthaŵi inayake atakanganakangana, Yesu anawafunsa kuti: “Munalikutsutsana ninji?” Iwo sanayankhe, popeza “anatsutsana wina ndi mnzake . . . kuti wamkulu ndani?” (Marko 9:33, 34) Ngakhale pausiku woti Yesu akufa maŵa, “kunakhala kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkulu.” (Luka 22:24) Chotero pochita Paskha, Yesu “anathira madzi m’nsambidwe, nayamba kusambitsa mapazi a akuphunzira ake.” Linali phunziro lalikulu bwanji! Yesu anali Mwana wa Mulungu, wachiŵiri kwa Yehova yekha m’chilengedwe chonse. Komabe, anaphunzitsa ophunzira ake phunziro lochitira ena ulemu mwa kuwasambitsa mapazi. Iye anati: “Ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.”—Yohane 13:5-15.
Paulo Anachitira Ena Ulemu
11, 12. Kodi Paulo anaphunziranji atakhala Mkristu, ndipo anagwiritsa ntchito motani phunziro limeneli pa Filemoni?
11 Monga wotsanza Kristu, mtumwi Paulo anachitira ena ulemu. (1 Akorinto 11:1) Iye anati: “Kapena sitinakhala ofuna ulemerero wa kwa anthu . . . Komatu tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga mmene mlezi afukata ana ake a iye yekha.” (1 Atesalonika 2:6, 7) Mlezi amasamalira ana ake aang’ono. Paulo atakhala Mkristu, anaphunzira kukhala wodzichepetsa ndipo anapatsa Akristu anzake ulemu mwa kuchita nawo zinthu mofatsa. Pochita zimenezo, analemekezanso ufulu wawo wa kusankha, monga momwe chochitika china chomwe chinachitika pamene anali wandende ku Roma chinasonyezera.
12 Kapolo wotchedwa Onesimo yemwe anathaŵa kwa mbuyake analabadira chiphunzitso cha Paulo. Iye anakhala Mkristu komanso bwenzi la Paulo. Mbuye wa kapoloyo anali Filemoni, Mkristunso yemwe ankakhala ku Asia Minor. M’kalata yake yopita kwa Filemoni, Paulo analemba za kufunika kwa Onesimo kwa iye, nati: “Ameneyo ndikadafuna ine kum’sunga akhale nane.” Koma Paulo anam’bweza Onesimo kwa Filemoni, popeza analemba kuti: “Wopanda kudziŵa mtima wako sindinafuna kuchita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwaufulu.” Paulo sanagwiritse ntchito ulamuliro wake monga mtumwi, koma analemekeza Filemoni mwa kusam’pempha kuti Onesimo akhalebe naye ku Roma. Komanso, Paulo analimbikitsa Filemoni kuti achitire Onesimo ulemu, kumuona monga “woposa kapolo, mbale wokondedwa.”—Filemoni 13-16.
Kuchitira Ena Ulemu m’Tsiku Lathu
13. Kodi Aroma 12:10 amatiuza kuchita chiyani?
13 Mawu a Mulungu amalangiza kuti: “Mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.” (Aroma 12:10) Zimenezi zikutanthauza kuti sitiyenera kudikira kuti ena ayambe kutichitira ulemu, koma ifeyo tiyenera kuyamba kuwachitira ulemu. “Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.” (1 Akorinto 10:24; 1 Petro 3:8, 9) Ndiye chifukwa chake atumiki a Yehova amafunitsitsa kuchitira ulemu apabanja pawo, Akristu anzawo mumpingo, ngakhalenso anthu osakhala a mumpingo.
14. Kodi mwamuna ndi mkazi wake amachitirana bwanji ulemu?
14 Baibulo limati: “Mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna.” (1 Akorinto 11:3) Yehova amalamula mwamuna kuchitira mkazi wake ulemu monga momwe Kristu anachitira ndi mpingo. Pa 1 Petro 3:7, mwamuna akulangizidwa kuchitira mkazi wake “ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu.” Angachite zimenezi mwa kusonyeza kuti amamvetseradi ndiponso mwa kuchitapo kanthu pa malingaliro a mkazi wake. (Genesis 21:12) Angatsatire malingaliro ake ngati palibe cholakwika chilichonse, ndipo amam’chitira zinthu ndi kukhala naye mokoma mtima. Nayenso “mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.” (Aefeso 5:33) Amamvetsera mwamuna wakeyo, sayesa kuti nthaŵi zonse azingochita zokomera iye, sam’nyozera kapena kum’peza zifukwa nthaŵi zonse. Amadzichepetsa mwa kusayesa kulamulira mwamuna wake, ngakhale ngati zinthu zina amatha kuzichita bwino kuposa mwamuna wakeyo.
15. Kodi achikulire ayenera kulingaliridwa motani, ndipo iwo ayenera kutani?
15 Mumpingo wachikristu, muli ena oyenereradi ulemu, monga ngati anthu achikulire. “Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba.” (Levitiko 19:32) Ziyeneradi kutero makamaka kwa awo amene atumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri chifukwa chakuti “imvi ndiyo kolona wa ulemu, i[ta]pezedwa m’njira yachilungamo.” (Miyambo 16:31) Oyang’anira ayenera kupereka chitsanzo mwa kusonyeza ulemu woyenerera kwa Akristu anzawo amene ali aakulu kwa iwo. Inde, achikulire nawonso ayenera kusonyeza ulemu kwa abale aang’ono msinkhu, makamaka amene ali ndi udindo woŵeta gulu la nkhosa.—1 Petro 5:2, 3.
16. Kodi makolo ndi ana amachitirana ulemu motani?
16 Ana ayenera kulemekeza makolo awo: “Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi n’chabwino. Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko.” Nawonso makolo ayenera kuchitira ana awo ulemu, popeza amauzidwa kuti ‘asakwiyitse ana awo; komatu awalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.’—Aefeso 6:1-4; Eksodo 20:12.
17. Kodi ndani amene ayenera kulandira “ulemu woŵirikiza”?
17 Enanso oyenera kuwachitira ulemu ndi awo amene amalimbikira kutumikira mpingo: “Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu woŵirikiza, makamaka iwo akuchititsa m’mawu ndi m’chiphunzitso.” (1 Timoteo 5:17) Njira imodzi imene tingawachitire ulemu ndiyo mwa kuchita zimene Ahebri 13:17 amanena kuti: “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere.”
18. Kodi tiyenera kuchitanji kwa anthu a kunja kwa mpingo?
18 Kodi tiyenera kuchitira ulemu anthu a kunja kwa mpingo? Inde. Mwachitsanzo, timalangizidwa kuti: “Anthu onse amvere maulamuliro aakulu.” (Aroma 13:1) Ameneŵa ndiwo olamulira a dziko amene Yehova walola kulamulira kufikira pamene Ufumu wake utadzaloŵe m’malo mwawo. (Danieli 2:44) Chotero ‘timapereka kwa anthu onse mangaŵa awo; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa; kuopa kwa eni ake a kuwaopa; ulemu kwa eni ake a ulemu.’ (Aroma 13:7) Tiyenera ‘kuchitira ulemu anthu onse.’—1 Petro 2:17.
19. Kodi ndi motani mmene ‘tingachitire ena chokoma’ ndi kuwachitira ulemu?
19 Pamene zili zoona kuti tiyenera kuchitira ulemu ngakhale anthu a kunja kwa mpingo, taonani zimene Mawu a Mulungu amagogomeza: “Monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) Inde, njira yabwino kwambiri imene ‘tingachitire chokoma’ kwa ena ndiyo kukulitsa ndi kukhutiritsa zosoŵa zawo zauzimu. (Mateyu 5:3) Tingachite zimenezi mwa kumvera chikumbutso cha mtumwi Paulochi: “Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.” Pamene mwanzeru tichitira umboni pa mpata uliwonse, ‘kukwaniritsa utumiki wathu,’ ndiye kuti tikuchita zokoma kwa onse ndi kuwachitiranso ulemu.—2 Timoteo 2:15; 4:5.
Kupatsa Ulemu Yehova
20. N’chiyani chinachitikira Farao ndi asilikali ake, ndipo n’chifukwa chiyani?
20 Yehova amalemekeza zolengedwa zake. Chotero n’kwanzeru kuti ifenso tiyenera kum’lemekeza. (Miyambo 3:9; Chivumbulutso 4:11) Mawu a Yehova amatinso: “Amene andilemekeza ine, inenso ndidzawalemekeza iwoŵa, ndipo akundipeputsa ine, adzapeputsidwa.” (1 Samueli 2:30) Farao wa Igupto atauzidwa kuti alole anthu a Mulungu kupita, anayankha mwamwano kuti: “Yehova ndani, kuti ndimvere mawu ake?” (Eksodo 5:2) Farao atatumiza asilikali ake kuti akawononge Aisrayeli, Yehova anapatula madzi a Nyanja Yofiira kuti Aisrayeli adutse. Koma Aigupto atawatsatira, Yehova anapangitsa madziwo kubwerera m’malo mwake. “Magareta a Farao ndi nkhondo yake [Yehova] anawaponya m’nyanja.” (Eksodo 14:26-28; 15:4) Chotero popeza kuti Farao anakana monyada kulemekeza Yehova, iye anawonongedwa.—Salmo 136:15.
21. N’chifukwa chiyani Yehova anatsutsa Belisazara, ndipo n’chiyani chinamuchitikira?
21 Mfumu Belisazara ya Babulo anakana kulemekeza Yehova. Paphwando limene panali kumwa kwadzaoneni, iye ananyoza Yehova mwa kumwera vinyo m’zotengera zopatulika zagolide ndi zasiliva zimene zinatengedwa m’kachisi ku Yerusalemu. Nthaŵi imodzimodziyo iye anali kutamanda milungu yake yachikunja. Koma Danieli mtumiki wa Yehova anamuuza kuti: “Simunadzichepetsa m’mtima mwanu, . . . koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba.” Usiku womwewo Belisazara anaphedwa, ndipo ufumu wake unatengedwa ndi anthu ena.—Danieli 5:22-31.
22. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anakwiyira atsogoleri a Israyeli ndi anthu awo? (b) Kodi ndani amene Yehova anayanja, ndipo panatsatira chiyani?
22 M’zaka za zana loyamba C.E., Mfumu Herode anali kuyankhula pamsonkhano, ndipo anthu anafuula kuti: “Ndiwo mawu a Mulungu, si a munthu ayi.” Mfumu yonyadayo sinawatsutse koma inafuna ulemererowo. Pamenepo, “mngelo wa Ambuye anam’kantha, chifukwa sanam’patsa Mulungu ulemerero.” (Machitidwe 12:21-23) Herode anadzipatsa ulemerero, sanapatse Yehova, ndipo anaphedwa. Atsogoleri achipembedzo a panthaŵiyo ananyoza Mulungu mwa kukonza chiwembu choti aphe Mwana wake, Yesu. Olamulira ena ankadziŵa kuti Yesu akuphunzitsa choonadi koma sanam’tsatire, “pakuti anakonda ulemerero wa anthu koposa ulemerero wa Mulungu.” (Yohane 11:47-53; 12:42, 43) Mtundu wonsewo sunachitire ulemu Yehova kapena Woimira wake yemwe anamuikayo, Yesu. Chotero, Yehova sanapitirize kuwalemekeza ndipo anawasiya ndi kusiyanso kachisi wawo kuti awonongedwe. Koma anasunga amoyo awo amene anachitira iye ndi Mwana wake ulemu.—Mateyu 23:38; Luka 21:20-22.
23. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tidzakhale m’dziko latsopano la Mulungu? (Salmo 37:9-11; Mateyu 5:5)
23 Onse amene akufuna kukhala m’dziko latsopano la Mulungu dongosolo lilipoli litawonongedwa ayenera kuchitira ulemu Mulungu ndi Mwana wake, Kristu Yesu, ndi kuwamvera. (Yohane 5:22, 23; Afilipi 2:9-11) Awo amene sasonyeza ulemu umenewu “adzalikhidwa m’dziko.” Koma owongoka mtima amene amachitira ulemu Mulungu ndi Kristu ndi kuwamvera “adzakhala m’dziko.”—Miyambo 2:21, 22.
Kubwereza
◻ Kodi kuchitira ena ulemu kumatanthauzanji, ndipo Yehova anachita motani zimenezi?
◻ Ndi motani mmene Yesu ndi Paulo anachitira ena ulemu?
◻ Kodi ndani ali oyenerera kuwachitira ulemu m’tsiku lathu?
◻ N’chifukwa chiyani tiyenera kuchitira ulemu Yehova ndi Yesu?
[Chithunzi patsamba 17]
Yehova anachitira Abrahamu ulemu mwa kumvera pempho lake
[Chithunzi patsamba 18]
M’maukwati abwino, amuna ndi akazi awo amachitirana ulemu