Kodi Mumakumbukira?
Kodi mwasangalala ndi kuŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Chabwino, onani ngati mukhoza kuyankha mafunso otsatirawa:
◻ Kodi abusa auzimu ali ndi maziko otani akukhala oyamba kufikira anthu ena ochotsedwa kuwona ngati angasonkhezeredwe kulapa?
Ngakhale pamene Aisrayeli anali muukapolo ndipo osalapa, Yehova, mofanana ndi mbusa, anayamba kuwafunafuna, mwakuwatumizira aneneri. Abusa Achikristu ali okondweretsedwa kuthandiza alionse olapa amene angakhale ngati nkhosa yosokera. (Yerekezerani ndi Luka 15:4-7.)—4/15, masamba 21-3.
◻ Kodi ndimotani mmene fanizo la Yesu la mwana woloŵerera limasonyezera mmene malingaliro athu ndi zochita ziyenera kukhalira pamene winawake wabwezeretsedwa mumpingo Wachikristu? (Luka 15:22-32)
Chonulirapo chathu chiyenera kukhala chakutsanzira tateyo, yemwe anasonyeza chimwemwe pamene mwana wake woloŵererayo anabwerera. Chifukwa chake, tiyenera kulankhula momasuka ndi mbale wobwezeretsedwayo ndi kumlimbikitsa tsopano kupita patsogolo m’chowonadi.—4/15, tsamba 25.
◻ Kodi ndimalangizo othandiza otani amene angatsatiridwe kuti tipeŵe kukhala mnkhole wa upandu?
Pamene kuli kothekera, peŵani kukhala m’madera aupandu nthaŵi yausiku. Bisani zokometsera zanu, ndipo nyamulirani ziŵiya zonga ngati kamera m’chola chogulira zinthu. Chenjerani ndi kuyenda pafupi ndi m’mphepete mwa msewu mwenimweni, makamaka ngati mwanyamula brifikesi kapena chola chakumanja. (Onani Miyambo 3:21-23.)—5/1, masamba 5-6.
◻ Kodi nchifukwa ninji ulosi wa pa Zefaniya 2:3 umati: “Kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova”?
Chifukwa chakuti kupulumutsidwira ku moyo kumadalira pa kukhulupirika ndi chipiriro. (Mateyu 24:13) Nchifukwa chake, awo okha amene amamamatira ku miyezo yolungama ya Mulungu napitirizabe kulankhula chinenero choyera ndiwo adzabisika patsiku la mkwiyo wa Yehova. (Zefaniya 2:1, 2)—5/1, tsamba 14.
◻ Kodi nchiyani chimene chimaloŵetsedwamo m’kuika Mulungu patsogolo m’moyo wabanja?
Makolo ndi ana ayenera kulambira Yehova ndi kukwaniritsa miyezo yake yondandalikidwa m’Baibulo.—5/15, tsamba 5.
◻ Kodi Nchifukwa ninji Yehova samalanga ochimwa panthaŵi yomweyo?
Chifukwa chimodzi nchakuti dzina la Mulungu liyenera kudziŵikitsidwa padziko lonse lapansi. (Yerekezerani ndi Aroma 9:17.) Chifukwa china ndicho chakulola nthaŵi yothetsera nkhani za ulamuliro wa Mulungu ndi umphumphu wa anthu, zomwe zinabuka pachipanduko m’Edene. Ndiponso, kuleza mtima kwa Mulungu kumapereka mpata kwa ochimwa kuti alape ndi kuwongolera njira zawo. (2 Petro 3:9)—5/15, masamba 11-12.
◻ Kodi ndimaumboni otani amene amatsimikiziritsa kuti Baibulo liri ndi chiyambi choposa chaumunthu?
Baibulo linalembedwa ndi olemba osiyanasiyana pafupifupi 40, ochokera kumbali zosiyanasiyana za moyo ndipo anakhala ndi moyo m’nyengo yoposa zaka 1,600; komabe olemba onseŵa anatsatira mutu wankhani waukulu umodzi. Kugwirizana kwamkati kumeneku kwa Baibulo kukakhala kosatheka ngati kunali kwamwaŵi kapena kotsogozedwa ndi anthu.—6/1, tsamba 5.
◻ Kodi nchochitika ndi ntchito yachilendo yotani, zoloseredwa pa Yesaya 28:21, zimene Yehova adzachita m’tsiku lathu?
Chenjezo la pa Chibvumbulutso 17:16 limasonyeza kuti mabwenzi andale zadziko a Babulo Wamkulu adzamuukira tsiku lina. Monga chotulukapo, Chikristu Chadziko chidzawonongedwa kotheratu pamodzi ndi zipembedzo zina zonse zonyenga. Chimenechi chidzakhala chochitika ndi ntchito yachilendo ya Yehova m’tsiku lathu.—6/1, masamba 22-3.
◻ Kodi akazi Achikristu ayenera kukumbukiranji ponena za kugwiritsira ntchito zokometsera ndi zodzoladzola?
Baibulo silimaletsa kugwiritsira ntchito zokongoletsa zoterozo. (Eksodo 32:2, 3; Estere 2:7, 12, 15) Koma payenera kukhala kudekha. Mkazi akhoza kutsanzira masitaelo akudziko mosavuta, akumagwiritsira ntchito mopambanitsa mafuta opaka pamilomo, utoto wopaka m’masaya, kapena utoto wodetsa maso, monga momwedi anachitira Yezebeli. (2 Mafumu 9:30) Chisamaliro chiyenera kukhalapo kotero kuti zodzoladzola zisagwiritsiridwe ntchito mopambanitsa ndikuti zokometsera zisakhale zonkitsa.—6/1, masamba 30-1.
◻ Kodi ndimotani mmene Aisrayeli anapulumukira “nthenda zoipa ziri zonse za Aigupto” zimene zinali zowanda kalelo? (Deuteronomo 7:15)
Mwachiwonekere iwo anapulumuka nthenda zoterozo kwakukulukulu chifukwa cha kutsatira miyezo yapamwamba yaukhondo yolamulidwa ndi pangano Lachilamulo.—6/15, tsamba 4.
◻ Kodi nchifukwa ninji Mulungu analamula kuti anthu sayenera kudya mwazi? (Genesis 9:3, 4; Levitiko 17:10, 11; Machitidwe 15:22-29)
Moyo ndimphatso yochokera kwa Mulungu ndipo moyo wa anthu umadalira pa madzi amthupi ochirikiza moyo otchedwa mwazi. (Salmo 36:9) Mwakulemekeza mwazi monga chinthu chapadera, anthu amasonyeza kudalira kwawo Mulungu kaamba ka moyo. Chotero, chifukwa chachikulu cha lamulo la Mulungu lonena za mwazi chinali, osati kuti kudya mwazi kukakhala kwaupandu ku thanzi, koma kuti mwazi unali ndi tanthauzo lapadera kwa Mulungu.—6/15, masamba 8-9.
◻ Kodi ndimotani mmene makolo ndi achichepere Achikristu angalimbitsire kuthekera kwakuti chifukwa chokanira kuthiridwa mwazi cha wachichepere chidzalemekezedwa?
Ngakhale kuti mwalamulo sali wachikulire, wachichepere Wachikristu ayenera kukhala wokhoza kufotokoza momvekera bwino ndipo mwamphamvu chimene chiri chifukwa chake chachipembedzo chokanira kuthiridwa mwazi. Makolo angalinganize magawo akuyeseza ndi ana awo kotero kuti anawo akhale ozoloŵera kufotokoza zikhulupiriro zawozawo.—6/15, tsamba 18.
◻ Kodi ndimotani mmene akazi anadalitsidwira kwakukulu m’nthaŵi yauminisitala wa Yesu wapadziko lapansi?
Yesu anayamba ntchito yomwe inadzetsa mpumulo, chiyembekezo, ndi ulemu watsopano kwa akazi a mafuko onse. Anaphunzitsa akazi chowonadi chauzimu chozama. (Yohane 4:7, 24-26) Mkati mwa uminisitala wake, iye anavomereza kutumikiridwa ndi akazi pamene ankayendayenda m’dziko. (Marko 15:40, 41)—7/1, masamba 14-15.
◻ Kodi ndimaluso ophunzitsira otani a Yesu amene makolo apeza kukhala ogwira mtima kwa ana awo?
Makolo adzachita bwino kugwiritsira ntchito mafanizo kupangitsa chowonadi Chachikristu kukopa mitima ya ana awo achichepere, ndipo angagwiritsire ntchito mafunso olingaliridwa bwino kuti azindikire zimene ana awo okulirapo amaganizadi. (Yerekezerani ndi Mateyu 17:24-27.)—7/1, tsamba 26.
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulondola kukoma mtima kwachikondi?
Mkhalidwe wa kukoma mtima kwachikondi umatipangitsa kukondedwa ndi Mulungu ndi ena. Umapititsa patsogolo kuchereza ndipo umatipangitsa kukhala olingalira ena koposapo. Umalimbitsa maunansi mkati mwa banja ndi mpingo Wachikristu. Koposa zonse, kukoma mtima kwachikondi kumadzetsa ulemerero kwa Yehova.—7/15, tsamba 22.
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kotheka kwa Mkristu kunyengedwa m’zamayanjano? (1 Akorinto 15:33)
Munthu angawoneke kukhala waubwenzi ndi wovomerezeka, koma ngati iye sagwirizana nanu m’nkhaŵa yanu ya utumiki wa Yehova kapena sakhulupirira Baibulo, ali woyanjana naye woipa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti moyo wake ngwozikidwa pa malamulo amakhalidwe osiyana, ndipo zinthu zofunika kwambiri kwa Mkristu zingakhale zamtengo wotsika kwa iye.—7/15, tsamba 23.
◻ Kodi nchifukwa ninji Tsiku Lachiweruzo liri nthaŵi ya chiyembekezo?
Tsiku Lachiweruzo ndinyengo ya zaka chikwi. Lidzalamulidwa ndi Mulungu iye mwini ndi Mwana wake, Kristu Yesu, woikidwa ndi Mulungu kukhala Woweruza. Imeneyi idzakhala nthaŵi yakubwezeretsera anthu ku moyo wangwiro waumunthu umene Adamu anataira mbadwa zake. (1 Akorinto 15:21, 22)—8/1, masamba 5-7.