Kufesa Mbewu za Choonadi cha Ufumu
“Mamaŵa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako.”—MLALIKI 11:6.
1. Kodi Akristu akufesa mbewu m’lingaliro lotani lerolino?
ULIMI unali wofunika kwambiri kwa Ahebri akale. Ichitu n’chifukwa chake Yesu, amene anathera nthaŵi ya moyo wake wonse waumunthu m’Dziko Lolonjezedwa, ankatchulatchula nkhani za ulimi m’mafanizo ake. Mwachitsanzo, iye anayerekezera kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi kufesa mbewu. (Mateyu 13:1-9, 18-23; Luka 8:5-15) Kufikira lerolino, kaya tikukhala kuchimake kwa ulimi kapena ayi, kufesa mbewu zauzimu m’njira imeneyi ndiyo ntchito yofunika kwambiri imene Akristu akuichita.
2. Kodi ntchito yathu yolalikira n’njofunika motani, ndipo n’zinthu zina ziti zomwe zikuchitika lerolino pokwaniritsa ntchitoyi?
2 Ndi mwayitu waukulu kwabasi kutenga nawo mbali pa kufesa choonadi cha Baibulo m’nthaŵi yamapeto ino. Aroma 10:14, 15, akufotokoza bwino lomwe kufunika kwa ntchito imeneyi: “Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira? Ndipo adzalalikira bwanji ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” Kugwira ntchito yopatsidwa ndi Mulunguyi mwakhama ndiponso ndi mtima woyamikira, sikunakhalepo kofunika kwambiri chomwechi n’kale lonse. Pachifukwa chimenecho Mboni za Yehova n’zotanganidwa zedi kupanga ndi kufalitsa mabaibulo ndi mabuku othandiza pophunzira Baibulo m’zinenero 340. Kupanga ndi kufalitsa mabuku ameneŵa kumafuna antchito odzifunira oposa 18,000 kulikulu lawo ndi m’maofesi anthambi m’mayiko osiyanasiyana. Ndipo Mboni pafupifupi mamiliyoni asanu ndi imodzi padziko lonse zikutenga nawo mbali m’kufalitsa mabuku ofotokoza Baibuloŵa.
3. Kodi kufesa mbewu za choonadi cha Ufumu kukukwaniritsanji?
3 Kodi zipatso zantchito yadzaoneni imeneyi n’zotani? Monga momwe zinalili pomwe Chikristu chimayamba kumene, anthu ambiri lerolino akulandira choonadi. (Machitidwe 2:41, 46, 47) Komabe, chofunika kwambiri kuposa chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu atsopano obatizidwa n’chakuti umboni waukuluwu umathandiza kuyeretsa dzina la Yehova ndi kutsimikizira kuti iye ndiye Mulungu woona yekha. (Mateyu 6:9) Komanso, chidziŵitso cha Mawu a Mulungu chikusintha miyoyo ya anthu ambiri ndipo chingaŵatsogolere ku chipulumutso chawo.—Machitidwe 13:47.
4. Kodi atumwi anali kudera nkhaŵa motani anthu omwe anawalalikira?
4 Atumwi ankadziŵa bwino zedi kufunika kwa uthenga wabwino wopatsa moyowu, ndipotu anali kudera nkhaŵa kwambiri omwe anali kuwalalikira. Zimenezi n’zoonekeratu m’mawu a mtumwi Paulo, pamene analemba kuti: “Ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.” (1 Atesalonika 2:8) Posonyeza kudera nkhaŵa anthu kwenikweniko, Paulo ndi atumwi ena anali kutsanzira Yesu ndi angelo kumwamba, omwenso ali kalikiliki pa ntchito yopulumutsa moyoyi. Tiyeni tipende mbali zofunika kwambiri zomwe atumiki a Mulungu akumwamba ameneŵa akuchita pofesa choonadi cha Ufumu, ndipo tione mmene chitsanzo chawocho chikutilimbikitsira kukwaniritsa mbali yathu.
Yesu—Wofesa Choonadi cha Ufumu
5. Kodi ndi ntchito yofunika yotani yomwe Yesu anatanganidwa nayo pomwe anali padziko lapansi?
5 Munthu wangwiroyo Yesu, anali ndi mphamvu yakuti akanakhoza kupereka zinthu zabwino zambiri mwakuthupi kwa anthu m’nthaŵi yake. Mwachitsanzo, iye akanatha kuthetsa malingaliro ambiri olakwa m’zamankhwala a m’tsiku lake, kapena akanapititsa patsogolo nzeru za anthu m’masayansi ena ndi ena. M’malo mwake, iye anafotokoza momveka kuchiyambi kwenikweni kwa utumiki wake kuti ntchito yake inali yolalikira uthenga wabwino. (Luka 4:17-21) Ndipo cha kumapeto kwa utumiki wake, iye anafotokoza kuti: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” (Yohane 18:37) Chotero anatanganidwa zedi ndi ntchito yofesa mbewu za choonadi cha Ufumu. Kuphunzitsa anthu okhalako m’nthaŵiyo ponena za Mulungu ndi zifuno Zake kunali kofunika kwambiri kuposa maphunziro ena alionse omwe Yesu akanawapatsa.—Aroma 11:33-36.
6, 7. (a)N’lonjezo losaiŵalika liti lomwe Yesu anapereka asanakwere kumwamba, ndipo akulikwaniritsa motani? (b) Kodi kaonedwe ka Yesu ka ntchito yolalikirayi kamakukhudzani motani inuyo panokha?
6 Yesu anadzitcha Wofesa choonadi cha Ufumu. (Yohane 4:35-38) Iye anamwaza mbewu za uthenga wabwino pa mpata ulionse. Ngakhale pamene anali kufa pamtengo paja, Yesu analengeza uthenga wabwino wonena za paradaiso wam’tsogolo wa padziko lapansi. (Luka 23:43) Kuwonjezera pamenepo, chifuno chake chachikulucho chakuti uthenga wabwino ulalikidwe sichinathe chifukwa chakuti anaphedwa pamtengo wozunzirapo ayi. Iye asanakwere kumwamba, analamula atumwi kupitirizabe kufesa mbewu za choonadi cha Ufumu ndi kupanga ophunzira. Kenako Yesu anapanga lonjezo losaiŵalika. Iye anati: “Onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.”—Mateyu 28:19, 20.
7 Ndi mawu ameneŵa Yesu anadzipereka kuchirikiza, kutsogolera, ndi kuteteza ntchito yolalikira uthenga wabwino ‘masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.’ Kudzafika m’tsiku lathu lino, chidwi cha Yesu pantchito yolalikirayi chikupitirizabe. Iye ndiye Mtsogoleri wathu, woyang’anira ntchito yofesa choonadi cha Ufumu. (Mateyu 23:10) Monga Mutu wa mpingo wachikristu, ali ndi udindo pamaso pa Yehova wa ntchito yapadziko lonse imeneyi.—Aefeso 1:22, 23; Akolose 1:18.
Angelo Akulengeza Uthenga Wabwino
8, 9. (a)Kodi angelo asonyeza motani chidwi chenicheni pa zochita za anthu? (b) Kodi tinganene kuti angelo amatipenyerera kuchita ngati tili m’bwalo la seŵero m’lingaliro lotani?
8 Yehova atalenga dziko lapansi, angelo ‘anaimba limodzi mokondwera, ndi . . . kufuula ndi chimwemwe.’ (Yobu 38:4-7) Chiyambire nthaŵiyo, zolengedwa zakumwamba zimenezi zasonyeza chidwi chachikulu pa zochita za anthu. Yehova wagwiritsa ntchito zolengedwa zimenezi kupereka zilengezo zaumulungu kwa anthu. (Salmo 103:20) Zimenezi zilidi choncho makamaka mogwirizana ndi kufalitsidwa kwa uthenga wabwino m’tsiku lathu. M’chivumbulutso chopatsidwa kwa iye, mtumwi Yohane anaona “mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga.” Iyeyu anali nawo “Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu; ndi kunena ndi mawu aakulu, Opani Mulungu, m’patseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake.”—Chivumbulutso 14:6, 7.
9 Baibulo limatcha angelo “mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzaloŵa chipulumutso.” (Ahebri 1:14) Angeloŵa pogwira mwakhama ntchito zomwe apatsidwa, ali ndi mwayi wa kutionerera ndi kupenda ntchito zathu. Monga pa bwalo lochitira seŵero loonetsa bwino kwambiri zomwe zikuchitika, timagwira ntchito yathu pamaso pa openyerera akumwamba. (1 Akorinto 4:9) N’kolimbikitsatu ndi kosangalatsa zedi kudziŵa kuti sitili tokha pogwira ntchitoyi monga ofesa choonadi cha Ufumu!
Timakwaniritsa Mbali Yathu Mwachangu
10. Kodi malangizo othandiza a pa Mlaliki 11:6 angakhudze motani ntchito yathu yolalikirayi?
10 N’chifukwa chiyani Yesu ndi angelo ali ndi chidwi chotere ndi ntchito yathu? Yesu anapereka chifukwa chimodzi pamene anati: “Ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.” (Luka 15:10) Mofananamo nafenso tili ndi chidwi chenicheni mwa anthu. Choncho, timachita mulimonse momwe tingathere kufalitsa mbewu za choonadi cha Ufumu pena paliponse. Mawu a pa Mlaliki 11:6 angatanthauze ntchito yathuyi. Baibulo pamenepo likutilimbikitsa kuti: “Mamaŵa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziŵa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziŵiri zidzakhala bwino.” Zoonadi, pa munthu aliyense amene walandira uthenga wathu kumakhala mazanamazana ngakhalenso zikwizikwi za okana uthengawu. Koma monga angelo, timakondwera pamene ngakhale “wochimwa mmodzi” yekha alandira uthenga wa chipulumutso.
11. Kodi kugwiritsa ntchito zofalitsa zofotokoza Baibulo kungakhale kopindulitsa motani?
11 N’zambiri zochitika pa kulalikidwa kwa uthenga wabwino. Chinthu chothandiza pantchito imeneyi chofunika kwambiri ndicho mabuku ozikidwa pa Baibulo osindikizidwa ndi kugwiritsidwa ntchito ndi Mboni za Yehova. M’lingaliro lina, zofalitsa zimenezi zilinso ngati mbewu zomwe zikumwazidwa ponseponse. Sitikudziŵa kuti n’kuti komwe zofalitsa zathuzi zidzapambana. Nthaŵi zina chofalitsa chingachoke kwa munthu wina n’kupita kwa wina chisanaŵerengedwe ndi aliyense. Yesu ndi angelo angathe kutsogolera zochitika zoterezi nthaŵi zina n’cholinga chofuna kupindulitsa oongoka mtima. Lingalirani zochitika zina zomwe zikusonyeza momwe Yehova angachitire zinthu zosayembekezeka ndi zosangalatsa pogwiritsa ntchito mabuku omwe asiyidwa kwa anthu.
Ntchito ya Mulungu Woona
12. Kodi magazini yakale inathandiza motani banja linalake kum’dziŵa Yehova?
12 M’chaka cha 1953, Robert ndi Lila, limodzi ndi ana awo anasamuka mu mzinda waukulu ndi kukaloŵa nyumba yopasukapasuka yakalekale pa famu ina m’dera lakumidzi ku Pennsylvania, m’dziko la United States of America. Posapita nthaŵi atangosamukira m’nyumba imeneyi, Robert anaganiza zopanga malo ena otchingika, kunsi kwa masitepe okwerera kumka m’chipinda chapamwamba kukhala bafa. Atachotsa matabwa angapo, anapeza kuti m’mphepete mwa khomalo, makoswe anali ataunjika mapepala ong’ambika, makoko a mtedza, ndi zinyalala zina zambiri. Pamenepo, pakati pa zinyalala zonsezo, panalinso magazini ya The Golden Age. Chomwe chinam’chititsa chidwi kwambiri Robert chinali nkhani yokhudza kulera ana. Anakopeka kwambiri ndi chitsogozo chomveka bwino cha m’Baibulo chomwe magaziniyo inapereka kotero kuti anauza Lila kuti adzaloŵa “chipembedzo cha The Golden Age.” M’milungu yoŵerengeka chabe, a Mboni za Yehova anafika pakhomo pawo, koma Robert anawauza kuti banjalo linali n’chidwi ndi “chipembedzo cha The Golden Age” chokha basi. Mbonizo zinafotokoza kuti tsopano The Golden Age ili ndi dzina latsopano lakuti Galamukani! Robert ndi Lila anayamba kuphunzira Baibulo mokhazikika ndi Mbonizo, ndipo pambuyo pake anabatizidwa. Ndiyeno nawonso anafesa mbewu za choonadi mwa ana awo ndi kututa za mwanaalirenji. Lerolino, anthu oposa 20 a m’banja limeneli, kuphatikizapo ana onse asanu ndi aŵiri a Robert ndi Lila, ndi atumiki obatizidwa a Yehova Mulungu.
13. N’chiyani chomwe chinasonkhezera mwamuna wina ndi mkazi wake kuchita chidwi ndi Baibulo ku Puerto Rico?
13 Zaka ngati 40 zapitazo, William ndi Ada, mwamuna ndi mkazi wake a ku Puerto Rico, analibe n’komwe chidwi chophunzira Baibulo. Nthaŵi zonse Mboni za Yehova zikagogoda pachitseko chawo, banjali linali kungokhala phee kuchita ngati panyumbapo palibe anthu. Tsiku lina William anapita kumalo ogulitsira ziŵiya zakale zosiyanasiyana kukagula chipangizo chinachake chofunika pantchito ina kunyumba kwawoko. Atangoyamba ulendo wake wobwerera kunyumba, anaona buku lobiriŵirirako m’chimgolo chachikulu chotayamo zinyalala. Linali lakuti Religion (Chipembedzo), buku losindikizidwa ndi Mboni za Yehova kalero mu 1940. William anatenga bukulo n’kupita nalo kunyumba ndipo anakondwa kwabasi kuŵerenga nkhani ya kusiyana kwa chipembedzo chonyenga ndi chipembedzo choona. Nthaŵi inayake Mboni za Yehova zitafika, William ndi Ada anamvetsera mosangalala uthenga wawo ndipo anayamba kuphunzira nawo Baibulo. Patapita miyezi ingapo anabatizidwa pa Msonkhano Wamayiko wa Chifuno cha Mulungu mu 1958. Chiyambire nthaŵiyo, nawonso athandiza anthu oposa 50 kukhala abale athu achikristu.
14. Monga momwe chochitika china chasonyezera, kodi mabuku athu ofotokoza Baibulo angakhoze kuchitanji?
14 Karl anali ndi zaka 11 zokha zakubadwa ndipo anali wopulupudza. Iye ankaona ngati kuti nthaŵi zonse ankaloŵa m’vuto. Abambo ake, mlaliki wampingo wa German Methodist, anali atam’phunzitsa kuti anthu oipa amakapsa m’moto wa helo akamwalira. Choncho Karl ankaopa kwambiri helo. Tsiku lina m’chaka cha 1917, Karl anaona pepala losindikizidwapo mawu mumsewu ndipo analitola. Pamene anali kuliŵerenga, mwamsanga maso ake anangolunjika pafunso lakuti: “Kodi helo n’chiyani?” Pepalalo linali kuitanira anthu ku nkhani yapoyera yokhudza helo, yokonzedwa ndi Ophunzira Baibulo, omwe lerolino amadziŵika monga Mboni za Yehova. Pafupifupi chaka chimodzi chitatha, Karl ataphunzira Baibulo kambirimbiri, anabatizidwa, potero anakhala mmodzi wa Ophunzira Baibulo. M’chaka cha 1925 anaitanidwa kukagwira ntchito ku likulu lapadziko lonse la Mboni za Yehova—komwe akutumikirabe pakali pano. Ntchito yachikristu yomwe wakhala akuigwira kwa zaka zoposa makumi asanu ndi atatu inayambira pa kapepala mumsewu.
15. Kodi Yehova angachitenji, m’njira yomwe iye wasankha?
15 N’zoona kuti n’kosatheka kuti munthu anene ngati angelo analoŵerera mwachindunji m’zochitika zimenezi ndi kuti anatero pamlingo wotani. Komabe, sitiyenera kukayika kuti Yesu limodzi ndi angelo amatengamo mbali mwakhama m’ntchito yolalikira ndi kuti Yehova angatsogoze zinthu m’njira yomwe iye wasankha. Zochitika zimenezi ndi zina zambiri zofananazo zikusonyeza kuthekera konse kwakuti pamene tagaŵira mabuku zotsatira zabwino zingakhalepo.
Tapatsidwa Chuma
16. Kodi tingaphunzirenji m’mawu a pa 2 Akorinto 4:7?
16 Mtumwi Paulo ananena za “chuma m’zotengera zadothi.” Chuma chimenecho ndicho ntchito yolalikira yopatsidwa ndi Mulungu, ndipo zotengera zadothizo ndiwo anthu omwe Yehova wawapatsa chuma chimenechi. Popeza kuti anthu amenewo n’ngopanda ungwiro ndi olephera m’zinthu zina, Paulo anapitiriza kunena kuti zotsatira za kupatsidwa kwawo ntchito imeneyo n’zakuti “mphamvu yoposa yachibadwa ikhale ya Mulungu ndipo osati yochokera mwa ife eni.” (2 Akorinto 4:7 NW) Inde, tiyenera kudalira Yehova kuti ndiye adzapereka mphamvu zofunikira kuti tikhoze kukwaniritsa ntchito yomwe talandirayi.
17. Pamene tikufesa mbewu za choonadi cha Ufumu, kodi tidzakumana ndi zotani, ndipo ngakhale kuti zidzatero, n’chifukwa chiyani tiyenera kukhalabe ndi malingaliro abwino?
17 Kaŵirikaŵiri timafunikira kudzimana. Kungakhale kosautsa kapena kovuta kugwira ntchito m’magawo ena. Kuli madera ena kumene anthu ambiri amaoneka ngati amphwayi, mwinanso ankhanza. Munthu angayesetse mwakhama m’madera oterowo koma popanda phindu lililonse. Komatu khama lathulo n’loyenereradi makamaka pamene ambiri chotero ali pangozi. Kumbukirani, mbewu zomwe mukufesa zingapatse anthu chimwemwe tsopano lino komanso moyo wosatha m’tsogolo. Nthaŵi zambiri mawu a pa Salmo 126:6 asonyeza kukhala oona. Mawuwo amati: “Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbewu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.”
18. Kodi utumiki wathu tingaupenyerere motani nthaŵi zonse, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kutero?
18 Tigwiritsetu ntchito mpata uliwonse woyenerera kufesa mbewu za choonadi cha Ufumu mowoloŵa manja. Tisaiwaletu kuti, ngakhale ndife amene timadzala ndi kuthirira mbewuzo, koma ali Yehova yemwe amazikulitsa. (1 Akorinto 3:6, 7) Komabe, monga momwe Yesu ndi angelo akukwaniritsira mbali yawo pantchito imeneyi, Yehova akuyembekezera kuti nafenso timalize utumiki wathu kotheratu. (2 Timoteo 4:5) Tidzipenyereretu nthaŵi zonse ndi chiphunzitso chathu, maganizo athu, ndinso changu chathu muutumiki. Chifukwa chiyani? Paulo akuyankha kuti: “Pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.”—1 Timoteo 4:16.
Kodi Taphunziranji?
• Kodi ntchito yathu yofesa ikukhala n’zotsatira zabwino m’njira ziti?
• Kodi Yesu Kristu ndi angelo akuloŵetsedwa motani m’ntchito yolalikira lerolino?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala owoloŵa manja monga ofesa choonadi cha Ufumu?
• Pamene tikumana ndi anthu amphwayi kapena kuchitiridwa nkhanza muutumiki wathu, n’chiyani chomwe chiyenera kutisonkhezera kulimbikirabe?
[Chithunzi patsamba 15]
Mofanana ndi alimi a m’Israyeli wakale, Akristu lerolino akufesa mbewu za choonadi cha Ufumu mowoloŵa manja
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Mboni za Yehova zimasindikiza ndi kugawira zofalitsa zosiyanasiyana zofotokoza Baibulo m’zinenero 340