Wolembedwa ndi Luka
8 Pasanapite nthawi yaitali, Yesu anayamba kuyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi nʼkumalalikira komanso kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.+ Ndipo atumwi 12 aja anali naye limodzi. 2 Analinso ndi azimayi ena amene anawatulutsa mizimu yoipa komanso kuwachiritsa matenda awo. Ena mwa iwo anali Mariya amene ankatchulidwanso kuti Mmagadala, amene anamutulutsa ziwanda 7. 3 Jowana+ mkazi wa Kuza amene anali kapitawo wa Herode, Suzana ndi azimayi ena ambiri, amene ankatumikira Yesu ndi atumwiwo pogwiritsa ntchito chuma chawo.+
4 Ndiyeno gulu lalikulu la anthu litasonkhana, limodzi ndi ena amene ankamulondola kuchokera mʼmizinda yosiyanasiyana, Yesu anafotokoza fanizo lakuti:+ 5 “Wofesa mbewu anapita kukafesa mbewu zake. Pamene ankafesa, zina zinagwera mʼmbali mwa msewu nʼkupondedwapondedwa ndipo zinadyedwa ndi mbalame zamumlengalenga.+ 6 Zina zinagwera pathanthwe. Koma zitamera, zinauma chifukwa panalibe chinyezi.+ 7 Mbewu zina zinagwera paminga ndipo mingazo zinkakulira limodzi ndi mbewuzo ndipo zinalepheretsa mbewuzo kukula.+ 8 Koma zina zinagwera panthaka yabwino, ndipo zitakula, zinabereka zipatso kuwirikiza maulendo 100.”+ Atanena zimenezi, analankhula mokweza mawu kuti: “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+
9 Koma ophunzira ake anamufunsa tanthauzo la fanizo limeneli.+ 10 Iye anati: “Inu mwapatsidwa mwayi woti mumvetse zinsinsi zopatulika za Ufumu wa Mulungu. Koma kwa enawo, zonse ndi mafanizo okhaokha.+ Izi zili choncho kuti kuyangʼana aziyangʼana ndithu, koma kukhale kopanda phindu, kumvanso azimva ndithu, koma asamamvetse zimene zikunenedwa.+ 11 Tsopano fanizoli tanthauzo lake ndi ili: Mbewuzo ndi mawu a Mulungu.+ 12 Zogwera mʼmbali mwa msewuzo ndi anthu amene amamva mawuwo. Kenako Mdyerekezi amabwera nʼkudzachotsa mawuwo mʼmitima yawo kuti asakhulupirire ndiponso kupulumuka.+ 13 Zogwera pathanthwe ndi anthu amene amati akangomva mawuwo, amawalandira mosangalala, koma oterewa alibe mizu. Amakhulupirira kwa kanthawi, koma nthawi yoyesedwa ikafika amagwa.+ 14 Zimene zinagwera paminga, ndi anthu amene amva mawu a Mulungu koma chifukwa chotengeka ndi nkhawa, chuma+ ndi zosangalatsa za moyo uno,+ amalephera kukula bwino ndipo zipatso zawo sizikhwima.+ 15 Koma zogwera panthaka yabwino, ndi anthu amene pambuyo pomva mawuwo ndi mtima wabwino kwambiri,+ amawagwiritsitsa nʼkubereka zipatso mopirira.+
16 Palibe amene amati akayatsa nyale, amaivindikira ndi chiwiya kapena kuiika pansi pa bedi. Koma amaiika pachoikapo nyale kuti amene akulowa aone kuwala.+ 17 Chifukwa palibe chobisika chimene sichidzaululika. Ndipo zinthu zonse zosungidwa mwachinsinsi kwambiri zidzadziwika, sizidzabisika mpaka kalekale.+ 18 Choncho muzimvetsera mwatcheru kwambiri. Chifukwa amene ali nazo, adzapatsidwa zochuluka,+ koma amene alibe, adzalandidwa ngakhalenso zimene akuganizira kuti ali nazo.”+
19 Ndiyeno mayi ake ndi azichimwene ake+ anabwera kumeneko, koma chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, analephera kufika kumene iyeyo anali.+ 20 Koma ena anamuuza kuti: “Mayi anu ndi azichimwene anu aima panjapo akufuna kuonana nanu.” 21 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Mayi anga ndi azichimwene anga ndi awa amene amamvetsera mawu a Mulungu nʼkumawachita.”+
22 Tsiku lina Yesu ndi ophunzira ake anakwera ngalawa ndipo anawauza kuti: “Tiyeni tiwolokere tsidya lina la nyanja.” Choncho iwo anayamba kupalasa.+ 23 Koma ulendowo uli mkati, Yesu anagona tulo. Kenako panyanjapo panayamba kuwomba mphepo yamkuntho, ndipo madzi anayamba kudzaza mʼngalawamo moti akanatha kumira.+ 24 Kenako anapita kukamudzutsa ndipo anamuuza kuti: “Mlangizi, Mlangizi, tikufa!” Atamva zimenezi anadzuka nʼkudzudzula mphepo ndi mafunde amphamvuwo, moti zinasiya, ndipo panyanjapo panakhala bata.+ 25 Ndiyeno anawafunsa kuti: “Chikhulupiriro chanu chili kuti?” Koma iwo anagwidwa ndi mantha ndipo anathedwa nzeru, moti anayamba kufunsana kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi ndani kwenikweni? Nanga taonani, akutha kulamula mphepo ndi madzi ndipo zikumumvera.”+
26 Ndiyeno anaimika ngalawa ija mʼdera la Agerasa,+ tsidya linalo, moyangʼanizana ndi Galileya. 27 Yesu atangotsika nʼkufika kumtunda, anakumana ndi munthu wina wogwidwa ndi chiwanda wochokera mumzindawo. Kwa nthawi yaitali ndithu, munthuyo ankangokhala wosavala, komanso sankakhala mʼnyumba, koma kumanda.*+ 28 Munthuyo ataona Yesu, anafuula kwambiri nʼkudzigwetsa pansi pamaso pake. Kenako anafuula mwamphamvu kuti: “Kodi mukufuna chiyani kwa ine, Yesu, Mwana wa Mulungu Wamʼmwambamwamba? Chonde ndikukupemphani, musandizunze.”+ 29 (Chifukwa Yesu ankauza mzimu wonyansawo kuti utuluke mwa munthuyo. Mzimu umenewu unamugwira mwamphamvu maulendo ambiri.*+ Mobwerezabwereza ankamumanga ndi maunyolo komanso matangadza nʼkumamuyangʼanira. Koma chifukwa cha mphamvu ya chiwandacho, ankadula maunyolowo nʼkuthawira kumalo opanda anthu.) 30 Yesu anamufunsa kuti: “Dzina lako ndi ndani?” Iye anayankha kuti: “Khamu,” chifukwa mwa iye munalowa ziwanda zambiri. 31 Ziwandazo zinkamuchonderera mobwerezabwereza kuti asazilamule kuti zipite kuphompho.+ 32 Ndiyeno gulu lalikulu la nkhumba+ linkadya paphiri kumeneko. Choncho ziwandazo zinamuchonderera kuti azilole kukalowa munkhumbazo ndipo iye anazilola.+ 33 Zitatero ziwandazo zinatuluka mwa munthuyo nʼkukalowa munkhumbazo. Nkhumba zonsezo zinathamangira kuphedi nʼkulumphira mʼnyanja ndipo zinamira. 34 Koma abusa a ziwetozo ataona zimene zinachitikazo, anathawa nʼkukanena zimenezi mumzinda ndi mʼmidzi.
35 Kenako anthu anapita kukaona zomwe zinachitikazo. Iwo atafika kwa Yesu anapeza munthu amene anamutulutsa ziwanda uja atakhala pansi pafupi ndi Yesu. Munthuyo anali atavala bwino komanso maganizo ake ali bwinobwino ndipo iwo anachita mantha. 36 Amene anaona zimene zinachitikazo anawafotokozera mmene munthu wogwidwa ziwandayo anamuchiritsira. 37 Kenako gulu lonse lochokera mʼmidzi yapafupi ya Agerasa linamupempha kuti achoke kwawoko, chifukwa linagwidwa ndi mantha aakulu. Zitatero iye anakwera ngalawa kuti azipita. 38 Ndiyeno munthu amene anamutulutsa ziwanda uja anamupempha mobwerezabwereza kuti aziyenda naye. Koma Yesu anauza munthuyo kuti apite kwawo. Iye anati:+ 39 “Pita kunyumba ndipo ukafotokoze zimene Mulungu wakuchitira.” Choncho munthu uja anapitadi ndipo ankafalitsa mumzinda wonsewo zimene Yesu anamuchitira.
40 Yesu atabwerera ku Galileya, gulu la anthu linamulandira ndi manja awiri, chifukwa onse ankamuyembekezera.+ 41 Kenako panafika munthu wina dzina lake Yairo. Munthu ameneyu anali mtsogoleri wa sunagoge. Ndiyeno anadzigwetsa pamapazi a Yesu nʼkuyamba kumuchonderera kuti apite kunyumba kwake.+ 42 Yairo anachita zimenezi chifukwa mwana wake wamkazi amene anali ndi zaka pafupifupi 12, mwana yekhayo amene anali naye, anali atatsala pangʼono kumwalira.
Pamene Yesu ankapita, anthu ambiri anamutsatira ndipo ankamupanikiza. 43 Ndiyeno panali mayi wina amene ankadwala matenda otaya magazi+ kwa zaka 12, ndipo palibe aliyense amene anatha kumuchiritsa.+ 44 Mayiyu anatsatira Yesu kumbuyo nʼkugwira ulusi wopota wamʼmphepete mwa malaya ake akunja.+ Nthawi yomweyo magazi ake anasiya kutuluka. 45 Ndiyeno Yesu anafunsa kuti: “Ndi ndani amene wandigwira?” Onse atakana, Petulo anati: “Mlangizi, simukuona kuti anthu onsewa akuzungulirani ndipo akukupanikizani?”+ 46 Koma Yesu anati: “Ndithu wina wandigwira, chifukwa ndamva mphamvu+ ikutuluka mwa ine.” 47 Mayiyo ataona kuti zimene wachitazo zadziwika, anapita kwa Yesu akunjenjemera ndipo anagwada nʼkuulula pamaso pa anthu onse chimene chinamuchititsa kuti amugwire, komanso mmene wachirira nthawi yomweyo. 48 Koma iye anauza mayiyo kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere.”+
49 Ali mkati molankhula, panafika nthumwi ya mtsogoleri wa sunagoge uja, ndipo anamuuza kuti: “Mwana wanu uja wamwalira. Musiyeni Mphunzitsiyu musamuvutitse.”+ 50 Yesu atamva zimenezi, anamuuza kuti: “Usaope, ingokhala ndi chikhulupiriro basi, ndipo mwana wakoyo akhalanso ndi moyo.”*+ 51 Atafika kunyumbako sanalole kuti aliyense alowe naye limodzi mʼnyumba kupatulapo Petulo, Yohane ndi Yakobo komanso bambo ndi mayi a mtsikanayo. 52 Koma anthu onse ankalira komanso kudziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni. Choncho Yesu anawauza kuti: “Tontholani,+ chifukwa mwanayu sanamwalire, koma akugona.”+ 53 Atanena zimenezi, anthuwo anayamba kumuseka monyoza, chifukwa ankadziwa kuti mwanayo wamwalira. 54 Koma iye anamugwira dzanja nʼkumuitana kuti: “Mtsikana iwe, dzuka!”+ 55 Zitatero mzimu* wake+ unabwerera ndipo nthawi yomweyo anadzuka.+ Ndiyeno Yesu anawauza kuti amupatse chakudya mtsikanayo. 56 Pamenepo, makolo akewo anasangalala kwambiri, koma Yesu anawalangiza kuti asauze aliyense zimene zachitikazo.+