Lino Ndilo Tsiku la Chipulumutso!
“Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso.”—2 AKORINTO 6:2.
1. Kodi chofunika nchiyani kuti tikhale ndi kaimidwe kovomerezeka pamaso pa Mulungu ndi Kristu?
YEHOVA waika tsiku loti adzaweruze anthu. (Machitidwe 17:31) Ngati tikufuna kudzapulumuka patsiku limenelo, tiyenera kukhala m’kaimidwe kovomerezeka kwa iye limodzi ndi Woweruza amene wamuika, Yesu Kristu. (Yohane 5:22) Kaimidwe kameneko kamafuna kukhala ndi khalidwe logwirizana ndi Mawu a Mulungu ndi kukhalanso ndi chikhulupiriro chimene chimatisonkhezera kuthandiza ena kukhala ophunzira oona a Yesu.
2. Kodi nchifukwa chiyani dziko la anthu lili lotalikirana ndi Mulungu?
2 Chifukwa cha uchimo wobadwa nawo, dziko la anthu nlotalikirana ndi Mulungu. (Aroma 5:12; Aefeso 4:17, 18) Choncho, anthu amene tikuwalalikirawa angapulumuke pokhapokha ngati ayanjananso naye. Mtumwi Paulo anamveketsa bwino mfundo imeneyi polembera Akristu a ku Korinto. Tatiyeni tiyang’ane 2 Akorinto 5:10–6:10, tione zimene Paulo ananena za chiweruzo, kuyanjana ndi Mulungu, kenako chipulumutso.
“Tikopa Anthu”
3. Kodi Paulo ‘ankakopa bwanji anthu,’ ndipo nchifukwa chiyani ifenso lero tiyenera kuchita chimenecho?
3 Paulo anagwirizanitsa chiweruzo ndi kulalikira pamene analemba kuti: “Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa ku mpando wa kuweruza wa Kristu, kuti yense alandire zochitika m’thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa. Podziŵa tsono kuopsa kwa Ambuye, tikopa anthu.” (2 Akorinto 5:10, 11) Mtumwiyo ‘ankakopabe anthu’ mwa kulalikira uthenga wabwino. Nanga ifeyo? Popeza kuti dongosolo lazinthu loipali latsala pang’ono kutha, tiyeni tichite zimene tingathe kuwakopa anthu kuti achite zimene afunikira kuchita kuti Yesu adzawaweruze mwachifundo ndi kutinso akhale pamtendere ndi Mwini chipulumutso, Yehova Mulungu.
4, 5. (a) Kodi nchifukwa chiyani sitiyenera kudzitama ngati tikuchita zambiri mu utumiki wa Yehova? (b) Kodi Paulo anadzitama bwanji ‘m’malo mwa Mulungu’?
4 Komabe, ngati Mulungu watidalitsira utumiki wathu, tisadzitame. Ku Korinto ena ankadzitukumula kapena kutama anthu ena, ndiye zimenezo zinapangitsa magawano mumpingo. (1 Akorinto 1:10-13; 3:3, 4) Ponena za mkhalidwe umenewo, Paulo analemba kuti: “Sitidzivomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nawo iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima. Pakuti ngati tili oyaruka, titero kwa Mulungu; ngati tili a nzeru zathu, titero kwa inu.” (2 Akorinto 5:12, 13) Anthu onyada sankafuna kuona mpingo ukugwirizana ndiponso uli pamtendere wauzimu. Ankafuna kudzitama ndi maonekedwe akunja m’malo mothandiza okhulupirira anzawo kukhala ndi mtima wabwino pamaso pa Mulungu. Choncho, Paulo anaudzudzula mpingowo ndiyeno nkudzati: “Iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye.”—2 Akorinto 10:17.
5 Kodi iye Pauloyo sanadzitame? Mwina ena anaganiza choncho chifukwa cha zimene iyeyo ananena za kukhala kwake mtumwi. Koma anali kudzitama ‘m’malo mwa Mulungu.’ Anadzitama za kuyeneretsedwa kwake kukhala mtumwi, kuchitira kuti Akorinto asamusiye Yehova. Paulo anachita zimenezi kuti awabwezere kwa Mulungu chifukwa atumwi onyenga ankawasocheretsa. (2 Akorinto 11:16-21; 12:11, 12, 19-21; 13:10) Komabe, si kuti nthaŵi zonse Paulo ankayesetsa kupangitsa aliyense kuona kuti iyeyo anachita zambiri.—Miyambo 21:4.
Kodi Chikondi cha Kristu Chimakusonkhezerani?
6. Kodi chikondi cha Kristu chiyenera kutikhudza motani?
6 Paulo, monga mtumwi weniweni, ankaphunzitsa ena za nsembe ya Yesu yadipo. Nsembeyo inakhudza kwambiri moyo wa Paulo, chifukwa analemba kuti: “Pakuti chikondi cha Kristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa; ndipo adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa Iye amene adawafera iwo, nauka.” (2 Akorinto 5:14, 15) Yesu anasonyezadi chikondi mwa kupereka moyo wake kutifera! Chimenechodi chiyenera kukhala chotisonkhezera m’moyo wathu. Ngati tikuyamikira Yesu chifukwa chopereka moyo wake kutifera, tiyenera kusonyeza kuyamikirako mwa kugwira ntchito mwakhama polengeza uthenga wabwino wachipulumutso womwe Yehova wapereka kupyolera mwa Mwana wake wokondedwayo. (Yohane 3:16; yerekezerani ndi Salmo 96:2.) Kodi “chikondi cha Kristu” chikukusonkhezerani kugwira ntchito mwakhama pantchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira?—Mateyu 28:19, 20.
7. Kodi akutanthauzanji mawu akuti ‘osadziŵa munthu monga mwa thupi’?
7 Odzozedwa, mwa kugwiritsa ntchito miyoyo yawo mwa njira yosonyeza kuyamikira kwawo zimene Kristu anawachitira, ‘sakukhalanso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa iye.’ Paulo anati, “Kotero kuti ife sitidziŵanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Kristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.” (2 Akorinto 5:16) Akristu sayenera kuona anthu monga mwa thupi, kapena kukonda Ayuda kuposa Akunja kapena kukonda olemera kuposa osauka. Odzozedwa ‘sadziŵanso munthu tsopano monga mwa thupi,’ chifukwa kwa iwowo, chofunika kwambiri ndicho kukhala ndi okhulupirira anzawo paunansi wauzimu. Anthu amene ‘anazindikira Kristu monga mwa thupi’ si okhawo amene anamuona pamene anali padziko lapansi. Ngakhale kuti ena amene ankayembekezera Mesiya anamuona mwa thupi panthaŵi ina, iwo sanapitirize kumuona motero. Anapereka thupi lake likhale dipo ndiyeno anaukitsidwa ali mzimu wopatsa moyo. Ena amene anaukitsidwa kuti akakhale ndi moyo wakumwamba anasiya matupi awo anyama popanda kumuona Yesu Kristu nthaŵi ina monga mwa thupi.—1 Akorinto 15:45, 50; 2 Akorinto 5:1-5.
8. Kodi anthu akhoza bwanji ‘kukhala mwa Kristu’?
8 Paulo, pouzabe odzozedwa, anawonjezera kuti: “Ngati munthu aliyense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.” (2 Akorinto 5:17) ‘Kukhala mwa Kristu’ kumatanthauza kukhala ndi maganizo amodzi ndi iyeyo. (Yohane 17:21) Unansi umenewu unayambika pamene Yehova anamkokera munthuyo kwa Mwana wake ndi kumbala munthuyo mwa mzimu woyera. Monga mwana yemwe Mulungu anabala mwa mzimu, munthuyo anali “wolengedwa watsopano” wokhala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi Kristu mu Ufumu wakumwamba. (Yohane 3:3-8; 6:44; Agalatiya 4:6, 7) Akristu odzozedwa amenewo apatsidwa mwayi waukulu wautumiki.
“Yanjanitsidwani ndi Mulungu”
9. Kodi Mulungu wachitanji kuti pakhale chiyanjano pakati pa anthu ndi iye?
9 Ha, mmene Yehova wayanjira ‘olengedwa atsopanowo’! Paulo anati: “Zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Kristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso; ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Kristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye yekha, osawaŵerengera zolakwa zawo; ndipo anaikiza kwa ife mawu a chiyanjanitso.” (2 Akorinto 5:18, 19) Mtundu wa anthu wamtalikira Mulungu kuyambira pamene Adamu anachimwa. Koma mwachikondi Yehova anatsegulanso njira kudzera mwa nsembe ya Yesu kuti ayanjanenso ndi anthu.—Aroma 5:6-12.
10. Kodi Yehova anaikiza m’manja mwa ndani utumiki wa chiyanjanitso, ndipo iwo akuuchita motani?
10 Yehova waikiza m’manja mwa odzozedwa utumiki wa chiyanjanitso, choncho Paulo anati: “Chifukwa chake tili atumiki, [“akazembe”, NW], m’malo mwa Kristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m’malo mwa Kristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.” (2 Akorinto 5:20) Kale, akazembe ankatumizidwa kwenikweni panthaŵi yachidani kuti akakambirane ndi adani awo pofuna kupeŵa nkhondo. (Luka 14:31, 32) Ndiye poti anthu ochimwa ali otalikirana ndi Mulungu, watumiza akazembe ake odzozedwa kuti akauze anthu mfundo za mmene anthuwo angayanjanirane ndi Mulungu. Monga oimira Kristu, odzozedwa akupempha kuti: “Yanjanitsidwani ndi Mulungu.” Pempho limeneli nchifundo chosonkhezera anthu kuti afune Mulungu kuti adzawapulumutse kudzera mwa Kristu.
11. Mwakukhulupirira dipo, kodi ndani makamaka adzalandira kaimidwe kolungama pamaso pa Mulungu?
11 Anthu onse amene amakhulupirira dipo angayanjanenso ndi Mulungu. (Yohane 3:36) Paulo anati: ‘[Yesu] yemwe sanadziŵa uchimo, [Yehova] anamyesera uchimo m’malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.’ (2 Akorinto 5:21) Munthu wangwiroyo Yesu anali nsembe yoperekera machimo a ana onse a Adamu kuti awomboledwe ku uchimo wobadwa nawo. Amakhala “chilungamo cha Mulungu” kudzera mwa Yesu. Chilungamo chimenechi, kapena kaimidwe kolungama pamaso pa Mulungu, choyamba kamafika kwa oloŵa nyumba limodzi ndi Kristu a 144,000. Mu Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi, kaimidwe kolungama monga anthu angwiro kadzafika kwa ana apadziko lapansi a Atate Wosatha, Yesu Kristu. Adzawathandiza kukhala olungama ndiponso angwiro kuti adzakhale okhulupirika kwa Mulungu, mpaka atalandira mphatso ya moyo wosatha.—Yesaya 9:6; Chivumbulutso 14:1; 20:4-6, 11-15.
“Nyengo Yabwino Yolandiridwa”
12. Kodi ndi utumiki wofunika wotani umene akuuchita akazembe limodzi ndi nthumwi za Yehova?
12 Kuti tidzapulumuke, tiyenera kumvera mawu a Paulo, akuti: ‘Monga ochitira pamodzi [ndi Yehova] tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu, pakuti anena, M’nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, ndipo m’tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza; taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso.’ (2 Akorinto 6:1, 2) Akazembe odzozedwa a Yehova limodzi ndi nthumwi zake a “nkhosa zina,” salandira chisomo cha Mulungu kwachabe. (Yohane 10:16) Mwa khalidwe lawo labwino ndi khama lawo pochita utumiki wawo m’nyengo “yolandiridwa” ino, akufuna kuyanjidwa ndi Mulungu ndiponso akuuza anthu padziko lapansi kuti lino ndilo “tsiku lachipulumutso.”
13. Kodi mfundo yaikulu pa Yesaya 49:8 ndi iti, ndipo inakwanira bwanji?
13 Paulo ananena mawu a pa Yesaya 49:8, akuti: “Atero Yehova, nthawi yondikomera ndakuyankha Iwe, ndi tsiku la chipulumutso ndakuthandiza; ndipo ndidzakusunga ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, kuti ukhazikitse dziko, nuwaloŵetse m’zoloŵa zopasuka m’malo abwinja.” Ulosi umenewu unakwanira choyamba pamene Aisrayeli anamasulidwa kuukapolo ku Babulo ndiyeno nkudzabwerera kudziko lawo labwinja.—Yesaya 49:3, 9.
14. Kodi Yesaya 49:8 anakwaniritsidwa motani kwa Yesu?
14 Ulosi wa Yesayawo, potsirizika kukwanira kwake, Yehova anapatsa “mtumiki” wake Yesu akhale ‘kuunika kwa amitundu, kuti [Mulungu] adzapulumutse anthu mpaka kumalekezero a dziko lapansi.’ (Yesaya 49:6, 8; yerekezerani ndi Yesaya 42:1-4, 6, 7; Mateyu 12:18-21.) Zikuoneka kuti ‘nthaŵi yokomera Yehova,’ kapena “nthaŵi yolandiridwa,” inafika pamene Yesu anali padziko lapansi. Anapemphera, ndipo Mulungu ‘anamyankha.’ Kwa Yesu, limenelo linalidi “tsiku la chipulumutso” chifukwa anakhulupirikabe moti “anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha.”—Ahebri 5:7, 9; Yohane 12:27, 28.
15. Kodi Aisrayeli auzimu anayambira liti kuyesetsa kusonyeza kuti ngoyenerera chisomo cha Mulungu, ndipo ndi cholinga chotani?
15 Paulo anasonyeza kuti mawu a Yesaya 49:8 akugwira ntchito kwa Akristu odzozedwa, nawapempha kuti ‘asalandire chisomo cha Mulungu kwachabe’ mwa kulephera kukhala naye pamtendere panthaŵi “yolandiridwa” ndi kulephera kuyamikira “tsiku la chipulumutso” limene wapereka. Paulo anawonjezera kuti: “Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso.” (2 Akorinto 6:1-2) Chiyambire 33 C.E. pa Pentekoste, Aisrayeli auzimu akhala akuyesetsa kusonyeza kuti ngoyenerera chisomo cha Mulungu kotero kuti ‘nthaŵi yolandiridwayi’ kwa iwo ikhaledi “tsiku la chipulumutso.
‘Kudzitsimikiza Tokha Monga Atumiki a Mulungu’
16. Kodi pamene Paulo anadzitsimikiza yekha monga mtumiki wa Mulungu, anali m’mikhalidwe yovuta yotani?
16 Anthu ena omwe anali mumpingo wa Korinto sanali kudzisonyeza kuti anali oyenerera chisomo cha Mulungu. Ankamnena Paulo miseche namayesetsa kumuwonongera mbiri ya udindo wake monga mtumwi, ngakhale kuti iyeyo ‘sankakhumudwitsa aliyense.’ Iye anadzitsimikiza yekha monga mtumiki wa Mulungu “m’kupirira kwambiri, m’zisautso, m’zikakamizo, m’zopsinja, m’mikwingwirima, m’ndende, m’mapokoso, m’mavutitso, m’madikiro, m’masalo a chakudya.” (2 Akorinto 6:3-5) Kenaka, Paulo anati ngati adani akewo anali atumiki, ‘makamaka iye ndiye anali mtumiki’ chifukwa anaponyedwa m’ndende kambirimbiri, anakwapulidwa, kuona mikwingwirima, ndi kusala chakudya.—2 Akorinto 11:23-27.
17. (a) Kodi tingadzitsimikize tokha monga atumiki a Mulungu mwa kusonyeza mikhalidwe yotani? (b) Kodi “chamuna cha chilungamo” nchiyani?
17 Ifenso tingadzitsimikize tokha monga atumiki a Mulungu, monga anachitira Paulo ndi mabwenzi ake. Motani? “M’mayeredwe,” kapena kukhala oyera, ndi kuchita zinthu malinga ndi chidziŵitso cholongosoka cha m’Baibulo. Tingadzitsimikize tokha “m’chilekerero,” kupirira moleza mtima zimene ena amatilakwira kapena kutikhumudwitsa nazo, ndi “m’kukoma mtima” pochitira ena zinthu zothandiza. Ndiponso, tingadzitsimikize tokha monga atumiki a Mulungu mwa kulola mzimu wake kutitsogoza, kusonyeza ‘chikondi chosanyenga,’ kulankhula choonadi, ndi kudalira kuti iye adzatipatsa mphamvu yochitira utumiki wathu. Paulo anasonyeza kuti analidi m’Mkristu “mwa chamuna cha chilungamo kulamanja ndi kulamanzere.” M’nkhondo zakale, asilikali ankagwira lupanga ndi dzanja lamanja, chikopa nkuchigwira ndi lamanzere. Pankhondo yauzimu yomenyana ndi aphunzitsi onyenga, Paulo sanagwiritse ntchito zida za thupi lochimwa—mphulupulu, chinyengo. (2 Akorinto 6:6, 7; 11:12-14; Miyambo 3:32) Anagwiritsa ntchito “chamuna” cha chilungamo, [“zida za chilungamo,” NW], kapena njira zolungama, kuti achirikize kulambira koona. Ifenso tizitero.
18. Ngati tili atumiki a Mulungu, kodi khalidwe lathu liyenera kukhala lotani?
18 Ngati tili atumiki a Mulungu, khalidwe lathu likhale ngati la Paulo ndi la antchito anzake. Tizichita monga Akristu kaya anthu atilemekeze kapena atinyoze. Ngakhale anthu angatinenere zoipa zotani, ife sitileka ntchito yathu yolalikira, ngakhale anene zabwino za ife, sitichita nazo matama. Tizingolankhula choonadi basi ndipo anthu adzatizindikira mwa ntchito zimene tikuchitira Mulungu. Ngati tagwera m’vuto, m’manja mwa adani, tidzadalira Yehova. Ndipo tidzalandira chilango moyamikira.—2 Akorinto 6:8, 9.
19. Kodi zimatheka bwanji ‘kulemeretsa ambiri’ mwauzimu?
19 Pomaliza nkhani yake yonena za kuyanjanitsa anthu ndi Mulungu, Paulo anati iyeyo limodzi ndi mabwenzi ake anali “monga akumva chisoni, koma akukondwera nthaŵi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.” (2 Akorinto 6:10) Ngakhale kuti atumiki amenewo analidi ndi chifukwa chomveka pochita chisoni, anali ndi chimwemwe mumtima. Anali osauka inde, koma ‘analemeretsa ambiri’ mwauzimu. Tingotero kuti, ‘anali ndi zinthu zambiri’ chifukwa chikhulupiriro chawo chinawalemeretsa mwauzimu—anali ndi chiyembekezo chokakhala ana a Mulungu kumwamba. Ndipo anali ndi moyo wachikwanekwane ndiponso wosangalatsa monga atumiki a Kristu. (Machitidwe 20:35) Ifenso ‘tingalemeretse ambiri’ mwauzimu mwa kuchita utumiki woyanjanitsa anthu ndi Mulungu tsopano lino—tsiku la chipulumutso lomwe lino!
Dalirani Chipulumutso cha Yehova
20. (a) Kodi Paulo ankakhumba kwambiri chiyani, ndipo nchifukwa chiyani anafunikira kuchita zinthu mwachangu? (b) Kodi nchiyani chikuchitika tsiku lino la chipulumutso limene tikukhalamo?
20 Pamene Paulo analembera Akorinto kalata yake yachiŵiri cha m’ma 55 C.E., panali patangotsala zaka 15 kuti dongosolo lazinthu la Ayuda lithe. Mtumwiyo anakhumbadi kuti Ayuda ndi Akunja ayanjanenso ndi Mulungu kudzera mwa Kristu. Limenelo linali tsiku la chipulumutso, ndipo anafunikira kuchita zinthu mwachangu. Ifenso tili m’nyengo yofananayo ya mapeto a dongosolo lazinthu chiyambire 1914. Ntchito yapadziko lonse yolalikira Ufumu yomwe ikugwiridwa tsopano lino ikusonyeza kuti lino ndilodi tsiku la chipulumutso.
21. (a) Kodi ndi lemba liti limene lasinkhidwa kuti likhale lemba la chaka cha 1999? (b) Kodi tiyenera kukhala tikuchitanji tsiku lino la chipulumutso?
21 Anthu amitundu yonse afunikira kumva mmene Mulungu wakonzera njira yowapulumutsira kudzera mwa Yesu Kristu. Nthaŵi isawonongeke. Paulo analemba kuti: “Taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso.” Mawu amenewa a pa 2 Akorinto 6:2 adzakhala lemba lachaka cha 1999 la Mboni za Yehova. Nloyeneradi, chifukwa tatsala pang’ono kuona chiwonongeko choposa cha Yerusalemu ndi kachisi wake! Posachedwapa dongosolo lazinthu lonseli lidzatha, ndipo zidzakhudza aliyense padziko lapansi. Nthaŵi yochitapo kanthu ndiyo tsopano lino—osati maŵa. Ngati tikukhulupirira kuti amene amapulumutsa ndi Yehova, ngati timamkonda, ndipo ngati timaona moyo wosatha monga chinthu chopambana, sitidzalandira chisomo cha Mulungu pachabe. Mumtima mwathu ngati tikukhumbadi kulemekeza Yehova, tidzasonyeza mwa mawu ndi zochita zathu kuti tikunenetsadi tikamalengeza kuti: “Taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso.”
Kodi Mungayankhe Bwanji?
◻ Kodi nchifukwa chiyani kuyanjana ndi Mulungu kuli kofunika kwambiri?
◻ Pautumiki wakuyanjanitsawu, kodi akazembe ndani ndipo nthumwi ndani?
◻ Kodi tingadzitsimikize tokha bwanji monga atumiki a Mulungu?
◻ Kodi lemba la Mboni za Yehova la chaka cha 1999 likutanthauzanji kwa inu?
[Zithunzi patsamba 17]
Kodi mukulalikira mwachangu, namuthandiza ena kuyanjananso ndi Mulungu, monga ankachitira Paulo?
United States
France
Côte d’Ivoire
[Chithunzi patsamba 18]
Tsiku lino la chipulumutso, kodi muli pakati pa anthu amene akuyanjana ndi Yehova Mulungu?