‘Munagulidwa ndi Mtengo’
‘Munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m’thupi lanu.’—1 AKORINTO 6:20.
1, 2. (a) Kodi nchiyani chomwe chinatsegula njira “zopulumutsira kuimfa”? (b) Kodi chinafunikira kuchitidwa nchiyani kupangitsa nsembe ya Kristu kugwira ntchito mwalamulo, monga momwe zinachitiridwa chithunzi ndichiyani?
WAMASALMO anati: ‘Mulungu akhala kwa ife Mulungu wa chipulumutso; ndipo Yehova Ambuye ali nazo zopulumutsira kuimfa.’ (Salmo 68:20) Nsembe ya Yesu Kristu inatsegula njira imeneyo. Koma kuti nsembeyo igwire ntchito mwalamulo, Kristu adafunikira kukawonekera mwiniyekha pamaso pa Mulungu.
2 Ichi chinachitiridwa chithunzi pa Tsiku Lotetezera pamene mkulu wansembe analoŵa m’Malo Opatulikitsa. (Levitiko 16:12-15) Mtumwi Paulo adalemba kuti: ‘Koma atafika Kristu, mkulu wansembe . . . [analoŵa, NW] osati ndi mwazi wa mbuzi ndi ana a ng’ombe, koma mwa mwazi wa iye yekha, analowa kamodzi ku malo opatulika, atalandirapo chiombolo chosatha. Pakuti Kristu sanaloŵa m’malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu m’mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.’—Ahebri 9:11, 12, 24.
Mphamvu ya Mwazi
3. (a) Kodi mwazi umalingaliridwa motani ndi alambiri a Yehova, ndipo nchifukwa ninji? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti mwazi uli ndi mphamvu yalamulo yotetezera machimo?
3 Kodi mwazi wa Kristu umachita mbali yotani m’chipulumutso chathu? Kuchokera m’tsiku la Nowa, alambiri owona akhala akuwulingalira mwazi kukhala wopatulika. (Genesis 9:4-6) Mwazi umachita mbali yofunika m’dongosolo la moyo, pakuti Baibulo limati “pakuti moyo wa nyama ukhala m’mwazi.” (Levitiko 17:11) Chotero Chilamulo cha Mose chinafunikiritsa kuti nyama itaperekedwa nsembe, mwazi wake udafunikira kuthiridwa pamaso pa Yehova. Nthaŵi zina mwazi unapakidwanso panyanga za guwa lansembe. Mwachiwonekere, mphamvu yotetezera ya nsembeyo inali m’mwazi wake. (Levitiko 8:15; 9:9) “Pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi mwazi mogwirizana ndi Chilamulo, ndipo popanda mwazi kukhetsedwa palibe chikhululukiro chimachitika.”—Ahebri 9:22, NW.
4. (a) Kodi kuika malire kwa kugwiritsiridwa ntchito kwa mwazi kochitidwa ndi Mulungu kunatumikira chifuno chotani? (b) Kodi njira imene Yesu anaphedwera inasonyezanji?
4 Chotero, nkosadabwitsa kuti pansi pa Chilamulo, kugwiritsira ntchito molakwa mwazi kulikonse kudadzetsa chilango cha imfa! (Levitiko 17:10) Tonsefe timadziŵa kuti chinthu chitakhala chosawonekawoneka, kapena ngati kuchigwiritsira ntchito kwake kutaikiridwa malire mosamalitsa, mtengo wake umakwera. Kuletsa kwa Yehova kuwugwiritsira ntchito mwazi kunatsimikizira kuti ukalingaliridwa, osati monga chinthu wamba, koma monga wamtengo wapatali, waphindu. (Machitidwe 15:29; Ahebri 10:29) Ichi chinagwirizana ndi chifuno chokwezeka chimene mwazi wa Kristu ukatumikira. Moyenerera, iye anafa m’njira yomwe inapangitsa mwazi wake kukhetsedwa. Chotero, kunali kwachiwonekere kuti Kristu sanangopereka nsembe thupi lake lokha komanso anauthira moyo wake, anaupereka nsembe moyo wake weniweniwo monga munthu wangwiro! (Yesaya 53:12) Kristu sanataye kuyenerera kwalamulo ku moyowo chifukwa cha kupanda ungwiro, chotero mwazi wake wothiridwa udali ndi mtengo waukulu ndipo ukaperekedwa pamaso pa Mulungu kaamba ka kutetezera machimo a anthu.
5. (a) Kodi Kristu anaperekanji kumwamba, ndipo nchifukwa ninji? (b) Kodi kunatsimikiziridwa motani kuti Mulungu anavomereza nsembe ya Kristu?
5 Kristu sakadanyamula mwazi wake weniweni kunka nawo kumwamba. (1 Akorinto 15:50) Mmalomwake, iye ananyamula chomwe mwaziwo unaphiphiritsira: mtengo walamulo wa moyo wake waumunthu wangwiro woperekedwa nsembe. Atafika pamaso pa Mulungu, iye anaupereka moyowo mwalamulo monga dipo losinthanitsa ndi anthu ochimwa. Kuivomereza kwake Yehova nsembeyo kunachitiridwa umboni pa Pentekoste wa 33 C.E., pamene mzimu woyera unadza pa ophunzira 120 okhala m’Yerusalemu. (Machitidwe 2:1-4) Fuko la anthu tsopano lidapatidwa ndi Kristu mwakuligula, kunena kwake titero. (Agalatiya 3:13; 4:5; 2 Petro 2:1) Chotero, madalitso a dipo akakhoza kunka kwa anthu.
Oyamba Kupindula ndi Dipolo
6. Kodi Mulungu wapanga makonzedwe otani operekera mapindu a dipo la Kristu?
6 Komabe, ichi sichinatanthauze kuti anthu akapatsidwa ungwiro wakuthupi pomwepo, pakuti nkokha chibadwa chochimwa cha anthu chitalakidwa, apo phuluzi ungwiro wa kuthupi sukathekera nkomwe. (Aroma 7:18-24) Kodi ndimotani ndipo ndiliti pamene uchimo ukalakidwa? Choyamba Mulungu anakonza kuti a 144,000 akumwamba ‘ansembe kwa Mulungu wathu alamulire monga mafumu padziko lapansi’ ndi Kristu Yesu. (Chibvumbulutso 5:9, 10; 7:4; 14:1-3) Kupyolera mwa iwo mapindu a dipo adzagaŵiridwa pang’onopang’ono kwa anthu m’nyengo ya zaka chikwi.—1 Akorinto 15:24-26; Chibvumbulutso 21:3, 4.
7. (a) Kodi pangano latsopano nchiyani, kodi lapangidwa pakati pa anthu ati, ndipo kodi limatumikira chifuno chotani? (b) Kodi nchifukwa ninji panafunikira imfa kuchititsa pangano latsopano kukhala lothekera, ndipo kodi ndi mbali yotani imene mwazi wa Kristu umachita?
7 Kutsogolera ku zinthuzo, mafumu ansembe a 144,000 “anagulidwa mwa anthu.” (Chibvumbulutso 14:4) Ichi chikukwaniritsidwa mwa “pangano latsopano.” Panganoli nlopangidwa pakati pa Yehova Mulungu ndi Israyeli wauzimu wa Mulungu kuti ziŵalo zake zitumikire monga mafumu ndi ansembe. (Yeremiya 31:31-34; Agalatiya 6:16; Ahebri 8:6-13; 1 Petro 2:9) Komabe, kodi pangano pakati pa Mulungu ndi anthu opanda ungwiro nlothekera motani? Paulo akulongosola motere: ‘Pakuti pamene pali pangano [pakati pa Mulungu ndi anthu opanda ungwiro], pafunika pafike imfa ya wolemberayo. Pakuti pangano liona mphamvu atafa mwini wake; popeza lilibe mphamvu konse pokhala wolemberayo ali ndi moyo.’—Ahebri 9:16, 17.
8, 9. Kodi dipo limagwirizana motani ndi pangano latsopano?
8 Chotero, nsembe yadipo njofunika ku pangano latsopano, limene Yesu ndiye Nkhoswe. Paulo analemba kuti: “Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi nkhoswe imodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, munthuyo, Kristu Yesu, amene anadzipereka dipo lolinganira kwa onse—ichi ndicho chimene chiyenera kuchitiridwa umboni pa nthaŵi zapadera.” (1 Timoteo 2:5, 6, NW) Mawuwo amagwira ntchito makamaka kwa a 144,000, omwe wapangana nawo pangano latsopanoli.
9 Pamene Mulungu anapanga pangano ndi Israyeli wakuthupi, ilo silinagwire ntchito mwalamulo kufikira pamene mwazi wanyama unakhetsedwa monga nsembe. (Ahebri 9:18-21) Mofananamo, kuti pangano latsopano ligwire ntchito, Kristu anafunikira kukhetsa “mwazi wa pangano.” (Mateyu 26:28; Luka 22:20) Pokhala ndi Kristu akuchita monga ponse paŵiri Mkulu Wansembe ndi “nkhoswe ya pangano latsopano,” Mulungu akugwiritsira ntchito mtengo wa mwazi wa Yesu kwa obweretsedwa m’pangano latsopanolo, akumawafupa mwalamulo ndi chilungamo chaumunthu. (Ahebri 9:15, NW; Aroma 3:24; 8:1, 2) Pamenepo Mulungu angaŵalowetse m’pangano latsopano kukhala mafumu ansembe akumwamba! Monga Nkhoswe yawo ndi Mkulu Wansembe, Yesu amaŵathandiza kusunga kaimidwe koyera pamaso pa Mulungu.—Ahebri 2:16; 1 Yohane 2:1, 2.
Kusonkhanitsa Zinthu pa Dziko Lapansi
10, 11. (a) Kodi dipo limawakhudza motani ena osakhala Akristu odzozedwa? (b) Kodi khamu lalikulu ndani, ndipo kodi ali ndi kaimidwe kotani ndi Mulungu?
10 Kodi ndi Akristu odzozedwa okha omwe angamasulidwe mwa dipo, kukhululukidwa machimo awo? Ayi, Mulungu akuyanjanitsa kwa iyemwini zinthu zina zonse mwakupanga mtendere kupyolera m’mwazi wokhetsedwa pamtengo wozunzirapo, monga momwe Akolose 1:14, 20 akusonyezera. Uku kukuphatikizapo zinthu zakumwamba (a 144,000) limodzinso ndi zinthu za padziko lapansi. Zapadziko lapansi ndiwo awo omwe akuyembekezera moyo wa padziko lapansi, anthu omwe adzasangalala ndi moyo wangwiro m’Paradaiso wapadziko lapansi. Makamaka chiyambire 1935 mpamene pakhala kuyesayesa kogwirizana kusonkhanitsa otereŵa. Chibvumbulutso 7:9-17 chikuŵalongosola kukhala ‘khamu lalikulu’ limene limayembekezera chipulumutso kuchokera kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa. Iwo afunikirabe kupulumuka ‘chisautso chachikulu’ ndi ‘kutsogozedwa ku akasupe a madzi amoyo,’ popeza kuti Chibvumbulutso 20:5 chikusonyeza kuti otereŵa adzakhala amoyo kotheratu, nakhala ndi moyo waumunthu wangwiro, pofika kumapeto kwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu. Pamenepo awo omwe adzapyola chiyeso chomalizira mumkhalidwe wawo waumunthu wangwiro adzalengezedwa kukhala olungama kaamba ka moyo wosatha padziko lapansi.—Chibvumbulutso 20:7, 8.
11 Komabe, monga chinthu choyamba kuchita, khamu lalikulu ‘latsuka [kale] zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.’ (Chibvumbulutso 7:14) Kristu sakuchita monga Nkhoswe ya pangano latsopano kwa iwo, komabe akupindula nalo panganoli kupyolera m’ntchito ya Ufumu wa Mulungu. Komabe, Kristu akuŵachitirabe monga Mkulu Wansembe, mwa amene Yehova akugwiritsira ntchito dipo kufikira iwo tsopano akulengezedwa kukhala olungama monga mabwenzi a Mulungu. (Yerekezerani ndi Yakobo 2:23.) Mkati mwa Zaka Chikwi, iwo pang’onopang’ono ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi [kufikira potsirizira pake], kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.’—Aroma 8:21.
12. Kodi Mulungu anachita ndi anthu okhulupirika a m’nthaŵi za Chikristu chisadakhale pamaziko otani?
12 Ponena za kaimidwe kawo ndi Mulungu, kungawonekere ngati kuti awo a khamu lalikulu amasiyana pang’ono ndi alambiri a Chikristu chisanakhale. Komabe, akalewo Mulungu anachita nawo akulingalira za makonzedwe a dipo amtsogolo. (Aroma 3:25, 26) Iwo anakhululukidwa machimo awo mongopatsidwa mwaŵi. (Salmo 32:1, 2) Mmalo mwa kuwamasula kotheratu ku ‘chikumbumtima cha machimo,’ nsembe zanyama zinatumikira monga ‘chikumbukiro cha machimo.’—Ahebri 10:1-3.
13. Kodi ndimwaŵi wotani umene tiri nawo woposa atumiki a Mulungu a m’nthaŵi za Chikristu chisanakhale?
13 Nzosiyana ndi Akristu owona lerolino. Iwo amalambira pamaziko a dipo lomwe lalipiridwa! Kupyolera mwa Mkulu wawo Wansembe, iwo ‘amafikira ndi ufulu wakulankhula ku mpando wachifumu wa kukoma mtima kwapadera.’ (Ahebri 4:14-16, NW) Kuyanjanitsidwa ndi Mulungu sindiko chinthu choyembekezeredwa kuchitika kutsogolo koma chenicheni chimene chiripo tsopano lino! (2 Akorinto 5:20) Atachimwa, iwo angakhululukidwe mowonadi. (Aefeso 1:7) Iwo amasangalaladi ndi chikumbumtima choyeretsedwa. (Ahebri 9:9; 10:22; 1 Petro 3:21) Madalitsowa ndiwo kalambula bwalo wa ufulu waulemerero wa ana a Mulungu umene atumiki a Yehova adzasangalala nawo mtsogolo!
Kuya kwa Nzeru ndi Chikondi cha Mulungu
14, 15. Kodi dipo limagogomezera motani nzeru zakuya za Yehova, limodzinso ndi chilungamo ndi chikondi chake?
14 Dipo ndimphatso yodabwitsa chotani nanga yochokera kwa Yehova! Nlosavuta kulimvetsetsa, komabe nlakuya kwambiri mokhozadi kuwopsa luntha lalikulu. Kulingalirapo kwathu pa malinganizidwe a dipo kwangovumbula zochepa zokha. Chikhalirechobe, timafuula ndi mtumwi Paulo kuti: ‘Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!’ (Aroma 11:33) Nzeru za Yehova zimasonyezedwa mwakuti anali wokhoza ponse paŵiri kupulumutsa anthu ndikulemekeza ufumu wake. Kupyolera m’dipo, ‘chilungamo cha Mulungu chaoneka . . . Mulungu anamuika poyera [Kristu] akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m’mwazi wake.’—Aroma 3:21-26.
15 Mulungu sangasulizidwe mwanjira iriyonse chifukwa chokhululukira machimo amene anachitidwa kumbuyoko ndi alambiri a m’nthaŵi ya Chikristu chisadakhale. Kuwonjezera apa, Yehova sangasulizidwe chifukwa choŵalengeza odzozedwa kukhala olungama monga ana ake kapena khamu lalikulu monga mabwenzi ake. (Aroma 8:33) Powonongeredwa mokulira, Mulungu wakhala walamulo, kapena wowongoka mwangwiro m’zochita zake, akumatsutsa kotheratu bodza la Satana lakuti Yehova ndiwolamulira wopanda chilungamo! Chikondi cha Mulungu chopanda dyera kaamba ka zolengedwa zake chasonyezedwa mofananamo mosakaikirika.—Aroma 5:8-11.
16. (a) Kodi ndim’njira yotani mmene dipo lathandizira kuthetsa nkhani ya umphumphu wa atumiki a Mulungu? (b) Kodi dipo limatipatsa motani maziko a chikhulupiriro m’dziko latsopano lolungama likudzalo?
16 Njira yomwe dipo linaperekedwera inathetsanso nkhani zokhudza umphumphu wa atumiki a Mulungu. Chimvero cha Yesu chokha chinakwaniritsa zimenezo. (Miyambo 27:11; Aroma 5:18, 19) Koma kuwonjezera pazimenezo ndi njira ya moyo wa Akristu a 144,000 omwe, mosasamala kanthu za chitsutso cha Satana, amakhala okhulupirika kufikira imfa! (Chibvumbulutso 2:10) Dipo limawatheketsa ameneŵa kulandira moyo wosakhoza kufa monga mphotho yawo—moyo wosawonongeka! (1 Akorinto 15:53; Ahebri 7:16) Ichi chimapangitsa kunena kwa Satana kuti atumiki a Mulungu ngosakhulupirika kukhala kwabodza lamkunkhuniza! Dipo latipatsanso maziko amphamvu akuika chikhulupiriro m’malonjezo a Mulungu. Tikhoza kuwona kukonzedwa kwa chipulumutso chomwe “chikhazikika palamulo” kupyolera m’nsembe ya dipolo. (Ahebri 8:6, NW) Chotero dziko latsopano lolungama nlotsimikizirika!—Ahebri 6:16-19.
Musaphonye Chifuno Chake
17. (a) Kodi ena amasonyeza motani kuti achiphonya chifuno cha dipo? (b) Kodi nchiyani chingatisonkhezere kukhalabe oyera mwamakhalidwe?
17 Kuti tipindule ndi dipo, nkoyenera kuti munthu apeze chidziŵitso, asonyeze chikhulupiriro, ndikukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo ya Baibulo. (Yohane 3:16; 17:3) Komabe, ngochepa kwambiri omwe ali ofunitsitsa kuchita tero. (Mateyu 7:13, 14) Ngakhale pakati pa Akristu owona, ena “achivomereza chisomo cha Mulungu ndi kuphonya chifuno chake.” (2 Akorinto 6:1, NW) Mwachitsanzo, kwa zaka zambiri, anthu zikwi zambiri achotsedwa chifukwa cha mkhalidwe woipa wachisembwere. Nzamanyazi chotani nanga polingalira zinthu zimene Yehova ndi Kristu atichitira! Kodi kuyamikira dipo sikuyenera kusonkhezera munthu kupeŵa kukhala ‘woiwala matsukidwe ake potaya zoipa zake zakale’? (2 Petro 1:9) Pamenepo, Paulo akuŵakumbutsa Akristu moyenerera kuti: ‘Munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m’thupi lanu.’ (1 Akorinto 6:20) Kukumbukira ichi kumatipatsa chisonkhezero champhamvu cha kukhala oyera mwamakhalidwe!—1 Petro 1:14-19.
18. Kodi ndimotani mmene Mkristu amene wagwera m’tchimo lalikulu angapindulire ndi dipo?
18 Bwanji ngati munthu wagwera kale m’tchimo lalikulu? Iye ayenera kupindula ndi chikhululukiro chimene dipo limachitheketsa, akumalandira thandizo kuchokera kwa akulu achikondi. (Yakobo 5:14, 15) Ngakhale ngati chilango champhamvu chikufunikira, Mkristu wolapa sayenera kukhumudwa ndi chiwongolerocho. (Ahebri 12:5) Tiri ndi chitsimikiziro chodabwitsa ichi cha m’Baibulo: ‘Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chirichonse.’—1 Yohane 1:9.
19. Kodi Mkristu angakhale ndi lingaliro lotani la mayendedwe ake olakwika omwe anaŵachita asanaphunzire chowonadi?
19 Nthaŵi zina Akristu amakhala olefulidwa mosafunikira chifukwa cha mayendedwe oipa akalelo. Mbale wina wokhumudwitsidwa analemba kuti: “Tisanadziŵe chowonadi, mkazi wanga ndi ine tinayambukiridwa ndi matuza a kumpheto. Nthaŵi zina timadzilingalira kuti sitiri oyera, ngati kuti ‘sitikuyenerera’ m’gulu loyera la Yehova.” Kunena zowona, ngakhale pambuyo pa kukhala Akristu, ena angakhalebe ndi mavuto akutiakuti a zophophonya zawo zakumbuyo. (Agalatiya 6:7) Chikhalirechobe, palibe chifukwa chodzilingalira kukhala wodetsedwa m’maso mwa Yehova ngati munthuwe walapa. “Mwazi wa Kristu” ngwokhoza ‘kuyeretsa chikumbumtima chathu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa.’—Ahebri 9:14.
20. Kodi kukhulupirira dipo kungammasule motani Mkristu kuliŵongo losafunika?
20 Inde, chikhulupiriro m’dipo chingatithandize kumasula mavuto osafunikira akudzimva waliŵongo. Mlongo wina wachichepere anavomereza kuti: “Ndakhala ndikulimbana ndi chizoloŵezi chodetsedwa cha kuchita psotopsoto kwa zaka zoposa 11 tsopano. Nthaŵi ina ndinakhala nenene kuchoka mumpingo, ndikumalingalira kuti Yehova sangafune munthu wonyansa chotero kuipitsa mpingo wake.” Komabe, tiyenera kukumbukira kuti, Yehova ‘ngwabwino ndi wokhululukira’ malinga ngati timenyera mwakhama kutsutsana ndi kusayeruzika, osakugonjera!—Salmo 86:5.
21. Kodi dipo liyenera kuyambukira motani kulingalira kwathu anthu otichimwira?
21 Dipo liyeneranso kugwira ntchito m’zochita zathu ndi ena. Mwachitsanzo, kodi mumayankha motani ngati Mkristu mnzanu wakulakwirani? Kodi mumamsonyeza chikhululukiro chonga cha Kristu mofunitsitsa? (Luka 17:3, 4) Kodi ndinu ‘wachifundo, wakukhululukira ena, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu’? (Aefeso 4:32) Kapena kodi mumakonda kusungira zinthu kumtima kapena kufuna kubwezera? Ndithudi kuteroko kukakhala kuphonya chifuno cha dipo.—Mateyu 6:15.
22, 23. (a) Kodi dipo liyenera kukhala ndi chiyambukiro chotani pa zonulirapo ndi njira yathu ya moyo? (b) Kodi Akristu onse ayenera kupanga chosankha chotani ponena za dipo?
22 Chomalizira, kuyamikira dipo kuyenera kukhala ndi chiyambukiro chakuya pa zonulirapo ndi njira yathu ya moyo. Paulo anati: ‘Munagulidwa ndi mtengo wake; musakhale akapolo a anthu.’ (1 Akorinto 7:23) Kodi zosoŵa zachuma—nyumba, ntchito, zakudya, zovala—zidakali zinthu zazikulu m’moyo wanu? Kapena kodi mukufunafuna Ufumu choyamba, kukhulupirira malonjezo a Mulungu kuti adzakupatsani? (Mateyu 6:25-33) Kodi mungakhale kapolo wa bwana wanu koma nkulephera kupeza mpata wokwanira kaamba ka ntchito zateokratiki? Kumbukirani kuti, Kristu ‘anadzipereka yekha m’malo mwa ife . . . nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.’—Tito 2:14; 2 Akorinto 5:15.
23 ‘Tiyamika Mulungu mwa Yesu Kristu’ kaamba ka mphatso yabwino koposayi—dipo! (Aroma 7:25) Tisachiphonyetu chifuno cha dipo koma tichilole chikhale chisonkhezero chenicheni m’miyoyo yathu. M’malingaliro, m’mawu, ndi m’zochita, tiyeni nthaŵi zonse tilemekeze Mulungu, tikumakumbukira moyamikira kuti tinagulidwa ndi mtengo.
Mafunso Obwereramo
◻ Kodi nchifukwa ninji mwazi umalingaliridwa kukhala wopatulika, ndipo kodi ndimotani mmene mwazi wa Kristu unaperekedwera pamaso pa Yehova kumwamba?
◻ Kodi mwazi wa Kristu unachita mbali yotani m’kutsimikizira pangano latsopano?
◻ Kodi ndimotani mmene dipo limapi- ndulitsira odzozedwa ndi khamu lalikulu?
◻ Kodi tingasonyeze motani kuti sitinaphonye chifuno cha dipo?
[Chithunzi patsamba 16]
Mphamvu ya nsembe yotetezera iri m’mwazi wake wamoyo
[Chithunzi patsamba 17]
Munthu amene amayamikira kukhululukira kwa Mulungu amakhala wofunitsitsa kukhululukira ena