Dziŵani Bwino Abale Anu
1 Unansi wathu ndi olambira anzathu umaphatikizapo zoposa kungofika pamisonkhano pamodzi nawo pa Nyumba Yaufumu. Ndife ochita chifuniro cha Mulungu, ndipo zimenezo zimatiloŵetsa muunansi wauzimu ndi Yesu. (Marko 3:34, 35) Zimenezonso, zimatiloŵetsa muunansi wabanja wauzimu ndi ena mumpingo Wachikristu, abale ndi alongo athu auzimu, amene tikulamulidwa kuwakonda. (Yoh. 13:35) Motero, awo amene amayanjana ndi “a banja la Mulungu,” ayenera kuyesayesa kudziŵana bwino.—Aef. 2:19.
2 Dziŵani Abale Anu ndi Dzina: Kodi mumadziŵa maina a abale ndi alongo onse a m’Phunziro lanu Labuku Lampingo? Kaŵirikaŵiri kaguluko kamakhala kakang’ono, kukupangitsa kukhala kosavuta kudziŵa maina a ambiri, kapena onse amene amafikapo. Ngati simudziŵa nkomwe maina awo, kodi munganene kuti mumawadziŵa bwino?
3 Bwanji ponena za kudziŵa ena, kuphatikizapo ana, amene amafika pamisonkhano ku Nyumba Yaufumu? Tingakhale ndi chizoloŵezi cha kuyanjana ndi kagulu kakang’ono ka mabwenzi. Pamene kuli kwakuti sikulakwa kusangalala ndi mayanjano anthaŵi zonse ndi ena, sitidzafuna kulekezera moni waubwenzi ndi makambitsirano omangirira kwa oŵerengeka okha. Tiyenera ‘kukulitsidwa,’ tikumapanga kuyesayesa kudziŵa bwino abale ndi alongo athu onse. (2 Akor. 6:11-13) Mwachidziŵikire, zimenezo zikaphatikizapo kuwadziŵa ndi dzina.
4 Abale amene amachititsa misonkhano yampingo ayenera kuyesayesa kudziŵa maina a onse amene amafikapo. Kutchula aliyense ndi dzina lake kuchokera pa pulatifomu kumawapangitsa kulingalira kuti ndemanga zawo zimayamikiridwa, ndipo panthaŵi imodzimodziyo, zimathandiza ena kudziŵa maina awo. Ndithudi, nthaŵi zonse padzakhala achatsopano kapena alendo mwa omvetsera, kukupanga kukhala kovuta kwa aliyense kudziŵa dzina lililonse. Komabe, kuyesayesa kopitiriza koona mtima kumakhala kolimbikitsa kwa ena ndipo kumasonyeza chikondwerero chenicheni chaumwini.—Aroma 1:11, 12.
5 Khalani Woyamba Kuchitapo Kanthu Kuti Muwadziŵe: Oyang’anira oyendayenda kaŵirikaŵiri amakhala okhoza kudziŵa bwino chiŵerengero chachikulu cha abale ndi alongo. Kodi amachita zimenezi motani? M’njira zitatu zazikulu: (1) Nthaŵi zambiri amagwira nawo ntchito muutumiki wakumunda; (2) ngati mikhalidwe yawo ilola, amavomera ziitano za kuwachezera m’nyumba zawo; ndi (3) amakhala oyamba kupatsa moni akulu ndi ana omwe pamisonkhano.
6 Kodi mungaone njira zokulitsira mayanjano anu ndi kudziŵa bwino abale anu? Tikhoza kupempha ena kutsagana nafe muutumiki wakumunda. Kupita kunyumba ndi nyumba, kupanga maulendo obwereza, kupita kumaphunziro a Baibulo, kapena kuchita umboni wa magazini wa m’khwalala, zonsezo ndi njira zabwino koposa zodziŵanirana. Nkwabwinonso kuitana ena kubwera kunyumba kwanu, mwinamwake kudyera pamodzi chakudya kapena zakumwa zoziziritsa kukhosi. Kukhala woyamba kufikira atsopano kapena amene amachita manyazi sikudzangowamangirira mwauzimu komanso kudzabweretsa madalitso olemera.—Mac. 20:35; 1 Ates. 5:11.
7 Paulo anadziŵa bwino abale ake. Kutchula kwake ambiri a iwo ndi dzina m’makalata ake kuli umboni wa chikondwerero chake chopanda dyera ndi chikondi chake chenicheni kwa iwo. (1 Ates. 2:17; 2 Tim. 4:19, 20) Zoyesayesa zathu za kudziŵa bwino abale athu zidzatanthauza madalitso kwa tonsefe.