Tito—‘Wantchito Mnzanga Pokuthandizani’
MUMPINGO wachikristu wa m’zaka za zana loyamba munkabuka mavuto nthaŵi zina. Mavutowa anayenera kuthetsedwa, ndipo zimenezi zinafunikira kulimba mtima ndi kumvera. Mwamuna amene anakumana ndi mavuto amenewa kangapo ndi kuwathetsa anali Tito. Monga munthu amene anagwira ntchito ndi mtumwi Paulo, iye anayesetsa ndi mtima wonse kuthandiza ena kuchita zinthu m’njira ya Yehova. Choncho Paulo anauza Akristu a ku Korinto kuti Tito anali ‘wantchito mnzake powathandiza.’—2 Akorinto 8:23, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono.
Kodi Tito anali yani? Kodi anachita mbali yotani pothetsa mavuto? Ndipo kodi kudziŵa khalidwe lake kungatipindulitse motani?
Nkhani ya Mdulidwe
Tito anali Mgiriki wosadulidwa. (Agalatiya 2:3)a Popeza kuti Paulo anamutcha kuti “mwana wanga weniweni monga mwa chikhulupiriro cha ife tonse,” mwina Tito anali mmodzi wa ana auzimu a mtumwiyo. (Tito 1:4; yerekezerani ndi 1 Timoteo 1:2.) Tito anali ndi Paulo, Barnaba, ndi ena ochokera ku Antiokeya, Suriya, pamene anapita ku Yerusalemu cha m’chaka cha 49 C.E. kukakambirana nkhani ya mdulidwe.—Machitidwe 15:1, 2; Agalatiya 2:1.
Ena amati popeza kuti ku Yerusalemu kunali nkhani yokhudza kutembenuka kwa Akunja osadulidwa, Tito anatengedwa kukasonyeza kuti Ayuda ndi anthu osakhala Ayuda angapeze chiyanjo cha Mulungu kaya akhale odulidwa kapena osadulidwa. Ena a mumpingo wa ku Yerusalemu amene anali Afarisi asanalandire Chikristu ankanena kuti otembenuka Akunja ayenera kudulidwa ndi kutsatira Chilamulo, koma malingaliro amenewa anatsutsidwa. Kukakamiza Tito ndi Akunja ena kuti adulidwe kukanakhala kutsutsa mfundo yakuti chipulumutso chimadalira pa chisomo cha Yehova ndi kukhulupirira Yesu Kristu m’malo modalira ntchito za Chilamulo. Kukanakhalanso kukana umboni wakuti Akunja, kapena anthu amitundu, analandira mzimu woyera wa Mulungu.—Machitidwe 15:5-12.
Atumidwa ku Korinto
Nkhani ya mdulidwe itathetsedwa, Paulo ndi Barnaba anapatsidwa ufulu wonse wolalikira kwa amitundu. Panthaŵi imodzimodziyo, iwo anayesetsanso kukumbukira aumphaŵi. (Agalatiya 2:9, 10) Zoonadi, pamene Tito atchulidwanso m’malemba ouziridwa patapita zaka ngati zisanu ndi chimodzi, iye ali ku Korinto monga nthumwi ya Paulo imene ikulinganiza zopereka za oyera mtima. Koma pamene Tito anali kuchita ntchito imeneyi, anakumananso ndi mavuto ena ambiri.
Makalata a Paulo opita kwa Akorinto akusonyeza kuti choyamba anawalembera kuti ‘asayanjane ndi achigololo.’ Anawauza kuchotsa wachigololo wosalapayo amene anali pakati pawo. Inde, Paulo anawalembera kalata yamphamvu, kuchita zimenezo “ndi misozi yambiri.” (1 Akorinto 5:9-13; 2 Akorinto 2:4) Zidakali choncho, Tito anatumidwa ku Korinto kukathandiza kusonkhanitsa zinthu za Akristu osoŵa a ku Yudeya zimene zinali kusonkhanitsidwa kumeneko. Mwina anatumidwanso kuti akaone mmene Akorinto akulabadirira kalata ya Paulo.—2 Akorinto 8:1-6.
Kodi Akorinto anatani ndi uphungu wa Paulo? Pofunitsitsa kudziŵa, Paulo ayenera kuti anatumiza Tito kuchokera ku Efeso kutsidya kwa Nyanja ya Aegean kupita ku Korinto, atalangizidwa kuti abwere ndi lipoti mwamsanga. Ngati akanamaliza ntchito imeneyi zombo zisanasiye kuyenda chifukwa cha chisanu (chapakati pa November), Tito akanapita ku Trowa pachombo kapena akanadzera njira yaitalipo ya pamtunda yodzera ku Hellespont. Paulo ayenera kuti anafika msanga pamalo amene anagwirizana kuti adzakumane ku Trowa, popeza kuti chipoloŵe chimene osula siliva anayambitsa chinampangitsa kuti anyamuke msanga ku Efeso panthaŵi imene sanayembekezere. Ku Trowa, maso ali kunjira, Paulo anazindikira kuti Tito sadzadzera panyanja. Choncho, Paulo anauyamba ulendo wa pamtunda nchiyembekezo chokumana naye m’njira. Atafika ku Ulaya, Paulo anadzera msewu wa Via Egnatia, ndipo pomalizira pake anakumana ndi Tito ku Makedoniya. Paulo anamva mpumulo waukulu nasangalala kwambiri chifukwa chakuti mbiri yochokera ku Korinto inali yabwino. Mpingowo unatsatira uphungu wa mtumwiyo.—2 Akorinto 2:12, 13; 7:5-7.
Ngakhale kuti Paulo anadera nkhaŵa za mmene nthumwi yake adzailandirira, Mulungu anathandiza Tito kukwaniritsa ntchito yake. Tito analandiridwa ndi “mantha ndi kunthunthumira.” (2 Akorinto 7:8-15) Kugwiritsa ntchito mawu a wothirira ndemanga W. D. Thomas: “Tinganene kuti popanda kuchepetsa mphamvu ya chidzudzulo cha Paulo, [Tito] anachonderera Akorinto mwaluso ndiponso mwanzeru; kuwatsimikizira kuti Paulo, polankhula momwe analankhuliramo, anali kungowafunira zabwino zauzimu.” M’kupita kwa nthaŵi, Tito anawakonda kwambiri Akristu a ku Korinto chifukwa cha mzimu wawo womvera ndi kusintha kwabwino kumene anapanga. Mzimu wawo wabwinowo unamlimbikitsa.
Nanga za mbali inayo ya ulendo wa Tito wa ku Korinto—kulinganiza zopereka zopita kwa oyera mtima a ku Yudeya? Malinga ndi chidziŵitso chimene timapeza pa 2 Akorinto, tinganene kuti Tito anali kuchitanso zimenezo. Kalata imeneyo iyenera kuti inalembedwa ku Makedoniya chakumapeto kwa 55 C.E., Tito ndi Paulo atangokumana kumene. Paulo analemba kuti Tito, amene anayambitsa zoperekazo, anali atatumidwanso komweko ndi omthandiza ena aŵiri amene sanawatchule maina kuti akamalizitse ntchitoyo. Pokhala wowaderadi nkhaŵa Akorinto, Tito anali wofunitsitsa kubwerera. Pamene Tito anali paulendo wobwerera ku Korinto, ayenera kuti anali atanyamula kalata yachiŵiri youziridwa ya Paulo yopita kwa Akorinto.—2 Akorinto 8:6, 17, 18, 22.
Tito sanali chabe wolinganiza wabwino koma analinso mwamuna amene anatha kupatsidwa ntchito zovuta m’mikhalidwe yovuta. Anali wolimba mtima, wofikapo, ndiponso wochirimika. Mwachionekere, Paulo anaona kuti Tito akhoza kulimbana nawo mavuto ochititsidwa ndi “atumwi oposatu” a ku Korinto. (2 Akorinto 11:5) Tikutsimikizira kuti Tito anali wotero pamene akutchulidwanso m’Malemba, ali pantchito inanso yovuta.
Pachisumbu cha Krete
Nthaŵi inayake pakati pa 61 ndi 64 C.E., Paulo ayenera kuti analemba kalata kwa Tito, amene panthaŵiyo anali kutumikira pachisumbu cha Krete ku Mediterranean. Paulo anamsiya komweko kuti ‘alongosole zosoŵa’ ndi ‘kuika akulu m’midzi yonse.’ Akrete ankadziŵika kukhala “amabodza . . . , zilombo zoipa, aumbombo, aulesi.” Choncho, ku Krete, Tito anafunikira kuti alimbe mtima ndiponso achirimike. (Tito 1:5, 10-12) Imeneyo inali ntchito yofunika kwambiri, chifukwa chakuti tsogolo la Chikristu pachisumbucho linadalira pantchitoyo. Mouziridwa, Paulo anathandiza Tito mwa kutchula zinthu zenizeni zimene ayenera kuona mwa anthu amene angakhale oyang’anira. Ziyeneretso zimenezo nzimene zimafunidwanso poika akulu achikristu.
Malemba sanena pamene Tito anachoka ku Krete. Anakhalako kwautali woti Paulo anampempha kusamalira Zena ndi Apolo, amene, paulendo wawo, anali kudzaima kumeneko panthaŵi inayake yosatchulidwa. Koma Tito sanakhalepo nthaŵi yaitali kwambiri pachisumbucho. Paulo anali kukonzekera kutumizako Artema kapena Tukiko, ndiyeno Tito anayenera kukakumana ndi mtumwiyo ku Nikopoli, umene uyenera kuti unali mzinda waukulu kumpoto cha kumadzulo kwa Girisi.—Tito 3:12, 13.
Nthaŵi yomaliza pamene Baibulo litchula Tito mwachidule, tikuphunzirapo kuti cha mu 65 C.E., Paulo ayenera kuti anamtuma kupitanso kwina. Iye anapita ku Dalimatiya, dera la kummaŵa kwa Nyanja ya Adriatic kumene tsopano ndi ku Croatia. (2 Timoteo 4:10) Sitikuuzidwa kuti Tito anapita kukatani kumeneko, koma ena akuti anatumidwa kukasamalira nkhani zina za mumpingo ndi kuchita umishonale. Ngati zili motero, Tito anali kuchita ntchito yofanana ndi imene anali kuchita ku Krete.
Timawathokoza chotani nanga oyang’anira achikristu ofikapo onga Tito! Kumvetsa kwawo bwino mapulinsipulo a m’Malemba ndi kuwagwiritsa ntchito kwawo molimba mtima zimathandiza kuteteza mkhalidwe wauzimu wa mpingo. Tiyeni titsanzire chikhulupiriro chawo ndi kukhala monga Tito mwa kuchirikiza zinthu zauzimu za okhulupirira anzathu.—Ahebri 13:7.
[Mawu a M’munsi]
a Agalatiya 2:3 amanena kuti Tito anali Mhelene (Helʹlen). Zimenezi zingatanthauze kuti makolo ake anali Agiriki. Komabe, ena amati olemba Chigiriki ena ankagwiritsa ntchito liwu lochulukitsa zinthu (Helʹle·nes) ponena za anthu osakhala Agiriki amene anali Agiriki chifukwa cha chinenero ndi chikhalidwe chawo. Nzotheka kuti Tito anali Mgiriki m’lingaliro limeneli.
[Chithunzi patsamba 31]
Tito anali wantchito mnzake wa Paulo wolimba mtima pothandiza Akristu a ku Korinto ndi a kumalo ena