Mpatsi wa “Mphatso Iliyonse Yabwino”
“Nthaŵi ina ndinaitanidwa ndi mbusa wa tchalitchi cha Reformed. Iye anafuna kudziŵa mmene ndinayendetsera tchalitchi changa. Ndinati kwa iye: . . . ‘Sitimalandiritsa malipiro; palibe chochititsa anthu kukangana. Sitimasonkhetsa chopereka.’ ‘Kodi ndalama mumazipeza bwanji?’ iye anafunsa motero. Ndinayankha kuti, ‘Onani, Bambo——, ngati ndikuuzani chowonadi chenicheni simudzakhulupirira konse. Pamene anthu akondwerera m’njirayi, samaona mbale ya chopereka ikupititsidwa kwa iwo. Koma amaona kuti pali zinthu zofuna ndalama. Iwo amaganiza paokha kuti, “Nyumba yosonkhanirayi imafuna ndalama. . . . Kodi ndingapeze motani kandalama koti ndithandizire?”’ Anandiyang’ana monga ngati kuti analingalira kuti, ‘Kodi wandiyesa ndani—mlendo wosadziŵa kanthu?’ Ndinati, ‘Tsopano, Bambo——, ndikukuuzani chowonadi. . . . Pamene wina apeza dalitso ndipo ali nacho chuma, amafuna kuchigwiritsira ntchito kwa Ambuye. Ngali alibe chuma, nkumuvutitsiranji kuti mpaka apereke?’”
—Charles T. Russell, prezidenti woyamba wa Watch Tower Society, “The Watch Tower,” July 15, 1915.
TIMAPATSA chifukwa chakuti Yehova Mulungu anali woyamba kupatsa. Kupatsa kwake kunayamba ndi chilengedwe kalekale zaka zosaŵerengeka—cholengedwa chake choyamba chenichenicho, “Mwana wake wobadwa yekha.” (Yohane 3:16) Chifukwa cha chikondi, iye anapatsa mphatso ya moyo kwa ena.
Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, ndiye mphatso yaikulu koposa imene Yehova watipatsa. Koma kupatsa kwa Mulungu sikunathere pakupereka Mwana wakeyo. “Chisomo choposa cha Mulungu,” ndimmene mtumwi Paulo akutchulira ‘mphatso yosatheka kuneneka’ ya Yehova. (2 Akorinto 9:14, 15) Mwachionekere mphatso imeneyi imaphatikizapo maubwino onse ndi kukoma mtima kwachikondi kumene Mulungu amapereka kwa anthu ake kupyolera mwa Yesu. Chisomo choposa chimenecho nchodabwitsa kwakuti sichitha kulongosoleka ndi munthu. Komabe, palinso mbali zina za kupatsa kwa Mulungu.
Kalekale, mfumu ina mwanzeru ndi modzichepetsa inavomereza kuti zinthu zabwino zilizonse zimene inazipereka monga mphatso zinali kwenikweni za Yehova. Iyo inati: “Pakuti zonse zam’mwamba ndi padziko lapansi ndizanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse. . . . Koma ndiye yani, ndi anthu anga ndiwo ayani, kuti tidzakhoza kupereka mwaufulu motere? popeza zonsezi zifuma kwanu; takupatsani zofuma ku dzanja lanu.”—1 Mbiri 29:11-14.
Chitsanzo cha Mulungu
Yakobo, wophunzira wa Yesu Kristu, anadziŵa kuti Yehova Mulungu ndiye magwero a chinthu chilichonse chabwino m’njira iliyonse. Mphatso zangwiro zokha nzimene zichokera kwa iye. Yakobo analemba kuti: “Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.”—Yakobo 1:17.
Ngakhale m’nkhani ya kupereka mphatso, Yakobo anaona mmene Mulungu aliri wosiyana ndi anthu. Anthu akhoza kupatsa mphatso zabwino koma samatero nthaŵi zonse. Mphatso zimenezi zingapatsidwe ndi cholinga chadyera, kapena zingagwiritsiridwe ntchito kunyenga munthu kuti achite choipa. Kwa Yehova kulibe chisanduliko; iye sasintha. Chifukwa chake, mtundu wa mphatso zake sumasintha. Nthaŵi zonse zimakhala zenizeni. Nthaŵi zonse zimachirikiza ubwino ndi chimwemwe cha mtundu wa anthu. Nthaŵi zonse zimakhala za kukoma mtima ndi zothandiza, zosavulaza konse.
Zolinga Zoperekera Mphatso
M’masiku a Yakobo, atsogoleri achipembedzo otchuka anali kupereka mphatso ndi cholinga cha kungoonedwa ndi anthu. Iwo anapatsa ndi cholinga choipa. Pofunitsitsa kuthokozedwa ndi anthu, iwo analolera molakwa miyezo yawo yachilungamo. Komabe, Akristu anafunikira kukhala osiyana. Yesu anawalangiza kuti: “Pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamawomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m’masunagoge, ndi m’makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, iwo alandiriratu mphotho zawo. Koma iwe popatsa mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziŵe chimene lichita dzanja lako lamanja; kotero kuti mphatso zako za chifundo zikhale zamseri; ndipo Atate wako wakuona mseri adzakubwezera iwe.”—Mateyu 6:2-4.
Chifukwa cha Mkristu choperekera mphatso ndicho kuthandiza ena kukwaniritsa chosoŵa kapena kuwachititsa kukhala achimwemwe kapena kuchirikiza kulambira kowona. Sikuli kaamba ka kudzitamandira. Ndi iko komwe, maso a Yehova akhoza kuona za mkati mwenimweni mwa mtima wathu. Iye akhoza kuona cholinga cha mkati cha mphatso zathu zachifundo.
Mboni za Yehova zikuyesetsa kutsanzira chitsanzo cha Yehova ndi Mwana wake m’kupereka mphatso. Izo zimapereka zimene zili nazo. Zili ndi mbiri yabwino ya Ufumu, ndipo zimaipereka kuti ena adalitsike. Zimadziŵa kuti lemba la Miyambo 3:9 limati: “Lemekeza Yehova ndi chuma chako, ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha.” Chifukwa chakuti ofesi ya nthambi iliyonse, mpingo, ndi munthu aliyense mowona mtima amafuna kuthandizira ubwino wa onse, gulu lonse la abale limalimbitsidwa mwauzimu ndi kulemerera. Kulemerera kwakuthupi sikumatsogolera ku kulemerera kwauzimu, koma kulemerera kwauzimu kumadzetsa kulemerera kwakuthupi kokwanira kuchitira ntchito ya Yehova.
Njira Zokhaliramo ndi Mbali
Pali njira zambiri zimene aliyense angapatsire chopereka kuchirikiza mbiri yabwino. Imodzi ya njirazo ndiyo ya Nyumba Zaufumu. Ziŵalo zonse za mpingo zimagwiritsira ntchito Nyumba Yaufumu. Winawake anapereka ndalama kuti imangidwe kapena kulipirira ngongole, magetsi, ziŵiya zofunditsa kapena kuziziritsa, ndi kuisamalira. Popeza kuti kuchirikiza mpingo kwa aliyense nkofunika, mabokosi a zopereka amaikidwa mu Nyumba Yaufumu, ndipo zopereka zaufulu zolandiridwazo zimagwiritsiridwa ntchito kulipirira zowonongedwa za mpingo. Kuchokera pa zotsalapo, zopereka zikhoza kutumizidwa kunthambi yamomwemo ya Watch Tower mogwirizana ndi chosankha cha mpingo.
Zopereka zikhoza kutumizidwa kunthambi ya Sosaite kaamba ka kuphunzitsa ndi kuchirikiza amishonale ndi apainiya apadera m’mbali za dziko kumene mbiri yabwino siinafikire anthu ochuluka. Zolipirira zina m’kufalitsidwa kwa mbiri yabwino zimaloŵetsamo ntchito ya oyang’anira oyendayenda. Mtumwi Paulo, amene anapereka chitsanzo cha ntchito yoyendayenda m’zaka za zana loyamba, anayamikira mpingo mu Filipi kuti: “Munanditumizira pachosoŵa changa kamodzi kapena kaŵiri.” (Afilipi 4:14-16) Kuwonjezera pa zolipirira za mbali zimenezi za utumiki wa nthaŵi yonse, zimene nthambi zonse zili nazo, palinso kusamalira nyumba ya Beteli iliyonse ndi awo amene amakhalapo ndi kugwira ntchito pamenepo. Kulembedwa ndi kusindikizidwa kwa mabuku amene ali ndi uthenga wabwino kwambiri wa mbiri yabwino kulidi mwaŵi wopatsidwa ndi Mulungu, koma kufalitsidwa kwa mabukuwo kulinso kofunika, ndipo kumafuna ndalama. Ndiyeno pamafunika ndalama zolipirira misonkhano yadera ndi yachigawo, kuphatikizaponso milandu ya m’khoti imene yaimbidwa “kuchinjiriza ndi kukhazikitsa mwalamulo uthenga wabwino.”—Afilipi 1:7, NW.
Nthaŵi yowonongeredwa m’kulalikira mbiri yabwino ndi mtumiki aliyense wa Yehova njodzifunira, ndipo kupereka kwake ndalama kulinso motero. Kupatula ndalama kokhazikika zogwiritsiridwa ntchito m’kuchirikiza kulambira kowona kukulangizidwa ndi mtumwi Paulo kuti: “Koma za chopereka cha kwa oyera mtima, . . . tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula.”—1 Akorinto 16:1, 2.
Pamene munthu apatsa chopereka, iye samadziŵa nthaŵi zonse mmene chidzagwiritsidwira ntchito kwenikweni, koma amaona zotulukapo zake m’kufutukuka kwa kulalikira Ufumu. Malipoti a mu 1993 Yearbook of Jehovah’s Witnesses amasonyeza kuti mbiri yabwino ya Ufumu ikulalikidwa ndi atumiki Achikristu oposa 4,500,000 m’maiko oposa 200 kuphatikizapo zisumbu za m’nyanja. Malipoti ameneŵa ali othutsa mtima. Motero, mphatso iliyonse, mosasamala kanthu za ukulu wake, imathandiza m’kufalitsidwa kwa mbiri yabwino padziko lonse.
Ntchito imeneyi imalipiriridwa mwa kupereka kwa onse. Ena ali okhoza kupereka zambiri, zimene zimathandiza ntchito yolalikira pamlingo waukulu. Ena amapereka zocheperapo. Koma awo amene amapereka zochepa sayenera kukhala amanyazi kapena kulingalira kuti mbali yawo njosafunikira. Ndithudi Yehova samalingalira mwanjirayo. Yesu anamveketsa zimenezi bwino lomwe pamene anasonyeza mmene Yehova anayamikirira kwambiri kandalama ka mkazi wamasiye. “Ndipo anaona mkazi wina wamasiye waumphaŵi alikuika momwemo timakobiri tiŵiri. Ndipo iye anati, Zowonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphaŵi anaikamo koposa onse; pakuti onse ameneŵa anaika mwa unyinji wawo pa zoperekazo; koma iye mwa kusoŵa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo.”—Luka 21:2-4.
Zilibe kanthu kuti mkhalidwe wathu wa ndalama uli wotani, tikhoza kupatsa m’njira zokondweretsa Yehova. Wamasalmo akutchula bwino mwachidule mmene tingaperekere ulemerero kwa Mfumu ndi Woweruza wathu. Iye akuti: “Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lake; bwerani nacho chopereka, ndipo fikani kumabwalo ake.” (Salmo 96:8) Chifukwa chake, tiyeni titsanzire chitsanzo chachikondi cha Atate wathu wakumwamba mwa kupatsa kwathu mphatso mokondwerera chifukwa chakuti iye anayamba kutipatsa.
[Bokosi patsamba 30]
MMENE ENA AMAPATSIRA ZOPEREKA KU NTCHITO YOLALIKIRA UFUMU
◻ ZOPEREKA ZA NTCHITO YAPADZIKO LONSE: Ambiri amaika pambali kapena kulinganiza ndalama zimene amaika m’mabokosi azopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito Yapadziko Lonse ya Sosaite—Mateyu 24:14.” Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalamazi kaya ku malikulu a dziko lonse ku Brooklyn, New York, kapena ku ofesi yanthambi yapafupi.
◻ MPHATSO: Zopereka zodzifunira za ndalama zingatumizidwe mwachindunji ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 25 Columbia Heights, Brooklyn, New York 11201, kapena ku ofesi ya Sosaite ya nthambi yakwanuko. Zokongoletsa kapena zinthu zina zamtengo wapatali zingaperekedwenso. Kalata yachidule yofotokoza kuti zimenezo zaperekedwa monga mphatso iyenera kutsagana ndi zoperekazo.
◻ CHOPEREKA CHOTCHEDWA CONDITIONAL-DONATION: Ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society kuti ziyikiziridwe kumeneko kufikira imfa ya woperekayo, limodzi ndi makonzedwe akuti ngati pakhala kusoŵa kwaumwini, zidzabwezeredwa kwa woperekayo.
◻ INSHUWALANSI: Watch Tower Society ingalembetsedwe kuti ndiyo idzapatsidwa mapindu a inshuwalansi kapena penshoni. Sosaite iyenera kuuzidwa za makonzedwe alionse otero.
◻ MAAKAUNTI A KU BANKI: Maakaunti a banki, zikalata zoikizira ndalama, kapena maakaunti a anthu opuma ntchito angalembedwe moikizira ku Watch Tower Society kapena kulembedwa kuti wolipiridwa pambuyo pa imfa akhale Watch Tower Society, mogwirizana ndi malamulo a mabanki amomwemo. Sosaite iyenera kuuzidwa za makonzedwe aliwonse.
◻ STOCK NDI BOND: Stock ndi bond ingapatsidwe monga chopereka ku Watch Tower Society kaya monga mphatso yachindunji kapena mwa kakonzedwe kamene ndalama zolandiridwa zikupitirizabe kulipiridwa kwa woperekayo.
◻ REAL ESTATE: Chuma chotchedwa real estate chokhoza kugulitsidwa chingaperekedwe ku Watch Tower Society kaya mwa kuchipereka monga mphatso yachindunji kapena mwakusungidwa kwa chumacho ndi mwini wake amene angapitirizebe kukhala nacho kufikira imfa yake. Munthuyo ayenera kuuza Sosaite asanailoŵetse m’pangano la chuma chilichonse chotero.
◻ WILL NDI TRUST: Chuma kapena ndalama zingakhale choloŵa ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania kudzera mwa pangano la amene adzatenga chuma chamasiye lovomerezedwa mwa lamulo, kapena Sosaite ingalembetsedwe kukhala yodzapindula ndi pangano loikizira chuma. Pangano loikizira chuma lopindulitsa gulu lachipembedzo lingakhale ndi mapindu ena olandira msonkho. Kope la pangano la will kapena trust liyenera kutumizidwa ku Sosaite.
Kuti mupeze chidziŵitso chowonjezereka pankhani zotere, lemberani ku Treasurer’s Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku ofesi ya Sosaite ya nthambi yakwanuko.
[Zithunzi patsamba 31]
Mmene zopereka zanu zimagwiritsidwira ntchito:
1. Odzipereka a pa Beteli
2. Kumanga ofesi ya nthambi
3. Zothandiza patsoka
4. Nyumba Zaufumu
5. Amishonale