Ana—Musanyengedwe
“Satana yemwe adziwonetsa ngati mngelo wakuunika.”—2 AKORINTO 11:14.
1. (a) Kodi ndi’mnjira zotani m’zimene unyinji wa ife tanyengedwera? (b) Kodi ndani, amene kawirikawiri, amanyengedwa mosavuta?
MOSAKAIKIRA tonsefe tinanyengedwapo panthawi ina. Mwinamwake munali kusewera sewero m’limene wosewera wotsutsana nayeyo anachita mwachinyengo nakuchotsani pamalo anu ndipo motero nagoletsa kuwina sewerolo. Kapena mungakhale mutagula chovala chamawonekedwe abwino, ndiyeno nkupeza kuti mutachivala nthawi yaifupi ndipo mutachichapa chovalacho sichinali chamkhalidwe umene chinawonekera kukhala. Kodi ndani, amene kawirikawiri amanyengedwa mosavuta kwambiri, ndiko kuti, kupusitsidwa kapena kunamizidwa? Kodi siawo amene ali ndi chidziwitso chocheperapo? Ndipo kawirikawiri zotulukapo ziri zowopsa kwambiri kuposa kuluza sewero kapena kunyengedwa pa chinthu chogulidwa.
2. Kodi ndimotani mmene ana ena alowetsedwera m’kuchita choipa chachikulu?
2 Mwachitsanzo, Julie wophunzira wokhala m’chaka chachiwiri chabe m’sukulu yapamwamba, monga momwe iyemwini, ananenera, “anapalana ubwenzi” ndi “mnyamata wokongola koposa ndi wotchuka pasukulu ponsepo.” Iye akulongosola kuti: “Ndinamuuza kuti sindinakonzekere kuchita zimene anali kufuna, koma anapitirizabe kundiuza mmene anandikondera kwambiri, ndi kuti zonse zikayenda bwino. Pamene ndinanenabe kuti ayi, mpamene anandinyengerera kwambiri. Iye nati, ‘ndimakuderadi nkhawa, ndipo ndinaganiza kuti iwe umalingalira mwanjira yofananayo. Ngati sudzanditsimikizira, ndiganiza kuti tidzangofunikira kuleka kukondana.’ ” Chotero Julie analepa nachita dama lachigololo. Tsiku lotsatira, pamene anamva kuti mnyamatayo anadzitamandira ponenaza “chilakiko” chake, msungwanayo anazindikira mmene anali atanyengedwera kotheratu. Iye akanadziwa kuti ngati mnyamatayo anamkondadi sakanachita motero.
3. (a) Kodi nchifukwa ninji dama la chigololo liri uchimo wowopsa motero? (b) Kodi nchiyani chimene chiri cholinga cha Satana Mdyerekezi?
3 Chimene Julie anapusitsidwa kapena kunyengedwa kuti alowemo ndicho kuswedwa kwa lamulo la Mulungu kowopsa. Chifukwa cha chimenecho Baibulo limalimbikitsa kuti: “Thawani dama.” Ndipo limalongosola momvekera bwino kuti: “Wadama yense . . . alibe cholowa mu ufumu wa Kristu ndi Mulungu.” (1 Akorinto 6:18; Aefeso 5:5) Chotero pamene kuli kwakuti Satana Mdyerekezi angakhale wosadera nkhawa kuti kaya mudzawina kapena kuluza seŵero lampira kapena kugula mwanzeru kapena ayi, iye akuyesa motsimikizira kukusochezani kuti muswe lamulo la Mulungu. “Mdani wanu Mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire,” Baibulo limachenjeza. (1 Petro 5:8) Ndithudi, akugwiritsira ntchito kuganiza kwake kwamachenjera, kuphatikizapo kuchita ngati mngelo wakuunika, kutifufunula m’kutumikira Yehova Mulungu! Kodi limenelo siliri lingaliro lochenjeza?—2 Akorinto 11:14.
Phunzirani m’Zimene Zinachitikira Hava
4. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti ana ali chandamale chapadera cha Satana?
4 Koma kwa achicheperenu iri liridi lingaliro lochenjeza kwambiri lakuti: Ndinu chandamale chapadera cha Satana. Chifukwa ninji ziri choncho? Chifukwa cha ubwana wanu, muli ndi nthawi yochepa imene mwapeza chidziwitso ndi nzeru ndipo Satana amasankha achidziwitso chocheperapo. Iye anachita motero pachiyambi penipeni pa chipanduko chake. Kumbukirani kuti anafika kwa Hava m’munda wa Edene, osati kwa mwamuna wake amene analengedwa zaka zambiri mkaziyo asanalengedwe. Ndipo. Satana anapeza chipambano. Ananyenga, inde, anasocheza mwamawonekedwe onyenga wocheperapoyo ndi wachidziwitso chochepa Hava. “Pakuti Adamu anayamba kulengedwa,” limalongosola motero Baibulo, “pamenepo Hava. Ndipo Adamu sananyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa analoŵa m’kulakwa.”—1 Timoteo 2:13, 14.
5. (a) Kodi sitiyenera kunyengedwa konse kulingalira motani? (b) Kodi nchiyani chimene chinali nkhawa ya mtumwi Paulo, ndipo nchifukwa ninji inali yoyenerera?
5 Musakopedwere m’kulingalira kuti njira za Satana sizingagwire ntchito pa inu, kuti iye sangathe konse kukuchititsani kuswa malamulo a Mulungu. Kumbukirani chenjezo laumulungu lakuti “Satana yemwe adziwonetsa ngati mngelo wakuunika.” (2 Akorinto 11:14) Mtumwi Paulo anali wodera nkhawa moyenerera kuti Wonyenga Wamkulu angapeze chipambano m’kufikira kwake Akristu anzake a Paulo a chidziwitso chocheperepo. Paulo analemba kuti: “Ndiwopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Hava ndi kuchenjera kwake, maganizo anu angaipitsidwe kusiyana nako kuwona mtima ndi kuyera mtima ziri mwa Kristu.”—2 Akorinto 11:3.
6. Kodi kunyengedwa kumatanthauzanji?
6 Tawonani kuti Hava sanangonamizidwa kokha kapena kupusitsidwa; iye ananyengedwanso. Ichi chitanthauza kuti anakokedwera m’njira yowononga mwachinyengo chokopa kapena chiyeso. Mogwirizana ndi kunena kwa Webster’s Third New International Dictionary kunyenga kumatanthauza “kukopedwera m’kusamvera,” “kukopa kapena kupeza mwa kapena monga ngati kuti ndi nyambo ya machenjera yobisika.” Kwenikweni, m’bukhu lomasulira mawu limeneli limati, kunyenga kumatanthauza “kunyengerera (mkazi) kuti mugone naye kwanthawi yoyamba.” Tingathe kupindula mwa kupenda njira ya Satana ya kunyengera Hava (ngakhale kuti panthawi iyi kugonana sikunaphatikizidwe), ndiponso mwa kuyang’anitsitsa njira zofananazo zimene amagwiritsira ntchito lerolino.
7, 8. (a) Kodi nchiyani chimene chinali chifuno cha funso la Satana kwa Hava? (b) Kodi ndimotani mmene Satana anapangitsira kudya za m’mtengo kuwonekera kukhala kosonkhezera mtima motero?
7 Pachiyambi penipeni pa kufika kwake, Satana, mwanjira yamachenjera, anagwiritsira ntchito njoka kuchititsa Hava kuyamba kukaikira lamulo la Mulungu. Mwa mawu olinganizidwa mosamalitsa kudzutsa chikaikiro ndi kunyumwa, iye anafunsa kuti: “Kodi anatitu Mulungu, usadye mitengo yonse ya m’mundamu? Mwa funso lotchera msampha limemeli, Satana anali kutanthauza kuti kunali komvetsa chisoni kuti sanali wokhoza kudya m’mitengo yonseya m’munda. Kwenikweni, iye anatsutsa kuti, mmalo mwa kufa monga momwe Mulungu adanenera, kudya za mtengo woletsedwa kukampindulitsadi. “Adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu wakudziwa zabwino ndi zoipa.”—Genesis 3:1-5.
8 Ndimachenjera oipa chotani nanga a Satana a kupereka lingaliro lakuti Mulungu anali kuyesa kumana chidziwitso chopindulitsa kwa Hava! Mogwirizana ndi kunena kwa Satana, Mulungu anali kugwiritsiradi ntchito chiwopsezo chopanda pake cha imfa kumletsa kugwiritsira ntchito luso la kudzisankhira. ‘Wawona nanga, ukuluza!’ Kwenikweni, iye, anauza Hava. ‘Simudzafai. Mungathe kusangalala ndi zimene Mulungu amasangalala nazo. Mungathe kudzisankhira inumwini chabwino kapena choipa.’ Zinakondweretsa Hava kukhala wokhoza kudzipangira zosankha za iyemwini popanda kufunikira kuwerengera kwa munthu aliyense.
9. Monga momwe kwasonyezedwera m’Yakobo1:14, 15; kodi ndimtandadza wa zochitika zotani umene unatsogolera kuuchimo wa Hava ndipopotsirizira pake imfa?
9 Monga chotulukapo, Hava anayamba kuyang’ana mtengowo ndi chilakolako. “Pamenepo anawona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma mmaso, mtengo wolakalakika wa kupatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya.” (Genesis 3:6) Koma pambuyo pake, pamene Hava anapeza kuti sanalandira zimene analonjezedwa, anadandaula kuti: “Njoka—inandinyenga ine.” (Genesis 3:13) Kwenikweni, inali itamnyengerera, ikumamchititsa kugonjera chilakolako chokopa kapena chiyeso kufikira chikhumbo chadyera chinamchititsa kuchimwa ndipo, monga chotulukapo, potsirizira pake kufa.—Yakobo 1:14, 15.
Chenjerani ndi Machenjera a Satana
10. Kodi nchifukwa ninji sitimafunikira kukhala opulukira pamachenjera a Satana, ndipo ndimalangizo ati amene kuli kwanzeru kuwatsatira?
10 Satana amagwiritsira ntchito machenjera ofanana, ndiko kuti, ziwembu, maluso, ndi ukapsala, kunyenga ndi kunyengerera ana lerolino. Koma popeza kuti Baibulo limapereka mbiri yachikwanekwane yanjira za chinyengo za Satana, simufunikira kukhala opulukira kumachenjera ake. (2 Akorinto 2:11) Chimene mufunikira ndicho kukhala ndi tcheru la kulabadira machenjezo ndi malangizo amene Yehova Mulungu amapereka kudzera mwa Mawu ake ndi gulu.—Miyambo 2:1-6; 3:1-7, 11, 12; 4:1, 2, 20-27; 7:1-4.
11. Kodi ndimotani mmene kawirikawiri Satana amanyengera kapena kunyengererera ana kulowa m’kuchita cholakwa?
11 Kodi ndimotani mmene Satana amanyengerera kawirikawiri kapena kukopa achichepere kulowa m’kuchita cholakwa? Iye amatero mwa kupangitsa zimene Mulungu amatsutsa, kapena ntchito zimene zingatsogolere ku kutayikiridwa ndi chiyanjo cha Mulungu, kuti ziwonekere kukhala zokongola, chikhalirechobe panthawi imodzimodziyo monga zosavulaza, monga momwedi chipatso chinawonekerera kwa Hava. Ndipo monga momwe anachitira kwa Hava, iye adzayesa kugwiritsira ntchito lingaliro lakuti mukuluza kanthu kena kokondweretsa mosayenerera. Motero, mwanjira ya machenjera, yonyenga Satana amayesayesa kufooketsa kuchitira ulemu kwanu Mawu a Yehova, kudzanso malangizo operekedwa ndi makolo anu owopa Mulungu ndi gulu la Mulungu. Motero pali chifukwa chabwino kuti Baibulo limalimbikitsa kuti, ‘Chirimikani pokana machenjero [kapena monga momwe The Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures imanenera kuti, “machitachita aukapsala,”] a Mdyerekezi.”—Aefeso6:ll.
12. (a) Kodi ndichenicheni chotani chonena za Satana chimene tonsefe tiyenera kuchiwona mwamphamvu, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi timawona motani zimene zanenedwa pa 1 Yohane 2:15 ndi Yakobo 4:4? (c) Kodi Satana akanafuna kuti akunyengeni kuti mukhulupirire chiyani?
12 Mwachiwonekere, Hava anapusa kukhulupiria bodza la Mdyerekezi. Komabe mofananamo kodi ana ambiri lerolino samawawona mopepuka machenjezo ndi Mawu a Yehova kapena operekedwa ndi makolo awo kapena akulu Achikristu? Bwanji ponena za inu? Mwachitsanzo, kodi mumawona mwamphamvu chenicheni chakuti Satana Mdyerekezi ali wolamulira wa dziko lino ndi kuti monga mulungu wa dongosolo iri la zinthu akuchititsa khungu maganizo a anthu? (1 Yohane 5:19; Yohane 12:31; 14:30; 16:11; 2 Akorinto 4:4) Kodi mumayesayesadi kulabadira lamulo la Mulungu lakuti: “Musakonde dziko lapansi kapena za m’dziko lapansi”? (1 Yohane 2:15) Ndipo dzifunseni kuti: ‘Kodi ine ndimakhulupiriradi mawu a m’Malemba akuti, “lye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu” ’? (Yakobo 4:4) Satana akanakonda kukunyengani kuti mukhulupirire kuti dziko siriri lowopsa konse, kuti machitachita amene limapititsa patsogolo ngosavulaza. Chenjerani! Musanyengedwe!
Zokopa Zonyenga Lerolino
13. Kodi ndimwambo wotani umene wafikira kukhala wofalikira m’maiko ambiri, ndipo Satana akanafuna kuti tikhulupirire chiyani ponena za uwo?
13 Kawirikawiri Satana amanyenga anthu kulowa m’kuchita zolakwa mwa zinthu zimene mwa izo zokha siziri zolakwa kapena siziri zotsutsidwa kotheratu m’Baibulo. Mwachitsanzo, pamene okwatirana ambiri ali ndi zikumbukiro zokondweretsa za nthawi zosanguluka zimene anasangalalira m’masiku awo akutomerena, pali maupandu othekera pamene anthu ali okha pamodzi pocheza. Kwenikweni, kucheza kwa opalana ubwenzi kuli makamaka mwambo wamakono umene wafikira kukhala wotchuka m’malo ambiri kuyambira kokha itatha Nkhondo Yadziko I. Satana akanakonda kuti mukhulupirire kuti mwambo uwu uli kokha mpangidwe wa kusanguluka kumene kumakhozetsa anthu achichepere kuzolowerana ndi aziwalo zosiyana pamlingo wa aŵiriaŵiri. Koma, kunena zowona, mwambowu ngodzala ndi maupandu a makhalidwe abwino.
14. (a) Kodi ndimotani mmene mwambo wa kuchita pangano lokacheza pakati pa mnyamata ndi msungwana lingawonedwere? (b) Kodi ndimalingaliro otani amene angabuke m’mkhalidwe wa kucheza kwa mnyamata ndi msungwana?
14 Akulu, Akristu a chikulire, chifukwa cha chidziwitso chawo, amadziwa bwino kwambiri maupandu amenewa ndipo chotero angathe kupereka chitsogozo chothandiza. (Miyambo 27: 12) Koma mwinamwake inu mukulingalira kuti palibe upandu m’kucheza kwa mnyamanta ndi msungwana ndi kuti makolo anu amaletsa mopambanitsa, akumakuberani ‘chisangalalo Komabe monga momwedi anthu angaweruzidwire mwa zipatso zimene amapatsa, choteronso miyambo yonga kupangana kwa kuyendera limodzi kwa mnyamata ndi msungwana. (Miyambo 20:11; Mateyu 7:16) Mwachitsanzo, wazaka 18 amene nthawi zonse anapangana kuyendera limodzi ndi mnyamata, ndi amene anatenga mimba anati: “Ndinali mmodzi wa ana zikwi zambiri amene analingalira kuti sizikanachitika kwa ine.” Msungwanayo anavomereza kuti pambuyo pa kuchita pangano la kuyenda ndi mnyamata kwanthawi yakutiyakuti ‘kugwirana manja kumeneko ndi kupsopsonana kumazolowereka.” Mofananamo, Msungwana wazaka 17 zakubadwa amene anapangana kuyenda ndi mnyamata kawirikawiri, akusimba kuti: “Kupsopsonana ndi kugwirana mpheto kumakula kufikira ndithedwa nzeru kupangitsa mnyamatayo kundisonyeza chikondi.” Kodi ndilingaliro lachilendo? Kutalitali.
15. Kodi ndimatsoka otani amene mapangano ocheza a mnyamata ndi msungwana ali ndi thayo lalikulu?
15 Pamene achichepere okhumbirana mwakuthupi adzilekanitsa, monga momwe kuliri kofala pamapangano a kucheza kwa mnyamata ndi msungwana, chikhumbo cha kugonana chingakhoze kukula kufikira chigonjetsa ngakhale achichepere okhala ndi zolinga zabwino kuswa lamulo la Mulungu. Talingalirani kuti Asungwana azaka 13-19 zakubadwa oposa kwambiri miliyoni imodzi mu United States amatenga mimba chaka chirichonse ndipo zikwi mazana ambiri za iwo zimataya mimba kapena kubala ana apathengo. Mwachisoni, nthawi ndi nthawi ena a asungwana azaka 13-19 zakubadwa amene wa ali ana a Mboni za Yehova ndipo chomwechonso anyamata amene amawapatsa mimba. Mwambo wamakono wa kuchita pangano la kucheza kwa mnyamata ndi msungwana liyenera kukhala ndi thayo lalikulu la matsoka amenewa, kuphatikizapo mwinamwake zochitika zina zatsopano mamiliyoni ambiri anthenda zopatsirana mwa kugonana chaka chirichonse.
16. (a) Kodi nkuti kokha kumene zikhumbo za kugonana zimakhutiritsidwa moyenerera? (b) Kodi nchiyani chimene chimachitika kwa anthu a Mulungu amene amachita dama la chigololo?
16 Mulungu analinganiza kuti chikhumbo cha kugonana chikhutiritsidwe mkati mwa zomangira zaukwati, kumene chingadzetse chikondwerero ndi chikhutiro. (Ahebri 13:4; Miyambo 5:15-19) Komabe, Satana mwa machenjera wagwiritsira ntchito mphatso yoperekedwa ndi Mulungu iyi kunyengera anthu kuti agwiritsire ntchito molakwa kugonana ndi kuchita dama la chigololo. M’nthawi zakale, Aisrayeli 24, 000 anaphedwa m’tsiku limodzi kaamba ka tchimo iri motsutsana ndi Mulungu, ndipo pakali pano zikwi zambiri chaka chirichonse zimachotsedwa m’mpingo Wachikristu chifukwa cha chadama lachigololo. Chotero samalani. Mvetserani uphungu ndi chitsogozo. Musadzilole kunyengedwa.—Numeri 25:1-9, 16-18; 31:16.
17. (a) Kodi ndilingaliro lonyenga lotani limene Satana wapititsa patsogolo lonena za zinthu zonga masewera, nyimbo, ndi kuvina? (b) Kodi nchifukwa ninji zosangulutsa zadziko zimapereka chiwopsezo chotero kwa anthu a Mulungu?
17 Ndiponso, khalani maso, kumachenjera ena a Satana. Mwachitsanzo, masewera, nyimbo, ndi kuvina, zafikira kukhala mbali yotchuka ya zosangulutsa za dziko lake. Ndithudi, zinthu zimenezi mwa izo zokha siziri kwenikweni zoipa ndipo zingathe kukhala zokondweretsa ndipo ngakhale kupindulitsa. (1 Timoteo 4:8; Zekariya 8:5; Luka 15:25) Komabe, Satana, mwachinyengo wapititsa patsogolo lingaliro lakuti izo siziri zowopseza, ngakhale pamene zichitidwa nthawi zonse limodzi ndi anthu adziko. Mawu a Mulungu amachenjeza kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Talingalirani za ichi. Ngati chipembedzo ndi ndale zadziko ziri mbali ya dongosolo la Satana, kodi sikuli kupusa kukhulupirira kuti zosangulutsa zochitidwa ndi dziko ziri zopanda chisonkhezero chake? Mufunikira kukhala maso mosalekeza ‘kusalola dziko lokuzingani kukupanikizirani m’chikombole chake.’—Aroma 12:2, The New Testament in Modern English, la J. B. Phillips.
Makonzedwe Otetezera Ana
18. Kodi nchifukwa ninji muyenera kuyamikira makolo amene amakulangizani ndi kukutsogozani?
18 Yehova Mulungu mwachikondi wapanga makonzedwe otetezera achicheperenu kuti musanyengedwe. Choyamba, iye wakupatsani makolo okulangizani ndi kukutsogozani. Ndipo mungathe kukhala achimwemwe pamene iwo atero. Wazaka 18 zakubadwa wina wachisoni, amene anabala mwana wapathengo, anadandaula kuti sizikanachitika “ngati makolo anga akanachita ntchito yawo monga momwe makolo ayenera kuchitira, nandiuza mbuna za kukhala ndi bwenzi lachinyamata lanthawi zonse, ndi kundiletsa kuyenda naye nthawi zonse.” Chotero yamikirani ngati muli ndi makolo owopa Mulungu. Iwo saali kuyesa kukutsekerezani ndi kupangitsa moyo kukhala wosakondweretsa mwa ziletso zimene amaziika pa inu. Mmalo mwake, amakukondani ndipo amafuna kukutetezerani. Pindulani ndi chidziwitso chawo ndi nzeru mwa kufunafuna uphungu wawo.
19. Kodi ndizithandizo zowonjezereka zotani zimene zaperekedwa kutetezera ana?
19 Kuwonjezera apa, Yehova wagawira gulu lake la padziko lapansi kukuthandizani, mwachitsanzo, kope lirilonse la Galamukani! limakhala ndi nkhani yakuti “Achichepere Akufunsa Kuti . . .” imene imasonyeza phindu la miyezo ya Yehova. Mofananamo, kabukhu kotchedwa School and Jehovah’s Witnesses kanaperekedwera kukuthandizani kuti muchite mogwirizana ndi malamulo a Mulungu limodzi ndi malamulo a makhalidwe abwino a sukulu. Chilimbikitso china ndi uphungu zaperekedwa kupyolera m’masamba a Nsanja ya Olonda ndi pamisonkhano yampingo, misonkhano yadera, ndi misonkhano yachigawo. Ndithudi, nkhani yeniyeni ino yakuti, “Ana—Musanyengedwe,” inali nkhani pamsonkhano wachigawo posachedwapa kudzanso nkhani pa gawo lamsonkhano wautumiki.
20. (a) Kodi nchifukwa ninji zithandizo zambiri zimapatsidwa kwa achichepere? (b) Kodi ndilingaliro lotani limene lidzakuthandizani kukaniza zoyesayesa za Satana kukunyengani?
20 Musaganize konse kuti mwachisamaliro chonsechi tikuyesa kukuzingani ndi kukuberani chisangalalo chanu. Mmalo mwake, gulu la Mulungu limakukondani, ndipo chirichonse chimene chisindikizidwa ndi kunenedwa chimalinganizidwira kukutetezerani—kupulumutsa moyo wanu! Phunzirani kuyamikira makonzedwe amenewa. Pangani chizolowezi cha kuchita phunziro Labaibulo ndi mabukhu a Sosaite; lolani chowonadi Chabaibulo kukupatsani chiyamikiro. Mukhaletu ndi maganizo ofanana ndi a wazaka 18 zakubadwa amene, pambuyo pa kulingalira uphungu womvekera bwino wolunjikitsidwa kwa achichepere, analemba kuti: “Unangondichititsa kuzindikira mmene achicheperefe tiri amwawi kukhala m’chowonadi! Palibe gulu lina padziko lapansi limene limasamalira ndi kukonda achichepere ake motero!” Timamatiranetu pamodzi ndi kukaniza zoyesayesa za Mdyerekezi zotinyenga, chifukwa chakuti machenjera ake timawadziwa!
BOKOSI LOPENDA
◻ Kodi nchifukwa ninji achichepere ali chandamale chapadera cha Satana?
◻ Kodi Satana ananyenga motani Hava kuchita cholakwa?
◻ Kodi ndimotani mmene Satana amanyengera kawirikawiri achichepere kulowa m’kuchita cholakwa?
◻ Kodi ndimakonzedwe otani amene ali opezeka otetezera achichepere?
[Chithunzi pa tsamba 10]
Monga mmene Satana anasankha kusokeza Hava, yemwe anali ndi chidziwitso chochepa kuposa Adamu, inu ana muli chandamale chapadera cha Satana
[Chithunzi pa tsamba 13]
Pamene achichepere adzilekanitsa, zilakolako za kugonana zingathe kukula ndi kutsogolera ku kuswa lamulo la Mulungu