Miyambo
2 Usunge malamulo anga kuti upitirize kukhala ndi moyo.+
Uteteze malangizo* anga ngati mwana wa diso lako.
4 Nzeru uiuze kuti: “Ndiwe mchemwali wanga,”
Ndipo kumvetsa zinthu ukutche “mʼbale wanga,”
6 Ndinayangʼana pansi
Kuchokera pawindo la nyumba yanga,
7 Ndipo pamene ndinkayangʼanitsitsa anthu osadziwa zinthu,
Ndinazindikira kuti pakati pa achinyamata pali mnyamata wina wopanda nzeru.*+
8 Iye ankadutsa mumsewu pafupi ndi mphambano,
Ndipo ankalowera kunyumba ya mkaziyo
9 Pa nthawi yamadzulo kuli kachisisira,+
Kutatsala pangʼono kuda.
10 Kenako ndinaona mkazi akubwera kudzakumana naye,
Atavala ngati hule+ ndipo anali ndi mtima wachinyengo.
11 Ndi wolongolola ndiponso wamakani.+
Ndipo sakhala pakhomo.*
12 Pasanapite nthawi amapezeka kuti ali panja, kenako amapezeka mʼmabwalo a mzinda,
Amadikirira anthu pafupi ndi mphambano iliyonse.+
13 Iye wagwira mnyamatayo nʼkumupatsa kisi.
Mʼmaso muli gwaa! akumuuza kuti:
14 “Ndinayenera kupereka nsembe zamgwirizano.+
Lero ndakwaniritsa zimene ndinalonjeza.
15 Nʼchifukwa chake ndabwera kudzakumana nawe,
Kudzakufunafuna ndipo ndakupeza.
17 Ndawaza pabedi panga zonunkhiritsa za mule, aloye ndi sinamoni.+
18 Bwera tisonyezane chikondi mpaka mʼmawa ndipo chitikwane.
Tiye tisangalatsane pochita zachikondi,
19 Chifukwa mwamuna wanga sali panyumba.
Iye wachoka, wapita kutali.
20 Wanyamula chikwama cha ndalama,
Ndipo adzabwera kunyumba tsiku limene mwezi udzaoneke wathunthu.”
21 Wasocheretsa mnyamatayo pochita zinthu zambiri zomukopa.+
Wamunyengerera ndi mawu okopa.
22 Mwadzidzidzi mnyamatayo akuyamba kulondola mkaziyo, ngati ngʼombe yamphongo imene ikupita kukaphedwa,
Ndiponso ngati munthu wopusa amene akuyenera kulangidwa pomuika mʼmatangadza.+
23 Iye akulondola mkaziyo mpaka muvi utaboola chiwindi chake,
Ngati mbalame imene ikuthamangira kumsampha ndipo sakudziwa kuti zichititsa kuti ataye moyo wake.+
24 Choncho ana anga, ndimvereni.
Mvetserani mawu amene ndikukuuzani.
25 Musalole kuti mtima wanu upatukire kunjira zake.