Kalata Yachiwiri Yopita kwa Atesalonika
3 Pomaliza abale, pitirizani kutipempherera+ kuti mawu a Yehova* apitirize kufalikira mofulumira+ komanso kulemekezedwa ngati mmene akuchitira pakati panu. 2 Muzitipemphereranso kuti tipulumutsidwe kwa anthu oipa kwambiri,+ chifukwa si anthu onse amene ali ndi chikhulupiriro.+ 3 Koma Ambuye ndi wokhulupirika ndipo adzakulimbitsani ndi kukutetezani kwa woipayo. 4 Komanso monga otsatira a Ambuye, tili ndi chikhulupiriro mwa inu kuti mukutsatira malangizo amene tinakupatsani ndipo mupitiriza kuwatsatira. 5 Ambuye apitirize kutsogolera mitima yanu kuti muzikonda Mulungu+ komanso kuti muzipirira+ chifukwa cha Khristu.
6 Tsopano abale tikukupatsani malangizo mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti muzipewa mʼbale aliyense amene akuyenda mosalongosoka+ komanso amene akuchita zinthu zosagwirizana ndi malangizo amene* tinakupatsani.*+ 7 Ndipotu inuyo mukudziwa zimene mukuyenera kuchita potitsanzira,+ chifukwa sitinachite zinthu zosalongosoka pakati panu, 8 kapena kudya chakudya cha wina aliyense kwaulere.*+ Mʼmalomwake, tinagwira ntchito mwakhama komanso ndi mphamvu zathu zonse usiku ndi usana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza.+ 9 Sikuti tinachita zimenezi chifukwa choti tilibe ulamuliro wokupemphani kuti mutithandize,+ koma tinkafuna kuti tikupatseni chitsanzo choti muzitsanzira.+ 10 Ndipotu pamene tinali ndi inu, tinkakupatsani lamulo lakuti: “Ngati wina sakufuna kugwira ntchito, asadye.”+ 11 Chifukwa tikumva kuti ena akuyenda mosalongosoka pakati panu,+ sakugwira ntchito nʼkomwe, koma akulowerera nkhani zimene sizikuwakhudza.+ 12 Anthu otero tikuwalamula ndi kuwachonderera mwa Ambuye Yesu Khristu kuti azigwira ntchito mwakhama popanda kulowerera nkhani za anthu ena ndipo azidya chakudya chimene iwowo achigwirira ntchito.+
13 Koma inuyo abale, musasiye kuchita zabwino. 14 Koma ngati wina sakumvera mawu athu amene ali mʼkalatayi, muikeni chizindikiro ndipo musiye kuchitira naye zinthu limodzi+ kuti achite manyazi. 15 Komabe musamuone ngati mdani, koma pitirizani kumulangiza+ monga mʼbale.
16 Tsopano Ambuye wamtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mʼnjira iliyonse.+ Ambuye akhale nanu nonsenu.
17 Landirani moni wanga, amene ineyo Paulo ndalemba ndi dzanja langa.+ Nthawi zonse ndimalemba chonchi mʼmakalata anga onse, kuti mudziwe kuti ndine amene ndalemba. Umu ndi mmene ndimalembera.
18 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu nonsenu.