Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
Okondedwa Abale ndi Alongo:
Atate wathu wakumwamba, Yehova, amatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yoh. 4:8) Ngakhale kuti Yehova ndi Wamphamvuyonse, Mawu ake sananenepo kuti, “Mulungu ndiye mphamvu.” Choncho chilichonse chimene amachita polamulira, amachichita chifukwa cha chikondi. Izitu n’zimene zimachititsa kuti tizimukonda kwambiri.
N’zosangalatsa kuti Yehova samatikakamiza kuti tizim’tumikira. Iye si wolamulira wopondereza. Yehova amafuna kuti tizimutumikira chifukwa chakuti tikumukonda kuchokera pansi pa mtima. Tikamachita zimenezi, timasonyeza kuti tikufuna kuti iye azitilamulira chifukwa tikukhulupirira kuti amalamulira m’njira yoyenera komanso mwachikondi. Umboni wa zimenezi wakhala ukuoneka kuchokera pachiyambi penipeni m’mbiri ya anthu.
Mwachitsanzo, m’malo mokakamiza Adamu ndi Hava kuti amumvere, Yehova anawapatsa ufulu wosankha. Iwo akanatha kukana zofuna za Satana zoti apandukire Mulungu ngati akanakhala ndi chikondi chenicheni pa Yehova komanso kuyamikira zinthu zabwino zimene ankawachitira.
Patapita nthawi, pamene Mose ankalankhula komaliza kwa mtundu wa Isiraeli, anati: “Taona, ine ndikuika pamaso pako lero moyo ndi zinthu zabwino, imfa ndi zinthu zoipa.” (Deut. 30:15) Anthuwo anali ndi ufulu wosankha zoyenera kuchita pa moyo wawo. Nayenso Yoswa anauza Aisiraeli kuti: “Ngati kutumikira Yehova kukukuipirani, sankhani lero amene mukufuna kum’tumikira.” Poyankha, anthuwo anauza Yoswa kuti: “Sitingayerekeze kusiya Yehova.” (Yos. 24:15, 16) Umu ndi mmene ifenso timamvera masiku ano. Popeza timakonda Yehova, “sitingayerekeze” n’komwe kumusiya.
Monga Akhristu oona, timadziwa pomwe ufulu umenewu umalekezera. Ngakhale kuti akulu anapatsidwa udindo wopereka malangizo komanso chilango, iwo salamulira moyo kapena chikhulupiriro cha ena. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Sikuti ndife olamulira chikhulupiriro chanu, koma ndife antchito anzanu kuti mukhale ndi chimwemwe, pakuti ndinu okhazikika chifukwa cha chikhulupiriro chanu.”—2 Akor. 1:24.
Zimakhala zosangalatsa kwambiri ngati tikuchita zinthu chifukwa chakuti tafuna tokha osati chifukwa chakuti tachita kukakamizidwa. Yehova akutipempha kuti tizichita zabwino chifukwa chomukonda. Mawu ouziridwa a Paulo akusonyeza ubwino wochita zimenezi. Iye anati: “Ngati ndapereka zanga zonse kudyetsa ena, ndipo ngati ndapereka thupi langa kuti ndidzitame, koma ndilibe chikondi, sindinapindule m’pang’ono pomwe.”—1 Akor. 13:3.
Yehova amasangalala kwambiri akamaona abale ndi alongo ambirimbiri akumutumikira chifukwa chomukonda ndi mtima wonse.
Nayenso Yehova amakonda kwambiri atumiki ake onse, kuphatikizapo ana ndi achinyamata nonsenu amene mukusonyeza kuti mumakonda Yehova osati dzikoli ndi zinthu zake zokopa. Tikufuna kukutsimikizirani kuti ifenso timakukondani kwambiri.—Luka 12:42, 43.
Chifukwa chokonda Yehova, chaka chathachi inuyo abale ndi alongo komanso achinyamata munathera maola 1,748,697,447 polalikira uthenga wabwino. Chifukwa cha chikondi, anthu okwana 7,782,346 anagwira ntchito yolalikira padziko lonse. Tikusangalalanso kuti anthu atsopano 268,777 anabatizidwa posonyeza kudzipereka kwawo kwa Yehova. Ambiri mwa anthu amenewa anali achinyamata. Izi zikutanthauza kuti anthu 5,168 ankabatizidwa mlungu uliwonse. Zimenezi n’zosangalatsa kwambiri.
M’nthawi yamapeto ino, ifeyo anthu a Mulungu tikupirira mavuto ambirimbiri monga kuzunzidwa, matenda ndiponso mavuto a ukalamba. Koma tatsimikiza ndi mtima wonse kuti ‘sitibwerera m’mbuyo.’ Pomaliza, dziwani kuti nonsenu timakukondani kwambiri.—Aheb. 10:39; 2 Akor. 4:16.
Ndife abale anu,
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova