Kuwanditsa Fungo Lokoma la Chidziŵitso Chonena za Mulungu
“Ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m’chigonjetso mwa Kristu, namveketsa fungo la chidziŵitso chake mwa ife pamalo ponse.”—2 AKORINTO 2:14.
1. Kodi panopa tikukambitsirana fungo lanji, ndipo mwaŵi wa kuliwanditsa uyenera kuwonedwa motani?
NUNKHIZANI, Nunkhizani! M-m-m-m! Kodi mukununkhiza fungo lokoma? Panopa sitikulankhula za fungo lokoma la maluŵa ophukira, mmalo mwake, tikunena za fungo lokoma lophiphiritsira lotuluka m’zolembedwa zabwino koposa padziko lapansi. Zolembedwa zimenezi sizochokera kwa anthu wamba koma ziri duŵa lophiphiritsira louziridwa ndi Amene analenganso maluŵa onunkhira okongoletsa dziko lapansi. Mwaŵi wa kuwanditsa fungo lokoma la chidziŵitso chonena za Mulungu umenewu ulidi chuma chachikulu. Inde, uli utumiki wamtengo wapatali mwapadera—wosakhala wa onse, ndi wosagaŵanidwa ndi anthu onse.
2. Kodi ophunzira Akristu adayamba liti kuwanditsa fungo lokoma lophiphiritsira, ndipo ndichotulukapo chotani?
2 Chuma chamtengo wapatali chimenechi chinaperekedwa kwa ophunzira a Kristu pamene anapatsidwa utumiki wokangalika kwa Yehova Mulungu patsiku la Pentekoste wa chaka cha 33 C.E. Nyengo Yathu ino. Atadzazidwa ndi mzimu woyera, iwo anayamba kuwanditsa fungo lokoma lophiphiritsira, akumaphunzitsa “zazikulu za Mulungu.” (Machitidwe 2:1-4, 11) Kupyolera mwa iwo fungo lokoma la chidziŵitso chonena za Mulungu likafalikira kwa ena, osati kwa Ayuda odulidwa akuthupi okha komanso kwa amitundu, mafuko, anthu, ndi manenedwe osadulidwa. (Machitidwe 10:34, 35) Ophunzira owona anaona utumiki umenewu kukhala wamtengo wapatali koposa chuma chakuthupi chirichonse chimene anthu akudzikundikira.
3. Kodi ntchito ya kuwanditsa fungo lokoma la chidziŵitso chonena za Mulungu ikuchitidwa pamlingo waukulu motani, ndipo ndifunso lotani limene tifunikira kudzifunsa tokha?
3 Lerolino, ntchito yaikulu ya kuwanditsa fungo lokoma la chidziŵitso chonena za Mulungu ikuchitidwa padziko lonse lapansi—pamlingo wokulira koposa ndi kalelonse m’mbiri ya anthu. Iyo imaphatikizapo kuchitira umboni kwa mtundu wonse wa anthu ponena za Ufumu wa Mulungu umene tsopano wakhazikitsidwa pansi pa Mfumu yake yoikidwa, Yesu Kristu. (Mateyu 6:10; Machitidwe 1:8) Kodi mumawona utumiki wa kulengeza Mfumu ndi Ufumu wake monga chuma chamtengo wapatali? Yesu Kristu, yemwe anatsogolera kulalikidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu umenewo, anauwona mwanjira imeneyo, akumakhazikitsa chitsanzo.—Mateyu 4:17; 6:19-21.
Kuika Mankhwala Onunkhira Panjira ya Ligubo Lachigonjetso
4. Mogwirizana ndi 2 Akorinto 2:14, kodi ndimotani mmene Mulungu tsopano akutsogolerera atumiki ake padziko lapansi, ndipo kodi mawu a Paulo akusonya kukachitidwe kakale kotani?
4 Kodi nchifukwa ninji kutumikira Mulungu kuli chinthu choyenera kuonedwa kukhala chamtengo wapatali? Chifukwa chimodzi nchakuti ngakhale tsopano awo otumikira Yehova ali ndi mwaŵi wapadera wa kutsogozedwa ndi Mulungu m’ligubo lalikulu lachigonjetso. Mogwirizana ndi New International Version, 2 Akorinto 2:14 imati: “Ayamikike Mulungu, wotitsogoza nthaŵi zonse m’ligubo lachigonjetso mwa Kristu ndi amene kupyolera mwa ife afalitsa ponseponse fungo lokoma la chidziŵitso chake [“amapangitsa chidziŵitso chathu cha iye kufalikira m’dziko lonse ngati mankhwala onunkhira bwino!” Phillips].” Mawu amenewo a mtumwi Paulo akuwoneka kukhala akusonya kukachitidwe kakale ka kukhala ndi maligubo achilakiko.a
5, 6. (a) Kodi nchiyani chinkachitika m’maligubo achigonjetso a Roma wakale, ndipo kodi fungo lokomalo linatanthauzanji kwa anthu osiyanasiyana? (b) Kodi nditanthauzo lauzimu lotani liri pa 2 Akorinto 2:14-16?
5 M’masiku a lipabuliki ya Roma, umodzi wa ulemu waukulu womwe Bungwe Landuna linkapereka kwa kazembe wolakika unali kumlola iye kusangalalira chilakiko chake mwakulinganiza ligubo lachilakiko lodya ndalama zochuluka. Oguba Achiroma anayenda pang’onopang’ono motsatira Via Triumphalis ndi kukwera kudzera njira yokhwetakhweta yonka kukachisi wa Jupiter pamwamba pa Phiri la Capitoline. Mafumu, akalonga, ndi akazembe ankhondo ogwidwa ukapolo m’nkhondoyo, limodzi ndi ana awo ndi akalinde, ankayendetsedwa muunyolo, kaŵirikaŵiri ali amaliseche, kuwaseka ndi kuwachititsa manyazi.
6 Pamene ogubawo ankapyola mumzinda wa Roma, nzikazo zinali kuponya maluŵa kutsogolo kwa galeta la wolakayo, ndi kutentha zonunkhira zofukiza m’njira yonseyo. Fungo lokoma limenelo linatanthauza ulemu ndi moyo wosungika koposerapo kwa asirikali olakika. Koma linatanthauza imfa kwa akapolo osakhululukidwa amene anali kuphedwa pakutha kwa kugubako. Izi zikuvumbula tanthauzo lauzimu la fanizo la Paulo pa 2 Akorinto 2:14-16. Chithunzi chimenecho chimasonyeza Paulo ndi Akristu anzake monga nzika zodzipereka za Mulungu, ‘limodzi ndi Kristu,’ onse akutsatira mumzera wa Mulungu wachilakiko natsogozedwa ndi Iye m’ligubo lalikulu lachilakiko pamsewu woikidwa mankhwala onunkhira.
Fungo Labwino la Moyo kapena Kununkha kwa Imfa
7, 8. (a) Kodi Mboni za Yehova zikuwanditsa motani fungo lokoma la chidziŵitso chonena za Mulungu? (b) Pamene Mboni za Yehova zikuwanditsa fungo lophiphiritsiralo, kodi opulumutsidwawo akulabadira motani? (c) Kodi achiwonongeko akulabadira motani?
7 Mwakufalitsa kulikonse chowonadi cha Baibulo chonena za Ufumu wa Mulungu pansi pa Kristu, Mboni za Yehova zikuwanditsa, kuwonetsera, ndi kuzindikiritsa kulikonse fungo labwino la kudziŵa Mulungu wachisomo amene chowonadi chake chawamasula ku chipembedzo chonyenga. Iwo akuguba mwachilakiko muutumiki wa Yehova. Nsembe zawo zautumiki monga Mboni zake ndi za Mfumu yake ziri ngati zofukiza zonunkhira kwa Yehova. Motero, tingamvetsetse chomwe mtumwiyo anatanthauza pamene anati: “Ife ndife fungo labwino la Kristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuwonongeka; kwa ena fungo la imfa kuimfa; koma kwa ena fungo la moyo kumoyo. [“Fungo lokoma lofunika lodzetsa moyo,” The New English Bible; “fungo lokoma lotsitsimula moyo weniweniwo,” Phillips.]”—2 Akorinto 2:15, 16.
8 Anthu owona mtima amaganizo onga nkhosa amazindikira ukoma wa chidziŵitso chonena za Yehova monga momwe chikuwanditsidwira ndi Mboni zake. Kwa anthu oterowo ntchito yochitira umboni iri ndi fungo lathanzi labwino ndi moyo, la kukhala ndi moyo, mogwirizana ndi chowonadi chopatsa moyo. Iwo amapereka zithokozo kwa Yehova ndi kwa Mfumu yake, amene akupitira naye limodzi m’ligubo lake lachilakiko, ndi kufuula mwamphamvu kuti: “Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:10) Iwo akupuma mpweya wa chowonadi cha Ufumu, umene uli fungo lotsitsimula la moyo umene umatsogolera ku moyo. Koma Satana ndi ziŵanda zake aipitsa mphamvu za kunukhiza za awo okangamira kuchipembedzo chonyenga, kotero kuti amatseka mphuno zawo ndi kukana chowonadi monyozera. Kwa “awo achiwonongeko,” chowonadicho ndi ochinyamula ake okhulupirika amawanditsa fungo la imfa lotsogolera ku imfa. Kapena monga momwe New International Version ikunena kuti: “Kwa amene tiri fungo la imfa.” Matembenuzidwe a Phillips amati: “Kwa otchulidwa pambuyo pakewo likuonekera kukhala fungo la imfa la chiwonongeko.”
9. Kodi Paulo akufunsa funso lotani tsopano, ndipo kodi mungayakhe motani, ndipo nchifukwa ninji?
9 Kenaka Paulo akufunsa kuti: “Ndipo azikwanira ndani izi?” (2 Akorinto 2:16) Ndiko kuti, “ndipo kodi ndani angayeneretsedwe kaamba ka ntchito yonga iyi?” (The Jerusalem Bible) “Ndipo woyeneretsedwa ndani kaamba ka ntchito yonga iyi?” (Weymouth) Yankho Lamalemba nlakuti: Mboni za Yehova! Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ali odzipereka okha amene ali okhulupirika, owona mtima, ndi osafuna phindu ladyera ndi olankhula chowonadi poyera, ndi mosagonjera kuchipembedzo chonyenga, ndiwo ali oyeneretsedwa kaamba ka ntchitoyi ya kufalitsa fungo lokoma la chidziŵitso chonena za Mulungu.—Akolose 1:3-6, 13; 2 Timoteo 2:15.
10. Kodi nchifukwa ninji atsogoleri achipembedzo sakuyeneretsedwa kaamba ka ntchito ya kuwanditsa fungo lokoma la chidziŵitso chonena za Mulungu?
10 Atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko, omwe amafuna dzina labwino ndi dziko lino, akulephera kukhala oyeneretsedwa ndi kuyenerera kaamba ka utumiki wopanda dyera umenewu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti iwo akulephera kufikiritsa ziyeneretso zosonyezedwa ndi ndemanga ya Paulo yakuti: “Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nawo mawu a Mulungu; koma monga mwa chowona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Kristu.” (2 Akorinto 2:17) Kapena monga momwe New International Version ikunenera kuti: “Mosiyana ndi ambiriwo, sitichita malonda ndi mawu a Mulungu kaamba ka phindu. Mmalo mwake, tilankhula mwa Kristu pamaso pa Mulungu ndi kuwona mtima, monga anthu otumidwa kuchokera kwa Mulungu.”
11, 12. (a) Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova siziri “akuchita malonda ndi mawu a Mulungu” pamene zikulandira zopereka? (b) Mosiyana ndi mtundu woipitsidwa wa chiphunzitso Chachikristu chimene ambiri akuchigula, kodi Mboni za Yehova zikuperekanji?
11 Mboni za Yehova zikutumidwa kuchokera kwa Mulungu, ndipo zikuchita ntchito yawo ya kuchitira umboni pansi pa chiyang’aniro cha Mulungu. Pamene kuli kwakuti akupereka kwa anthu okondwerera mabuku opindulitsa ndi zofalitsidwa zina zolongosola Mawu a Mulungu ndi kulandira zopereka zodzifunira kaamba ka ntchito yapadziko lonse ya kulalikira Ufumu, kachitidwe koteroko sikali kuchita malonda kapena kuipitsa Mawu a Mulungu. Kwenikweni, zopereka zoterozo zangokhala thandizo la kufalitsira chidziŵitso chonena za Mulungu kwa enanso.
12 Ambiri lerolino, modziŵa kapena mosadziŵa, agula mtundu wa chiphunzitso Chachikristu choipitsidwa, popeza kuti chimayenderana ndi zikhumbo zawo zadyera ndipo sichimadodometsa njira yawo ya moyo. Iwo amakhulupirira kuti Mulungu amawalandira chifukwa cha kudzinenera kwawo kwakuti amamkonda m’mitima yawo. Komabe, pamene Mawu a Mulungu awoneka kukhala akusemphana ndi zikhulupiriro zawo ndi machitidwe, amapotoza Malembawo kotero kuti akweze malingaliro a iwo eni pamwamba pa chidziŵitso choyenerera cha Baibulo. (Mateyu 15:8, 9; 2 Petro 3:16) Koma Mboni za Yehova zimapereka chowonadi choyera chochokera m’Baibulo chosaipitsidwa, motero akupereka fungo lokoma lolandirika kwa Mulungu ndi kwa alambiri ake owona. Mwakutero iwo amachotsa miyambo yonse yachipembedzo ndi zopinga zoletsa kuti akhale ndi chidziŵitso chowona chonena za Mulungu.
13. Kodi ndani, kuwonjezera pa Akristu odzozedwa, amene ali m’ligubo la Mulungu lachigonjetso, ndipo kodi iwo akuchitanji kulikonse amkako?
13 Ndithudi, kukhala m’ligubo la Mulungu lachigonjetso limodzi ndi Kristu kuli mwaŵi wosayerekezereka wosangalalidwa osati ndi Akristu odzozedwa okha komanso ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” ngakhale tsopano lino, popeza kuti chigonjetso cha Ufumuwo chayandikira. (Chivumbulutso 7:4, 9; Yohane 10:16) Pamene tikuyembekezera zigonjetso zowonjezereka za Mfumu yathu yogonjetsa, kulikonse kumene tipitako timawanditsa chidziŵitso chonena za Mulungu chopatsa moyo monga mankhwala onunkhira, kapena zofukiza zamtengo wapatali, kwa awo amene mitima yawo ikulakalaka chowonadi ndi chilungamo. Ha, ndimwaŵi wotani nanga kwa awo oyeneretsedwa kaamba ka ntchito yapadera imeneyi!—Yohane 17:3; Akolose 3:16, 17.
Ololedwa Kukhala Anthu Opereka Mankhwala Onunkhira
14. Kodi nchifukwa ninji awo owanditsa fungo lokoma la chidziŵitso cha Mulungu safunikira satifiketi yachivomerezo yochokera kwa anthu?
14 Koma kodi awo owanditsa fungo lokoma la chidziŵitso chonena za Mulungu ndi Ufumu wake amafunikira dipuloma kapena satifiketi yachivomerezo yochokera kwa anthu? Ayi! Tinapatsidwa kale ntchitoyo, kapena kuikidwa, monga Mboni za Wamkulukuluyo wa chilengedwe chonse. Motero, sitifunikira kuzengereza kuloŵa m’munda kukafalitsa fungo lokoma la mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Kumbukirani kuti Yehova akutitsogolera. Uminisitala wa Yesu unachitidwa pamaso pa “ochimwa otsutsa.” (Ahebri 12:3) Komabe, cholembera cha Yesu cha ntchito yakumunda, monga chiriri m’Baibulo, chikali chikhalirebe chowona, ndipo ntchito yake ya m’munda ikumchitira umboni ndi kumchirikiza kukhala minisitala wowona wa Yehova Mulungu.
15. Kodi ndimotani mmene mtumwi Paulo anasonyezera kuti Akristu owona safunikira ‘makalata achivomerezo’?
15 Mtumwi Paulo anakumana ndi mkhalidwe wachitokoso wofananawo m’tsiku lake mwa kupereka chigomeko ichi: “Kodi tirikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisoŵa, monga ena, akalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu? Inu ndinu kalata wathu, wolembedwa m’mitima yathu, wodziŵika ndi woŵerengedwa ndi anthu onse; popeza mwawonetsedwa kuti muli kalata wa Kristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iyayi, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; osati m’magome a miyala, koma m’magome a mitima yathupi.”—2 Akorinto 3:1-3.
16. Kodi ndikalata yamtundu wotani imene Mboni za Yehova zimapereka monga umboni wakuti uminisitala wawo ngwochokera kwa Mulungu?
16 Maulamuliro adziko sakuzindikira ntchito yathu monga Mboni za Yehova. Koma lolani ntchito yathu ya kuwanditsa fungo lokoma la chidziŵitso chonena za Yehova ilankhule yokha! Ntchitoyi siingafafanizidwe, ngakhale kuti anthu ena akukana kuŵerenga umboni wotsimikizirira umenewu wa uminisitala wathu. Atsogoleri achipembedzo amapereka zikalata zawo zachivomerezo zochokera ku mabungwe olamulira tchalitchi. Komabe, zimenezi ziri kokha mapepala wamba, mawu a munthu. Mboni za Yehova, kuwonjezera pa kugwira mawu ochirikizira kuchokera m’Mawu a Mulungu, ndizo umboni mumpangidwe wa thupi ndi mwazi. Khamu lalikulu la nkhosa zina limene lafikiridwa ndi mbiri yabwino ya Ufumu lasonkhanitsidwiranso kudzanja lamanja la Mfumu ya Yehova. (Mateyu 25:33, 34) Zonsezi ziri kalata yathu yachivomerezo, kalata imene ife monga Mboni za Yehova timanyamulira pamitima ndi maganizo athu kunka nayo kulikonse ndipo tingayiwonetsere ndi chidaliro. Awo otenga kaimidwe kaamba ka ulamuliro wa Mulungu wa chilengedwe chonse ndi kukhala ndi phande m’kutumikira Mulungu mogwirizana ndi Mboni za Yehova iwo eniwo ali makalata achivomerezo amene sangapeŵedwe kuŵerengedwa ndi kudziŵidwa ndi anthu onse.
17. Kodi ndimotani mmene “kalata [yathu ya] Kristu” ikulembedwera, ndipo nchifukwa ninji Paulo akuti iyo imazokotedwa pamitima?
17 Ndithudi, izi zimakwiitsa achipembedzo chonyenga ndi kudukidwa pamene awaŵerenga. Komabe, khamu lalikulu lomawonjezereka la nkhosa zina liri kalata yachivomerezo yochokera kwa Yesu Kristu, Mbusa Wabwino, yemwe akugwiritsira ntchito Mboni za Yehova zonse m’ntchito yake yaupasitala. Ife ndife peni, kapena chiŵiya chaumunthu, chimene amagwiritsira ntchito kulemba kalatayi. Kalata imeneyi siikulembedwa ndi inki imene ingafafanizidwe, koma imazokotedwa ndi mphamvu yogwira ntchito, kapena mzimu, wa Mulungu, umene umagwira ntchito mwa ife. Siziri zofanana ndi chochitika cha Mose pamene chilamulo cha Malamulo Khumi chinalembedwa ndi chala cha Mulungu pamagome aŵiri amiyala. Kalata yathu ikulembedwa pamiyala yanyama ya mitima ya anthu, popeza kuti uminisitala wathu wauzimu umapangitsa kusintha kwa maganizo ndi mitima ya olandira fungo lokoma la mbiri yabwino.
18. Kodi nchotulukapo chotani chimene chimapangitsa olandira mbiri yabwino kukhala kalata yachivomerezo?
18 Ntchito yathu ya Mawu a Mulungu yazokota pa olandira mbiri yabwino oyamikira ndipo yadzetsa masinthidwe aakulu. Chosankha chawo chakutumikira Mulungu chatsimikizira kusakhala mchitidwe wamwadzidzidzi wochititsidwa ndi kutengeka maganizo kosonkhezeredwa ndi mlaliki womafuula. Mmalo mwake, chimaimira kusandulizika kwachikhalire kwa miyoyo yawo kozikidwa pa chowonadi chomvekera bwino cha Baibulo Lopatulika. Kukonda Mulungu wowona, Yehova, kumawasonkhezera ‘kuvula umunthu wawo wakale ndi zikhumbo zake zachinyengo ndi kuvala umunthu watsopano,’ umene umawonetsera “chipatso cha mzimu.” (Aefeso 4:20-24; Agalatiya 5:22, 23) Chotero, chotulukapo, chimawapangitsa kukhala kalata yachivomerezo. Iyo imalankhula momvekera bwino kuposa kalata iriyonse imene ife tingalembe pamanja kapena yolembedwa ndi gulu lirilonse lowoneka ndi maso limene lingatitumize.
19. Kodi Paulo akulongosola motani ziyeneretso za “atumiki a pangano latsopano,” ndipo kodi ntchito yawo yakhala ndi chiyambukiro chotani pakhamu lalikulu?
19 Pa 2 Akorinto 3:4-6 Paulo akupitirizabe kuti: “Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tiri nako mwa Kristu: sikuti tiri okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu; amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano.” Ngakhale kuti ngosalira odzozedwa okha amene ali “atumiki a pangano latsopano,” ntchito yawo yakhala ndi chiyambukiro pakhamu lalikulu la nkhosa zina, ndipo idzayambukirabe ziŵerengero zosaŵerengeka za nkhosa zina zoterozo zooti zisonkhanitsidwebe. Ichi ndicho chidaliro chimene Mboni za Yehova zonse kupyolera mwa Kristu Yesu zirinacho kulinga kwa Yehova Mulungu. Moyamikira otsalirawo amalimbikitsa khamu lalikulu la nkhosa zina kukhala ndi phande mwamtima wonse muuminisitala ‘wolemba kalata’ umene Yesu Kristu ananeneratu pa Mateyu 24:14 ndi Mateyu 28:19, 20.
20. (a) Kodi lipoti la Yearbook likusonyeza chiyani ponena za awo owanditsa fungo lokoma la chidziŵitso chonena za Mulungu? (b) Kodi tonsefe tinganenenji paziyeneretso zathu za uminisitala wa kulemba kalata?
20 Ndicho chimene achichita, monga momwe kukuchitiridwa umboni ndi lipoti la mu 1990 Yearbook m’limene Mboni za Yehova zasonyezedwa kukhala zikuwanditsa fungo lokoma la chidziŵitso chonena za Mulungu m’maiko 212. Iwo ali m’chiŵerengero cha ofalitsa oposa 3,787,000 okangalika, ndipo chaka chatha chokha anathera maola pafupifupi 835,000,000 m’kulalikira mbiri yabwino imeneyi ya Ufumu. Pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye chaka chatha, 9,479,064 anapezekapo. Onse aŵiri otsalira odzozedwa ndi ziŵalo za khamu lalikulu la nkhosa zina anganene kuti: “Kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu.” Kapena monga mmene The Jerusalem Bible ikunenera kuti: “Ziyeneretso zathu zonse zichokera kwa Mulungu.”
21. Kodi tonsefe tiyenera kumachitanji, ndipo nchifukwa ninji?
21 Chotero, falitsani fungo lokoma lopereka moyo, la chidziŵitso chonena za Mulungu m’malo alionse! Dzazani gawo la mpingo wanu ndi fungo la kununkhira kwa chidziŵitso chonena za Yehova. Pamenepo, monga Kazembe Wankhondo wateokratiki wogonjetsa, adzakutsogolerani m’ligubo lake lachilakiko pamene Mboni zake zonse zikupita patsogolo muuminisitala wamakono umenewu waulemerero!
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka tsatanetsatane wowonjezereka, wonani Insight on the Scriptures, Voliyamu 2, masamba 1128-9, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi Paulo akugwiritsira ntchito fanizo lotani pa 2 Akorinto 2:14-16?
◻ Kodi kuwanditsa fungo lokoma la chidziŵitso cha Mawu a Mulungu kuli ndi chiyambukiro chotani pa ena?
◻ Kodi ndiati okha ali oyeneretsedwa kaamba ka ntchito iyi, ndipo nchifukwa ninji?
◻ Kodi nchifukwa ninji anthu opereka mankhwala onunkhira satofunikira makalata achivomerezo olembedwa pamanja kaamba ka ntchito yawo?