Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira
7 Zimenezi zitatha, ndinaona angelo 4 ataimirira mʼmakona 4 a dziko lapansi. Iwo anali atagwira mwamphamvu mphepo 4 za dziko lapansi, kuti mphepo iliyonse isawombe padziko lapansi, panyanja kapena pamtengo uliwonse. 2 Ndinaonanso mngelo wina akukwera kuchokera kotulukira dzuwa,* ali ndi chidindo cha Mulungu wamoyo. Iye anafuula mokweza mawu kwa angelo 4, amene anapatsidwa mphamvu zowononga dziko lapansi ndi nyanja aja, 3 kuti: “Musawononge dziko lapansi, kapena nyanja, kapena mitengo, mpaka titadinda chidindo+ pazipumi za akapolo a Mulungu wathu.”+
4 Ndiyeno ndinamva chiwerengero cha amene anadindidwa chidindo. Anthu okwana 144,000,+ ochokera mʼfuko lililonse la ana a Isiraeli, anadindidwa chidindo:+
5 Mu fuko la Yuda, anadindamo anthu 12,000.
Mu fuko la Rubeni, 12,000.
Mu fuko la Gadi, 12,000.
6 Mu fuko la Aseri, 12,000.
Mu fuko la Nafitali, 12,000.
Mu fuko la Manase,+ 12,000.
7 Mu fuko la Simiyoni, 12,000.
Mu fuko la Levi, 12,000.
Mu fuko la Isakara, 12,000.
8 Mu fuko la Zebuloni, 12,000.
Mu fuko la Yosefe, 12,000.
Ndipo mu fuko la Benjamini, anadindamo anthu 12,000.
9 Zimenezi zitatha, nditayangʼana ndinaona khamu lalikulu la anthu, amene palibe munthu aliyense amene anatha kuwawerenga, ochokera mʼdziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chilankhulo chilichonse.+ Iwo anali ataimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala mikanjo yoyera+ ndiponso atanyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo.+ 10 Iwo anapitiriza kufuula ndi mawu okweza akuti: “Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wachifumu,+ ndi kwa Mwanawankhosa.”+
11 Angelo onse anali ataima kuzungulira mpando wachifumu, akulu+ komanso angelo 4 aja. Ndipo onse anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi, pamaso pa mpando wachifumuwo ndi kulambira Mulungu. 12 Iwo ankanena kuti: “Ame! Mulungu wathu ndi amene ali ndi nzeru, mphamvu komanso nyonga ndipo ndi amene akuyenera kutamandidwa, kupatsidwa ulemerero ndi ulemu komanso kuyamikiridwa mpaka kalekale.+ Ame.”
13 Ndiyeno mmodzi wa akulu aja anandifunsa kuti: “Kodi amene avala mikanjo yoyerawa+ ndi ndani ndipo achokera kuti?” 14 Nthawi yomweyo, ndinamuyankha kuti: “Mbuyanga, mukudziwa ndinu.” Ndipo iye anandiuza kuti: “Amenewa ndi amene atuluka mʼchisautso chachikulu+ ndipo achapa mikanjo yawo nʼkuiyeretsa mʼmagazi a Mwanawankhosa.+ 15 Nʼchifukwa chake ali pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu. Iwo akumuchitira utumiki wopatulika usana ndi usiku mʼkachisi wake, ndipo Amene wakhala pampando wachifumuyo+ adzawaphimba ndi tenti yake kuti awateteze.+ 16 Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu. Dzuwa kapena kutentha kulikonse sikudzawawotcha,+ 17 chifukwa Mwanawankhosa,+ amene ali pambali* pa mpando wachifumu, adzawaweta+ nʼkuwatsogolera ku akasupe a madzi a moyo.+ Ndipo Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.”+