MUTU 14
“Tonse Tagwirizana”
Bungwe lolamulira linagwirizana chimodzi, ndipo zimenezi zinathandiza kuti m’mipingo mukhale mgwirizano
Nkhaniyi yachokera pa Machitidwe 15:13-35
1, 2. (a) Kodi bungwe lolamulira la mpingo wa Chikhristu m’nthawi ya atumwi linafunika kukambirana mafunso ovuta ati? (b) Kodi abalewa anathandizidwa bwanji kuti agwirizane mfundo imodzi yoyenera?
ATUMWI ndi akulu anali m’chipinda chinachake ku Yerusalemu ndipo anali atakambirana kwa nthawi yaitali ndithu. Tsopano nthawi yofunika kwambiri yoti agwirizane mfundo imodzi inafika ndipo aliyense ankayembekezera mwachidwi. Nkhani ya mdulidwe inayambitsa mafunso ovuta kwambiri. Kodi Akhristu anayenera kutsatira Chilamulo cha Mose? Kodi Akhristu a Chiyuda anafunika kukhala osiyana ndi Akhristu a mitundu ina?
2 Amuna amene ankatsogolerawo anakambirana umboni wosiyanasiyana wokhudza nkhaniyi. Iwo ankadziwa Mawu a Mulungu aulosi komanso anaona umboni wamphamvu wosonyeza kuti Yehova akuwadalitsa. Aliyense anali atanena maganizo ake momasuka pa nkhaniyi ndipo panali umboni wambiri umene ukanawathandiza kumanga mfundo imodzi. Zimenezi zinkasonyeza kuti mzimu wa Yehova ukuwatsogolera pa zokambiranazo. Kodi amuna amenewa akanalola kuti mzimuwo uwatsogolere?
3. Kodi kuphunzira nkhani yamuchaputala 15 cha buku la Machitidwe kungatithandize bwanji?
3 Abalewo anafunika kukhala ndi chikhulupiriro komanso kukhala olimba mtima kuti atsatire zimene mzimuwo unkawatsogolera pa nkhaniyi. Izi zinali choncho chifukwa zikanachititsa kuti atsogoleri achipembedzo a Chiyuda ayambe kudana nawo kwambiri. Komanso iwo ankatsutsidwa ndi Akhristu anzawo amene ankafuna kuchititsa kuti anthu a Mulungu ayambenso kutsatira Chilamulo cha Mose. Kodi bungwe lolamulira likanachita chiyani? Tiyeni tione. Tikamakambirana nkhani imeneyi, tiona mmene amuna amenewa anasonyezera chitsanzo chimene Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova masiku ano limatsatira. Ifenso tiyenera kutsanzira chitsanzo chimenechi tikamasankha zochita kapena tikafuna kuthana ndi mavuto pa moyo wathu monga Akhristu.
“Zikugwirizana ndi Zimene Aneneri Analemba” (Machitidwe 15:13-21)
4, 5. Kodi Yakobo analankhula mawu ati amene aneneri analemba?
4 Yakobo, yemwe anali mchimwene wake wa Yesu komanso wophunzira wake analankhula.a Zikuoneka kuti iye anali tcheyamani pamsonkhanowu ndipo anaphera mphongo mfundo zonse zimene abalewo anagwirizana. Yakobo analankhula kwa abale amene anasonkhanawo kuti: “Sumiyoni wafotokoza bwino mmene Mulungu anacheukira anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti pakati pawo atengepo anthu odziwika ndi dzina lake. Ndipo zimenezi zikugwirizana ndi zimene aneneri analemba.”—Mac. 15:14, 15.
5 Mawu amene Sumiyoni, kapena kuti Simoni Petulo analankhula komanso umboni umene Baranaba ndi Paulo anapereka, ziyenera kuti zinathandiza Yakobo kukumbukira malemba ogwirizana ndi nkhani imene ankakambiranayo. (Yoh. 14:26) Atalankhula mawu akuti “zikugwirizana ndi zimene aneneri analemba,” Yakobo anagwira mawu apalemba la Amosi 9:11, 12. Buku limeneli linali m’gulu la mabuku a Malemba a Chiheberi amene “aneneri analemba.” (Mat. 22:40; Mac. 15:16-18) Mungaone kuti mawu amene Yakobo analankhula akusiyanako ndi mawu amene amapezeka m’buku la Amosi masiku ano. Izi zili choncho chifukwa chakuti mwina mawuwo anali mu Baibulo la Chigiriki lomasulira Malemba a Chiheberi la Septuagint.
6. Kodi Malemba anathandiza bwanji abale a m’bungwe lolamulira kumvetsa mfundo zina pamene ankakambirana?
6 Kudzera mwa mneneri Amosi, Yehova ananeneratu kuti nthawi idzafika pamene adzadzutsa “nyumba ya Davide,” kutanthauza kuti banja lachifumu limene lidzatulutse Ufumu wa Mesiya. (Ezek. 21:26, 27) Kodi zimenezi zinatanthauza kuti Yehova adzayambiranso kuona Ayuda ngati mtundu wake wapadera? Ayi, chifukwa ulosiwo ukupitiriza kunena kuti “mitundu yonse ya anthu” idzasonkhanitsidwa pamodzi kuti ikhale “anthu otchedwa ndi dzina [la Mulungu].” Kumbukirani kuti Petulo anali atangonena kuti Mulungu “sanasiyanitse m’pang’ono pomwe pakati pa ife [Akhristu a Chiyuda] ndi iwo [Akhristu a mitundu ina]. Koma anayeretsa mitima yawo chifukwa cha chikhulupiriro chawo.” (Mac. 15:9) Izi zikutanthauza kuti Mulungu ankafuna kuti Ayuda komanso anthu a mitundu ina adzalamulire nawo mu Ufumu wake. (Aroma 8:17; Aef. 2:17-19) Ulosi wouziridwa umenewu sunanenepo pena paliponse kuti anthu a mitundu ina ayenera kudulidwa choyamba kapena kulowa chipembedzo cha Chiyuda kuti akhale Akhristu ovomerezeka.
7, 8. (a) Kodi Yakobo anapereka maganizo otani? (b) Kodi mawu amene Yakobo ananena ankatanthauza chiyani?
7 Atamvetsera umboni wa m’Malemba umenewo komanso umboni wina wamphamvu, Yakobo ananena maganizo ake kuti: “Choncho chigamulo changa n’chakuti, anthu a mitundu ina amene ayamba kulambira Mulungu, tisawavutitse. Koma tiyeni tiwalembere kuti apewe zinthu zoipitsidwa ndi mafano, chiwerewere, zopotola ndi magazi. Chifukwa kuyambira kalekale, anthu akhala akulalikira mumzinda ndi mzinda mawu ochokera m’mabuku a Mose, popeza mabuku amenewa amawerengedwa mokweza m’masunagoge sabata lililonse.”—Mac. 15:19-21.
8 Ponena kuti “choncho chigamulo changa n’chakuti,” kodi Yakobo ankasonyeza kuti ali ndi mphamvu kuposa abale enawo ndipo ankagamula yekha zoyenera kuchita pa nkhaniyo, mwina chifukwa chakuti anali tcheyamani pamsonkhanowu? Ayi ndithu. Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “chigamulo changa n’chakuti” angatanthauzenso kuti “ndikuona kuti” kapena “maganizo anga ndi akuti.” Apa Yakobo sankagamula yekha zoyenera kuchita pa nkhaniyo, koma ankapereka maganizo ake kuti bungwelo liganizire mogwirizana ndi umboni umene anamva komanso zimene Malemba amanena pa nkhaniyo.
9. Kodi maganizo amene Yakobo anapereka anathandiza bwanji?
9 Kodi maganizo a Yakobo amenewa anali abwino? N’zoonekeratu kuti anali abwino chifukwa atumwi komanso akulu atakambirana, anagwirizana nawo. Kodi zimenezi zinathandiza bwanji? Choyamba, zimene anagwirizanazo zinathandiza kuti ‘asavutitse’ Akhristu a mitundu ina powakakamiza kuti azitsatira Chilamulo cha Mose. (Mac. 15:19) Chachiwiri, zimenezi zinasonyeza kuti akulemekeza chikumbumtima cha Akhristu a Chiyuda, amene kwa zaka zambiri ankamva ‘mawu ochokera m’mabuku a Mose, akuwerengedwa mokweza m’masunagoge sabata lililonse.’b (Mac. 15:21) Zimene anagwirizanazo zinathandiza kuti Akhristu a Chiyuda ndi a mitundu ina azigwirizana kwambiri. Komanso chofunika kwambiri n’chakuti zinasangalatsa Yehova Mulungu chifukwa zinali zogwirizana ndi chifuniro chake. Imeneyitu inali njira yabwino kwambiri yothetsera nkhani imene ikanasokoneza mgwirizano komanso mtendere wa anthu a Mulungu mumpingo. Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwambiri ku mpingo wa Chikhristu masiku ano.
10. Kodi Bungwe Lolamulira masiku ano limatsanzira bwanji chitsanzo cha bungwe lolamulira la m’nthawi ya atumwi?
10 Monga tinaonera m’mutu wapitawo, mofanana ndi bungwe lolamulira la m’nthawi ya atumwi, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova masiku ano nthawi zonse limadalira Yehova, Wolamulira wa Chilengedwe Chonse komanso Yesu Khristu yemwe ndi Mutu wa mpingo kuti aziwatsogolera pa china chilichonse.c (1 Akor. 11:3) Kodi limachita bwanji zimenezi? Albert D. Schroeder, amene anatumikira m’Bungwe Lolamulira kuchokera m’chaka cha 1974 mpaka pamene anamaliza moyo wake wapadziko lapansi mu March 2006, anafotokoza kuti: “Abale a m’Bungwe Lolamulira amakumana Lachitatu lililonse, ndipo asanayambe msonkhano wawo, amapemphera kuti Yehova awatsogolere ndi mzimu wake woyera. Amayesetsa kuti nkhani iliyonse komanso mfundo iliyonse imene amanga ikhale yogwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu, omwe ndi Baibulo, amanena.” Nayenso Milton G. Henschel, amene anatumikira m’Bungwe Lolamulira kwa nthawi yaitali, ndipo anamaliza moyo wake wapadziko lapansi mu March 2003, anafunsa funso lofunika kwambiri kwa abale ndi alongo amene anamaliza maphunziro awo m’kalasi ya nambala 101 ya Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo. Iye anafunsa kuti, “Kodi palinso bungwe lina padziko lapansi limene atsogoleri ake amagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu Baibulo, posankha zochita pa nkhani zofunika?” Yankho lake ndi lodziwikiratu.
“Anagwirizana Zosankha Amuna Pakati Pawo, Kuti Awatumize” (Machitidwe 15:22-29)
11. Kodi bungwe lolamulira linatani kuti mipingo idziwe zimene linagwirizana?
11 Bungwe lolamulira la ku Yerusalemu linagwirizana chimodzi pa nkhani ya mdulidwe. Koma kuti abale m’mipingo achite zinthu mogwirizana, anafunika kuwadziwitsa zimene anagwirizanazo momveka bwino komanso m’njira yolimbikitsa. Kodi akanachita bwanji zimenezi? Nkhaniyi ikuti: “Atumwi ndi akulu pamodzi ndi mpingo wonse, anagwirizana zosankha amuna pakati pawo, kuti awatumize ku Antiokeya limodzi ndi Paulo ndi Baranaba. Choncho anasankha Yudasi wotchedwa Barasaba ndi Sila, omwe ankatsogolera abale.” Komanso analemba kalata n’kupatsira amuna amenewa kuti ikawerengedwe m’mipingo yonse ku Antiokeya, ku Siriya ndi ku Kilikiya.—Mac. 15:22-26.
12, 13. Kodi panali ubwino wotani chifukwa chotumiza (a) Yudasi ndi Sila? (b) kalata yochokera ku bungwe lolamulira?
12 Monga amuna “omwe ankatsogolera abale,” Yudasi ndi Sila anali oyenera kuimira bungwe lolamulira. Zimene bungwe lolamulira linachita potumiza amuna 4 amenewa zinathandiza Akhristu kuona kuti uthenga umene anabwera nawo sunali wongokhudza nkhani ya mdulidwe ija basi, koma anabweranso ndi malangizo atsopano ochokera ku bungwe lolamulira. Kutumizidwa kwa ‘amuna amene anasankhidwawo’ kukanathandiza kuti Akhristu a Chiyuda a ku Yerusalemu azigwirizana kwambiri ndi Akhristu a mitundu ina omwe anali m’mipingo ina. Pamenepatu bungwe lolamulira linachita zinthu mwanzeru komanso mwachikondi. Mosakayikira, zimenezi zinachititsa kuti anthu a Mulungu azikhala mwamtendere komanso mogwirizana.
13 Kalatayo inapereka malangizo omveka bwino kwa Akhristu a mitundu ina pa nkhani ya mdulidwe komanso zimene iwo anayenera kuchita kuti Yehova aziwakonda ndiponso kuti awadalitse. Mfundo yaikulu m’kalatayo inali yakuti: “Mzimu woyera komanso ifeyo taona kuti ndi bwino kuti tisakusenzetseni mtolo wolemera, kupatula zinthu zofunika zokhazi zomwe ndi kupitiriza kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano, magazi, zopotola ndi chiwerewere. Mukamapewa zinthu zimenezi mosamala kwambiri, zinthu zidzakuyenderani bwino. Tikukufunirani zabwino zonse!”—Mac. 15:28, 29.
14. Kodi zimatheka bwanji kuti anthu a Yehova masiku ano azichita zinthu mogwirizana mosiyana ndi anthu ambiri m’dzikoli?
14 Masiku ano, a Mboni za Yehova onse, omwe ndi oposa 8 miliyoni, m’mipingo yoposa 100,000 padziko lonse, amakhulupirira zinthu zofanana ndiponso amachita zinthu mogwirizana. Kodi zimenezi zimatheka bwanji makamaka poona kuti anthu ambiri ali ndi maganizo atsankho komanso zipwirikiti n’zofala m’dzikoli? Chifukwa chachikulu chimene chimachititsa kuti tikhale ogwirizana n’chakuti Yesu Khristu, amene ndi Mutu wa mpingo amatipatsa malangizo omveka bwino kudzera mwa “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru,” amene ndi Bungwe Lolamulira. (Mat. 24:45-47) Chifukwa china n’chakuti abale padziko lonse amatsatira ndi mtima wonse malangizo ochokera ku Bungwe Lolamulira.
“Anasangalala Chifukwa cha Mawu Olimbikitsawo” (Machitidwe 15:30-35)
15, 16. Kodi nkhani ya mdulidwe inathetsedwa bwanji, nanga n’chiyani chinathandiza kuti ithe bwino choncho?
15 Nkhani ya m’buku la Machitidwe ikupitiriza kutiuza kuti abale ochokera ku Yerusalemu aja atafika ku Antiokeya, “anasonkhanitsa gulu lonse la anthu n’kuwapatsa kalatayo.” Kodi abale kumeneko anatani atawerenga malangizo ochokera ku bungwe lolamulira? “Ataiwerenga [kalatayo], anasangalala chifukwa cha mawu olimbikitsawo.” (Mac. 15:30, 31) Komanso Yudasi ndi Sila “anawakambira abalewo nkhani zambiri ndipo anawalimbikitsa.” Tinganene kuti amuna awiriwa anali “aneneri” mofanana ndi Baranaba, Paulo komanso anthu ena amene ankatchedwa aneneri chifukwa chakuti ankalengeza kapena kuti ankalalikira za chifuniro cha Mulungu.—Mac. 13:1; 15:32; Eks. 7:1, 2.
16 N’zoonekeratu kuti Yehova anadalitsa zonse zimene bungwe lolamulira linachita poyesetsa kupeza njira yabwino yothetsera nkhaniyi. Kodi chinathandiza n’chiyani kuti zinthu ziyende bwino chonchi? Mosakayikira, zinatheka chifukwa cha malangizo omveka bwino komanso a panthawi yake amene bungwe lolamulira linapereka mothandizidwa ndi mzimu woyera komanso Mawu a Mulungu. Chinanso chimene chinathandiza n’choti bungwe lolamuliralo linatsatira njira yabwino ndi yachikondi podziwitsa mipingo zimene bungwelo linagwirizana.
17. Kodi oyang’anira madera masiku ano amachita zotani zimenenso zinkachitika m’nthawi ya atumwi?
17 Potsanzira chitsanzo chimenechi, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova masiku ano limapereka malangizo a panthawi yake kwa abale padziko lonse. Akasankha zochita pa nkhani zosiyanasiyana, amadziwitsa mipingo momveka bwino. Njira imodzi imene amadziwitsira mipingo ndi kudzera mwa oyang’anira madera. Abale odziperekawa amayenda m’mipingo yosiyanasiyana ndipo amapereka malangizo omveka bwino komanso amalimbikitsa mipingoyo. Mofanana ndi Paulo ndi Baranaba, “iwo pamodzi ndi anthu enanso ambiri” amakhala nthawi yaitali ali mu utumiki ‘kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wa mawu a Yehova.’ (Mac. 15:35) Iwo ‘amakambira abale nkhani zambiri ndipo amawalimbikitsa’ ngati mmene Yudasi ndi Sila ankachitira.
18. Kodi anthu a Mulungu ayenera kuchita chiyani kuti Yehova apitirize kuwadalitsa?
18 Nanga bwanji ponena za mipingo? Kodi n’chiyani chimene chimathandiza Akhristu m’mipingo padziko lonse kuti apitirize kukhala mogwirizana ndi mwamtendere m’dziko logawikanali? Kumbukirani kuti patapita nthawi, wophunzira Yakobo analemba kuti: “Nzeru yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera, kenako yamtendere, yololera, yokonzeka kumvera . . . Komanso, chilungamo ndi chipatso chimene anthu obweretsa mtendere amafesa mumtendere.” (Yak. 3:17, 18) Pamene ankalemba mawu amenewa, sitikudziwa ngati Yakobo ankaganizira zimene zinachitika pa msonkhano wa ku Yerusalemu uja kapena ayi. Koma zimene taona m’chaputala 15 cha buku la Machitidwe zikutitsimikizira kuti Yehova amadalitsa anthu ake pokhapokha ngati anthuwo akuchita zinthu mogwirizana komanso mwamtendere.
19, 20. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti mumpingo wa ku Antiokeya munali mtendere ndi mgwirizano? (b) Kodi Paulo ndi Baranaba anayamba kuchita chiyani?
19 Zinali zoonekeratu kuti tsopano mumpingo wa ku Antiokeya munali mtendere ndi mgwirizano. M’malo mokangana ndi abale amene anachokera ku Yerusalemu, abale a ku Antiokeya anayamikira kwambiri kuchezeredwa ndi Yudasi komanso Sila. Nkhaniyi imati: “Atakhala kumeneko kwakanthawi, abalewo anawaperekeza ndipo anabwerera mwamtendere kwa amene anawatuma.”d (Mac. 15:33) Tikukhulupiriranso kuti abale a ku Yerusalemu anasangalala kwambiri pamene amuna awiriwa ankawafotokozera mmene anayendera ku ulendo wawo. Yehova anawasonyeza kukoma mtima kwakukulu powathandiza kuti akwanitse kuchita zimene anatumidwa.
20 Tsopano Paulo ndi Baranaba amene anatsalira ku Antiokeya anayamba kutsogolera mwakhama ntchito yolengeza uthenga wabwino, mofanana ndi mmene oyang’anira madera amachitira masiku ano akamayendera mipingo m’dera lawo. (Mac. 13:2, 3) Abale amenewa anali dalitso lalikulu kwa anthu a Yehova. Komabe, kodi Yehova anapitiriza kudalitsa komanso kugwiritsa ntchito olalikira awiri akhamawa m’njira zina ziti? Tikambirana zimenezi m’mutu wotsatira.
a Onani bokosi lakuti “Yakobo Anali ‘Mchimwene wa Ambuye.’”
b Mwanzeru, Yakobo anatchula mabuku a Mose mmene simumangopezeka Chilamulo chokha, koma mumapezekanso zinthu zina zimene Mulungu anachita. Mabukuwa amanenanso zimene Mulungu anachita posonyeza chifuniro chake asanapereke Chilamulo kwa anthu ake. Mwachitsanzo, m’buku la Genesis tingaone mosavuta kuti Mulungu amadana ndi anthu achigololo, olambira mafano komanso ogwiritsa ntchito magazi molakwika. (Gen. 9:3, 4; 20:2-9; 35:2, 4) Choncho Yehova anapereka mfundo zimene zimagwira ntchito kwa anthu onse, kaya ndi Ayuda kapena a mitundu ina.
c Onani bokosi lakuti “Mmene Bungwe Lolamulira Limagwirira Ntchito Masiku Ano.”
d Mabaibulo ena amaika mawu pavesi 34 osonyeza kuti Sila anasankha kukhalabe ku Antiokeya. (Malembo Oyera komanso Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Koma zimaoneka kuti mawuwa amapezeka m’mipukutu ina yakale ndipo anachita kuwonjezeredwa patapita nthawi.