Amosi
9 Ndinaona Yehova+ ataima pamwamba pa guwa lansembe ndipo anati: “Menya mutu wa chipilala ndipo maziko ake adzagwedezeka. Udulenso mitu ya zipilala zonse ndipo anthu otsalawo ndidzawapha ndi lupanga. Aliyense amene adzathawa ndidzamuphabe, aliyense amene adzayese kuthawa sadzapulumuka.+
2 Akadzakumba Manda* kuti abisalemo,
Ndidzawatulutsa ndi dzanja langa.
Ndipo akadzakwera kumwamba,
Ndidzawatsitsira pansi.
Ndipo akadzathawa pamaso panga nʼkubisala pansi pa nyanja,
Ndidzalamula njoka kuti iwalume pomwepo.
4 Akadzatengedwa ndi adani awo kupita ku ukapolo,
Kumeneko ndidzalamula lupanga kuti liwaphe.+
Ndidzakhala tcheru kuti ndiwabweretsere tsoka, osati kuwapatsa madalitso.+
5 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa, ndi amene amakhudza dziko lapansi,
Moti limasungunuka+ ndipo onse okhala mmenemo adzalira.+
Dziko lonse lidzasefukira ngati mtsinje wa Nailo,
Ndipo kenako lidzaphwa ngati mtsinje wa Nailo wa ku Iguputo.+
6 ‘Amene amamanga makwerero ake kumwamba,
Nʼkumanga nyumba yake pamwamba pa dziko lapansi.
Ndiponso amasonkhanitsa madzi amʼnyanja
Nʼkuwakhuthulira pansi,+
Dzina lake ndi Yehova.’+
7 Yehova akufunsa kuti, ‘Inu Aisiraeli, kodi kwa ine simuli ngati anthu a ku Kusi?
Kodi si ine amene ndinatulutsa Aisiraeli mʼdziko la Iguputo,+
Amenenso ndinatulutsa Afilisiti ku Kerete+ komanso Asiriya ku Kiri?’+
8 Yehova wanena kuti, ‘Taonani, ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndikuyangʼana ufumu wochimwawo,
Ndipo ndidzaufafaniza padziko lapansi.+
Koma nyumba ya Yakobo sindidzaifafaniza yonse.’+
9 ‘Taonani, ine ndikupereka lamulo
Ndipo ndidzagwedeza nyumba ya Isiraeli pakati pa mitundu yonse,+
Ngati mmene munthu amachitira posefa,
Ndipo mwala sudzadutsa nʼkugwera pansi.
10 Anthu anga onse ochimwa adzaphedwa ndi lupanga.
Amene akunena kuti: “Tsoka silitiyandikira kapena kutigwera.”’
11 ‘Pa tsiku limenelo, ndidzadzutsa nyumba* ya Davide+ imene inagwa,
Ndi kukonza malo amene khoma lake linawonongeka.
Ndidzaikonza kuti isakhalenso bwinja.
Ndipo ndidzaimanga kuti ikhale ngati mmene inalili kale.+
12 Ndidzachita zimenezi kuti anthu anga atenge zinthu zotsala za Edomu.+
Ndiponso za mitundu yonse ya anthu imene inkaitanira pa dzina langa,’ watero Yehova, amene akuchita zimenezi.
13 Yehova wanena kuti, ‘Masiku adzafika,
Pamene wolima adzapitirira wokolola,
Ndipo woponda mphesa adzapitirira wonyamula mbewu.+
Mʼmapiri akuluakulu mudzatuluka vinyo wotsekemera+
Ndipo mʼmapiri angʼonoangʼono muzidzatuluka vinyo wambiri.+