Yehova, Mulungu “Wokhululukira”
“Inu, Ambuye [“Yehova,” NW], ndinu wabwino, ndi wokhululukira.”—SALMO 86:5.
1. Kodi ndi katundu wolemera uti amene Mfumu Davide ananyamula, nanga anachipeza motani chitonthozo cha mtima wake wosweka?
MFUMU DAVIDE wa Israyeli wakale anadziŵa kuti chikumbumtima chosweka chingakhale monga katundu wolemera. Iye analemba kuti: “Mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga: ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera. Ndafooka ine, ndipo ndachinjizidwa: ndabangula chifukwa cha kumyuka mtima wanga.” (Salmo 38:4, 8) Komabe, Davide anapeza chitonthozo cha mtima wake wosweka. Iye anadziŵa kuti ngakhale kuti Yehova amadana ndi tchimo, iye sadana ndi wochimwa—ngati wochimwayo alidi wolapa nasiya machimo ake. (Salmo 32:5; 103:3) Pokhala ndi chikhulupiriro chachikulu chakuti Yehova amafunitsitsa kuchitira chifundo olapa, Davide anati: “Inu, Ambuye [“Yehova,” NW], ndinu wabwino, ndi wokhululukira.”—Salmo 86:5.
2, 3. (a) Pamene tichimwa, kodi ndi katundu wolemera uti amene tinganyamule monga chotsatirapo chake, ndipo nchifukwa ninji zimenezi zili zofunika? (b) Kodi ndi ngozi yotani imene ingakhalepo mwa ‘kumizidwa’ ndi malingaliro akuti ndife ochimwa? (c) Kodi Baibulo likutipatsa chitsimikizo chotani ponena za kufunitsitsa kwa Yehova kuti atikhululukire?
2 Pamene tichimwa, ifenso tinganyamule katundu wolemera wa chikumbumtima chosweka monga chotsatirapo chake. Kusweka mtima koteroko nkwachibadwa, komanso nkofunika. Kungatisonkhezere kuchitapo kanthu kuti tikonze zolakwa zathu. Komabe, Akristu ena afooka chifukwa cholingalira kuti iwo ali ochimwa basi. Mtima wawo wodziimba mlandu ungalingalire kuti Mulungu sadzawakhululukira konse, mosasamala kanthu kuti kaya angalape motani. “Zimakhala zopweteka mtima polingalira kuti mwina Yehova sangakukondenso,” anatero mlongo wina, pokumbukira cholakwa chimene iye anachita. Ngakhale pamene anali atalapa ndi kulandira uphungu wothandiza wa akulu a mumpingo, iye anapitirizabe kulingalira kuti Mulungu sangamkhululukire. Iye akufotokoza kuti: “Tsiku lililonse ndimapempha Yehova kuti andikhululukire.” Ngati ‘tamizidwa’ ndi malingaliro akuti ndife ochimwa, Satana angayese kutifooketsa, kutipangitsa kulingalira kuti sitiyenerera kutumikira Yehova.—2 Akorinto 2:5-7, 11.
3 Komatu Yehova saganiza nkomwe zoterozo! Mawu ake amatitsimikizira kuti ngati tisonyeza kulapa kwenikweni kochokera pansi pa mtima, Yehova ali wofunitsitsa, inde wokonzeka, kutikhululukira. (Miyambo 28:13) Choncho, ngati mukulingalira kuti Mulungu sangakukhululukireni, mwinamwake chimene chingafunike ndicho kudziŵa bwino chifukwa chake ndi mmene iye amakhululukira.
Nchifukwa Ninji Yehova Ali “Wokhululukira”?
4. Kodi Yehova amakumbukiranji ponena za mapangidwe athu, nanga zimenezi zimakhudza bwanji mmene iye amachitira nafe?
4 Timaŵerenga kuti: “Monga kummaŵa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa iye.” Nchifukwa ninji Yehova amachitira chifundo? Vesi lotsatira likuyankha kuti: “Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:12-14) Ndithudi, Yehova saiŵala konse kuti ndife zolengedwa zochokera kufumbi, zokhala ndi zophophonya, kapena zifooko, monga zotsatirapo za kupanda ungwiro. Mawu akuti adziŵa “mapangidwe athu” akutikumbutsa kuti Baibulo limayerekezera Yehova ndi woumba ndipo limayerekezera ifeyo ndi zinthu zimene iye anaumba.a (Yeremiya 18:2-6) Woumba amagwira mbiya zake zadothi mwamphamvu komatu mosamala, pokumbukira mpangidwe wake nthaŵi zonse. Chomwechonso, Yehova, Woumba Wamkulu, amachita nafe mosapambanitsa popeza kuti ndife ofooka chifukwa cha uchimo.—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 4:7.
5. Kodi buku la Aroma limafotokoza motani za kumamatira mwamphamvu kwa tchimo pathupi lathu lopanda ungwiro?
5 Yehova amadziŵa kuti uchimo ngwamphamvu zedi. Malemba amafotokoza kuti uchimo uli ngati mphamvu yaikulu imene inagwira munthu kwakuti atha kufa. Kodi mphamvu imeneyo njaikulu motani? M’buku la Aroma, mtumwi Paulo wouziridwayo anafotokoza zimenezi m’mawu omveka bwino kuti: Ndife ‘ogwidwa ndi uchimo,’ mongadi ankhondo amene amalamuliridwa ndi mkulu wankhondo (Aroma 3:9); ‘wachita ufumu’ pakati pa anthu monga mfumu (Aroma 5:21); ‘ukukhalabe’ mkati mwathu (Aroma 7:17, 20); “lamulo” lake likupitirizabe kugwira ntchito mwa ife, kwenikweni kuyesetsa zolimba kulamulirabe mayendedwe athu. (Aroma 7:23, 25) Tili pankhondo yovutadi yolimbana ndi uchimo umene unamamatira zolimba pathupi lathu lopanda ungwiro!—Aroma 7:21, 24.
6. Kodi Yehova amawaona motani amene amafunafuna chifundo chake ndi mtima wosweka?
6 Choncho, Mulungu wathu wachifundo amadziŵa kuti sitingathe kumumvera mwangwiro, mosasamala kanthu kuti mitima yathu ingayesetse motani kumchitira zimenezo. (1 Mafumu 8:46) Iye akutitsimikizira mwachikondi kuti ngati tifunafuna chifundo chake monga atate athu ndi mtima wolapa, iye adzatikhululukira. Wamasalmo Davide anati: “Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.” (Salmo 51:17) Yehova sadzakana, kapena kufulatira, mtima wosweka ndi wolapa chifukwa cha kulemetsedwa ndi uchimo. Zimenezo zikufotokoza bwino chotani nanga kufunitsitsa kukhululukira kwa Yehova!
7. Nchifukwa ninji sitiyenera kuika pachiyeso chifundo cha Mulungu?
7 Komabe, kodi zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kuika pachiyeso chifundo cha Mulungu chifukwa chakuti ndife anthu opanda ungwiro? Kutalitali! Yehova satengeka maganizo. Chifundo chake chili ndi malire. Iye sadzakhululukira konse awo amene moumitsa khosi amachimwa mwadala ndi modzifunira, osafuna kulapa. (Ahebri 10:26-31) Ndiponso, pamene aona mtima umene uli “wosweka ndi wolapa” iye ‘amakhululukira.’ (Miyambo 17:3) Tiyeni tilingalirepo ena mwa mawu amene amagwiritsiridwa ntchito m’Baibulo pofotokoza momveka bwino kuti Mulungu amakhululukira kotheratu.
Kodi ndi Motani Mmene Yehova Amakhululukira Kotheratu?
8. Kodi Yehova amachitanji kwenikweni pamene akhululukira machimo, ndipo kodi zimenezi zingatisonkhezere kuchitanji?
8 Mfumu Davide wolapayo anati: ‘Ndinavomera choipa changa kwa inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.’ (Salmo 32:5) Mawu akuti “munakhululukira” anatembenuzidwa kuchokera ku mawu achihebri amene kwenikweni amatanthauza “kunyamula,” “kutenga.” Panopa agwiritsiridwa ntchito kutanthauza ‘kutaya mlandu, kutaya tchimo, kutaya cholakwa.’ Choncho Yehova ananyamula machimo a Davide nawataya, kunena kwake titero. (Yerekezerani ndi Levitiko 16:20-22.) Mosakayika konse, zimenezi zinachepetsa malingaliro amene Davide anali nawo akuti anali wochimwa. (Yerekezerani ndi Salmo 32:3.) Ifenso tingadalire Mulungu amene amakhululukira machimo a amene amafuna kukhululukidwa mwa kukhulupirira kotheratu nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. (Mateyu 20:28; yerekezerani ndi Yesaya 53:12.) Awo amene machimo awo anyamulidwa ndi kutayidwa ndi Yehova sayenera kumavutikabe maganizo chifukwa cha zolakwa za machimo awo akale.
9. Kodi Yesu anatanthauzanji m’mawu ake akuti: “Mutikhululukire mangaŵa athu”?
9 Yesu anagwiritsira ntchito zimene zimachitika pakati pa obwereketsa ndi amangaŵa pochitira fanizo mmene Yehova amakhululukira. Mwachitsanzo, Yesu anatilangiza kupemphera kuti: “Mutikhululukire mangaŵa athu.” (Mateyu 6:12) Choncho Yesu anayerekezera “machimo” ndi “mangaŵa.” (Luka 11:4) Pamene tichimwa, timakhala “amangaŵa” kwa Yehova. Verebu lachigiriki lotembenuzidwa kuti “kukhululukira” lingatanthauze “kuiŵala, kusiya mangaŵa, mwa kusafunsanso za mangaŵawo.” Kwenikweni, pamene Yehova akhululuka, iye amafafaniza mangaŵa amene tikanafunsidwa kupereka. Choncho ochimwa amene ali olapa sayenera kuda nkhaŵa. Yehova sadzafuna konse kuti alipidwe mangaŵa amene iye anafafaniza!—Salmo 32:1, 2; yerekezerani ndi Mateyu 18:23-35.
10, 11. (a) Kodi ndi fanizo liti limene likugwiritsiridwa ntchito ndi mawu akuti “afafanizidwe,” opezeka pa Machitidwe 3:19? (b) Kodi kukhululukira kotheratu kwa Yehova kukufotokozedwa motani?
10 Pa Machitidwe 3:19, Baibulo likugwiritsira ntchito fanizo lina labwino kwambiri pofotokoza kukhululuka kwa Mulungu motere: “Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu.” Mawu akuti “afafanizidwe” anatembenuzidwa kuchokera ku verebu lachigiriki limene, ngati ligwiritsiridwa ntchito mwafanizo, lingatanthauze “kupukuta, kuchotsa, kufafaniza kapena kusakaza.” Malinga nkunena kwa akatswiri ena azamaphunziro, lingaliro lake ndilo la kufufuta zolemba. Kodi zimenezi zinatheka motani? Inki imene anali kugwiritsira ntchito m’nthaŵi zakale anali kuipanga ndi msanganizo umene unaphatikizapo mkala, manthova a mtengo, ndi madzi. Atatha kugwiritsira ntchito inki imeneyi, munthu ankatha kutenga chinkhupule chonyoŵa ndi kufufuta zolembazo.
11 Amenewo ndi mafotokozedwe abwino kwambiri a mmene Yehova amakhululukira kotheratu. Pamene iye atikhululukira machimo athu, zili monga ngati akutenga chinkhupule ndi kuwafufuta. Sitiyenera kuda nkhaŵa kuti mwina iye adzatiimbanso mlandu chifukwa cha machimo amenewo mtsogolo, popeza kuti Baibulo limavumbula chinachake ponena za chifundo cha Yehova chimene chilidi chodabwitsa likumati: Atakhululuka, iye amaiŵala!
“Sindidzakumbukira Tchimo Lawo”
12. Pamene Baibulo limanena kuti Yehova amaiŵala machimo athu, kodi zimenezi zimatanthauza kuti iye sangathe kuwakumbukira, ndipo nchifukwa ninji mukuyankha motero?
12 Kupyolera mwa mneneri Yeremiya, Yehova analonjeza anthu a m’pangano latsopano kuti: “Ndidzakhululukira mphulupulu yawo, ndipo sindidzakumbukira tchimo lawo.” (Yeremiya 31:34) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti pamene Yehova akhululuka ndiye kuti sangathenso kukumbukira machimowo? Zimenezi sizingatanthauze choncho ayi. Baibulo limatiuza za machimo a anthu ambiri amene anakhululukidwa ndi Yehova, kuphatikizapo Davide. (2 Samueli 11:1-17; 12:1-13) Ndithudi Yehova amakumbukirabe machimo awo, ndipo ifenso tiyenera kutero. Nkhani zonena za machimo awo, kuphatikizapo kulapa kwawo ndi kukhululukidwa kwawo ndi Mulungu, zasungidwa mpaka lero kuti zitipindulitse. (Aroma 15:4) Nanga Baibulo limatanthauzanji pamene linena kuti Yehova ‘sakumbukira’ machimo a anthu amene iye wawakhululukira?
13. (a) Kodi tanthauzo la mneni wachihebri wotembenuzidwa kuti “ndidzakumbukira” limaphatikizapo chiyani? (b) Pamene Yehova anena kuti, “Sindidzakumbukira tchimo lawo,” kodi iye amatitsimikizira chiyani?
13 Mneni wachihebri wotembenuzidwa kuti “ndidzakumbukira” amatanthauza zambiri koposa kungokumbukira zakale chabe. Malinga nkunena kwa buku lotchedwa Theological Wordbook of the Old Testament, kumaphatikizapo “kuchitaponso kanthu kenakake.” Choncho titagwiritsira ntchito lingaliro limeneli, ‘kukumbukira’ tchimo kumaphatikizapo kuchita kanthu kenakake kwa ochimwa. Pamene mneneri Hoseya ananena za Aisrayeli oloŵerera kuti, “[Yehova] adzakumbukira mphulupulu yawo,” mneneriyo anatanthauza kuti Yehova anafuna kuchita kanthu kenakake kwa iwo chifukwa chakuti iwo sanafune kulapa. Choncho, vesilo likumaliza mwakuwonjezera kuti: “Adzalanga zochimwa zawo.” (Hoseya 9:9) Ndiponso, pamene Yehova anena kuti, “Sindidzakumbukira tchimo lawo,” iye akutitsimikizira kuti pamene iye akhululukira wochimwa amene walapa, sadzachita kanthu kenakake kwa iye mtsogolo chifukwa cha machimo amenewo. (Ezekieli 18:21, 22) Choncho iye amaiŵala m’lingaliro lakuti iye satikumbutsa machimo athuwo mobwerezabwereza ncholinga chotiimba mlandu kapena kutilanga mopitirizabe. Pamenepa Yehova akupereka chitsanzo chabwino koposa chakuti ifeyo tichitsanzire pamene tichimwirana ndi ena. Ngati tasemphana maganizo, sibwino kumakumbutsa zolakwa zakale zimene tinagwirizana kuti tinakhululukirana.
Nanga Bwanji za Zotsatirapo Zake?
14. Nchifukwa ninji kukhululukidwa sikutanthauza kuti wochimwa amene walapa ndiye kuti wamasulidwanso ku zotsatirapo zonse za zolakwa zake?
14 Kodi kukhululuka kwa Yehova kumatanthauza kuti wochimwa amene walapa ndiye kuti wamasulidwanso ku zotsatirapo zonse za zolakwa zake? Kutalitali. Machimo athu adzakhala ndi zotsatirapo zake. Paulo analemba kuti: “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” (Agalatiya 6:7) Tingayang’anizane ndi zotsatirapo za zochita zathu kapena zovuta zake, koma pamene iye akhululukira, Yehova sapangitsa kuti tsoka litigwere. Pamene mavuto abuka, Mkristu sayenera kuganiza kuti, ‘Mwinamwake Yehova akundilanga chifukwa cha machimo amene ndinachita kale.’ (Yerekezerani ndi Yakobo 1:13.) Komanso, Yehova satitetezera ku zotsatirapo zosiyanasiyana za zolakwa zathu. Chisudzulo, mimba zapathengo, matenda opatsirana mwa kugonana, kusadaliridwanso kapena kudzichotsa ulemu—zonsezi zingakhale zotsatirapo zomvetsa chisoni za uchimo, ndipo Yehova sadzatitetezera pazimenezi. Kumbukirani kuti ngakhale kuti iye anakhululukira Davide pamachimo ake okhudzana ndi Bateseba ndi Uriya, Yehova sanatetezere Davide ku masoka amene anatsatirapo.—2 Samueli 12:9-14.
15, 16. Kodi lamulo lolembedwa pa Levitiko 6:1-7 linathandiza motani onse aŵiri wodandaula ndi wopalamula?
15 Machimo athu angakhalenso ndi zotsatirapo zina. Mwachitsanzo, talingalirani za nkhani yolembedwa pa Levitiko chaputala 6. Nkhaniyi ikunena za maweruzo operekedwa m’Chilamulo cha Mose pamene munthu achita cholakwa chachikulu mwa kutenga katundu wa Mwiisrayeli mnzake mwachifwamba, kumlanda, kapena mwachinyengo. Kenaka wopalamulayo akukana kuti sanachite zimenezo, inde ngakhale kulumbira monama. Sizikudziŵika kuti akunena zoona ndani. Komabe pambuyo pake, chikumbumtima cha wopalamulayo chasweka ndipo akuulula tchimo lake. Kuti akhululukidwe ndi Mulungu, iye ayenera kuchita zinthu zina zitatu: kubwezera zimene anatenga, kulipira wodandaulayo faindi ya 20 peresenti, ndiponso kupereka nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopalamula. Kenaka, chilamulocho chinati: “Wansembeyo amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa.”—Levitiko 6:1-7; yerekezerani ndi Mateyu 5:23, 24.
16 Lamulo limeneli linali makonzedwe achifundo ochokera kwa Mulungu. Linathandiza wodandaulayo, amene katundu wake anabwezedwa ndiponso amene mosakayika konse anatonthozedwa kwambiri pamene wopalamulayo pomalizira pake anavomereza tchimo lake. Panthaŵi imodzimodziyo, lamulolo linali kuthandiza wopalamulayo amene chikumbumtima chake kenaka chinamsonkhezera kuvomereza zolakwa zake ndi kukonza zolakwazo. Ndithudi, ngati iye akanakana kutero, ndiye kuti sakanakhululukidwanso ndi Mulungu.
17. Pamene ena akhumudwa kapena kuvutika maganizo chifukwa cha machimo athu, kodi Yehova amatiyembekezera kuchitanji?
17 Ngakhale kuti sitikugwiritsira ntchito Chilamulo cha Mose, icho chimatithandiza kuzindikira zimene Yehova amalingalira, kuphatikizapo maganizo ake pankhani ya kukhululukira. (Akolose 2:13, 14) Pamene ena akhumudwa kapena kuvutika maganizo chifukwa cha machimo athu, zimakhala zosangalatsa kwa Yehova ngati ifeyo ‘tikonza cholakwacho’ mulimonse mmene tingathere. (2 Akorinto 7:11) Zimenezi zimaphatikizapo kuvomereza tchimo lathu, kuvomereza zolakwa zathu, ndiponso ngakhale kupepesa kwa wodandaulayo. Kenaka tingapemphere kwa Yehova pamaziko a nsembe ya Yesu ndi kupeza chitonthozo pokhala ndi chikumbumtima choyera ndiponso chitsimikizo chakuti takhululukidwa ndi Mulungu.—Ahebri 10:21, 22.
18. Kodi ndi chilango chotani chimene chingatsagane ndi kukhululukira kwa Yehova?
18 Monga kholo lililonse lachikondi, Yehova angakhululukire mwakupereka chilango chinachake. (Miyambo 3:11, 12) Mkristu wolapa angataye mwaŵi wake wa kutumikira monga mkulu, mtumiki wotumikira, kapena mpainiya. Zingakhale zopweteka kwa iye kutaya kwakanthaŵi mwaŵi umene unali wamtengo wapatali kwa iye. Komabe, chilango choterocho sichitanthauza kuti iye sadzayanjidwanso ndi Yehova kapena kuti Yehova sadzamkhululukira. Kuwonjezera pamenepo, tiyenera kukumbukira kuti pamene Yehova atilanga chimakhala chitsimikizo chakuti amatikonda. Ngati tichivomereza ndi kuchigwiritsira ntchito, chilangocho chingatithandize ndiponso chingatitsogolere ku moyo wosatha.—Ahebri 12:5-11.
19, 20. (a) Ngati mwachimwa, nchifukwa ninji simuyenera kuganiza kuti Yehova sangakuchitireni chifundo? (b) Kodi nkhani yotsatira idzafotokoza chiyani?
19 Nzotsitsimutsa mtima chotani nanga kuzindikira kuti tikutumikira Mulungu “wokhululukira”! Yehova sapenya machimo ndi zolakwa zathu zokha. (Salmo 130:3, 4) Iye amadziŵa zimene zili m’mitima mwathu. Ngati mukuganiza kuti mtima wanu wasweka ndiponso walapa chifukwa cha machimo amene munawachita kumbuyoku, musaganize kuti Yehova sangakuchitireni chifundo. Mosasamala kanthu kuti kaya munachita zolakwa zotani, ngati mwalapadi moona, kuchitapo kanthu kuti mukonze zolakwazo, ndiponso kupemphera mwaphamphu kuti Yehova akukhululukireni pamaziko a mwazi wokhetsedwa wa Yesu, mungakhale ndi chidaliro chachikulu chakuti mawu a pa 1 Yohane 1:9 akunena za inu kuti: “Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.”
20 Baibulo limatilimbikitsa kutsanzira mmene Yehova amakhululukira pamene tichimwirana wina ndi mnzake. Komabe kodi tingayembekezeredwe kukhululukira ndi kuiŵala machimo amene ena atichimwira kufikira pati? Zimenezi zidzafotokozedwa m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Nzosangalatsa kuti mawu achihebri otembenuzidwa kuti “mapangidwe athu” amagwiritsiridwa ntchito ponena za mbiya zadothi zopangidwa ndi woumba.—Yesaya 29:16.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Nchifukwa ninji Yehova ali “wokhululukira”?
◻ Kodi Baibulo limafotokoza motani ponena za mmene Yehova amakhululukira kotheratu?
◻ Pamene Yehova akhululuka, kodi iye amaiŵala m’lingaliro lotani?
◻ Kodi Yehova amatiyembekezera kuchitanji pamene ena akhumudwa ndi machimo athu?
[Chithunzi patsamba 12]
Pamene ena akhumudwa ndi machimo athu, Yehova amatiyembekezera kukonza zolakwazo