Hoseya
Popeza wasiya Mulungu wako chifukwa cha chiwerewere.+
Umakonda kulandira malipiro a uhule wako pamalo onse opunthira mbewu.+
2 Koma malo opunthira mbewu ndiponso oponderamo mphesa sadzakupatsa chakudya,
Ndipo sudzakhala ndi vinyo watsopano.+
3 Iwe sudzapitiriza kukhala mʼdziko la Yehova.+
Mʼmalomwake Efuraimu adzabwerera ku Iguputo,
Ndipo adzadya zinthu zodetsedwa kudziko la Asuri.+
Chifukwa zili ngati chakudya chapamaliro.
Onse amene adzadya chakudyacho adzadzidetsa.
Chakudya chake chidzangokhala cha iyeyo basi,
Ndipo sichidzalowa mʼnyumba ya Yehova.
5 Kodi mudzatani pa tsiku lamsonkhano,
Ndiponso pa tsiku lachikondwerero cha Yehova?
6 Inutu mudzachoka chifukwa dzikolo lidzawonongedwa.+
Iguputo adzakusonkhanitsani pamodzi+ ndipo Mofi adzakuikani mʼmanda.+
Zomera zoyabwa zidzamera pa zinthu zanu zamtengo wapatali zasiliva.
Ndipo mʼmatenti anu mudzamera zitsamba zaminga.
Mneneri wawo adzapusa ndipo munthu wolankhula mawu ouziridwa adzapenga.
Chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zako, ukudedwa kwambiri.”
8 Mlonda+ wa Efuraimu anali ndi Mulungu wanga.+
Koma tsopano njira zonse za aneneri ake+ zili ngati misampha ya wosaka mbalame.
Mʼnyumba ya Mulungu wake muli chidani.
9 Aisiraeli amira mʼzinthu zowononga ngati mʼmasiku a Gibeya.+
Mulungu adzakumbukira zolakwa zawo nʼkuwalanga chifukwa cha machimo awo.+
10 “Isiraeli ndinamupeza ali ngati mphesa zamʼchipululu.+
Ndinaona makolo anu ali ngati nkhuyu zoyambirira pamtengo wa mkuyu.
Koma anapita kwa Baala wa ku Peori,+
Anadzipereka kwa chinthu chochititsa manyazichi.*+
Ndipo anakhala onyansa ngati chinthu chimene ankachikondacho.
11 Ulemerero wa Efuraimu udzauluka ngati mbalame,
Sipadzakhalanso kubereka, kukhala woyembekezera ndiponso kutenga pakati.+
12 Ngakhale atakhala ndi ana,
Ine ndidzapha anawo mpaka sipadzatsala munthu aliyense.+
Tsoka kwa iwo ndikadzawachokera!+
13 Kwa ine, Efuraimu yemwe anadzalidwa pamalo odyetserapo ziweto, anali ngati Turo.+
Koma tsopano iye ayenera kupititsa ana ake kokaphedwa.”
14 Inu Yehova, apatseni zimene mukuyenera kuwapatsa.
Chititsani kuti akatenga mimba azipita padera ndipo mabere awo afote.
15 “Zoipa zawo zonse zinachitikira ku Giligala,+ ndipo ndinadana nawo kumeneko.
Chifukwa cha zochita zawo zoipa, ndidzawathamangitsa panyumba yanga.+
Ndipo sindidzawakondanso.+
Akalonga awo onse ndi amakani.
16 Efuraimu adzamudula ngati mtengo.+
Muzu wake udzauma ndipo sadzaberekanso zipatso.
Komanso ngati angabereke ana, ndidzapha ana ake okondedwawo.”