Chikhulupiriro-Chimatipatsa Mphamvu
CHIKHULUPIRIRO chimatipatsa mphamvu kwambiri. Mwachitsanzo, Satana amafunitsitsa kuwononga ubwenzi wathu ndi Yehova koma chikhulupiriro chimatithandiza ‘kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’ (Aef. 6:16) Chikhulupiriro chikhoza kutithandiza kuthana ndi mavuto aakulu okhala ngati phiri. Paja Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ngati mutakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Choka pano upite apo,’ ndipo lidzachokadi.” (Mat. 17:20) Popeza chikhulupiriro chingatipatse mphamvu zonsezi, ndi bwino kuti tikambirane mafunso awa: Kodi chikhulupiriro n’chiyani? N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi mtima wabwino kuti tikhale ndi chikhulupiriro? Kodi tingalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu? Nanga tiyenera kukhulupirira ndani?—Aroma 4:3.
KODI CHIKHULUPIRIRO N’CHIYANI?
Munthu amene ali ndi chikhulupiriro samangokhulupirira kuti zinthu zinazake ndi zoona. Tikutero chifukwa chakuti ngakhale ziwanda “zimakhulupirira [kuti kuli Mulungu] ndipo zimanjenjemera.” (Yak. 2:19) Ndiye kodi chikhulupiriro n’chiyani?
Baibulo limanena kuti chikhulupiriro chimakhala ndi mbali ziwiri. Choyamba, “chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa.” (Aheb. 11:1a) Ngati muli ndi chikhulupiriro mumakhulupirira ndi mtima wonse kuti chilichonse chimene Yehova amanena n’choona komanso chidzachitika. Mwachitsanzo, Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Ngati anthu inu mungathe kuphwanya pangano langa loti kukhale usana ndi pangano langa loti kukhale usiku, kuti usana ndi usiku zisafike pa nthawi yake, ndiye kuti inenso ndingathe kuphwanya pangano langa ndi Davide mtumiki wanga.” (Yer. 33:20, 21) Kodi mumaopa kuti dzuwa lingalephere kutuluka kapena kulowa n’kuchititsa kuti kusakhale masana kapena usiku? Ngati simukayikira malamulo a m’chilengedwe omwe amachititsa kuti dziko lizizungulira komanso kuyenda mozungulira dzuwa, palibe chifukwa choti muzikayikira kuti mawu a Mulungu, yemwe anapanga malamulowo, angakwaniritsidwe.—Yes. 55:10, 11; Mat. 5:18.
Chachiwiri, chikhulupiriro ndi “umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” M’mawu ena tingati chikhulupiriro ndi umboni wosatsutsika wa zinthu zimene sizioneka koma ndi zenizeni. (Aheb. 11:1b) Kodi pamenepa tikutanthauza chiyani? Yerekezerani kuti mwana wakufunsani kuti, ‘Kodi mumadziwa bwanji kuti kuli mpweya?’ Ngakhale kuti simunauonepo mukhoza kumufotokozera umboni wosonyeza kuti mpweyawo ulipo. Mwachitsanzo, mungamuuze zimene zimachitika tikamapuma kapena mphepo ikamawomba. Mwanayo akamvetsa umboni wake angayambe kukhulupirira kuti kuli mpweya ngakhale kuti sangauone. Mofanana ndi zimenezi, munthu amakhala ndi chikhulupiriro ngati wapeza umboni wosatsutsika.—Aroma 1:20.
MTIMA WABWINO NDI WOFUNIKA
Popeza munthu amayamba kukhulupirira zinthu ngati wapeza umboni wake, tiyenera kuyamba kaye ndi ‘kudziwa choonadi molondola.’ (1 Tim. 2:4) Koma si zokhazi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Munthu amakhala ndi chikhulupiriro mumtima mwake.” (Aroma 10:10) Choncho chofunika si kungokhulupirira mfundo za choonadi koma kuzionanso kuti ndi zamtengo wapatali. Tikatero m’pamene tingasonyeze kuti tili ndi chikhulupiriro pochita zinthu mogwirizana ndi mfundo za choonadi. (Yak. 2:20) Munthu amene alibe mtima woyamikira mfundo za choonadi akhoza kukhala wamakani ngakhale patakhala umboni wooneka bwinobwino. Angatero chifukwa choti safuna kusintha zimene amakhulupirira kapena akufuna kuti azingochita zimene amalakalaka. (2 Pet. 3:3, 4; Yuda 18) N’chifukwa chake m’mbuyomo anthu ena sankakhalabe ndi chikhulupiriro ngakhale kuti anaona zinthu zodabwitsa kwambiri. (Num. 14:11; Yoh. 12:37) Mzimu wa Mulungu umathandiza anthu amene amakonda choonadi, osati mabodza, kuti akhale ndi chikhulupiriro.—Agal. 5:22; 2 Ates. 2:10, 11.
KODI DAVIDE ANALIMBITSA BWANJI CHIKHULUPIRIRO CHAKE?
Mfumu Davide anali chitsanzo chabwino pa nkhani yokhala ndi chikhulupiriro. (Aheb. 11:32, 33) Koma si anthu onse a m’banja lake amene anali ndi chikhulupiriro. Mwachitsanzo, nthawi ina Eliyabu, yemwe anali mchimwene wake wamkulu, anasonyeza kuti alibe chikhulupiriro chifukwa anakalipira Davide pamene ankadandaula za mwano wa Goliyati. (1 Sam. 17:26-28) Munthu sabadwa ali kale ndi chikhulupiriro ndipo sachita kuchitengera kwa makolo. Choncho Davide anali ndi chikhulupiriro chifukwa choti iyeyo anali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu.
Salimo 27 limasonyeza zinthu zimene zinathandiza Davide kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. (Vesi 1) Iye ankaganizira kwambiri zimene zinachitika m’mbuyo komanso mmene Yehova anagonjetsera adani ake. (Vesi 2, 3) Ankayamikiranso kwambiri njira yolambirira imene Yehova anakhazikitsa. (Vesi 4) Iye ankalambira Mulungu limodzi ndi Aisiraeli anzake kuchihema. (Vesi 6) Ankakondanso kupemphera kwa Yehova kuchokera mumtima. (Vesi 7, 8) Komanso ankafuna kulangizidwa ndi Mulungu kuti aziyenda m’njira yake. (Vesi 11) Davide ankaona kuti chikhulupiriro n’chofunika kwambiri moti anafika ponena kuti: “Ndikanakhala wopanda chikhulupiriro . . . ndikanataya chiyembekezo.”—Vesi 13.
KODI TINGALIMBITSE BWANJI CHIKHULUPIRIRO CHATHU?
Mukhoza kukhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi cha Davide ngati mumachitanso zinthu zotchulidwa mu Salimo 27. Popeza kuti munthu ayenera kudziwa zinthu molondola kuti akhale ndi chikhulupiriro, muyenera kuphunzira kwambiri Mawu a Mulungu komanso mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Mukamatero simungavutike kukhala ndi chikhulupiriro chomwe ndi khalidwe lina limene mzimu wa Mulungu umatulutsa. (Sal. 1:2, 3) Mukamaphunzira muyenera kukhalanso ndi mpata woganizira mozama zimene mwaphunzirazo. Popanda kuganizira zinthuzo simungayambe kuzikonda komanso kuyamikira Yehova. Mukayamba kuyamikira kwambiri Yehova mudzakhala ndi mtima wofuna kusonyeza chikhulupiriro chanu pomulambira mumpingo ndiponso pouza ena za chiyembekezo chanu. (Aheb. 10:23-25) Timasonyezanso chikhulupiriro chathu ‘tikamapemphera nthawi zonse.’ (Luka 18:1-8) Choncho “muzipemphera mosalekeza” popanda kukayikira kuti Yehova “amakuderani nkhawa.” (1 Ates. 5:17; 1 Pet. 5:7) Chikhulupiriro chimatithandiza kuti tizichita zinthu zabwino ndipo tikamachita zinthu zabwinozo chikhulupiriro chathu chimalimba.—Yak. 2:22.
TIZIKHULUPIRIRA YESU
Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Khulupirirani Mulungu, khulupiriraninso ine.” (Yoh. 14:1) Choncho tiyenera kukhulupirira Mulungu komanso Yesu. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira Yesu? Tiyeni tikambirane njira zitatu.
Choyamba, muziona kuti dipo ndi mphatso imene Mulungu anapereka kwa inuyo panokha. Paja mtumwi Paulo ananena kuti: “Ndikukhala mokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.” (Agal. 2:20) Mukamakhulupirira Yesu, simungakayikire ngakhale pang’ono kuti dipo linaperekedwa chifukwa cha inuyo, lingathandize kuti machimo anu akhululukidwe, limakuthandizani inuyo kuti muziyembekezera moyo wosatha komanso limasonyeza kuti Mulungu amakukondani kwambiri. (Aroma 8:32, 38, 39; Aef. 1:7) Zimenezi zikhoza kukuthandizani kuti musamadzione ngati wachabechabe.—2 Ates. 2:16, 17.
Chachiwiri, muzikonda kupemphera n’kumalimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Dipo la Yesu ndi limene limatithandiza kuti tizipemphera kwa Yehova “ndi ufulu wa kulankhula, kuti atichitire chifundo ndi kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Aheb. 4:15, 16; 10:19-22) Kupemphera kumatithandizanso kuti tikhale ndi mtima wofuna kupeweratu mayesero.—Luka 22:40
Chachitatu, muzimvera Yesu. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha. Wosamvera Mwanayo sadzauona moyowu, koma mkwiyo wa Mulungu ukhalabe pa iye.” (Yoh. 3:36) Mwina mwaona kuti palembali Yohane anasiyanitsa kukhulupirira ndi kusamvera. Choncho munthu amene amakhulupirira Yesu amamumvera. Mungamvere Yesu poyesetsa kutsatira “chilamulo cha Khristu” chomwe ndi zinthu zonse zimene analamula komanso kuphunzitsa. (Agal. 6:2) Mungamverenso Yesu mukamatsatira malangizo amene amapereka pogwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Mukamamvera Yesu mudzakhala ndi mphamvu zokuthandizani kupirira mavuto okhala ngati mphepo yamkuntho.—Luka 6:47, 48.
‘MUZIDZILIMBITSA PAMAZIKO A CHIKHULUPIRIRO CHANU CHOYERA KOPAMBANA’
Nthawi ina, munthu anafuula n’kuuza Yesu kuti: “Chikhulupiriro ndili nacho! Limbitsani chikhulupiriro changa!” (Maliko 9:24) Munthuyo anali ndi chikhulupiriro koma anali wodzichepetsa ndipo anazindikira kuti ankafunika kuwonjezera chikhulupiriro chake. Mofanana ndi munthuyo, pa nthawi ina tonsefe tidzafunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kuposa chimene tili nacho panopa. Ndipo tikhoza kulimbitsa chikhulupiriro chathu pa nthawi inoyo. Monga taonera, timalimbitsa chikhulupiriro chathu tikamaphunzira Mawu a Mulungu komanso kuwaganizira mozama. Zili choncho chifukwa tikamatero timayamba kuyamikira kwambiri Yehova. Chikhulupiriro chathu chimalimbanso tikamalambira Yehova limodzi ndi Akhristu anzathu, tikamauza anthu ena za chiyembekezo chathu komanso tikamakonda kupemphera. Ndipo tikamalimbitsa chikhulupiriro chathu timalandira mphoto yaikulu kwambiri. Paja Mawu a Mulungu amasonyeza kuti tikamadzilimbitsa pamaziko a chikhulupiriro chathu choyera Mulungu adzapitiriza kutikonda.—Yuda 20, 21.