NKHANI YOPHUNZIRA 34
Zimene Tingachite Kuti Tizisangalalabe Utumiki Wathu Ukasintha
“Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.”—AHEB. 6:10.
NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-3. Kodi anthu a mu utumiki wa nthawi zonse angafunike kusintha utumiki pa zifukwa ziti?
M’BALE Robert ndi mkazi wake dzina lake Mary Jo ananena kuti: “Pambuyo pochita umishonale mosangalala kwa zaka 21, makolo athu onse anayamba kudwala kwambiri. Ngakhale kuti sitinadandaule kuti tiyenera kukawasamalira, zinatipweteka kwambiri kusiya utumiki wathu womwe tinkaukonda.”
2 M’bale William ndi mkazi wake Terrie anati: “Tinalira kwambiri titazindikira kuti sizitheka kupitiriza utumiki wathu chifukwa cha matenda. Zimene tinkafuna kuchita pa moyo wathu zinathera pomwepo.”
3 Aleksey ananena kuti: “Tinkadziwa kuti adani athu akufuna kutseka ofesi ya nthambi imene ndinkatumikirako. Koma zinandiwawabe ataitseka ife n’kuchoka ku Beteli.”
4. Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?
4 Palinso abale ndi alongo ena masauzande ambiri omwe ankatumikira pa Beteli kapena pa utumiki wina ndipo anasinthidwa.b Ziyenera kuti zinali zowawa kwambiri kwa abale ndi alongo okhulupirikawa kusiya utumiki womwe ankaukonda. Kodi n’chiyani chingawathandize kuti asavutike kwambiri? Nanga kodi mungawathandize bwanji? Mayankho a mafunsowa angatithandize tonse kuti tisamavutike zinthu zikasintha pa moyo wathu.
ZIMENE TINGACHITE UTUMIKI UKASINTHA
5. Kodi tingakumane ndi mavuto otani utumiki wathu ukasintha?
5 Kaya tikuchita utumiki wa pa Beteli kapena utumiki wina, timayamba kukonda anthu komanso dera limene tikukhala. Koma ngati tikufunika kusiya utumikiwo, zingatipweteke mumtima. Timasowana ndi abale amene tawasiya ndipo ngati tachoka chifukwa chozunzidwa timadera nkhawa abale athuwo. (Mat. 10:23; 2 Akor. 11:28, 29) Tikapatsidwa utumiki watsopano kapena kusiya utumiki n’kubwerera kwathu mwina tingafunike kuzolowera chikhalidwe chakuderalo. M’bale Robert ndi mkazi wake Mary Jo anati: “Zinali zovuta kuzoloweranso chikhalidwe chathu komanso kulalikira m’chilankhulo chathu. Ndipo tinkakhala ngati alendo m’dziko lathu lomwe.” Anthu ena amene utumiki wawo wasintha amakumana ndi mavuto azachuma. Zikatero angayambe kuchita mantha komanso kukhumudwa. Kodi n’chiyani chingawathandize?
6. Kodi tingatani kuti tisasiye kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?
6 Musasiye kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. (Yak. 4:8) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kudalira Yehova n’kumakumbukira kuti iye ndi “Wakumva pemphero.” (Sal. 65:2) Paja lemba la Salimo 62:8 limati: “Mukhuthulireni za mumtima mwanu.” Yehova “angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza.” (Aef. 3:20) Sikuti amangochita zimene timamupempha. Koma akhoza kuthetsa mavuto athu m’njira imene sitinkayembekezera kapena kuiganizira.
7. (a) N’chiyani chingatithandize kuti tikhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova? (b) Malinga ndi Aheberi 6:10-12, kodi chingachitike n’chiyani tikamatumikirabe Yehova mokhulupirika?
7 Kuti mukhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, muyenera kumawerenga Malemba tsiku lililonse komanso kuwaganizira mozama. M’bale wina amene anali mmishonale anati: “Muzichita kulambira kwa pabanja komanso muzikonzekera misonkhano ngati mmene munkachitira muli pa utumiki umene munkachita.” Muyeneranso kupitiriza kulalikira mwakhama uthenga wabwino mumpingo wanu watsopano. Yehova saiwala anthu amene amapitiriza kumutumikira mokhulupirika ngakhale kuti sangachite zambiri ngati kale.—Werengani Aheberi 6:10-12.
8. Kodi mawu a pa 1 Yohane 2:15-17 angakuthandizeni bwanji kuti mukhale ndi moyo wosalira zambiri?
8 Muzikhala moyo wosalira zambiri. Musalole kuti nkhawa zam’dziko la Satanali zikulepheretseni kutumikira Yehova. (Mat. 13:22) Musalolenso anzanu, achibale anu kapena anthu ena kuti akukakamizeni kufunafuna chuma m’dziko la Satanali. (Werengani 1 Yohane 2:15-17.) Muzidalira Yehova yemwe analonjeza kuti adzakuthandizani pa nthawi yoyenera kuti mukhale ndi chikhulupiriro cholimba, mukhale osangalala komanso mukhale ndi zinthu zonse zofunika pa moyo wanu.—Aheb. 4:16; 13:5, 6.
9. (a) Mogwirizana ndi Miyambo 22:3, 7, n’chifukwa chiyani tiyenera kupewa ngongole zosafunikira? (b) N’chiyani chingatithandize kusankha zochita mwanzeru?
9 Muzipewa ngongole zosafunikira. (Werengani Miyambo 22:3, 7.) Kusamuka kumafuna ndalama ndipo kupanda kusamala mukhoza kutenga ngongole zambiri. Kuti mupewe zimenezi, musamakonde kugula zinthu zosafunika kwenikweni pa ngongole. Tikapanikizika mwina posamalira wachibale amene akudwala, zingativute kusankha bwino kuchuluka kwa ndalama zimene tiyenera kukongola. Pa nthawi ngati imeneyi, muyenera kupemphera komanso kuchonderera Mulungu kuti akuthandizeni kusankha zochita mwanzeru. Mukatero, Yehova adzayankha mapemphero anu pokupatsani mtendere umene “udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu” kuti musachite zinthu mopupuluma.—Afil. 4:6, 7; 1 Pet. 5:7.
10. Kodi tingatani kuti tipeze anzathu atsopano?
10 Muzigwirizana ndi anthu abwino. Muzifotokoza zimene zili mumtima mwanu kwa anzanu abwino, makamaka anthu amene anakumanapo ndi zimene mukukumana nazo. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti maganizo anu akhale m’malo. (Mlal. 4:9, 10) Anzanu amene munapeza kumene munkatumikira adzakhalabe anzanu. Ndipo mu utumiki wanu watsopano muyenera kupeza anzanu ena. Koma kuti mupeze anzanu muyenera kucheza bwino ndi anthu. Kodi mungatani kuti mupeze anzanu atsopano? Muyenera kuwauza zinthu zabwino zimene zakuchitikirani potumikira Yehova kuti aone kuti mumasangalala ndi utumiki. Mwina anthu ena mumpingo sangamvetse chifukwa chake mumakonda kwambiri utumiki wa nthawi zonse. Pomwe ena angasangalale ndi chitsanzo chanu ndipo angafune kukhala anzanu. Koma muyenera kusamala kuti musamadzitame pofotokoza zimene mwachita komanso musamakonde kunena zinthu zimene zakukhumudwitsani.
11. Kodi mungatani kuti banja lanu lizikhalabe losangalala?
11 Ngati mwasiya utumiki wanu chifukwa choti mwamuna kapena mkazi wanu akudwala, musamamuimbe mlandu. Ndipo ngati ndinu amene mukudwala, musamadziimbe mlandu kapena kuganiza kuti mwalepheretsa zolinga zimene mnzanuyo anali nazo. Musaiwale kuti ndinu “thupi limodzi” ndipo munalonjeza pamaso pa Yehova kuti muzisamalirana zivute zitani. (Mat. 19:5, 6) Ngati mwasiya utumiki chifukwa chokhala ndi mimba yosakonzekera, muzithandiza mwana wanuyo kudziwa kuti iyeyo ndi wofunika kwambiri kwa inu kuposa utumiki umene munkachita. Muzitsimikizira mwana wanu kuti mumamuona kuti ndi “mphoto” yochokera kwa Mulungu. (Sal. 127:3-5) Komabe mungachite bwino kumuuza zinthu zabwino zimene zinakuchitikirani mu utumiki wanu. Mukamachita zimenezi mukhoza kuthandiza mwana wanu kuti nayenso azikonda kwambiri kutumikira Yehova ngati inuyo.
KODI ANTHU ENA ANGATHANDIZE BWANJI?
12. (a) Kodi tingathandize bwanji anthu amene ali mu utumiki wa nthawi zonse kuti asasiye utumikiwo? (b) Kodi tingawathandize bwanji kuti asavutike kuzolowera moyo watsopano?
12 Chosangalatsa n’chakuti mipingo komanso abale ndi alongo ambiri amachita zonse zimene angathe pothandiza anthu amene ali mu utumiki wa nthawi zonse kuti asasiye utumiki wawo. Mwachitsanzo, amawalimbikitsa kuti apitirize utumiki, amawapatsa ndalama kapena zinthu zina. Apo ayi, amawathandiza kusamalira achibale awo. (Agal. 6:2) Ngati munthu wina amene anali mu utumiki wa nthawi zonse wabwera mumpingo wanu, musamaganize kuti utumiki wake unasintha chifukwa cholephera kapena kulakwitsa chinachake.c M’malomwake, muziwathandiza kuti azolowere kusinthako. Muziwalandira bwino komanso kuwayamikira pa zimene achita ngakhale kuti panopa sangachite zambiri chifukwa cha matenda. Muziyesetsa kuti muwadziwe bwino komanso muziphunzira pa zimene achita, zimene akudziwa komanso zimene akumana nazo pa moyo wawo.
13. Kodi tingathandize bwanji anthu amene utumiki wawo wasintha?
13 Poyamba, anthu amene utumiki wawo wasintha angafunike kuwathandiza kuti apeze nyumba, ntchito komanso zinthu zina zofunika. Angafunenso kudziwa zinthu zina monga malamulo okhudza misonkho kapena mmene angapezere chithandizo chakuchipatala. Chimene amafuna kwambiri ndi kuwamvetsa osati kumangodandaula ndi zimene zawachitikira. Mwina akuvutika chifukwa cha matenda awo kapena a wachibale wawo. Mwinanso angakhale ndi chisoni chifukwa cha imfa ya mnzawo kapena wachibale wawo.d Akhozanso kumadandaula, mwina akakhala kwaokha, chifukwa choti akusowana ndi abale ndi alongo am’dera limene ankatumikira. Kuti maganizo a anthu ngati amenewa akhale m’malo, zingatenge nthawi yaitali.
14. Kodi abale ndi alongo anathandiza bwanji mlongo wina kuti azolowere utumiki watsopano?
14 Zimene inuyo mungachitire anthu oterewa komanso chitsanzo chanu zikhoza kuwathandiza kuti azolowere moyo watsopano. Mlongo wina amene anatumikira m’dziko lina kwa zaka zambiri anati: “Pamene ndinkachita utumiki, ndinkachititsa maphunziro a Baibulo tsiku lililonse. Koma utumikiwu utasintha, zinkandivuta ngakhale kungowerenga lemba kapena kuonetsa vidiyo mu utumiki. Chosangalatsa n’chakuti abale ndi alongo ankanditenga ku maulendo obwereza kapena maphunziro awo. Ndipo kuona Akhristu olimba mtima komanso akhamawa akuchititsa maphunziro a Baibulo kunkandilimbikitsa kwambiri. Ndinaphunzira mmene ndingayambire kukambirana ndi anthu m’gawo langa latsopano. Zonsezi zinandithandiza kuti ndiyambenso kukhala wosangalala.”
PITIRIZANI KUCHITA ZONSE ZIMENE MUNGATHE
15. Kodi mungatani kuti zinthu zizikuyenderani bwino mu utumiki wanu watsopano?
15 N’zotheka kumasangalala ndi utumiki wanu watsopano. Utumiki ukasintha, musamaganize kuti mwalephera kapena ndinu wosafunika. Koma muziona mmene Yehova akukuthandizirani panopa ndipo muzilalikirabe mwakhama. Muzitsanzira Akhristu okhulupirika akale. Kulikonse kumene ankakhala, ‘ankalengeza uthenga wabwino wa mawu opatulika.’ (Mac. 8:1, 4) Mukamalalikirabe mwakhama zinthu zikhoza kukuyenderani bwino kwambiri. Mwachitsanzo, apainiya amene anathamangitsidwa m’dziko lina anapita m’dziko loyandikana nalo komwe kunkafunikira anthu ambiri olalikira m’chilankhulo chawo. Patangopita miyezi yochepa, magulu atsopano anakhazikitsidwa ndipo anthu ambiri anayamba kusonkhana.
16. Kodi mungatani kuti muzisangalala ndi utumiki wanu watsopano?
16 Baibulo limati: “Chimwemwe chimene Yehova amapereka ndicho malo anu achitetezo.” (Neh. 8:10) Tiziona kuti timakhala osangalala chifukwa chokonda Yehova osati utumiki wathu ngakhale kuti timaukonda kwambiri. Choncho pitirizani kuyenda ndi Yehova komanso kumudalira kuti akupatseni nzeru, azikutsogolerani komanso kukuthandizani. Muzikumbukira kuti munayamba kukonda utumiki umene munkachita chifukwa chakuti munali ndi mtima wofunitsitsa kuthandiza anthu akuderalo. Ndiye muzichita zomwezo pa utumiki umene mukuchita panopa ndipo muziona mmene Yehova akukuthandizirani kuti muyambe kuukonda.—Mlal. 7:10.
17. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani pa nkhani ya utumiki umene tikuchita panopa?
17 Tizikumbukira kuti tidzatumikira Yehova mpaka muyaya, koma utumiki umene tikuchita panopa ukhoza kutha. Ndipotu m’dziko latsopano, tonsefe utumiki wathu ukhoza kudzasintha. Aleksey amene tamutchula kumayambiriro uja amaona kuti zimene zamuchitikira zamuthandiza kuti akonzekere zam’tsogolo. Iye ananena kuti: “Ndinkadziwa kuti Yehova ndi weniweni koma sindinkaona kuti ali pafupi kwambiri ndi ineyo. Ndinkadziwanso kuti kudzakhala dziko latsopano koma zinkaoneka kuti ndi kalekale. Koma panopa ndimaona kuti Yehova ali nane pafupi komanso dziko latsopano layandikira kwambiri.” (Mac. 2:25) Kaya panopa tikuchita utumiki wotani, tiyeni tipitirize kuyenda ndi Yehova. Iye sadzatisiya koma adzatithandiza kuti tizisangalala ndi zilizonse zimene tikuchita pomutumikira.—Yes. 41:13.
NYIMBO NA. 90 Tizilimbikitsana
a Nthawi zina, abale ndi alongo amene akuchita utumiki wa nthawi zonse amafunika kusiya utumiki kapena amapatsidwa utumiki watsopano. Munkhaniyi, tikambirana mavuto amene amakumana nawo komanso zimene angachite kuti asavutike kuzolowera. Tionanso zimene ena angachite powathandiza komanso mfundo zomwe zingathandize tonsefe zinthu zikasintha pa moyo wathu.
b Nawonso abale ambiri achikulire asiyira udindo wawo abale achinyamata. Onani nkhani yakuti “Akhristu Achikulire, Yehova Amayamikira Kukhulupirika Kwanu,” mu Nsanja ya Olonda ya September 2018 ndiponso yakuti “Tizikhalabe ndi Mtendere Wamumtima Zinthu Zikasintha,” mu Nsanja ya Olonda ya October 2018.
c Akulu a mpingo umene ankasonkhana ayenera kulemba msanga kalata yowadziwikitsa kuti asachedwe kuvomerezedwa kuti apitirize kutumikira monga mpainiya, mkulu kapena mtumiki wothandiza.
d Onani nkhani za mu Galamukani! ya Na. 3 ya 2018, yomwe ili ndi mutu wakuti “Mfundo Zothandiza Amene Aferedwa.”
e MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Banja likusiya umishonale ndipo akumva chisoni potsanzikana ndi abale ndi alongo.
f MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Ali kudziko la kwawo, akupemphera kwa Yehova pafupipafupi kuti awathandize pa mavuto amene akukumana nawo.
g MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Banja lija layambiranso utumiki wa nthawi zonse chifukwa chothandizidwa ndi Yehova. Iwo akugwiritsa ntchito chilankhulo chimene anaphunzira ali amishonale polalikira uthenga wabwino kwa anthu omwe asamukira m’gawo la mpingo wawo.