“Pitirizanibe Kuyenda Monga Ana a Kuunika”
“Valani umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chowona ndi m’kukhulupirika.”—AEFESO 4:24, NW.
1. Kodi alambiri a Yehova ngodalitsidwa ndi chiyani? Chifukwa ninji?
YEHOVA MULUNGU ali “Atate wa mauniko akumwamba,” ndipo “mwa iye monse mulibe mdima.” (Yakobo 1:17, NW; 1 Yohane 1:5) Mwana wake, Yesu Kristu, anati ponena za iye mwini: “Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata ine sadzayendanso mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.” (Yohane 8:12) Chifukwa chake, alambiri owona a Yehova, otsatira a Mwana wake, ali odalitsidwa ndi kuunikiridwa—kwa maganizo, makhalidwe, ndi kwauzimu—ndipo akuŵala “monga mauniko m’dziko lapansi.”—Afilipi 2:25.
2. Kodi nkusiyana kotani pakati pa anthu a Mulungu ndi dziko kumene kunanenedweratu?
2 Kalekale, mneneri Yesaya anauziridwa kuneneratu kusiyana uku: ‘Tawonani, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakutulukira, ndi ulemerero wake udzawoneka pa iwe.’ Kwenikweni, anthu onse opatuka kwa Yehova akunenedwa kukhala m’mphamvu ndi chisonkhezero cha ‘olamulira adziko a mdima uno.’—Yesaya 60:2; Aefeso 6:12.
3. Kodi nzifukwa zotani zimene tifunikira kwambiri kudziŵa tanthauzo la uphungu wapanthaŵi yake wa Paulo?
3 Mtumwi Paulo anali wodera nkhaŵa kwambiri kuti Akristu anzake akhalebe osayanjana konse ndi mdimawo. Iye anawafulumiza kuti ‘asayendenso monganso amitundu angoyenda’ koma kuti ‘apitirizebe kuyenda monga ana a kuunika.’ (Aefeso 4:17; 5:8) Iye anafotokozanso mmene iwo akapezera chipambano m’kuchita chimenechi. Lerolino, mdima ndi mdima wa bii umene ukuphimba amitundu wakhuthala kwambiri. Dziko lamira mozamirapo m’chithaphwi cha kululuzika kwa makhalidwe ndi mkhalidwe wauzimu. Alambiri a Yehova ali ndi nkhondo yomakulakula imene afunikira kuimenya. Chifukwa chake, tiri okondweretsedwa kwambiri ndi zimene Paulo ananena.
Phunzirani za Kristu
4. Kodi Paulo anali nchiyani m’maganizo pamene anati: “Simunaphunzira Kristu chotero”?
4 Atafotokoza kulondola zinthu zosapindulitsa ndi chidetso cha dziko, mtumwi Paulo anatembenuziranso maganizo ake pa Akristu anzake mu Efeso. (Chonde ŵerengani Aefeso 4:20, 21.) Paulo anali atatha pafupifupi zaka zitatu akulalikira ndi kuphunzitsa mumzindawo, ndipo ayenera kuti anazoloŵerana ndi ambiri mumpingowo. (Machitidwe 20:31-35) Chotero, pamene anati, ‘Simunaphunzira Kristu chotero,’ anali kusonyeza chidziŵitso chake chaumwini chakuti Akristu a ku Efeso sanaphunzitsidwe mtundu wa chowonadi cholekerera ndi choluluzika chimene chinalolera mipangidwe ina ya mayendedwe oipa kwambiri amene anawalongosola m’mavesi 17 mpaka 19. Iye anadziŵa kuti iwo anaphunzitsidwa bwino ndi molongosoka njira yowona ya moyo Wachikristu monga momwe inachitiridwa chitsanzo ndi Yesu Kristu. Chotero, iwo sanayendenso mumdima monga momwe amitundu anachitira, koma anali ana a kuunika.
5. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kukhala m’chowonadi kwachiphamaso chabe ndi kukhala nacho chowonadi mwa ife?
5 Pamenepo, nkofunika chotani nanga ‘kuphunzira Kristu’ mwanjira yoyenera! Kodi pali njira zolakwika zophunzirira Kristu? Indedi ziripo. Poyambirira, pa Aefeso 4:14, Paulo anali atachenjeza abalewo kuti: ‘Tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa.’ Mwachiwonekere panali ena amene anali ataphunzira za Kristu koma amene anayendabe m’njira za dziko ndipo anayesa ngakhale kukakamiza ena kuchita motero. Kodi izi zikusonyeza upandu wake wakungokhala m’chowonadi, monga momwe ena amanenera, mmalo mwakuti chowonadicho chikhale mwa ife? M’tsiku la Paulo awo amene anali ndi chidziŵitso chachiphamaso chabe anasocheretsedwa mosavuta ndi mwamsanga ndi ena, ndipo zofananazo zimachitika lerolino. Kuti apeŵe zimenezi, Paulo anapitiriza kunena kuti Aefesowo anafunikira kuti ‘akadamva ndi kuphunzitsidwa mwa Yesu.’—Aefeso 4:21.
6. Kodi ndimotani mmene tingaphunzirire, kumva, ndi kuphunzitsidwa ndi Kristu lerolino?
6 Mawu onse akutiwo “kuphunzira,” “kumva,” ndi “kuphunzitsidwa” ogwiritsiridwa ntchito ndi Paulo amapereka lingaliro la kachitidwe ka phunziro ndi malangizo, monga kusukulu. Ndithudi, sitingathe kumva, kuphunzira, kapena kuphunzitsidwa mwachindunji ndi Yesu iye mwini lerolino. Koma iye akuchititsa mkupiti wa kuphunzira Baibulo wa padziko lonse mwakugwiritsira ntchito “kapolo [wake] wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47; 28:19, 20) Tikhoza ‘kuphunzira Kristu’ bwino lomwe ndi molondola ngati timadya nthaŵi zonse chakudya chauzimu choperekedwa ndi gulu la kapolo, kuchiphunzira mwakhama kaya mwaumwini kapena mumpingo, kusinkhasinkha pa icho, ndi kugwiritsira ntchito zimene timaphunzira. Tiyeni titsimikizire kuti tikugwiritsira ntchito mokwanira makonzedwe onsewo kuti tikhoze kunena mowona mtima kuti ‘tamva iye ndipo tinaphunzitsidwa mwa iye.’
7. Kodi nditanthauzo lotani limene lingawonedwe m’mawu a Paulo akuti, “chowonadi chiri mwa Yesu”?
7 Nkokondweretsa kuti pa Aefeso 4:21, atagogomezera kachitidwe ka kuphunzira, Paulo anawonjezera kuti: ‘Monga chowonadi chiri mwa Yesu.’ Opereka ndemanga pa Baibulo ena amatchula chenicheni chakuti Paulo anagwiritsira ntchito mwakamodzikamodzi chabe dzina laumwini la Yesu m’zolembedwa zake. Ndithudi, ndim’chochitika chokhachi m’mene analigwiritsira ntchito motero m’kalata kwa Aefeso. Kodi pangakhale chifukwa chapadera chochitira motero? Mwinamwake Paulo anafuna kumveketsa chitsanzo choperekedwa ndi Yesu monga munthu. Kumbukirani kuti Yesu panthaŵi ina anati ponena za iye mwini: ‘Ine ndine njira, ndi chowonadi, ndi moyo.’ (Yohane 14:6; Akolose 2:3) Yesu anati: ‘Ine ndine . . . chowonadi’ chifukwa chakuti sanangochilankhula ndi kuchiphunzitsa koma anachikhalira moyo ndi kukhala chitsanzo chake changwiro. Inde, Chikristu chowona sichiri lingaliro chabe koma njira ya moyo. ‘Kuphunzira Kristu’ kumaphatikizapo kuphunzira kumtsanzira m’kukhalira moyo chowonadi. Kodi mumachititsa moyo wanu kutsatira chitsanzo cha Kristu? Kodi mumalondola mapazi ake mosamalitsa tsiku ndi tsiku? Kokha mwakutero ndipamene tingapitirize kuyenda monga ana a kuunika.
“Vulani Umunthu Wakale”
8. Kodi ndifanizo lotani limene Paulo anagwiritsira ntchito pa Aefeso 4:22, 24, ndipo nchifukwa ninji liri loyenerera?
8 Kusonyeza mmene tingapezere chipambano ‘m’kuphunzira Kristu’ ndi kuyenda monga ana a kuunika, Paulo anapitiriza kunena, pa Aefeso 4:22-24, kuti pali njira zitatu zimene tiyenera kutsatira. Yoyamba ya zimenezi ndiyi: “Muyenera kuvula umunthu wakale umene umagwirizana ndi njira yanu yakale yamayendedwe ndipo umene waluluzidwa malinga ndi zikhumbo zake zonyenga.” (Aefeso 4:22, NW) Mawu akuti “kuvula” (“kuchotsa,” Kingdom Interlinear) ndi “kuvala” (vesi 24) amasonyeza m’maganizo chithunzi chakuvula ndi kuvala malaya. Aŵa ndimawu okuluŵika amene Paulo anagwiritsira ntchito kaŵirikaŵiri, ndipo ali ogwira mtima. (Aroma 13:12, 14; Aefeso 6:11-17; Akolose 3:8-12; 1 Atesalonika 5:8) Pamene malaya athu adetsedwa kapena achita mathotho, monga ngati pakudya, timawasintha mwamsanga. Kodi sitiyenera kukhala odera nkhaŵa mofananamo ponena za kudetsedwa kulikonse kwa mkhalidwe wathu wauzimu?
9. Kodi ndimotani mmene munthu amavulira umunthu wakale?
9 Pamenepo, kodi ndimotani mmene munthu angavulire umunthu wakale? Mneni wakuti “kuvula” m’chinenero choyambirira ali mumpangidwe wotchedwa aorist Mchingelezi, wosonyeza kuchitika kamodzi. Amasonyeza kachitidwe kamene kachitika kamodzi kokha kapena kamodzi kwa nthaŵi yonse. Izi zimatisonyeza kuti “umunthu wakale” (“munthu wakale,” Kingdom Interlinear), limodzi ndi “njira [yathu] yakale ya kayendedwe,” ziyenera kuvulidwa mwakachitidwe kotsimikiza ndi kotheratu. Sichinthu chimene tingazengeleze nacho mwadala ndi kupezabe chipambano ayi. Chifukwa ninji ayi?
10. Kodi nchifukwa ninji munthu ayenera kukhala wotsimikiza mtima ndi wofunitsitsa kuvula umunthu wakale?
10 Mawu akuti “kululuzidwa” amasonyeza kuti “munthu wakaleyo” ali panjira yopitirizabe patsogolo ya kululuzika kwa makhalidwe, kuchokera pakuipa kufika pakuipitsitsa. Kunena zowona, chifukwa chakukana kuunikiridwa kwauzimu, mtundu wa anthu wonse ukumka numira nthaŵi zonse m’makhalidwe onyansa. Izi ziri chotulukapo cha ‘zikhumbo zonyenga,’ anatero Paulo. Zikhumbo zakuthupi nzonyenga chifukwa chakuti zingawoneke kukhala ziribe upandu, koma nzowononga potsirizira pake. (Ahebri 3:13) Ngati siziletsedwa, mapeto amakhala chidetso ndi imfa. (Aroma 6:21; 8:13) Ndicho chifukwa chake umunthu wakale uyenera kuvulidwa, kuchotsedwa motsimikizirika ndi kotheratu, monga momwe chovala chakale, chodetsedwa chimavulidwira.
“Mzimu wa Maganizo” Watsopano
11. Kodi kupangidwa watsopano mwauzimu kuyenera kuyambira kuti?
11 Munthu amene atuluka m’matope sangofunikira kuvula zovala zake zalitsirozo, komanso kusambika thupi lake bwino lomwe asanavale chovala china chatsopano ndi choyera. Zimenezo nzimenedi Paulo anafotokoza kukhala njira yachiŵiri yopezera kuunikiridwa kwauzimu. “Muyenera kukhala atsopano m’mphamvu yosonkhezera maganizo anu.” (Aefeso 4:23, NW) Monga momwe anatchulira poyamba, pamavesi 17 ndi 18, amitundu akuyenda “m’kusapindulitsa kwa maganizo awo” ndipo “ali mumdima wamaganizo.” Moyenerera, m’maganizo, phata la kuzindikira ndi chidziŵitso, ndim’mene kusintha kuyenera kuyambira. Kodi zimenezi zingachitidwe motani? Paulo anafotokoza kuti ndimwakuchititsa mphamvu yosonkhezera maganizo athu kukhala yatsopano. Kodi mphamvu imeneyo ndiyo chiyani?
12. Kodi mphamvu yosonkhezera maganizo nchiyani?
12 Kodi mphamvu yosonkhezera maganizo athu yotchulidwa ndi Paulo ndiyo mzimu woyera? Ayi. Mawu akuti “mphamvu yosonkhezera maganizo athu” m’lingaliro lenileni amaŵerengedwa kuti “mzimu wa maganizo ako.” Palibe m’Baibulo pamene mzimu woyera wa Mulungu umanenedwa kukhala wa munthu kapena mbali ya munthu. Liwulo “mzimu” kwakukulukulu limatanthauza “mpweya,” koma limagwiritsiridwanso ntchito m’Baibulo “kusonyeza mphamvu imene imachititsa munthu kusonyeza mkhalidwe wamaganizo wakutiwakuti, malingaliro, kapena mtima kutsatira kachitidwe kakutikakuti kapena njira.” (Insight on the Scriptures, Voliyamu 2, tsamba 1026.) Chotero “mzimu wa maganizo” ndiwo mphamvu imene imachititsa kapena kusonkhezera maganizo athu, mkhalidwe wa maganizo athu ndi chikhoterero cha mtima.
13. Kodi nchifukwa ninji chikhoterero chathu chamaganizo chiyenera kupangidwa chatsopano?
13 Chikhoterero chachibadwa cha maganizo opanda ungwiro chimakhala pa zinthu zowoneka, zakuthupi ndi za m’dziko. (Mlaliki 7:20; 1 Akorinto 2:14; Akolose 1:21; 2:18) Ngakhale ngati munthu avula umunthu wakale ndi machitidwe ake oipa, chikhoterero cha maganizo ake chauchimo ngati sichisinthidwa mwamsanga kapena pambuyo pake chidzamsonkhezera kubwerera ku zimene anasiya. Kodi ichi sichimene chachitika kwa ambiri amene, mwachitsanzo, ayesa kuleka kusuta, uchidakwa, kapena machitidwe ena oipa? Pamene sanachite kuyesayesa kulikonse kwakuti akhalebe atsopano mwa mphamvu yosonkhezera maganizo awo, kubwevuka kunali pafupifupi kosapeŵeka. Kusandulika kwenikweni kulikonse kuyenera kuloŵetsamo kusandulika kotheratu kwa maganizo.—Aroma 12:2.
14. Kodi ndimotani mmene mphamvu yosonkhezera maganizo ingapangidwire yatsopano?
14 Pamenepa, kodi ndimotani mmene munthu angachititsire mphamvu imeneyo kukhala yatsopano kuti isonkhezere maganizo ake m’njira yolungama? Mneni wakuti “kukhalitsidwa watsopano” m’malemba Achigiriki ali mumpangidwe wakuti, tsopano lino, kusonyeza kachitidwe kamene kakupitirizabe. Chotero mphamvu yosonkhezera maganizo imakhalitsidwa yatsopano mwakupitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu a chowonadi ndi kusinkhasinkha pa zimene amatanthauza. Asayansi amatiuza kuti muubongo mwathu, mauthenga mumpangidwe wa zizindikiro zolunzanitsidwa zamagetsi kapena zamakemiko amayenda kuchokera ku selo imodzi yotchedwa neuron kumka ku ina, akumadutsa mfundo zambiri zotchedwa synapses. “Chikumbukiro chakutichakuti chimapangika pa synapse (mfundo) ya minyewa pamene chizindikiro cha mphamvu yamagetsicho chidzerapo, chikumasiya chisindikizo chake,” limatero bukhu lakuti The Brain. Pamene chizindikiro chofananacho chidzerapo nthaŵi yotsatira, maselo a minyewayo amachizindikira ndipo amayankha mofulumira. M’kupita kwanthaŵi, zimenezi zimapanga njira yatsopano yakulingalira mwa munthuyo. Pamene tipitiriza kuloŵetsa chidziŵitso chabwino chauzimu, njira yatsopano yakulingalira imapangika, ndipo mphamvu yosonkhezera maganizo athu imakhalitsidwa yatsopano.—Afilipi 4:8.
‘Valani Umunthu Watsopano’
15. Kodi umunthu watsopano uli watsopano m’lingaliro lotani?
15 Potsirizira, Paulo akuti: “Muyenera kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chowona ndi m’kukhulupirika.” (Aefeso 4:24, NW) Inde, Mkristu amavala umunthu watsopano. “Watsopano” panopa umasonya, osati ku nthaŵi, koma ku mkhalidwe. Ndiko kuti, suli watsopano m’lingaliro la kukhala wampangidwe watsopano koposa. Uli umunthu watsopano kotheratu, “wolengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.” Pa Akolose 3:10, (NW), Paulo anagwiritsira ntchito kalankhulidwe kofananako nanena kuti “unapangidwa watsopano mogwirizana ndi chifanizo cha Uyo amene anaulenga.” Kodi umunthu watsopano umenewu umafikira kukhalapo motani?
16. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti umunthu watsopano ‘ngwolengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu’?
16 Yehova Mulungu analenga anthu aŵiri oyambirira, Adamu ndi Hava, m’chifanizo Chake ndi m’chikhalidwe. Iwo anapangidwa ndi mikhalidwe yabwino yakuthupi ndi yauzimu imene inawasiyanitsa kwambiri ndi chilengedwe cha zinyama. (Genesis 1:26, 27) Ngakhale kuti chipanduko chawo chinaloŵetsa mtundu wonse wa anthu mu uchimo ndi chivundi, ife, monga mbadwa za Adamu, tidakali ndi kuthekera kwakusonyeza mikhalidwe yabwino yakuthupi ndi yauzimu. Chifuniro cha Mulungu nchakuti awo amene amasonyeza chikhulupiriro m’nsembe yadipo ayenera kutaya umunthu wakale ndi kusangalala ndi “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”—Aroma 6:6; 8:19-21; Agalatiya 5:1, 24.
17. Kodi nchifukwa ninji chilungamo ndi kukhulupirika ili mikhalidwe yapadera mu umunthu watsopano?
17 Chilungamo chowona ndi kukhulupirika ndiyo mikhalidwe iŵiri yotchulidwa ndi Paulo monga yopezedwa mu umunthu watsopano. Ichi chimagogomezeranso kuti umunthu watsopano umapangidwa watsopano mogwirizana ndi chifanizo cha Uyo amene anaulenga. Salmo 145:17 limatiuza kuti: ‘Yehova ali wolungama m’njira zake zonse, ndi wachifundo m’ntchito zake zonse.’ Ndipo Chivumbulutso 16:5 chimati ponena za Yehova: ‘Muli wolungama, amene muli, nimunali, Wolungama inu.’ Kunena zowona, chilungamo ndi kukhulupirika ndimikhalidwe yofunika kwambiri ngati titi tikhale ndi moyo mogwirizana ndi kulengedwa m’chifanizo cha Mulungu, tikumasonyeza ulemerero wake. Tikhaletu ofanana ndi Zekariya, atate wa Yohane Mbatizi, amene anasonkhezeredwa ndi mzimu woyera kutamanda Mulungu kaamba ka kupatsa anthu Ake “mwaŵi wakupereka utumuki wopatulika mopanda mantha kwa iye limodzi ndi kukhulupirika ndi chilungamo.”—Luka 1:74, 75.
“Pitirizani Kuyenda Monga Ana a Kuunika”
18. Kodi ndimotani mmene Paulo watithandizira kuwona njira za dziko monga momwe ziriridi?
18 Pokhala kuti tapenda mwatsatanetsatane mawu a Paulo pa Aefeso 4:17-24, tiri ndi zochuluka zakuzilingalira. M’mavesi 17 mpaka 19, Paulo akutithandiza kuwona njira za dziko monga momwe ziriridi. Pokana chidziŵitso cha Mulungu ndi kuumitsa mitima yawo kwa iye, awo omwe adakali m’dziko adzichotsa okha ku magwero owona a moyo. Chotsatirapo, popanda chifuno chenicheni ndi njira, zolondola zawo zimangothera m’kupusa ndi kupanda pake. Iwo akumira mosalekeza muutchisi wamakhalidwe ndi wauzimu. Ndimkhalidwe womvetsa chisoni chotani nanga! Ndipo ndichifukwa champhamvu chotani nanga chakuti tikhalire otsimikiza mtima kupitirizabe kuyenda monga ana a kuunika!
19. Kodi nchilimbikitso chotsirizira chotani chimene Paulo akutipatsa chakupitiriza kuyenda monga ana a kuunika?
19 Ndiyeno, pamavesi 20 ndi 21, Paulo akugogomezera kufunika kwa kuphunzira chowonadi mwakhama kotero kuti sitimangogwirizanitsidwa ndi chowonadi koma kuchikhalira moyo monga momwe Yesu anachitira. Potsirizira, pamavesi 22 ndi 24, iye akutifulumiza kuvula umunthu wakale ndi kuvala watsopano—kotheratu, ndi motsimikiza mtima. Pakali pano, tiyenera kupitirizabe kutsogoza mikhalidwe yathu yamaganizo m’njira yabwino yauzimu. Koposa zonse, tiyenera kuyang’ana kwa Yehova kaamba ka chithandizo pamene tikupitirizabe kuyenda monga ana a kuunika. ‘Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzaŵala kutuluka mumdima, ndiye amene anaŵala m’mitima yathu kutipatsa chiŵalitsiro cha chidziŵitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Kristu.’—2 Akorinto 4:6.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndimotani mmene ‘tingaphunzirire Kristu’ Lerolino?
◻ Kodi nchifukwa ninji umunthu wakale uyenera kuvulidwa motsimikiza mtima?
◻ Kodi mphamvu yosonkhezera maganizo nchiyani, ndipo ndimotani mmene imapangidwira kukhala yatsopano?
◻ Kodi ndimikhalidwe yotani imene imasonyeza umunthu watsopano?
[Chithunzi patsamba 15]
Yesu anati: ‘Ine ndine njira, ndi chowonadi, ndi moyo’
[Chithunzi patsamba 16]
“Vulani umunthu wakale ndi zochita zake”—mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m’kamwa, ndi kunama.—Akolose 3:8, 9
[Chithunzi patsamba 17]
“Valani umunthu watsopano . . . wolengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chowona ndi m’kukhulupirika.”—Aefeso 4:24, NW