‘Valani Zida za Kuunika’
‘Usiku wapita, ndi dzuwa layandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ntivale [zida za, “NW”] kuunika.’—AROMA 13:12.
1, 2. Kodi ndimotani mmene Ayuda ambiri a m’zaka za zana loyamba anachitira kulinga ku “kuunika kweni kweni,” ndipo kodi anatero mosasamala kanthu za maubwino otani?
YESU KRISTU ndiye “kuunika kweni kweni, kumene kuunikira anthu onse.” (Yohane 1:9) Pamene iye anadza monga Mesiya mu 29 C.E., anafikira kwa mtundu womwe unasankhidwa ndi Mulungu kuti ukhale mboni Zake ndi umene, mwadzina chabe, udali wodzipatulira kwa Yehova. (Yesaya 43:10) Aisrayeli ambiri anakhala akudikirira Mesiya, ndipo ambiri anadziŵa ena a maulosi omwe akamzindikiritsa. Ndiponso, Yesu analalikira m’mbali zonse za Palestina, akumachita zizindikiro mowonekera kotheratu kwa makamu. Makamu anathamangira kukamva iye ndipo anakondweretsedwa ndi zimene anawona ndi kumva.—Mateyu 4:23-25; 7:28, 29; 9:32-36; Yohane 7:31.
2 Komabe, kumapeto kwake, Ayuda ambiri anamkana Yesu. Uthenga Wabwino wa Yohane ukuti: ‘Anadza kwa zake za iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamlandira iye.’ (Yohane 1:11) Kodi nchifukwa ninji zinali tero? Yankho la funso limenelo lidzatithandiza kupeŵa kubwereza chophophonya chawo. Lidzatithandiza ‘kuvula ntchito za mdima, nkuvala [zida za, NW] kuunika,’ mwakutero kupeŵa chiweruzo chopanda chiyanjo chonga chija cholandiridwa ndi Israyeli wa m’zaka za zana loyamba.—Aroma 13:12; Luka 19:43, 44.
Chitsutso Kuchokera kwa Olamulira Achipembedzo
3. Kodi ndimotani mmene atsogoleri achipembedzo Achiyuda anatsimikizira kukhala “atsogoleri akhungu”?
3 Mu Israyeli atsogoleri achipembedzo anali patsogolo kukana kuunikako. Mosasamala kanthu za kukhala aphunzitsi ‘achilamulo,’ iwo anakakamiza anthu ndi dongosolo lotopetsa la malamulo omwe nthaŵi zambiri ankasemphana ndi Chilamulo cha Mulungu. (Luka 11:45, 46) Chotero, iwo ‘anayesa achabe mawu a Mulungu mwa mwambo umene iwo anaupereka.’ (Marko 7:13; Mateyu 23:16, 23, 24) Iwo anali “atsogoleri akhungu,” otsekereza kuunikako kuti kusawalikire.—Mateyu 15:14.
4, 5. (a) Kodi Afarisi anachita motani pamene Ayuda ambiri anayamba kukaika kaya ngati Yesu anali Mesiya? (b) Kodi ndi mkhalidwe woipa wamtima wotani umene Afarisi anavumbula?
4 Panthaŵi ina pamene Aisrayeli ambiri anali kukaikira kuti kaya Yesu analidi Kristu, Afarisi ochititsidwa manthawo anatumiza anyamata ena kukamgwira. Anyamatawo anabwera ali chimanjamanja, namati: ‘Nthaŵi yonse palibe munthu analankhula chotero.’ Mosakondweretsedwa, Afarisiwo anafunsa anyamatawo kuti: ‘Kodi mwasokeretsedwa inunso? Kodi wina wa akulu anakhulupirira iye, kapena wa Afarisi? Koma khamu ili losadziŵa chilamulo, likhala lotembereredwa.’ Nikodemo, chiŵalo cha Bwalo la Akulu, anatsutsa nati sikunali kololedwa kuweruza munthu asanamve kwa munthuyo. Monyansidwa, Afarisi anatembenukira kwa iye nati: ‘Kodi iwenso uli wotuluka m’Galileya? Santhula, nuone kuti m’Galileya sauka mneneri.’—Yohane 7:46-52.
5 Kodi nchifukwa ninji atsogoleri achipembedzo a mtundu wodzipatulira kwa Mulungu anachita motero? Chifukwa chakuti anakulitsa mkhalidwe woipa wa mtima. (Mateyu 12:34) Lingaliro lawo loipidwa ndi anthu wamba linavumbula kunyada kwawo. Kunena kwawo kwakuti ‘wina wa akulu kapena Afarisi sanakhulupirira iye’ kunapereka lingaliro lonyada lakuti Mesiya akadakhala weniweni kokha ngati iwo anamvomereza. Ndiponso, iwo anali osawona mtima, akumayesa kunyoza Yesu chifukwa chakuti anachokera ku Galileya, pamene kuli kwakuti kusanthula kokhweka kukanavumbula kuti kwenikwenidi anabadwira m’Betelehemu, malo obadwira oloseredwa a Mesiya.—Mika 5:2; Mateyu 2:1.
6, 7. (a) Kodi atsogoleri achipembedzo anachita motani ndi kuuka kwa Lazaro? (b) Kodi Yesu ananenanji kuvumbula kukonda mdima kwa atsogoleri achipembedzo?
6 Chitsutso champhamvu cha atsogoleri achipembedzo ameneŵa ku kuunikako chinasonyezedwa mokhutiritsa pamene Yesu anaukitsa Lazaro. Kwa munthu woopa Mulungu, kachitidwe koteroko kakanakhala umboni wakuti Yesu anali ndi chichilikizo cha Yehova. Komabe, atsogoleri achipembedzowo anangowona chiwopsezo chakutaikiridwa malo awo apadera. Iwo anati: ‘Titani ife? chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri. Ngati timleka iye kotero, onse adzakhulupirira iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.’ (Yohane 11:44, 47, 48) Choncho anapanga upo wakupha onse aŵiri Yesu ndi Lazaro, mwinamwake akumayembekezera kuti mwanjirayi akazima kuunikako.—Yohane 11:53, 54; 12:9, 10.
7 Chotero, atsogoleri achipembedzo amenewo a mtundu wa Mulungu anatalikirana ndi kuunikako chifukwa cha kudzikuza, kunyada, kusawona mtima kwaukatswiri, ndi chikondwerero champhamvu chaumwini. Chakumapeto kwa uminisitala wake, Yesu anavumbula liŵongo lawo, akumati: ‘Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! chifukwa mutsekera anthu ufumu wa kumwamba pamaso pawo; pakuti inu nokha simuloŵamo, ndipo muŵaletsa amene alikuloŵa, kuti asaloŵe.’—Mateyu 23:13.
Dyera ndi Kunyada
8. Kodi ndizochitika zotani za ku Nazarete zimene zinavumbula mkhalidwe woipa wamtima wa anthu ena kumeneko?
8 Mwachisawawa, anthu Achiyuda a m’zaka za zana loyamba anatsanzira atsogoleri awo achipembedzo kukana kuunika chifukwa cha mkhalidwe wawo woipa wa mtima. Mwachitsanzo, panthaŵi ina Yesu anaitanidwa kukalankhula m’sunagoge ku Nazarete. Iye anaŵerenga nalongosola ndime ya mu Yesaya, ndipo poyamba, mpingowo unamvetsera iye. Koma pamene anasonyeza kufanana kwa mbiri yakale kumene kunavumbula dyera lawo ndi kusoŵa chikhulupiriro, iwo anakwiya nayesa kumupha. (Luka 4:16-30) Kunyada, pakati pa zikhoterero zina zoipa, ndiko kunawaletsa kuvomereza moyenera kuunikako.
9. Kodi ndimotani mmene malingaliro oipa a gulu lalikulu la Agalileya anavumbulidwira?
9 Pachochitika china, Yesu anadyetsa mozizwitsa khamu lalikulu m’mphepete mwa Nyanja ya Galileya. Mboni za chozizwitsachi zinati: “Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m’dziko lapansi.” (Yohane 6:10-14) Pamene Yesu anapita kumalo ena ndi ngalawa, khamulo linamtsatira. Komabe, Yesu anadziŵa kuti cholinga cha ambiri sichinali chikondi cha kuunikako. Iye anawauza kuti: ‘Mundifuna ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimunakhuta.’ (Yohane 6:26) Pasanapite nthaŵi yaitali, iye anatsimikiziridwa kukhala wolondola pamene ambiri amene anamtsata anabwerera kudziko. (Yohane 6:66) Mkhalidwe wadyera wakuti “palibe changa” unatsekereza kuunikako.
10. Kodi Akunja ambiri anachita motani ndi kuunikako?
10 Pambuyo pa imfa ndi kuuka kwa Yesu, Ayuda okhulupirira anapitiriza kupereka kuunikako kwa Ayuda ena, koma oŵerengeka okha anavomereza. Chifukwa chake, mtumwi Paulo ndi ena, akumatumikira monga “kuunika kwa amitundu,” anafalitsa mbiri yabwino kumaiko ena. (Machitidwe 13:44-47) Anthu ambiri osakhala Ayuda anavomereza, koma kachitidwe kachisawawa kanakhala monga kamene Paulo anakalongosola motere: ‘Tilalikira Kristu wopachikidwa, . . . [uthenga womwe uli] kwa amitundu chinthu chopusa.’ (1 Akorinto 1:22, 23) Anthu ambiri osakhala Ayuda anakana kuunikako chifukwa chakuti anachititsidwa khungu ndi malaulo achikunja kapena nthanthi zakudziko.—Machitidwe 14:8-13; 17:32; 19:23-28.
‘Kuitanidwa Kutuluka Mumdima’
11, 12. Kodi ndani omwe anavomereza kuunikako m’zaka za zana loyamba, ndipo kodi ndani amene amavomereza lerolino?
11 M’zaka za zana loyamba, mosasamala kanthu za kupanda chivomerezo kwachisawawa, anthu ambiri owongoka mtima ‘anaitanidwa kutuluka mumdima, kuloŵa kuunika kwa Mulungu kodabwitsa.’ (1 Petro 2:9) Ponena za ameneŵa mtumwi Yohane akulemba kuti: ‘Koma onse amene anamlandira [Kristu], kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake.’ (Yohane 1:12) Kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., okonda kuunika ameneŵa anabatizidwa ndi mzimu woyera ndipo anakhala ana a Mulungu ndi chiyembekezo chakulamulira ndi Yesu mu Ufumu wake wakumwamba.
12 M’tsiku lathu omalizira a ana odzozedwa a Mulungu asonkhanitsidwa, ndipo pokwaniritsa ulosi wa Danieli, iwo ‘akuwala ngati kunyezimira kwa thambo . . . kutembenuza ambiri atsate chilungamo.’ (Danieli 12:3) Iwo alola kuunika kwawo kuwalikira ku ukulu wakuti “nkhosa zina” zoposa mamiliyoni anayi zakokedwera ku chowonadi ndipo zikusangalala ndi kaimidwe kolungama pamaso pa Mulungu. (Yohane 10:16) Awanso, amawalitsa kuunikako padziko lonse, kotero kuti tsopano kuunikako kukuwala kuposa ndi kalelonse. M’tsiku lathu, mofanana ndi m’zaka za zana loyamba, ‘mdima [sunagonjetse, NW] kuunikaku.’—Yohane 1:5.
‘Mwa Mulungu Monse Mulibe Mdima’
13. Kodi ndichenjezo lotani limene mtumwi Yohane anatipatsa?
13 Komabe, sitiyenera kuiwala konse chenjezo la mtumwi Yohane ili: ‘Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa iye monse mulibe mdima. Tikati kuti tiyanjana ndi iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita chowonadi.’ (1 Yohane 1:5, 6) Mwachiwonekere, nkotheka kwa Akristu kuchita cholakwa chofanana ndi Ayuda ndipo, pamene tikukhala mboni za Mulungu mwadzina, kuchita ntchito zamdima.
14, 15. Kodi ndintchito za mdima zotani zimene zinawonekera mumpingo Wachikristu wa m’zaka za zana loyamba, ndipo kodi tikuphunziraponji?
14 Ndithudi, izi zinachitika m’zaka za zana loyamba. Timaŵerenga za mipatuko yowopsa m’Korinto. (1 Akorinto 1:10-17) Mtumwi Yohane anachenjeza Akristu odzozedwa kusadana, ndipo Yakobo anafunikira kupereka uphungu kwa ena kuti asamayanja olemera kuposa osauka. (Yakobo 2:2-4; 1 Yohane 2:9, 10; 3 Yohane 11, 12) Kuwonjezerapo, pamene Yesu anayendera mipingo isanu ndi iŵiri ya ku Asia Minor, monga momwe zasimbidwira m’bukhu la Chibvumbulutso, iye anasimba za kuloŵerera kwa ntchito za mdima, kuphatikizapo mpatuko, kulambira mafano, chisembwere, ndi kukondetsa zinthu zakuthupi. (Chibvumbulutso 2:4, 14, 15, 20-23; 3:1, 15-17) Chotero, m’masiku oyambirira amenewo a mpingo Wachikristu, ambiri analeka kuunika, ena anachotsedwa ndipo ena anangokokedwera ku “mdima wakunja.”—Mateyu 25:30; Afilipi 3:18; Ahebri 2:1; 2 Yohane 8-11.
15 Malipoti onseŵa a m’zaka za zana loyamba amasonyeza njira zosiyana zimene mdima wa dziko la Satana ungaloŵerere m’kuganiza kwa Mkristu aliyense payekha kapena ngakhale mipingo yonse. Tiyenera kuchenjera kuti chinthu choterocho chisatichitikire. Kodi zimenezi tingazichite motani?
Umunthu Watsopano
16. Kodi ndiuphungu wanzeru wotani umene Paulo anawapatsa Aefeso?
16 Paulo anafulumiza Aefeso kusakhalanso ‘odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu.’ Kuti asabwerere mumdima umenewo, anafunikira kukulitsa mkhalidwe wamtima wa kuunika. Paulo anati: “Muyenera kuvula umunthu wakale umene umagwirizana ndi njira yanu yakale ya khalidwe ndi umene uli kumaipitsidwa mogwirizana ndi zikhumbo zake zonyenga; koma . . . muyenera kupangidwa kukhala atsopano mwa mphamvu yosonkhezera maganizo anu, ndipo muyenera kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi kukhulupirika.”—Aefeso 4:18, 22-24, NW.
17. Kodi ndimotani mmene ifeyo lerolino tingapeŵere kubwerera mumdima?
17 Paulo panopo akupereka uphungu, opareshoni yaikulu yowongolera, kunena kwake titero—kuchotsa yomwe kale inali mbali yathu, umunthu wathu wakale, ndikulola kuyambika kwa mzimu watsopano ‘kusonkhezera maganizo athu.’ Ndipo iye sankalankhula ndi okondwerera chatsopano koma Akristu obatizidwa. Kusintha umunthu wathu sikumalekeka pa ubatizo. Iko ndikachitidwe kopitiriza. Titaleka kukulitsa umunthu watsopano, wakalewo ungayambikenso, limodzi ndi kunyada, kudzikuza, ndi dyera lake. (Genesis 8:21; Aroma 7:21-25) Ichi chingatsogolere kubwerera ku ntchito zamdima.
“M’kuunika Kwanu Tidzaona Kuunika”
18, 19. Kodi ndimotani mmene Yesu ndi Paulo anafotokozera njira yozindikirira “ana a kuunika”?
18 Kumbukirani kuti kupeza moyo wamuyaya kumadalira pakulandira kwathu chiweruzo chachiyanjo kuchokera kwa Mulungu, chiweruzo chomwe chiri chozikidwa pa ukulu umene timakondera kuunika. Pambuyo posonya kumbali yomalizirayi, Yesu anati: ‘Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake. Koma wochita chowonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake ziwonekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu.’—Yohane 3:19-21.
19 Paulo anachilikiza lingaliro limeneli pamene analembera Aefeso kuti: ‘Yendani monga ana a kuunika, pakuti chipatso cha kuunika tichipeza m’ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi chowonadi.’ (Aefeso 5:8, 9) Choncho ntchito zathu zimasonyeza kaya ndife ana a kuunika kapena a mdima. Koma ntchito zabwino zingangochokera mumtima wabwino. Ichi ndicho chifukwa chake tiyenera kuyang’anira mtima wathu, kukhala amaso ku kufunika kwakupitiriza kukonzanso umunthu wathu, kukhala osamala ndi mzimu wakusonkhezera maganizo athu.—Miyambo 4:23.
20, 21. (a) Kodi ndichitokoso chapadera chotani chimene ana obadwira m’mabanja Achikristu amayang’anizana nacho? (b) Kodi ndichitokoso chotani chimene ana onse a makolo Achikristu amayang’anizana nacho?
20 M’zochitika zina, izi zatsimikizira kukhala chitokoso chapadera kwa ana obadwa kwa Mboni zodzipatulira za Yehova. Chifukwa ninji? Eya, kumbali ina, ana oterowo amasangalala ndi madalitso abwino koposa. Kudziŵa chowonadi kuchokera ku ubwana kumatanthauza, m’chenicheni, kuti munthuyo safunikira konse kulawa kukhala mumdima wa dziko la Satana. (2 Timoteo 3:14, 15) Kumbali ina, ana ena a m’mkhalidwe woterewu amatenga chowonadi mopepuka ndipo samaphunzira konse kukondadi kuunikako. Uwu ndiwo unali mkhalidwe wa Ayuda ambiri a m’zaka za zana loyamba. Iwo anakulira mu mtundu wodzipatulira kwa Yehova, ndipo anali nacho chidziŵitso cha chowonadi ku mlingo wakutiwakuti. Koma sichinali m’mitima mwawo.—Mateyu 15:8, 9.
21 Makolo Achikristu ali ndi thayo pamaso pa Mulungu lakulera ana awo m’kuunika kumeneku. (Deuteronomo 6:4-9; Aefeso 6:4) Komabe, pomalizira pake, zimatsalira mwanayo kufikira pakukonda kuunika kuposa mdima. Iye afunikira kukupanga kuunika kwa chowonadi kukhala kwakekwake. Pamene akukula, mbali zina za dziko la Satana zingawonekere kukhala zokopa. Njira yamoyo yolekerera kapena yosasamala ya ausinkhu wake ingawonekere kukhala yosangalatsa. Kukaikira zinthu kophunzitsidwa m’sukulu kungakhale konyenga. Koma iye sayenera kuiwala konse kuti kunja kwa kuunika, ‘mdima uphimba dziko lapansi.’ (Yesaya 60:2) M’kupita kwanthaŵi, dziko lamdimali limakhala lopanda chabwino chirichonse chopereka.—1 Yohane 2:15-17.
22. Kodi Yehova amadalitsa motani awo amene amabwera ku kuunika, ndipo kodi ndimotani mmene adzawadalitsira mtsogolo?
22 Mfumu Davide analemba kuti: ‘Pakuti chitsime cha moyo chiri ndi inu [Yehova]: m’kuunika kwanu tidzaona kuunika. Tanimphitsani chifundo chanu pa iwo akudziŵa inu.’ (Salmo 36:9, 10) Awo amene amakonda kuunika amafikira pakudziŵa Yehova, ndipo ichi chingatanthauze moyo kwa iwo. (Yohane 17:3) M’kukoma mtima kwake kwachifundo, Yehova amawachilikiza iwo tsopano, ndipo pamene chisautso chachikulu chidzakantha, iye adzawapulumutsira m’dziko latsopano. Ichi ndicho chimene tingakumane nacho ngati tikana mdima wa dziko la Satana tsopano lino. M’dziko latsopano, anthu adzabwezeretsedwera ku moyo wangwiro m’Paradaiso. (Chibvumbulutso 21:3-5) Awo amene amalandira chiweruzo chachiyanjo panthaŵiyo adzakhala ndi chiyembekezo chakukhala m’kuunika kwa Yehova kwa nthaŵi yonse. Ha, nchiyembekezo chaulemerero chotani nanga! Ndipo nchisonkhezero champhamvu chotani nanga tsopano cha ‘kuvula ntchito za mdima, nkuvala zida za kuunika’!—Aroma 13:12.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji Ayuda ambiri a m’nthaŵi ya Yesu anakana kuunikako?
◻ Kodi kuunikako kwakhala kukuwala ku ukulu wotani m’nthaŵi zamakono?
◻ Kodi ndimachenjezo otani onena za dyera ndi kunyada amene zitsanzo za m’zaka za zana loyamba zikupereka?
◻ Kodi chofunika nchiyani ngati titi tikhalebe m’kuunika?
◻ Kodi ndimadalitso otani omwe akuyembekezera okonda kuunika?
[Chithunzi patsamba 14]
Ayuda ambiri a m’tsiku la Yesu sanavomereze kuunikako
[Zithunzi patsamba 17]
M’zaka makumi ambiri zapitazo njira zosiyanasiyana zagwiritsiridwa ntchito kulola kuunika kuwala m’kupanga ophunzira
[Chithunzi patsamba 18]
‘Muvule umunthu wakale . . . nimuvale umunthu watsopano’