Yendani Monga Anthu Anzeru
1 Yesu atapempha asodzi anayi kuti akhale otsatira ake, iwo sanazengereze koma ‘nthawi yomweyo anamutsatira.’ (Mat. 4:18-22) Saulo wa ku Tariso atatembenukira ku Chikhristu n’kuyambanso kupenya, iyenso sanachedwe koma “nthawi yomweyo anayamba kulalikira za Yesu m’masunagoge.” (Mac. 9:20) Nthawi sibwerera m’mbuyo, imati ikadutsa yadutsa. N’chifukwa chake n’kofunika kuti ‘tiziyenda monga anthu anzeru’ pankhani yogwiritsa ntchito nthawi yathu.—Aef. 5:15, 16.
2 Zongotigwera: Mwayi wotumikira Yehova womwe tili nawo lero mwina mawa sitingakhale nawo. (Yak. 4:14) Aliyense zinazake zikhoza ‘kum’gwera’ mwadzidzidzi. (Mlal. 9:11) Komanso, aliyense akunka nakalamba, ndipo m’dongosolo lino la zinthu, sitingapewe “masiku oipa” amene amadza ndi ukalamba ndiponso amene amatilepheretsa kuchita zambiri muutumiki wa Yehova. (Mlal. 12:1) Choncho, ndi nzeru kudzipereka kwa Mulungu mwamsanga m’malo mozengereza. Ndiponso si chinthu chanzeru kuganiza kuti tidzawonjezera utumiki zinthu zonse zikadzakhala bwino. (Luka 9:59-62) Abulahamu anapeza mtendere m’zaka za ukalamba wake, ndipo anafa ‘m’ukalamba wabwino’ chifukwa choti moyo wake anaugwiritsa ntchito mwanzeru mwakudzipereka ndi mtima wonse kwa Yehova.—Gen. 25:8.
3 Nthawi Yafupika: Timafunikanso kugwiritsa ntchito nthawi yathu mwanzeru chifukwa “nthawi yotsalayi yafupika.” (1 Akor. 7:29-31) Posachedwapa dongosolo la zinthu lilipoli litha. Nawonso mwayi wosonkhanitsa nawo anthu onga nkhosa m’nthawi ‘yokolola za dziko lapansi’ utha. (Chiv. 14:15) Motero, tiyenera kusamala kuti nkhawa za moyo ndiponso zinthu zina zotanganitsa zisatitayitse nthawi imene tikanathera mu utumiki. (Luka 21:34, 35) Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri kuganizira kuti tinagwira nawo mokwanira ntchito yokolola imeneyi.
4 Tiyenera kukhala tcheru nthawi zonse kuti tisaphonye mwayi wabwino wa utumiki umene tingaupeze. Tiyeni tikhale otsimikiza kuchita zonse zomwe tingathe kuti titumikire Yehova ‘nthawi iliyonse imene tikuti “Lero.”’ (Aheb. 3:13) Tikatero, tidzasonyeza kuti ndifedi anzeru, chifukwa “wochita chifuniro cha Mulungu akhalabe kosatha.”—1 Yoh. 2:17.