Kuleka Mawu Opweteka ndi Kunena Mawu Olamitsa
“Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo.”—MIYAMBO 18:21.
KUNYOZA—mchitidwe wadala wa kugwiritsira ntchito mawu otukwana, amwano—nkotsutsidwa momveka m’Baibulo. M’Chilamulo cha Mose, munthu amene ananyoza makolo ake anayenerera chilango cha imfa. (Eksodo 21:17) Motero, Yehova Mulungu samaona nkhaniyi mopepuka. Mawu ake, Baibulo, samachirikiza lingaliro lakuti chilichonse chimene chimachitika ‘mseri’ sichili ndi kanthu kwenikweni malinga ngati munthu amanena kuti amatumikira Mulungu. Baibulo limanena kuti: “Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.” (Yakobo 1:26; Salmo 15:1, 3) Chotero ngati mwamuna achitira mkazi wake nkhanza ya mawu, ntchito zake zina zonse zachikristu zingakhale zachabe pamaso pa Mulungu.a—1 Akorinto 13:1-3.
Ndiponso, Mkristu amene ali wolalata angathamangitsidwe mumpingo. Iye angadzitayitsedi madalitso a Ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 5:11; 6:9, 10) Mwachionekere, munthu amene amavulaza ndi mawu ake afunikira kupanga masinthidwe aakulu. Koma kodi zimenezi zingachitidwe motani?
Kusonyeza Vutolo
Mwachionekere, wolakwayo sadzasintha pokhapokhapo atazindikira bwino kuti ali ndi vuto lalikulu. Mwachisoni, monga momwe phungu wina ananenera, amuna ambiri amene amagwiritsira ntchito mawu amwano “samaona nkomwe khalidwe lawo monga nkhanza. Kwa amuna ameneŵa, machitidwe otero saali achilendo konse ndipo ali njira ‘yachibadwa’ imene amuna ndi akazi amachitiramo zinthu.” Chotero, ambiri samaona kufunika kwa kusintha kufikira atasonyezedwa mwachindunji mkhalidwewo.
Kaŵirikaŵiri, mkazi amakhala wosonkhezereka kulankhula atapenda mwapemphero za mkhalidwe wake—kaamba ka ubwino wake ndi wa ana ake ndiponso chifukwa chodera nkhaŵa kaimidwe ka mwamuna wake ndi Mulungu. Zoonadi, nthaŵi zonse pamakhala kuthekera kwakuti kutchula za nkhaniyo kungapangitse zinthu kukhala zoipa kwambiri ndi kuti mawu ake angatsutsidwe kwambiri. Mwina mkazi angaletse zimenezi kuchitika mwa kusinkhasinkha pasadakhale mmene adzayambira nkhaniyo. “Mawu oyenera a pa nthaŵi yake akunga zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva,” Baibulo limatero. (Miyambo 25:11) Kafikidwe kofatsa komabe kosabisa mawu pa nkhaniyo panthaŵi yabata kangafike mtima wake.—Miyambo 15:1.
M’malo moimba mlandu, mkazi ayenera kufotokoza zakukhosi kwake malinga ndi mmene mawu opwetekawo akumuyambukirira. Kaŵirikaŵiri kutchula kuti “Ine” kumakhala bwino koposa. Mwachitsanzo, kunena kuti ‘Ine ndimakhumudwa chifukwa . . . ’ kapena ‘Ine ndimathedwa mphamvu pamene mumati kwa ine . . . ’ Mawu ameneŵa angafikedi mtima, pakuti amalimbana ndi vuto m’malo mwa kulimbana ndi munthu.—Yerekezerani ndi Genesis 27:46–28:1.
Kuchitapo kanthu kwa mkazi kolimba komanso kwaluso kungakhale ndi zotulukapo zabwino. (Yerekezerani ndi Salmo 141:5.) Mwamuna wina amene tidzamutcha kuti Steven anapeza zimenezi kukhaladi choncho. “Mkazi wanga anazindikira mkhalidwe wa nkhanza mwa ine umene sindinkauona, ndipo analimbika mtima kundisonyeza,” iye akutero.
Kupeza Thandizo
Koma kodi mkazi angachitenji ngati mwamuna wake akukana kuvomereza vutolo? Zitatere akazi ena amakafunafuna thandizo kunja. M’nthaŵi zosautsa zimenezi, Mboni za Yehova zingafikire akulu a mpingo wawo. Baibulo limalimbikitsa amuna ameneŵa kukhala achikondi ndi okoma mtima poŵeta gulu la nkhosa la Mulungu ndipo, panthaŵi imodzimodziyo, “kutsutsa otsutsana” ndi chiphunzitso cholamitsa cha Mawu a Mulungu. (Tito 1:9; 1 Petro 5:1-3) Pamene kuli kwakuti sayenera kududukira m’nkhani zaumwini za anthu okwatirana, akulu amada nkhaŵa moyenera pamene wa muukwati wina avutika ndi mawu aukali a mnzake. (Miyambo 21:13) Pomamatira miyezo ya Baibulo, amuna ameneŵa samakankhira pambali kapena kuchepetsa mawu amwano.b
Akulu angatheketse kulankhulana pakati pa mwamuna ndi mkazi. Mwachitsanzo, mkulu wina anafikiridwa ndi mkazi amene anamsimbira za kuukiridwa ndi mawu kumene mwamuna wake, wolambira mnzake anamchitira kwa zaka zambiri. Mkuluyo analinganiza zokumana ndi anthu aŵiriwo. Iye anapempha kuti winayo azimvetsera popanda kudula mawu, pamene mnzake anali kulankhula. Pamene nthaŵi yakuti mkaziyo alankhule inafika, iyeyo anati sakanathanso kulekerera ukali waukulu wa mwamuna wake. Iye anafotokoza kuti kwa zaka zambiri, anali womangika thupi kwambiri pamapeto a tsiku lililonse, posadziŵa kaya ngati mwamunayo adzakhala mu mkhalidwe wamkwiyo pamene anali kuloŵa pakhomo. Pamene anayamba kukalipa, anali kunena zinthu zonyoza banja la mkaziyo, mabwenzi ake, ndiponso mkaziyo.
Mkuluyo anapempha mkaziyo kufotokoza mmene anamvera ndi mawu a mwamuna wakeyo. “Ndinamva ngati kuti munthu woipa amene sakanakondedwa ndi wina aliyense anali ineyo,” iyeyo anayankha motero. “Nthaŵi zina ndinkafunsa mayi wanga kuti, ‘Amayi, kodi ndine munthu wovuta kukhala naye? Kodi munthu sangandikonde?’” Pamene mkaziyo anali kulongosola malingaliro amene mawu a mwamunayo anampatsa, mwamuna wakeyo anayamba kulira. Kwa nthaŵi yoyamba, iyeyo anaona mmene anali kuvulazira kwambiri mkazi wake ndi mawu ake.
Mungasinthe
Akristu ena m’zaka za zana loyamba anali ndi vuto la kulankhula mawu amwano. Mtumwi wachikristu Paulo anawalangiza kutaya “mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa.” (Akolose 3:8) Komabe, kulankhula mwaukali kuli vuto lochokera mumtima osati kwenikweni la lilime. (Luka 6:45) Nchifukwa chake Paulo anawonjezera kuti: “Vulani umunthu wakale ndi ntchito zake, ndi kudziveka umunthu watsopano.” (Akolose 3:9, 10, NW) Chotero kusintha kumaloŵetsamo osati chabe kulankhula kosiyana ndi kwakale komanso kulingalira kosiyana ndi kwakale.
Mwamuna amene amagwiritsira ntchito mawu ovulaza angafunikire thandizo lakuti adziŵe chinthu chenicheni chimene chimasonkhezera khalidwe lake.c Iye angafunikire kukhala ndi maganizo onga a wamasalmo akuti: “Mundisanthule, Mulungu, nimudziŵe mtima wanga; mundiyese nimudziŵe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nawo mayendedwe oipa.” (Salmo 139:23, 24) Mwachitsanzo: Kodi nchifukwa ninji amalingalira kuti afunikira kulamulira mnzakeyo? Kodi nchiyani chimene chimayambitsa nkhondo ya mawuyo? Kodi kuukira kwakeko kuli zizindikiro za kukhumudwa kwakukulu? (Miyambo 15:18) Kodi amavutika ndi malingaliro akusadziŵerengera, mwinamwake okhalapo chifukwa cha kusulizidwa pa kukula kwake? Mafunso otero angathandize mwamuna kupeza mizu ya khalidwe lake.
Komabe kalankhulidwe kamwano nkovuta kukathetsa makamaka ngati kanaphunziridwa kwa makolo amene anali ndi kalankhulidwe kopweteka kapena amene amachirikiza mwambo wa kulamulira ena. Komatu zonse zimene timaphunzira zingathe—limodzi ndi nthaŵi ndi kuyesayesa—kuthetsedwa. Baibulo ndilo thandizo lalikulu koposa pa nkhaniyi. Lingathandize munthu kusintha ngakhale khalidwe lokhomerezeka kwambiri. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 10:4, 5.) Motani?
Lingaliro Loyenera la Mbali Zoperekedwa ndi Mulungu
Kaŵirikaŵiri, amuna amene amavulaza mwamawu ali ndi lingaliro lopotoka la mbali zoperekedwa ndi Mulungu kwa mwamuna ndi mkazi. Mwachitsanzo, wolemba Baibulo Paulo akunena kuti akazi ayenera ‘kumvera amuna awo a iwo eni’ ndi kuti “mwamuna ndiye mutu wa mkazi.” (Aefeso 5:22, 23) Mwamuna angalingalire kuti umutuwo umampatsa ulamuliro wonse. Komatu zimenezi sizili choncho. Ngakhale kuti mkazi wake ayenera kumumvera, iye saali kapolo wake. Iye ndiye “womthandiza” ndi “womkwaniritsa.” (Genesis 2:18, NW) Chotero, Paulo akuwonjezera kuti: “Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha; pakuti munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Kristu Eklesia.”—Aefeso 5:28, 29.
Monga mutu wa mpingo wachikristu, Yesu sananyoze ophunzira ake, akumawachititsa kuvutika mtima chifukwa chosadziŵa nthaŵi yotsatira imene adzawasuliza. M’malo mwake, iye anali wachikondi, motero akumasungitsa ulemu wawo. “Ine ndidzakupumulitsani inu,” iye anawalonjeza motero. “Ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.” (Mateyu 11:28, 29) Kusinkhasinkha mwapemphero ponena za mmene Yesu anachitira umutu wake kungathandize mwamuna kuona umutu wake mwanzeru kwambiri.
Pamene Mavuto Abuka
Kudziŵa mapulinsipulo a Baibulo ndi nkhani ina; kuwagwiritsira ntchito pamene muli pamavuto ndi kwinanso. Pamene mavuto abuka, kodi mwamuna angapeŵe motani kubwereranso kumkhalidwe wa kalankhulidwe kaukali?
Kulankhula mwaukali pamene mwamuna wakwiya sindiko umuna. Baibulo limanena kuti: “Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mudzi.” (Miyambo 16:32) Mwamuna weniweni amalamulira mzimu wake. Amasonyeza chifundo mwa kulingalira kuti: ‘Kodi mawu anga amayambukira motani mkazi wanga? Kodi ndikanamva bwanji ngati ndikanakhala m’malo mwake?’—Yerekezerani ndi Mateyu 7:12.
Komabe, Baibulo limavomereza kuti mikhalidwe ina ingayambitse mkwiyo. Ponena za mikhalidwe imeneyo wamasalmo analemba kuti: “Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe: nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.” (Salmo 4:4) Kwanenedwanso motere: “Kupsa mtima sikolakwa, koma kuukira munthu ndi mawu mwa kukhala wachipongwe, wonyazitsa, kapena wonyoza.”
Ngati mwamuna alingalira kuti sakutha kulankhula bwino, ayenera kuphunzira kutonthola. Mwina kungakhale kwanzeru kuchoka m’chipinda, kumka kukayenda, kapena kupeza malo ayekha okatsitsirako mtima. Miyambo 17:14 imati: “Kupikisana kusanayambe tasiya makani.” Pitirizani kukambitsirana pamene mitima yatsika.
Zoonadi, palibe munthu amene ali wangwiro. Mwamuna amene wakhala ali ndi vuto la kulankhula mwaukali angabwererenso mumkhalidwewo. Pamene zimenezi zichitika, iye ayenera kupepesa. Kuvala “umunthu watsopano” kuli mchitidwe wopitiriza, komano umene umapezetsa mfupo zazikulu.—Akolose 3:10, NW.
Mawu Olamitsa
Inde, “lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo.” (Miyambo 18:21) Kalankhulidwe kovulaza kayenera kuloŵedwa m’malo ndi mawu amene ali omangirira ndi olimbitsa ukwati. Mwambi wa Baibulo umati: “Mawu okoma ndiwo chisa cha uchi, otsekemera m’moyo ndi olamitsa mafupa.”—Miyambo 16:24.
Zaka zingapo zapitazo, kufufuza kunachitidwa kofuna kudziŵa zimene zinachititsa mabanja olimba kuyenda bwino. “Kufufuzako kunapeza kuti anthu a m’mabanja ameneŵa anali kukondana, ndipo anapitiriza kuuzana kuti anali kukondana,” akusimba motero katswiri wazaukwati David R. Mace. “Anatsimikizirana, kupatsana ulemu, ndi kugwiritsira ntchito mwaŵi uliwonse woyenera wa kulankhula ndi kuchita mwachikondi. Mwachibadwa, chotulukapo chake chinali chakuti anakondwera kukhalira pamodzi ndi kulimbitsana m’njira zimene zinapangitsa maunansi awo kukhala okhutiritsa kwambiri.”
Palibe mwamuna wowopa Mulungu amene moonadi anganene kuti amakonda mkazi wake ngati amamvulaza dala ndi mawu ake. (Akolose 3:19) Zoonadi, zili chimodzimodzinso kwa mkazi amene amamenya mwamuna wake ndi mawu. Ndithudi, ndi thayo la a muukwati aŵiri onse kutsatira chilangizo cha Paulo kwa Aefeso chakuti: “Nkhani yonse yovunda isatuluke m’kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.”—Aefeso 4:29.
[Mawu a M’munsi]
a Ngakhale kuti tikutchula wolakwayo kukhala mwamuna, mapulinsipulo amene ali mu nkhaniyi akukhudzanso akazi.
b Kuti mwamuna ayenerere kutumikira kapena kupitiriza kukhala mkulu, sayenera kukhala wandewu. Sayenera kukhala womenyana ndi anthu mwakuthupi kapena wowakadzulira mawu opweteka. Akulu ndi atumiki otumikira ayenera kuyang’anira bwino nyumba zawo. Mosasamala kanthu kuti amachita mokoma mtima kwambiri kwina, mwamuna sangayenerere ngati ali wotsendereza panyumba.—1 Timoteo 3:2-4, 12.
c Ndi chosankha cha munthu mwini ngati Mkristu akufunafuna kukalandira thandizo. Komabe, ayenera kutsimikizira kuti thandizo lililonse limene adzapatsidwa silidzawombana ndi mapulinsipulo a Baibulo.
[Chithunzi patsamba 25]
Mkulu wachikristu angakhoze kuthandiza anthu aŵiri okwatirana kulankhulana
[Chithunzi patsamba 26]
Amuna ndi akazi ayenera kuyesayesa mwamphamvu kumvetsetsana wina ndi mnzake