Kwa Aefeso
5 Choncho muzitsanzira Mulungu,+ monga ana ake okondedwa, 2 ndipo pitirizani kusonyeza chikondi+ ngati mmene Khristu anatikondera*+ nʼkudzipereka yekha chifukwa cha ife* ngati chopereka ndiponso ngati nsembe yafungo lokoma kwa Mulungu.+
3 Nkhani zachiwerewere* komanso chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe nʼkomwe pakati panu,+ chifukwa anthu oyera sayenera kuchita zimenezi.+ 4 Musatchule ngakhale nkhani zokhudza khalidwe lochititsa manyazi, nkhani zopusa kapena nthabwala zotukwana+ chifukwa ndi zinthu zosayenera. Mʼmalomwake muziyamika Mulungu.+ 5 Chifukwa mfundo iyi mukuidziwa ndipo mukuimvetsa bwino, kuti munthu wachiwerewere*+ kapena wodetsedwa kapena waumbombo,+ umene ndi kulambira mafano, sadzalowa mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.+
6 Munthu asakupusitseni ndi mawu opanda pake, chifukwa mkwiyo wa Mulungu udzafika pa ana a osamvera, amene akuchita zinthu zimene ndatchulazi. 7 Choncho musamachite zimene iwo amachita.* 8 Chifukwa poyamba munali ngati mdima, koma pano muli ngati kuwala+ popeza ndinu ogwirizana ndi Ambuye.+ Pitirizani kuyenda ngati ana a kuwala. 9 Chifukwa zipatso za kuwala ndi chilichonse chabwino, chilichonse cholungama ndi choona.+ 10 Nthawi zonse muzitsimikizira kuti chovomerezeka+ kwa Ambuye nʼchiti. 11 Ndipo musiye kuchita nawo ntchito zosapindulitsa zamumdima.+ Mʼmalomwake, muzisonyeza poyera kuti ndi zinthu zoipa. 12 Chifukwa zinthu zimene iwo amachita mwachinsinsi ndi zochititsa manyazi ngakhale kuzitchula. 13 Tsopano zinthu zimene zikuululidwa* zimaonekera poyera chifukwa cha kuwala, popeza chilichonse chimene chaonekera chimakhala kuwala. 14 Nʼchifukwa chake pali mawu akuti: “Dzuka, wogona iwe! Uka kwa akufa+ ndipo Khristu adzawala pa iwe.”+
15 Choncho samalani kwambiri kuti mukamayenda, musamayende ngati anthu opanda nzeru koma ngati anthu anzeru. 16 Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu*+ chifukwa masikuwa ndi oipa. 17 Pa chifukwa chimenechi, siyani kuchita zinthu ngati anthu opanda nzeru, koma pitirizani kuzindikira chifuniro cha Yehova.*+ 18 Ndiponso musamaledzere ndi vinyo+ chifukwa kuledzera kungachititse kuti muchite zinthu zoipa kwambiri, koma pitirizani kudzazidwa ndi mzimu. 19 Muziimbira limodzi masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndiponso nyimbo zauzimu.+ Muziimba nyimbo+ zotamanda Yehova* mʼmitima yanu.+ 20 Nthawi zonse muziyamika+ Mulungu, Atate wathu, pa zinthu zonse mʼdzina la Ambuye wathu Yesu Khristu.+
21 Muzigonjerana+ poopa Khristu. 22 Akazi azigonjera amuna awo+ ngati mmene amagonjerera Ambuye, 23 chifukwa mwamuna ndi mutu wa mkazi wake+ mofanana ndi Khristu amene ndi mutu wa mpingo,+ popeza iye ndi mpulumutsi wa thupi* limeneli. 24 Ndipotu, mofanana ndi mmene mpingo umagonjerera Khristu, akazinso azigonjera amuna awo pa chilichonse. 25 Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu+ ngati mmenenso Khristu anakondera mpingo nʼkudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo,+ 26 nʼcholinga choti auyeretse pousambitsa mʼmadzi a mawu a Mulungu.+ 27 Anachita zimenezi kuti iyeyo alandire mpingowo uli wokongola ndiponso waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapenanso chilichonse cha zinthu zoterezi,+ koma kuti ukhale woyera ndi wopanda chilema.+
28 Mofanana ndi zimenezi, amuna azikonda akazi awo ngati mmene amakondera matupi awo. Mwamuna amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, 29 chifukwa palibe munthu amene anadanapo ndi thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda, ngati mmene Khristu amachitira ndi mpingo 30 chifukwa ndife ziwalo za thupi lake.+ 31 “Chifukwa cha zimenezi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake nʼkudziphatika kwa* mkazi wake ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.”+ 32 Chinsinsi chopatulika+ chimenechi nʼchachikulu. Tsopano ndikulankhula za Khristu ndi mpingo.+ 33 Komabe, aliyense wa inu azikonda mkazi wake+ ngati mmene amadzikondera yekha komanso mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.+