Chitirani Ulemu Anthu Onse
‘Chitirani ulemu anthu onse. . . . Opani Mulungu, chitirani mfumu ulemu.’—1 PETRO 2:17.
1. (a) Kodi ndani ena pambali pa Mulungu ndi Kristu amachitiridwa ulemu moyenerera? (b) Kodi ndi m’mbali ziti mmene anthu ayenera kuchitiridwa ulemu mogwirizana ndi 1 Petro 2:17?
TAWONA kuti tikulamulidwa kuchitira ulemu Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Ichi nchinthu chabwino, chanzeru, ndi chokondeka kuchichita. Komabe Mawu a Mulungu amasonyezanso kuti tifunikiranso kulemekeza anthu anzathu. Tikuwuzidwa kuti: ‘Chitirani ulemu anthu onse.’ (1 Petro 2:17) Popeza kuti vesili likutsiriza ndi lamulo lakuti, ‘chitirani mfumu ulemu,’ tanthauzo nlakuti ulemu uyenera kusonyezedwa kwa anthu ofunikira kuwulandira chifukwa chaudindo wawo. Pamenepa, kodi ndani omwe ayenera kulemekezedwa molondola? Chiŵerengero cha anthu oyenerera kulemekezedwa chingaphatikizepo ambiri omwe ena sangawalingalire. Tinganene kuti pali mbali zinayi zomwe tiyenera kusonyezera ulemu anthu ena.
Chitirani Ulemu Olamulira Andale Zadziko
2. Kodi tikudziŵa bwanji kuti “mfumu” yotchulidwa pa 1 Petro 2:17 ikusonya kwa mfumu kapena wolamulira wandale zadziko aliyense?
2 Mbali yoyamba ya izi njogwirizana ndi maboma akudziko. Tiyenera kuchitira ulemu olamulira andale zadziko. Pamene Petro analangiza kuti: ‘Chitirani mfumu ulemu,’ kodi nchifukwa ninji tikunena kuti Petro ankasonya olamulira andale zadziko? Chifukwa chakuti akulankhula za mkhalidwe wokhala kunja kwa mpingo Wachikristu. Iye anali atangomaliza kumene kunena kuti: ‘Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse; kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye.’ Onaninso kuti Petro, anasiyanitsa Mulungu ndi “mfumu,” nati: ‘Opani Mulungu, chitirani mfumu ulemu.’ (1 Petro 2:13, 14) Chotero “mfumu” imene Petro akutichonderera kuichitira ulemu imatanthauza mafumu aumunthu kapena olamulira andale zadziko.
3. Kodi ndani omwe ali ‘maulamuliro aakulu,’ ndipo kodi iwo amafunikira chiyani?
3 Mofananamo mtumwi Paulo akulamulira kuti: ‘Mverani maulamuliro aakulu.’ ‘Maulamuliro aakulu’ ameneŵa sindiwo Yehova Mulungu kapena Yesu Kristu, koma ndi olamulira andale zadziko, akuluakulu aboma. Pokhala ndi aŵa m’malingaliro, Paulo akupitirizabe nati: ‘Perekani kwa anthu onse mangawa awo; . . . ulemu kwa eni ake a ulemu.’ Inde, anthu oterewo omwe aloledwa ndi Mulungu kulamulira mwandale zadziko afunikira kuchitiridwa ulemu.—Aroma 13:1, 7.
4. (a) Kodi ulemu ungasonyezedwe motani kwa olamulira andale zadziko? (b) Kodi nchitsanzo chiti chimene mtumwi Paulo anakhazikitsa cha kuchitira ulemu olamulira?
4 Kodi timaŵachitira ulemu motani olamulira andale zadziko? Njira imodzi njakuŵasonyeza ulemu wakuya. (Yerekezerani ndi 1 Petro 3:15.) Ndipo chifukwa chaudindo wawo, ulemu woterowo umawayenerera ngakhale atakhala anthu oipa. Tacitus katswiri wa mbiri yakale Wachiroma anamfotokoza Bwanamkubwa Felike kukhala mwamuna amene “analingalira kuti akachita choipa chirichonse mwaufulu.” Komabe Paulo anakapanga chodzikanira pamaso pa Felike mwaulemu. Mofananamo, Paulo mwaulemu anauza Mfumu Herode Agripa II kuti, ‘ndidziyesa wamwaŵi popeza nditi ndidzikanire lerolino pamaso panu,’ chinkana kuti Paulo anadziŵa kuti Agripa ankachita chigololo chapachibale. Mofananamo, Paulo anachitira ulemu Bwanamkubwa Festo, namutcha iye ‘Womvekatu,’ chinkana kuti Festo anali wolambira mafano.—Machitidwe 24:10; 26:2, 3, 24, 25.
5. Kodi ndinjira ina iti imene ulemu ungasonyezedwe kwa akuluakulu aboma, ndipo kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zingakhazikitsire chitsanzo chabwino cha kuchitira tero?
5 Njira ina imene timachitira ulemu akuluakulu aboma yasonyezedwa ndi mtumwi Paulo pamene analemba ponena za kupereka mangawa kwa akuluakulu aboma. Iye anati tipereke ‘msonkho kwa eni ake msonkho; kulipira kwa eni ake kulipira.’ (Aroma 13:7) Mboni za Yehova zimapereka mangawa oterowo mosasamala kanthu za dziko limene izo zikukhalamo padziko. Mu Italy nyuzipepala yotchedwa La Stampa inati: “Iwo ndiwo nzika zokhulupirika kwabasi omwe aliyense angaŵafune: iwo samazemba misonkho kapena kufuna kuphwanya malamulo oletsa kuti adzipindulitse.” Ndipo The Post ya ku Palm Beach, Florida, U.S.A., inanena motere ponena za Mboni za Yehova: “Iwo amakhoma misonkho yawo. Iwo ndiwo nzika zina zowona mtima kwambiri mu Lipabuliki.”
Chitirani Ulemu Okulembani Ntchito
6. Kodi mtumwi Paulo ndi Petro anati ulemu uyenera kusonyezedwanso kwayani?
6 Mbali yachiŵiri imene ulemu uyenera kusonyezedwa ndiyo pamalo athu antchito. Atumwi onse aŵiriwo Paulo ndi Petro akugogomezera kufunika kwa Akristu kulemekeza oŵayang’anira pantchito. Paulo analemba kuti: ‘Onse amene ali akapolo a m’goli, ayesere ambuye a iwo okha oyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi chiphunzitso zisachitidwe mwano. Ndipo iwo akukhala nawo ambuye okhulupirira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire.’ Ndipo Petro anati: “Anyamata inu, gonjerani ambuye anu ndi kuopa konse, osati abwino ndi aulere okha, komanso aukali.”—1 Timoteo 6:1, 2; 1 Petro 2:18; Aefeso 6:5; Akolose 3:22, 23.
7. (a) Kodi ndimotani mmene uphungu wa Baibulo kaamba ka “akapolo” kuchitira ulemu “ambuye” awo umagwirira ntchito bwino lerolino? (b) Kodi nchiyani chimene antchito Achikristu amene ali ndi oŵalemba ntchito Achikristu ayenera kusamala kutsatira?
7 Ndithudi, ukapolo siwosafala lerolino. Koma malamulo amakhalidwe abwino amene analamulira Akristu muunansi wa bwana ndi kapolo wake amagwira ntchito muunansi wa wantchito ndi womulemba ntchito. Chotero, olembedwa ntchito Achikristu ali ndi thayo la kuchitira ulemu ngakhale oŵalemba ntchito ovuta kukondweretsa. Ndipo bwanji ngati wolemba ntchitoyo ndi wokhulupirira mnzathu? Mmalo mwakuyembekezera kulingaliridwa mwapadera kapena kusamaliridwa choyamba chifukwa chaunansiwo, wantchitoyo ayenera kutumikira womlemba ntchito wake Wachikristuyo momvera kwenikweni, osamudyerera m’njira iriyonse.
Kuchitira Ulemu m’Banja
8, 9. (a) Kodi ana akulangizidwa kuchitira ulemu ndani? (b) Kodi nchifukwa ninji ana ayenera kusonyeza ulemuwu, ndipo ndimotani mmene angausonyezere?
8 Mbali yachitatu imene ulemu uyenera kusonyezedwa ndiyo m’banja. Mwachitsanzo, ana ali pansi pa thayo la kuchitira ulemu makolo awo. Ichi sichinali chofunika m’Chilamulo choperekedwa kwa Mose chokha komanso ndithayo la Akristu. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Lemekeza atate wako ndi amako.’—Aefeso 6:1, 2; Eksodo 20:12.
9 Kodi nchifukwa ninji ana ayenera kuchitira ulemu makolo awo? Iwo afunikira kuŵachitira ulemu chifukwa cha ulamuliro wa makolo awo wopatsidwa ndi Mulungu ndiponso chifukwa cha zimene makolo awo aŵachitira, kuŵabala ndikuŵalera kuchokera kuubwana mpaka atakula. Kodi ana ayenera kuŵachitira ulemu motani makolo awo? Iwo ayenera kuchita tero makamaka mwa kukhala omvera ndi kuŵagonjera. (Miyambo 23:22, 25, 26; Akolose 3:20) Kusonyeza ulemu woterowo kungafunikire kuti ana achikulire apereke chilikizo lowonjezereka kwa makolo awo okalamba lazinthu zakuthupi, limodzinso ndi zauzimu. Ichi chimafunikira kukhala wolinganizika mwanzeru ndi mathayo ena, monga ngati kusamalira ana anu ndikukhala ndi phande lokwanira m’kuyanjana Kwachikristu ndi uminisitala wakumunda.—Aefeso 5:15-17; 1 Timoteo 5:8; 1 Yohane 3:17.
10. Kodi nkwandani kumene akazi ali ndi thayo la kuchitira ulemu, ndipo kodi angachite tero m’njira zotani?
10 Koma ana sianthu okhawo m’banja amene akulamulidwa kuchitira ulemu ena. Akazi afunikira kuchitira ulemu amuna awo. Mtumwi Paulo ananenanso kuti “mkaziyo ayenera kukhala ndi ulemu waukulu kwa mwamuna wake.” (Aefeso 5:33, NW; 1 Petro 3:1, 2) Kuchitira amuna “ulemu waukulu” motsimikizirika kumatanthauza kuŵalemekeza. Sara anachitira ulemu mwamuna wake, Abrahamu, pamene anamutcha “mbuye.” (1 Petro 3:6) Chotero akazinu, tsanzirani Sara. Chitirani amuna anu ulemu mwakuvomereza zosankha zawo ndikuzichititsa kugwira ntchito. Mwakuchita zomwe mungathe kuthandiza amuna anu kupeputsidwa ndi katundu wawo, mmalo mwa kuwonjezerapo, inu mukuwachitira ulemu.
11. Ponena za kuchitira ulemu, kodi amuna ali ndi thayo lotani, ndipo nchifukwa ninji?
11 Nanga bwanji kwa amuna? Iwo akulangizidwa m’Mawu a Mulungu kuti: ‘Momwemonso amuna inu, khalani nawo [akazi anu] monga mwa chidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.’ (1 Petro 3:7) Motsimikizirika ichi chiyenera kuchititsa mwamuna aliyense kulingalira. Kuli ngati kuti mkazi adali ndi chikwangwani cholembedwapo mawu akuti “Chamtengo. Chosalimba. Chigwireni mosamala! Chichitireni ulemu!” Chotero amuna akumbukire kuti ayenera kuchitira akazi awo ulemu mwakuŵalingalira kwambiri, apo phuluzi iwo adzadodometsa unansi wawo ndi Yehova Mulungu, pakuti mapemphero awo adzaletsedwa. Zowonadi, nkopindulitsa zedi kwa ziŵalo zabanja kuchitirana ulemu.
Mumpingo
12. (a) Kodi ndani omwe ali ndi thayo la kuchitira ulemu mumpingo? (b) Kodi Yesu anasonyeza motani kuti kuli kolondola kulandira ulemu?
12 Palinso thayo limene aliyense ali nalo lakuchitirana ulemu mumpingo Wachikristu. Tikulangizidwa kuti: ‘Mutsogolerane ndi kuchitirana wina mnzake ulemu.’ (Aroma 12:10) Yesu anasonyeza m’limodzi la mafanizo ake kuti nkolondola kulandira ulemu. Iye anati titaitanidwa kuphwando, tiyenera kukhala pamalo akuthungo, pakuti titatero mpomwe mwiniwakeyo adzatipempha kukhala pamalo apamwamba, ndipo tidzakhala nawo ulemu pamaso pa oitanidwa anzathu onsewo. (Luka 14:10) Chotero, popeza kuti tonsefe timayamikira kuchitiridwa ulemu, kodi sitiyenera kukhala nacho chifundo ndikuchitirana ulemu? Kodi ichi tingachichite bwanji?
13. Kodi ndinjira zina ziti zomwe tingasonyezeremo ulemu mumpingo?
13 Mawu oyamikira ntchito yochitidwa bwino amafanana ndi kuchitira ulemu. Chotero tingachitirane ulemu mwa kupereka chiyamikiro, mwinamwake kaamba ka nkhani kapena ndemanga imene winawake angaipereke mumpingo. Kuwonjezera apa, tingachitirane ulemu mwa kuvala kudzichepetsa kulinga kwa abale ndi alongo athu Achikristu, mwa kuŵasonyeza ulemu waukulu. (1 Petro 5:5) Mwakutero timasonyeza kuti timaŵalingalira kukhala atumiki anzathu olemekezeka a Yehova Mulungu.
14. (a) Kodi ndimotani mmene abale mumpingo angachitire alongo ulemu woyenerera? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti kupereka mphatso ndiko njira ina yochitira ulemu?
14 Mtumwi Paulo analangiza Timoteo wachichepere kuchitira alongo Achikristu achikulire monga amayi ndi achichepere monga alongo akuthupi, “m’kuyera mtima konse.” Inde, pamene abale akhala osamala kusapambanitsa ndi alongo awo Achikristu, monga ngati kuzoloŵerana kopambanitsa, iwo amaŵachitira ulemu. Paulo anapitiriza kulemba kuti: ‘Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu.’ Njira imodzi imene wamasiye wosoŵa angachitiridwe ulemu ndiyo mwachirikizo la zinthu zakuthupi. Koma kuti aziyenerere izi, iye ayenera kukhala ‘wa mbiri ya ntchito zabwino.’ (1 Timoteo 5:2-10) Ponena za mphatso zakuthupi, Luka analemba ponena za anthu okhala pachisumbu cha Melita kuti: “Iwo anatichitiranso ulemu ndi mphatso zambiri ndipo, pochoka ife, anatiikira zotisowa.” (Machitidwe 28:10, NW) Chotero ulemu ungasonyezedwe kwa wina mwakumpatsa mphatso zakuthupi.
15. (a) Kodi ndikwandani komwe tiri ndi thayo lapadera la kuchitira ulemu? (b) Kodi ndinjira imodzi iti yomwe tingachitire ulemu otsogolera?
15 Popitiriza ndi kalata yake kwa Timoteo, Paulo analemba kuti: ‘Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa m’mawu ndi m’chiphunzitso.’ (1 Timoteo 5:17) Kodi akulu, kapena oyang’anira tingaŵachitire ulemu motani? Paulo anati: “Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Kristu.” (1 Akorinto 11:1) Pamene tilabadira mawu a Paulo akuti timutsanze, tikumchitira ulemu. Ichi chiyenera kugwira ntchito kwa omwe akutsogolera pakati pathu lerolino. Kuukulu umene timaŵatsanzira mwakutsatira chitsanzo chawo, tidzakhala tikuŵachitira ulemu.
16. Kodi ndinjira zowonjezereka ziti zimene ulemu ungasonyezedwe kwa otsogolera?
16 Njira ina imene timachitira oyang’anira ulemu njakulabadira kuchonderera kwakuti: “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera.” (Ahebri 13:17) Mofanana ndi mmene ana amachitira ulemu makolo awo mwa kukhala oŵamvera, chotero nafenso timachitira ulemu otsogolera pakati pathu mwa kukhala omvera ndi ogonjera kwa iwo. Ndipo, monga mmene Paulo ndi anzake anachitidwira ulemu ndi mphatso zakuthupi ndi nzika zachifundozo zokhala pa Melita, oimira oyendayenda ambiri a Sosaite achitiridwa ulemu mofananamo kaŵirikaŵiri. Koma, iwo ndithudi safunikira kutopempha mphatsozi kapena kupereka chizindikiro chakuti iwo akaziyamikira kapena kuti akuzifunikira.
17. Kodi ndithayo lotani limene awo okhala ndi mathayo auyang’aniro ali nalo ponena za kusonyeza ulemu?
17 Kumbali ina, onse okhala m’malo athayo m’gulu la teokratiki—kaya mukhale mumpingo wapamalopo, m’dera kapena m’chigawo monga woyang’anira woyendayenda, pa imodzi ya nthambi za Watch Tower Society, kapena m’banja—ali ndi thayo la kuchitira ulemu anthu omwe akuŵayang’anirawo. Ichi chimafunikiritsa kuti akhale ochitira chisoni ndi achifundo. Nthaŵi zonse afunikira kukhala ofikirika, pokhala ofatsa ndi odzichepetsa mtima, monga mmene Yesu Kristu ananenera kuti adali tero.—Mateyu 11:29, 30.
Gwirirani Ntchito pa Kuchitirana Ulemu
18. (a) Kodi nchiyani chomwe chingatidodometse kuchitira ulemu kwa ouyenerera? (b) Kodi nchifukwa ninji palibe chodzilungamitsa ponena za kulingalira kwachidani ndi kosuliza?
18 Tonsefe timafunikira kugwirira ntchito zolimba pakuchitirana ulemu, pakuti pali chotiletsa kuchita tero champhamvu. Choletsacho, kapena chopinga, ndicho mtima wathu wopanda ungwiro. Baibulo likuti: ‘Pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu iri yoipa kuyambira pa unyamata wake.’ (Genesis 8:21) Chimodzi cha zikhoterero za anthu chimene chingadodometse kusonyeza kuchitira ena ulemu ndicho kukhala ndi lingaliro lachidani, losuliza. Tonsefe ndife anthu ofooka, opanda ungwiro, ofunikira chifundo ndi chisomo cha Yehova. (Aroma 3:23, 24) Poyamikira zimenezi, tiyeni tikhale osamala kusakuza zifooko za abale athu kapena kuika zolinga zokaikira pa abale athu.
19. Kodi nchiyani chomwe chidzatithandiza kuchotsa mkhalidwe wamaganizo wachidani uliwonse?
19 Mankhwala a chikhoterero choipa chirichonse chotero ndiwo chikondi ndi kudziletsa. Tiyenera kukhala ndi mkhalidwe wabwino wachifundo, wokhulupirika ponena za abale athu, kuiwona mikhalidwe yawo yabwino. Ngati pali chomwe sitikumvetsetsa, tiyeni nthaŵi zonse tikhale ofunitsitsa kungochiponya kunkhongo ndi kulabadira uphungu uwu wa Petro: ‘Koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo.’ (1 Petro 4:8) Tiyenera kukhala ndi chikondi chamtunduwu ngati titi tichitire abale athu ulemu woŵafunikira.
20, 21. (a) Kodi nchikhoterero china chiti chimene mwachiwonekere chingadodometse kuchitirana kwathu ulemu? (b) Kodi nchiyani chomwe chidzatithandiza kuchotsa chikhotererochi?
20 Chikhoterero china chimene mwachiwonekere chingadodometse kuchitira kwathu ulemu ena ndicho cha kukwiya msanga, kapena kukhudzidwa msanga ndi zinthu mosayenerera. Kukhudzidwa msanga ndizinthu kuli ndi malo ake. Akatswiri azaluso amafunikira kukhudzidwa msanga atamva phokoso kapena atawona mitundu ya utoto monga mbali ya ntchito yawo. Koma kukhala wokhudzidwa msanga ndi zinthu mosayenerera, kapena kukwiya msanga muunansi wathu ndi ena ndiko mtundu wina wa dyera limene lingatilande mtendere wathu ndikutiletsa kuchitira ena ulemu.
21 Otipatsa uphungu wabwino pankhaniyi ndimawu awa opezeka pa Mlaliki 7:9: ‘Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m’chifuwa cha zitsiru.’ Chotero kukhala wokhudzidwa msanga ndi zinthu mosayenerera kapena kukwiyitsidwa msanga, kumasonyeza kupanda nzeru ndi kusalingalira bwino, limodzinso ndikupanda chikondi. Tiyenera kukhala ochenjera kuwopera kuti ndingaliro zathu zochimwa, zonga ngati chidani, kukhala wosuliza kwambiri, kapena kukhala wokhudzidwa msanga ndi zinthu mosayenerera, zingatiletse kuchitira ulemu onse owufunikira.
22. Kodi thayo lathu la kuchitira ulemu lingafotokozedwe mwachidule motani?
22 Zowonadi, tiri nazo zifukwa zambiri zochitira ena ulemu. Ndipo, monga mmene tawonera, pali njira zambirimbiri zimene tingachitire nazo ulemu woterowo. Tiyenera nthaŵi zonse kukhala ochenjera kuwopera kuti mkhalidwe wadyera kapena wachidani uliwonse ungadodometse kuchitira kwathu ulemu. Kwenikweni, tiyenera kukhala osamala kuchitira ulemu a m’banja lathu, amuna ndi akazi kwa wina ndi mnzake ndipo ana kulinga kwa makolo awo. Ndipo mumpingo, tiri ndi thayo la kuchitira ulemu alambiri anzathu, ndipo makamaka ogwira ntchito zolimba pakati pathu okhala m’malo auyang’aniro. M’mbali zonsezi, kuchitira ulemu woyenerera kwa omwe atchulidwa pamwambapo kumatipindulitsa, popeza kuti, Yesu anati: “Muli chimwemwe chambiri m’kupatsa koposa chimene chiri m’kulandira.”—Machitidwe 20:35, NW.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji ndipo ndimotani mmene tiyenera kuchitira ulemu akuluakulu aboma?
◻ Kodi ndiuphungu uti wa Baibulo umene ungagwiritsiridwe ntchito muunansi wa wantchito ndi womulemba ntchito?
◻ Kodi ndimotani mmene kuchitira ulemu kuyenera kusonyezedwera m’banja?
◻ Kodi ndikuchitira ulemu kwapadera kotani kumene kungasonyezedwe mumpingo, ndipo nchifukwa ninji?
◻ Kodi ndimotani mmene zifooko zaumunthu za kulephera kuchitira ulemu ena zingalakidwire?