Kukwaniritsa Zosowa za Okalamba Athu—Chitokoso cha Mkristu
MIYEZI itatu yapita. Komabe palibe ndi mwana mmodzi yense wa mkazi wokalambayo anabwera kumuchezera. Iye ali nzika yosungulumwa ya nyumba ya okalamba mu Cape Town, South Africa. Ana ake amakhala pafupi.
M’nyumba ya okalamba mu Johannesburg, mkazi wokalamba amathera yambiri ya nthaŵi yake pakhonde la chipinda chake. Iye nthaŵi zambiri amawonedwa akulira.
Zochitika zomvetsa chisoni zonga izi zikukhala zofala mowonjezerekawonjezereka, ngakhale m’maiko mmene okalamba mwamwambo anali kusamaliridwa bwino. Mu Soweto, mzinda waukulu wokhalidwa ndi anthu akuda pafupi ndi Johannesburg, “anthu achikulire [a]taya ulemu wa mwambo, ulamuliro ndi chisamaliro kuchokera ku mabanja awo,” mogwirizana ndi ripoti limodzi la pa nyuzipepala. Mkhalidwe wofananawo wakula pakati pa magulu ambiri a Amwenye mu South Africa. Ngakhale kuti Amwenye mwa mwambo anakhala ochitira ulemu kwa okalamba awo, nduna posachedwapa inalongosola kuti okwatirana achichepere Achimwenye ‘safuna kulemetsedwa ndi makolo awo.’
Akristu owona, ngakhale kuli tero, amalabadira lamulo la Baibulo: “Lemekeza atate wako ndi amako.” (Eksodo 20:12; Aefeso 6:2) Thayo limeneli silimasiya pamene makolo awo akalamba. Akutero 1 Timoteo 5:8: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye ndipo aipa koposa wosakhulupirira.” Makolo okalamba ali pakati pa awo amene Mkristu akayenera kusamalira, ngakhale ngati ichi chikaphatikizapo kudzipereka kokulira—mwa maganizo ndi mwa chuma.
Mokulira, ziwalo za mpingo Wachikristu lerolino zachita ntchito yokhumbirika yosamalira zosowa za malingaliro ndi zakuthupi za makolo awo. Nchiyani chimene chimachitika, ngakhale ndi tero, pamene Akristu okalamba alibe ana owopa Mulungu kapena adzukulu owasamalira? Ndimotani mmene zosowa zawo zimakwaniritsidwira?
Thayo la Mpingo
Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo.” Yakobo ananenanso kuti: “Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa nichikamsowa chakudya cha tsiku lake, ndipo wina wa inu akanena nawo: ‘Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta,’ osawapatsa iwo zosowa za pathupi, kupindula kwake nchiyani? Momwemonso, chikhulupiriro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa mkati mwakemo.”—Yakobo 1:27; 2:15-17.
Chotero ngati Mkristu wachikulire afunikira thandizo, iyi iri nkhani yodetsa nkhaŵa ku mpingo wonse. Akulu angatenge chitsogozo m’nkhaniyi. Monga mmene Paulo anatsogozera pa 1 Timoteo 5:4, iwo ayenera kugamulapo choyamba ngati wokalambayo ali ndi ana kapena adzukulu omwe ali ofunitsitsa “kubwezera akuwabala, pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.” Ngati ayi, akulu angafufuze kuwona ndi ndalama za chisungiko kapena zoperekedwa za boma zotani zimene ziripo. Chingakhale chakuti ena mu mpingo ali m’mkhalidwe wa kuthandiza mwachuma pamaziko aumwini.
Ngakhale kuli tero, ngati makonzedwe oterowo sangapangidwe, akulu angalingalire ngati munthuyo ayeneretsedwa kulandira thandizo kuchokera mu mpingowo. Paulo ananena kuti: “Asaŵerengedwe amasiye ngati sanafikire zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna mmodzi, wa mbiri ya ntchito zabwino.”—1 Timoteo 5:9, 10.
Kaŵirikaŵiri koposa, ngakhale ndi tero, si ndalama zimene zimafunidwa. Akulu angagamulepo kokha chimene chikufunikira. Kodi wokalambayo akufunikira thandizo m’kugula? Kodi iye ali wosungulumwa kapena akufunikira chilimbikitso? Kodi iye akufuna choyendera kupita ku misonkhano? Kodi iye akufuna winawake kumuŵerengera Baibulo ndi zofalitsidwa za Chikristu kwa iye? Ngati munthu wokalambayo ali mwakuthupi wosakhoza kupita ku misonkhano, kodi zojambulidwa za pa tepi zingapangidwe kotero kuti angamvetsere izo kunyumba? Chingatenge maulendo angapo ndi kucheza chithunzi chenicheni chisanapangidwe. Koma monga abusa, akulu ‘ayenera kuzindikira kawonekedwe ka nkhosa zawo.’—Miyambo 27:23.
Mmene Mipingo Yathandizira
Pamene zosowa za munthu wokalamba zadziŵika, makonzedwe achindunji angapangidwe. Kumene kuli mzimu wotentha, wosamalira, ndi wopanda dyera mu mpingo, sichiri chovuta kupeza unyinji wa abale ndi alongo ofunitsitsa kukhala othandiza. Chotero thayo losayenerera siliikidwa pa anthu oŵerengeka. Mwachitsanzo, mpingo umodzi wachita ndandanda kaamba ka ofalitsa kuchezera okalamba. Abalewo ndi alongo ali osangalatsidwa kukhala ndi kugawanamo m’kuchita ichi, ndipo palibe ndi mmodzi yense wa okalambawo amene akunyalanyazidwa.
Mu mpingo wina, Mboni yokalamba inanyalanyazidwa ndi ana ake osakhulupirira. Mboni zachichepere za kumaloko, ngakhale kuli tero, zinachapa, kusita, ndi kuyeretsa, limodzinso ndi kusamalira pa bwalo pake. Abalewo anathandiza kulipirira kaamba ka nyumba ndi chakudya chake. Anamtenga iye ku misonkhano yadera ndi misonkhano ya mpingo. Ndipo pamene anamwalira, anasamalira kaamba ka makonzedwe onse a maliro ndi ndalama zowonongedwa.
Mu mpingo umodzi waung’ono wa ku South Africa, mbale wokalamba wachikaladi (mmodzi wa chiyambi cha mafuko osakanikirana) anafa ziwalo kotheratu ndi stroke. Popeza panalibe wina aliyense wa mbanja lake kuti amuyang’anire iye, mlongo m’mpingo—mkazi wamasiye iyemwini—ndi mwana wake wa mwamuna anamtenga iye. Amuna mu mpingowo anasithana kumsambitsa. M’kuwonjezerapo, mbale wa chipainiya woyera anali kukankha mbale wachikulire ameneyu pa mpando wa magudumu kaamba ka kupita kunja. Chowoneka chimenechi, chachilendo mu South Africa, chinapangitsadi kuzizwitsidwa. Mpingowo unapereka kwa mbale wokalambayo chisamaliro chachikondi kufikira anamwalira.
Ngakhale ndi tero, uku sindiko kunena kuti, kukwaniritsa zosowa za abale ndi alongo okalamba kuli kopepuka. Iko kungatenge chiyambi ndi chigamulo chenicheni kulaka mavuto omwe angabuke.
Kupititsa Okalamba ku Misonkhano
Mlongo wokalamba, mkazi wamasiye ndipo wodwala nthenda ya mtima, anachezeredwa tsiku limodzi ndi mkulu. Pamene anali kumeneko, mnansi anabwera ndi kudandaula, akumanena kuti: “Ndimabwera muno kaŵirikaŵiri ndi kumpeza iye akulira chifukwa palibe amene amabwera kudzamtenga iye kupita ku Nyumba ya Ufumu.” Vutolo silinali lowopsya monga mmene mnansiyo analipangira ilo kuwoneka, popeza banja mu mpingowo linali kupereka choyenderamo chokhazikika. Ngakhale kuli tero, pa zochitika zochepa atate anagwira ntchito mowonjezereka ndipo analephera kubwera kaamba ka mlongoyo. Ndithudi, makonzedwe ena a choyendera akanayenera kupangidwa.
Chotero, icho chiri, chabwino kukumbukira kuti kupezeka pa misonkhano kuli kofunika koposa kaamba ka okalamba. (Ahebri 10:24, 25) Mkulu mmodzi nthaŵi zonse amafufuza kuwona ngati Mboni ina yake yokalamba iripo. Ngati iye salipo chifukwa chakuti makonzedwe a choyendera alephera, mkuluyo amathamangira ku galimoto yake ndi kukamtenga iye. Kumwetulira kwachikondi pa nkhope yake kumapereka mphatso kwa iye kaamba ka kuyesetsa kowonjezerekako.
Ochenjera koma Owumirira
Nthaŵi zina, ngakhale kuli tero, anthu achikulire amakonda kukhala odzidalira. Iwo angakhale osowa thandizo koma amakana kulandira ilo. Ndipo kokha ngati akulu, kapena ogawiridwa kupereka chithandizo, ali amaso, okalamba oterowo angakhale oyedzamira ku kuyesera ‘kuchita icho m’njira yawo.’
Mkazi mmodzi wamasiye wokalamba anali kudwala kansa koma anasunga matenda ake kwa iyemwini. Iye anafunikira thandizo kusamutsira zinthu zake zaumwini ku malo omwe anali pa mtunda wa mailosi imodzi kutali. M’malo modziŵitsa ena za chosowa chake, iye anapempha thandizo la bwenzi la zaka 84 zakubadwa. Onse pamodzi analonga zinthu zina mu ngolo ndi kuyesera kuikankha iyo iwo eni. Mwamsanga, ngakhale kuli tero, anazindikira kuti ntchitoyo inali yoposa kuthekera kwawo, ndipo bwenzi la mkazi wamasiyeyo anapita kwa mkulu wapafupipo kaamba ka thandizo.
Icho, chotero, chingatenge kufunsira kochenjera komabe koumirira ku mbali yathu kuti tigamulepo kokha chimene tingachite kuti tithandize anthu oterowo. Ngati ife tingopereka chopereka chopanda maziko, monga ngati: ‘Ngati pali chinachake mukufuna, ndidziŵitseni,’ pangakhale yankho losawona mtima: ‘Zikomo, koma sindikufuna chirichonse.’ Kumbukirani, ngakhale ndi tero, kuti pamene Lidiya anapereka kuchereza kwa mtumwi Paulo ndi ena, iye sanaletsedwe ndi kukana kwawo koyambirira. M’malomwake, ‘anawawumiriza iwo.’ (Machitidwe 16:15) Chotero khalani owumirira. Pezani zosowa ndi zofuna za okalamba asanakufunseni kaamba ka thandizo.
Ndithudi, okalamba ayenera kukhala oyamikira za zoyesayesa za ena ndipo sayenera kukhala ozindikira, ofunsira mopambanitsa, kapena osuliza. Ngati choyendera chikuperekedwa, mwachitsanzo, chopereka cha kuthandiza kulipirira kaamba ka ndalama zoyendera chingakhale choyenerera. Mlongo mmodzi wokalamba amaphika mkate ndi kuluka zinthu zochepera ndi kuzipereka monga mphatso kwa awo amene amamtenga kupita naye ku misonkhano ya mpingo. M’zochitika zambiri, ngakhale ndi tero, kokha liwu la chiyamikiro liri zonse zimene zimafunidwa.
Akristu lerolino amakalamira kumvera lamulo la pa Levitiko 19:32: “Pali a imvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba.” Atumiki a Yehova samatsatira chikhoterero cha kudziko cha kutaya anthu okalamba ndi kuika pambali thayo la ana. M’malomwake, ndi nthaŵi, kuleza mtima, ndi thandizo la Yehova, Akristu amagwira ntchito kukwaniritsa mwachipambano chitokoso cha kusamalira okalamba athu.
[Chithunzi patsamba 23]
Achichepere mu mpingo kaŵirikaŵiri angachite zochuluka kuthandiza anthu okalamba