Kodi ‘Mwazika Mizu ndi Kukhazikika pa Maziko’?
KODI munayamba mwaonapo mtengo waukulu ukuwombedwa ndi chimphepo chamkuntho? Chimphepocho chimawomba mwamphamvu koma mtengo osagwa ayi. Kodi zimatheka bwanji? Zimatheka chifukwa choti mtengowo uli ndi mizu yomwe inazika zolimba. Ifenso tingakhale ngati mtengo woterowo. Tikakhala pa mavuto, nafenso tingathe kupirira ngati titakhalabe ‘ozika mizu ndi kukhazikika pa maziko.’ (Aef. 3:14-17) Kodi maziko amenewa ndi chiyani?
Mawu a Mulungu amati “Khristu Yesuyo ndiye mwala wa pangodya wa kumaziko” a mpingo wachikhristu. (Aef. 2:20; 1 Akor. 3:11) Akhristufe tikulimbikitsidwa kuti: “Yendanibe mogwirizana naye. Khalanibe ozikika mozama . . . Pitirizani kumangidwa mwa iye ndi kukhazikika m’chikhulupiriro.” Tikatero, tingathe kulimbana ndi zinthu zonse zofuna kufooketsa chikhulupiriro chathu, kuphatikizapo zinthu monga “mfundo zokopa” zozikidwa pa “chinyengo chopanda pake” cha anthu.—Akol. 2:4-8.
“M’lifupi ndi M’litali ndi Kukwera ndi Kuzama”
Komano kodi tingakhale bwanji “ozikika mozama” ndi ‘okhazikika m’chikhulupiriro’? Njira imodzi yothandiza kwambiri kuzika mizu yathu mwauzimu, ndiyo kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu ouziridwa. Yehova amafuna kuti ‘tithe kudziwa bwino lomwe m’lifupi ndi m’litali ndi kukwera ndi kuzama’ kwa choonadi. (Aef. 3:18) Motero Mkhristu aliyense asamakhutire ndi kudziwa zinthu mwa apa ndi apo chabe, kapena kungodziwa “mfundo zoyambirira” za m’Mawu a Mulungu. (Aheb. 5:12; 6:1) M’malomwake, tonsefe tizikhala ofunitsitsa kudziwa mozama choonadi cha m’Baibulo.—Miy. 2:1-5.
Komabe sikuti kungodziwa zinthu zambirimbiri ndiye kuli kofunika kuti ‘tizikike mozama ndi kukhazikika m’chikhulupiriro.’ Tisaiwale kuti ngakhale Satana amadziwa zimene zili m’Baibulo. Choncho pali zinthu zinanso zofunikira zimene tiyenera kuchita. Tiyenera ‘kudziwa chikondi cha Khristu chimene chiposa kudziwa zinthu.’ (Aef. 3:19) Tikamaphunzira Mawu a Mulungu chifukwa chokonda Yehova ndiponso choonadi, zimene tikuphunzirazo zingathe kulimbitsa chikhulupiriro chathu.—Akol. 2:2.
Dziyeseni Kuti Muone Zimene Mukudziwa
Bwanji osadziyesa panopo kuti muone ngati mukumvetsa ziphunzitso zina zikuluzikulu za m’Baibulo? Kuchita zimenezi kungakulimbikitseni kuti muzichita khama pophunzira Baibulo. Mwachitsanzo, tawerengani mawu oyambirira a kalata ya Paulo kwa Aefeso. (Onani bokosi lakuti “Kwa Aefeso.”) Mukamaliza kuwerenga mavesi amenewa dzifunseni kuti, ‘Kodi mfundo za m’Baibulo zimene zalembedwa mopendeketsazi, ndikuzimvetsa matanthauzo ake?’ Tiyeni tione mfundo iliyonse payokha.
Anasankhidwiratu “Dziko Lisanakhazikitsidwe”
Paulo analemba mawu otsatirawa kwa Akhristu anzake: “[Mulungu] anatisankhiratu kuti adzatitenga kukhala ana ake kudzera mwa Yesu Khristu.” Inde, Yehova anakonza zoti adzatenga anthu ena kuti akakhale m’banja lake langwiro la kumwamba. Ana a Mulungu otengedwa padziko lapansiwa adzalamulira monga mafumu ndi ansembe pamodzi ndi Khristu. (Aroma 8:19-23; Chiv. 5:9, 10) Nthawi yoyamba imene Satana anatsutsa kalamuliridwe ka Yehova, Satanayo anasonyeza kuti pali cholakwika ndi mmene Mulungu analengera anthu. Moterotu m’pomveka kuti Yehova anasankha anthu omwewo kuti adzagwire nawo ntchito yochotsa zoipa zonse m’chilengedwe chonse, kuphatikizapo Satana Mdyerekezi, yemwe amayambitsa zoipa zonse. Komabe, sikuti Yehova anachita kusankhiratu munthu aliyense amene adzamutenge kuti akakhale m’gulu la ana ake. Koma anasankha gulu la anthu loti lidzalamulire ndi Khristu kumwamba.—Chiv. 14:3, 4.
Kodi ndi “dziko” liti limene Paulo ankanena m’kalata yake yopita kwa Akhristu yomwe ananenamo kuti iwowo, monga gulu, anasankhidwa “dziko lisanakhazikitsidwe”? Iye sankanena za nthawi imene Mulungu anali asanalenge dziko kapena anthu. Chifukwa zikanakhala choncho, ndiye kuti sichikanakhala chilungamo ngakhale pang’ono. Kodi zikanakhala zomveka kuimba mlandu Adamu ndi Hava ngati Mulungu akanakhala kuti anali atalemberatu kuti iwo adzachimwa asanawalenge n’komwe? Motero, kodi Mulungu anakonza liti zothetsa vuto limene linabwera Adamu ndi Hava ataukira ulamuliro wa Mulungu potsatira Satana? Yehova anakonza zimenezi makolo athu oyambirirawa atamuukira, koma anthu opanda ungwiro oti angathe kuwomboledwa asanayambe kubadwa.
“Malinga ndi Chuma cha Kukoma Mtima kwa M’chisomo Chake”
N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti dongosolo lotchulidwa m’mavesi oyambirira a buku la Aefesolo linakhalapo chifukwa cha “chuma cha kukoma mtima kwa m’chisomo cha” Mulungu? Ananena zimenezi pofuna kugogomezera kuti Yehova akanapanda kuwombola anthu, palibe amene akanamuimba mlandu.
Mwachibadwa, aliyense wa ife si woyenerera kuwomboledwa. Komano, chifukwa chokonda kwambiri anthu, Yehova anakhazikitsa dongosolo lapadera lotipulumutsira. Poganizira kuti ndife opanda ungwiro komanso ochimwa, m’pomveka kuti Paulo ananena kuti Mulungu anatiwombola chifukwa cha kukoma mtima kwa m’chisomo chake.
Chinsinsi Chopatulika Chonena za Cholinga cha Mulungu
Pachiyambi Mulungu sanafotokoze mmene adzachotsere zoipa zimene Satana anabweretsa. Chimenechi chinali “chinsinsi chopatulika.” (Aef. 3:4,5) Patsogolo pake, mpingo wachikhristu utakhazikitsidwa, Yehova anavumbula tsatanetsatane wa mmene adzakwaniritsire cholinga chimene analengera anthu ndi dziko lapansi. Paulo anati itatha “nyengo yonse ya nthawi zoikika,” Mulungu anakhazikitsa “dongosolo” lomwe cholinga chake ndi kugwirizanitsa anthu ndi angelo.
Mbali yoyamba ya ntchito yogwirizanitsa imeneyi, inayamba pa Pentekoste mu 33 C.E. pamene Yehova anayamba kusonkhanitsa anthu amene adzalamulire pamodzi ndi Khristu kumwamba. (Mac. 1:13-15; 2:1-4) Mbali yachiwiri ndi yosonkhanitsa anthu amene adzakhale padziko lapansi la paradaiso mu ulamuliro wa Ufumu wa Mesiya. (Chiv. 7:14-17; 21:1-5) Mawu akuti “dongosolo” sanena za Ufumu wa Mesiya, chifukwa Ufumuwo unali usanakhazikitsidwe mpaka m’chaka cha 1914. Koma mawuwa amanena za njira imene Mulungu akuchitira zinthu kuti akwaniritse cholinga chake chokhazikitsanso mgwirizano m’chilengedwe chonse
Pa “Luntha la Kuzindikira Khalani Aakulu Msinkhu”
N’zosakayikitsa kuti kukhala ndi chizolowezi chabwino chophunzira Baibulo, kungakuthandizeni kumvetsa choonadi “m’lifupi ndi m’litali ndi kukwera ndi kuzama” kwake komwe. Komabe, n’zosakayikitsanso kuti moyo wa masiku ano wochita zinthu mothamangawu, umachititsa kuti Satana asavutike kutisokoneza kuti tisiye zizolowezi zabwino ngati zimenezi. Musamulole kuti achite zimenezi kwa inu. Gwiritsani ntchito “nzeru” zimene Mulungu wakupatsani kuti ‘pa luntha la kuzindikira mukhale aakulu msinkhu.’ (Yoh. 5:20; 1 Akor. 14:20) Onetsetsani kuti mukumvetsa chifukwa chimene mumakhulupirira zinthu zimene mumakhulupirira ndiponso kuti ndinu wokonzeka nthawi zonse kupereka “chifukwa cha chiyembekezo chimene muli nacho.”—1 Pet. 3:15.
Tayerekezerani kuti munaliko ku Efesoko pa nthawi imene kalata ya Paulo inawerengedwa koyamba. N’zosakayikitsa kuti mawu akewa akanakulimbikitsani kuti mukule “pa kum’dziwa molondola Mwana wa Mulungu.” (Aef. 4:13, 14) Motero mawu ouziridwa a Paulowa akulimbikitseninso chimodzimodzi panopa. Kukonda kwambiri Yehova ndiponso kudziwa Mawu ake molondola kungakuthandizeni kuti “muzike mizu ndi kukhazikika pa maziko” a Khristu. Potero, mungathe kupirira mkuntho wa mayesero alionse amene Satana angakubweretsereni dongosolo lino lisanafike pamapeto pake penipeni.—Sal. 1:1-3; Yer. 17:7, 8.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]
“Kwa Aefeso”
“Adalitsike Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, pakuti watidalitsa ndi dalitso lililonse lauzimu m’malo akumwamba mogwirizana ndi Khristu. Wachita zimenezi monga muja anatisankhira kuti tikakhale ogwirizana ndi Yesuyo dziko lisanakhazikitsidwe, kuti tikakhale oyera ndi opanda chilema pamaso pa Mulungu m’chikondi. Pakuti anatisankhiratu kuti adzatitenga kukhala ana ake kudzera mwa Yesu Khristu, malinga ndi zom’komera iyeyo ndiponso chifuniro chake. Anatero kuti kukoma mtima kwaulemerero kwa m’chisomo kumene anatisonyeza kudzera mwa wokondedwa wake kutamandike. Kudzera mwa iyeyu, tinamasulidwa ndi dipo la magazi ake, inde, takhululukidwa machimo athu, malinga ndi chuma cha kukoma mtima kwa m’chisomo chake. Iye anatipatsa mochuluka kukoma mtima kumeneku mwa nzeru zonse ndi kuzindikira konse, mwakuti anatiululira chinsinsi chopatulika cha chifuniro chake. Chinsinsicho n’chogwirizana ndi zokomera mwiniwakeyo ndi zimene anafuna mu mtima mwake, kuti akakhazikitse dongosolo lake ikadzatha nyengo yonse ya nthawi zoikika. Dongosolo limenelo ndilo kusonkhanitsanso zinthu zonse pamodzi mwa Khristu, zinthu za kumwamba ndi zinthu za padziko lapansi.”—Aef. 1:3-10.