Achinyamata Musasunthike Polimbana ndi Mdyerekezi
“Valani zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu kuti musasunthike polimbana ndi zochita zachinyengo za Mdyerekezi.”—AEF. 6:11.
1, 2. (a) N’chiyani chimathandiza achinyamata kupambana pa nkhondo yolimbana ndi Satana ndi ziwanda zake? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
MTUMWI PAULO anayerekezera moyo wa Akhristufe ndi zimene zimachitika ndi msilikali amene wakumana ndi mdani pafupi n’kumamenyana naye. N’zoona kuti nkhondo imene tikumenya si yeniyeni koma yauzimu. Ngakhale zili choncho, adani athu ndi enieni. Satana ndi ziwanda zake ndi akatswiri pa nkhondo ndipo akhala akuimenya kwa zaka zambirimbiri. Kungoganizira zimenezi, munthu angaone kuti sangapambane. Makamaka achinyamata ndi amene amaoneka kuti akhoza kupezereredwa ndi adaniwa. Ndiye kodi angatani kuti apambane pa nkhondo yolimbana ndi Satana ndi ziwanda, omwe ndi amphamvu kwambiri? Chosangalatsa n’chakuti achinyamata akhoza kupambana pa nkhondoyi ndipo n’zimene zikuchitikadi. Zimenezi zikutheka chifukwa chakuti amapeza “mphamvu kuchokera kwa Ambuye.” Koma pali zinanso zimene amachita. Mofanana ndi asilikali ophunzitsidwa bwino, iwo amakhala okonzeka chifukwa choti amavala “zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu.”—Werengani Aefeso 6:10-12.
2 N’kutheka kuti pamene Paulo ankafotokoza fanizo lakeli, ankaganizira zida zankhondo zimene asilikali achiroma ankavala. (Mac. 28:16) Tiyeni tsopano tikambirane fanizoli n’kuona chifukwa chake ndi loyenerera. Tikamakambirana, tionanso zimene achinyamata ena afotokoza pa nkhani ya mavuto amene amakumana nawo komanso ubwino wovala zida zonse.
LAMBA WA “CHOONADI”
3, 4. Kodi mfundo zoona za m’Baibulo zimafanana bwanji ndi lamba amene msilikali wachiroma ankavala?
3 Werengani Aefeso 6:14. Lamba amene msilikali wachiroma ankavala ankakhala ndi zitsulo zimene zinkateteza chiuno chake. Lambayu ankapangidwa m’njira yoti azithandiza msilikali kuti asamalemedwe ndi zida zake. Malamba ena analinso ndi malo okolekapo lupanga komanso mpeni. Msilikali akamanga lamba wake ankatha kumenya bwino nkhondo.
4 Mofanana ndi zimenezi, mfundo zoona zimene timaphunzira m’Mawu a Mulungu zimatiteteza kuti tisamasokonezedwe ndi mfundo zabodza. (Yoh. 8:31, 32; 1 Yoh. 4:1) Tikamakonda kwambiri mfundo zoonazi, sitilemedwa ndi “chodzitetezera pachifuwa,” chomwe chikuimira mfundo zachilungamo zochokera kwa Mulungu. (Sal. 111:7, 8; 1 Yoh. 5:3) Komanso tikamamvetsa bwino mfundo za m’Mawu a Mulungu timatha kuzifotokoza bwino kwa anthu amene amatitsutsa.—1 Pet. 3:15.
5. N’chifukwa chiyani tiyenera kunena zoona nthawi zonse?
5 Tikamadziwa bwino komanso kukonda mfundo zoona zopezeka m’Baibulo, zimakhala zosavuta kuzitsatira pa moyo wathu komanso kunena zoona nthawi zonse. Tikutero chifukwa chakuti Satana ndi amene wakhala akugwiritsa ntchito mabodza popusitsa anthu. Munthu amene amanena mabodza komanso amene amawakhulupirira amakumana ndi mavuto. (Yoh. 8:44) Choncho ngakhale kuti si ife angwiro, tiyenera kuyesetsa kupewa bodza. (Aef. 4:25) Koma kuchita zimenezi si kophweka. Mtsikana wina wazaka 18 dzina lake Abigail ananena kuti: “Nthawi zina kunena zoona kungaoneke ngati kosathandiza. Izi zingachitike makamaka pamene kunama kungakuthandize kuti usakumane ndi vuto linalake.” Ndiye n’chifukwa chiyani Abigail amayesetsa nthawi zonse kuti azinena zoona? Iye anati: “Ndikamanena zoona ndimakhala ndi chikumbumtima chabwino. Komanso makolo anga ndiponso anzanga amandikhulupirira.” Mtsikana wina wazaka 23 dzina lake Victoria ananena kuti: “N’zoona kuti ukamanena zoona komanso kufotokozera anthu zimene umakhulupirira, ena angakuvutitse. Koma pali ubwino wake. Munthu akamanena zoona amasiya kudzikayikira, amalimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova komanso anzake amamulemekeza.” Mosakayikira, ‘kumanga kwambiri choonadi m’chiuno mwathu’ nthawi zonse n’kothandiza kwambiri.
“CHODZITETEZERA PACHIFUWA CHACHILUNGAMO”
6, 7. N’chifukwa chiyani chilungamo chimayerekezedwa ndi chodzitetezera pachifuwa?
6 Chodzitetezera pachifuwa chimene asilikali achiroma ankavala chinkakhala ndi zitsulo zolimba zomwe sizinkasiya mpata woti munthu n’kubayidwa. Zitsulozi zinkapindidwa bwino kuti zizigwira pachifuwa ponse ndipo ankazilumikiza pa chikopa. Cham’mapewamu munkakhalanso zitsulo zambiri zolumikizidwa pa chikopa. N’zoona kuti msilikali akavala zimenezi sankamasuka kwambiri ndipo ankafunika kuona pafupipafupi ngati chitsulo chilichonse chidakali pamalo ake bwinobwino. Koma chovala chimenechi chinkateteza msilikaliyo kuti mtima wake kapena ziwalo zina zofunika kwambiri zisabayidwe.
7 Fanizo limeneli likusonyeza bwino mmene mfundo zachilungamo za Yehova zingatetezere mtima wathu wophiphiritsa. (Miy. 4:23) Msilikali wanzeru sangavule chodzitetezera chachitsulo cholimba n’kuvala chachitsulo chosalimba. Nafenso, sitingayerekeze kusiya kutsatira mfundo za Yehova n’kumayendera zathu. Tikutero chifukwa chakuti nzeru zathu n’zoperewera ndipo sizingatiteteze bwinobwino. (Miy. 3:5, 6) Choncho ndi bwino kudzifufuza pafupipafupi kuti tione ngati mtima wathu wophiphiritsa ndi wotetezeka bwino ndi mfundo za Yehova.
8. N’chifukwa chiyani kutsatira mfundo za Yehova nthawi zonse n’kothandiza?
8 Kodi nthawi zina mumamva kuti mfundo zachilungamo za Yehova zimakupanikizani? Mnyamata wina wazaka 21 dzina lake Daniel anati: “Aphunzitsi komanso anzanga kusukulu ankandiseka chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Pa nthawi ina ndinayamba kudzikayikira mpaka kufika posokonezeka maganizo.” Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza? Iye anati: “Ndinadzazindikira ubwino wotsatira mfundo za Yehova. Zinali zomvetsa chisoni kuona kuti anzanga ena anayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo ena anasiya sukulu. Kunena zoona Yehova amatiteteza.” Mtsikana wina wazaka 15 dzina lake Madison anati: “Nthawi zina zimakhala zovuta kuti ndizitsatira mfundo za Yehova n’kumachita zinthu zosiyana ndi zimene anzanga amaona kuti ndi zobeba kapena zosangalatsa.” Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza? Iye anati: “Ndimangodzikumbutsa kuti ndimadziwika ndi dzina la Yehova ndipo mayesero amene ndikukumana nawo ndi njira imene Satana akufuna kundibayira ndi mivi yake. Ndipo ngati sindinagonje, ndimamva bwino kwambiri mumtima.”
“NSAPATO ZOKONZEKERA UTHENGA WABWINO WAMTENDERE”
9-11. (a) Kodi Akhristu amavala nsapato zophiphiritsa ziti? (b) N’chiyani chingatithandize kuti tisamavutike kulalikira?
9 Werengani Aefeso 6:15. Ngati msilikali wachiroma sanavale nsapato zake, sankakhala wokonzeka kupita kunkhondo. Popanga nsapatozi, ankaphatikiza zikopa zitatu. Zimenezi zinkathandiza kuti zizikhala zolimba komanso kuti zisamapweteke akamayenda nazo.
10 Nsapato zimene asilikaliwa ankavala zinkawathandiza kuti akhale okonzeka kukamenya nkhondo. Nazonso nsapato zophiphiritsa zimene Akhristu amavala zimawathandiza kuti azikhala okonzeka kulengeza uthenga wamtendere. (Yes. 52:7; Aroma 10:15) Ngakhale zili choncho, timafunika kulimba mtima kuti tilalikire. Mnyamata wina wazaka 20 dzina lake Bo anati: “Ndinkachita mantha kuti ndizilalikira anzanga kusukulu. Ndikuona kuti vuto langa linali manyazi. Sindikudziwa chifukwa chake ndinkamva choncho. Koma panopa ndimasangalala kulalikira anzanga.”
11 Achinyamata ambiri amaona kuti sizimawavuta kulalikira ngati akonzekera bwino. Ndiye kodi mungakonzekere bwanji? Mtsikana wina wazaka 16 dzina lake Julia ananena kuti: “Ndimakonda kuika mabuku ndi magazini m’chikwama chimene ndimatenga kusukulu. Komanso ndimamvetsera anzanga akusukulu akamafotokoza maganizo awo kapena zimene amakhulupirira. Ndikatero ndimadziwa zimene zingawathandize. Ndikakonzekera ndimatha kukambirana nawo nkhani zimene zingawathandize.” Mtsikana wina wazaka 23 dzina lake Makenzie anati: “Tikakhala okoma mtima komanso tikamamvetsera zimene anthu akulankhula tikhoza kudziwa zimene akukumana nazo. Ndimayesetsa kuti ndiziwerenga nkhani zonse zokhudza achinyamata n’cholinga choti ndizisonyeza anzanga malemba kapena nkhani za pa jw.org zomwe zingawathandize.” Zimene achinyamatawa ananena zimasonyeza kuti munthu akamakonzekera bwino zimakhala ngati wavala “nsapato” zake ndipo zamangidwa bwinobwino.
“CHISHANGO CHACHIKULU CHACHIKHULUPIRIRO”
12, 13. Kodi ‘mivi ina yoyaka moto’ imene Satana amagwiritsa ntchito ndi iti?
12 Werengani Aefeso 6:16. “Chishango chachikulu” cha asilikali achiroma chinkakhala chamakona 4 ndipo chinkaphimba kuchokera m’mapewa kufika m’maondo. Chishangochi chinkawateteza kuti asabayidwe ndi mivi kapena zida zina za adani.
13 ‘Mivi ina yoyaka moto’ imene Satana amagwiritsa ntchito imakhala mabodza okhudza Yehova. Mwachitsanzo, angakuchititseni kukhulupirira kuti Yehova sakuganizirani ndipo sangakukondeni. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtsikana wina wazaka 19 dzina lake Ida, yemwe nthawi zambiri amadziona kuti ndi wachabechabe. Iye anati: “Nthawi zambiri ndimaona kuti sindili pa ubwenzi ndi Yehova ndipo Yehovayo sakufuna kukhala Mnzanga.” Ndiye kodi amalimbana bwanji ndi maganizo amenewa? Ida anati: “Misonkhano ndi imene imandithandiza kwambiri. Poyamba ndinkangopita kumisonkhano koma sindinkayankha poganiza kuti palibe angafune kumva zimene ndinganene. Koma panopa ndimakonzekera bwino ndipo ndimayesetsa kuyankha kawiri kapena katatu. N’zoona kuti zimandivuta, koma ndimamva bwino ndikakwanitsa kuchita zimenezi. Abale ndi alongo amandilimbikitsanso kwambiri. Nthawi zonse ndikamachoka kumisonkhano ndimamva kuti Yehova amandikonda kwambiri.”
14. Kodi nkhani ya Ida ikutithandiza kuzindikira mfundo iti?
14 Nkhani ya Ida ikutithandiza kuzindikira mfundo yofunika kwambiri. Chishango cha msilikali chinkakhala cha saizi imodzi koma chikhulupiriro cha munthu chikhoza kukula kapena kuchepa malinga ndi zimene munthuyo amasankha kuchita. (Mat. 14:31; 2 Ates. 1:3) Choncho aliyense ayenera kuyesetsa kukulitsa chikhulupiriro chake.
“CHISOTI CHOLIMBA CHACHIPULUMUTSO”
15, 16. N’chifukwa chiyani chiyembekezo chathu chimayerekezeredwa ndi chisoti cholimba?
15 Werengani Aefeso 6:17. Chisoti cholimba chimene asilikali achiroma ankavala chinkawathandiza kuti asavulazidwe mutu, khosi ndi nkhope. Zisoti zina zinkakhala ndi chogwirira n’cholinga choti msilikali azitha kuchinyamula m’manja.
16 Mofanana ndi chisoti chimene chinkateteza ubongo wa msilikali, “chiyembekezo chachipulumutso” chimateteza maganizo athu. (1 Ates. 5:8; Miy. 3:21) Chiyembekezo chimatithandiza kuti tiziganizira malonjezo a Yehova nthawi zonse komanso kuti tizikhala ndi maganizo oyenera pa mavuto amene timakumana nawo. (Sal. 27:1, 14; Mac. 24:15) Koma kuti “chisoti” chathu chizititeteza, tiyenera kuchivala osati kungochinyamula m’manja.
17, 18. (a) Kodi Satana angatinyengerere bwanji kuti tivule chisoti chathu? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti sitikupusitsidwa ndi Satana?
17 Kodi Satana angatinyengerere bwanji kuti tivule chisoti chathu? Taganizirani zimene anachita poyesa Yesu. N’zosakayikitsa kuti Satana ankadziwa zoti Yesu akuyembekezera kudzalamulira anthu. Koma Yesu ankafunika kuyembekezera nthawi imene Mulungu ankafuna kuti ayambe kulamulirako. Ndipo anafunika kuvutika komanso kufa asanayambe kulamulira. Ndiyeno Satana anapatsa Yesu mwayi woti ayambe kulamulira mwamsanga. Anamuuza kuti akangomulambira kamodzi kokha, adzamupatsa ulamulirowo pompopompo. (Luka 4:5-7) Satana amadziwanso kuti Yehova adzatipatsa zinthu zimene timafuna m’dziko latsopano. Koma panopa tiyenera kudikira komanso kukumana ndi mavuto ena. Ndiyeno Satana amatipatsa mwayi woti tikhaliretu ndi moyo wofewa panopa. Iye amatinyengerera kuti tikhale ndi mtima wofunitsitsa kupeza zomwe timafuna pompopompo. Cholinga chake n’choti tiziika Ufumu pamalo achiwiri.—Mat. 6:31-33.
18 Mofanana ndi achinyamata ambiri, mtsikana wina wazaka 20 dzina lake Kiana salola kuti Satana amupusitse m’njira imeneyi. Iye anati: “Ndimadziwa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungathetseretu mavuto athu.” Kodi zimene akuyembekezerazi zimamuthandiza bwanji kuti azikhala ndi maganizo oyenera? Iye anati: “Zimene ndikuyembekezera m’Paradaiso zimandithandiza kuti ndisamatengeke ndi zinthu za m’dzikoli. Ndilibe mtima wofuna kudyerera luso langa kapena kupeza ntchito yapamwamba. M’malomwake ndimagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zanga pokwaniritsa zolinga zanga zauzimu.”
“LUPANGA LA MZIMU” LOMWE NDI MAWU A MULUNGU
19, 20. Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito mwaluso Mawu a Mulungu?
19 Lupanga limene asilikali achiroma ankagwiritsa ntchito pa nthawi imene Paulo analemba kalata yake yopita kwa Aefeso linkakhala lalitali masentimita 50. Linkapangidwa m’njira yoti msilikali akhoza kuligwiritsa ntchito bwino pomenyana pafupi ndi msilikali wina. Asilikali achiroma ankatha kugwiritsa ntchito lupanga lawo mwaluso chifukwa ankayeserera tsiku lililonse.
20 Paulo anayerekezera Mawu a Mulungu ndi lupanga. Koma tiyenera kuphunzira kuti tiziwagwiritsa ntchito mwaluso pofotokoza zimene timakhulupirira kapena kuti atithandize kusintha maganizo athu. (2 Akor. 10:4, 5; 2 Tim. 2:15) Kodi mungatani kuti muzigwiritsa ntchito Mawu a Mulungu mwaluso? Wachinyamata wina wazaka 21 dzina lake Sebastian ananena kuti: “Ndakhala ndikulemba vesi limodzi kuchokera m’chaputala chilichonse chimene ndawerenga m’Baibulo. Ndikusunga mavesi onse amene amandisangalatsa kwambiri. Zimenezi zikundithandiza kusintha maganizo anga kuti afanane ndi a Yehova.” Daniel yemwe tamutchula kale uja anati: “Ndikamawerenga Baibulo ndimasankha mavesi amene ndikuona kuti angathandize anthu mu utumiki. Ndaona kuti anthu ambiri amamvetsera akaona kuti timakonda kwambiri Baibulo komanso tikuyesetsa kuti tiwathandize.”
21. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa Satana kapena ziwanda zake?
21 Zimene achinyamata anena munkhaniyi zikusonyeza kuti sitiyenera kuopa Satana kapena ziwanda zake. N’zoona kuti ndi amphamvu koma sikuti ndi osagonjetseka. Komanso iwo sadzakhala ndi moyo mpaka kalekale. Posachedwapa, mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, adzamangidwa ndipo kenako adzawonongedwa. (Chiv. 20:1-3, 7-10) Timadziwa bwino mdani wathu, njira zimene amagwiritsa ntchito komanso zolinga zake. Koma Yehova akhoza kutithandiza kuti tisasunthike polimbana naye.