Makolo—Fikirani Mtima wa Mwana Wanu Kuyambira ku Ubwana
“Komatu muwalere iwo [ana anu] m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova].”—Aefeso 6:4.
1. Nchiyani chomwe chinachitika mkati mwa myengo yoyesa mwapadera m’moyo wa Yesu?
YESU KRISTU ndi ophunzira ake anali paulendo wawo kupita ku Yerusalemu. Osati kale chisanachitike chimenecho, pa zochitika ziŵiri zosiyana, Yesu anali atauza ophunzira ake kuti adzapita pansi pa kuvutika kokulira ndi kuphedwa mu mzinda umenewo. (Marko 8:31; 9:31) Mkati mwa nyengo yoyesa mwapadera imeneyi kaamba ka Yesu, mbiri ya Baibulo imanena kuti: “Ndipo anadza nawo kwa iye ana amakanda kuti awakhudze.” — Luka 18:15.
2. (a) Nchifukwa ninji ophunzirawo angakhale anayesera kuthamangitsa anthuwo? (b) Ndimotani mmene Yesu anavomerezera ku mkhalidwewo?
2 Ndi chivomerezo chotani chimene chinaliko ku ichi? Chabwino, ophunzirawo anadzudzula anthuwo ndi kuyesera kuwathamangitsa iwo, mosakaikira akumakhulupirira kuti iwo anali kuchita chiyanjo kwa Yesu mwakumchinjiriza iye kuchokera ku chisonkonezo ndi chididikizo chosayenerera. Koma Yesu anakwiya ndi ophunzira ake, nanena: “‘Lolani tiana tidze kwa ine; musatiletse’. . . Ndipo iye anatiyangata natidalitsa.” (Marko 10:13-16) Inde, mosasamala kanthu za zonse zomwe zinayenera kukhala m’malingaliro ndi mu mtima mwake, Yesu anatenga nthaŵi kaamba ka makanda.
Ndi Phunziro Lotani kwa Makolo?
3. Ndi phunziro lotani limene makolo ayenera kuphunzira kuchokera ku chochitikachi?
3 Phunziro kuchokera ku ichi kaamba ka makolo liyenera kukhala lakuti: Mosasamala kanthu za mathayo alionse amene muli nawo kapena mavuto amene mumayang’anizana nawo, kuthera nthaŵi ndi ana anu kumafunikira kupatsidwa malo oyambirira. Nthaŵi yowonongedwa pamodzi idzakutheketsani inu kuzika mapindu auzimu omwe adzachinjiriza mitima ya ana anu ndi kuwakhazikitsa iwo m’njira yabwino. (Deuteronomo 6:4-9; Miyambo 4:23-27) Yunike ndi Loisi, amayi ndi agogo a Timoteo, anatenga nthaŵi kumpatsa iye malangizo omwe anakhudza mtima wake waung’ono ndi kuwongolera moyo wake kotero kuti anakula kukhala mtumiki wodzipereka wa Mulungu. — 2 Timoteo 1:5; 3:15.
4. Kodi ana ali a mtengo wapatali motani, ndipo ndimotani mmene makolo ayenera kusonyezera kuti anayamikira iwo?
4 Makolo Achikristu sangathe kunyalanyaza ana amene Yehova Mulungu wapereka kwa iwo. Inde, ana ali mphatso yapadera yochokera kwe Yehova. (Masalmo 127:3) Chotero therani nthaŵi ndi iwo — fikirani mitima yawo—mongadi mmene amayi ndi agogo a Timoteo anaikira chitsanzo. Simuyenera kokha kuthera nthaŵi kulankhula ndi ana anu ponena za mkhalidwe ndi kuwalanga iwo koma mufunikiranso kudya zakudya ndi iwo, kuŵerenga ndi iwo, kuseŵera ndi iwo, kuwathandiza iwo kukonzekera kupita kukagona usiku. Nthaŵi yonseyi yowonongedwa ndi ana anu iri yofunika koposa.
5. Perekani chitsanzo cha tate mmodzi amene anasonyeza chiyamikiro kaamba ka mathayo ake a ukholo.
5 Mwamuna wa bizinesi wotchuka wa ku Japan yemwe anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova anazindikira nsonga imeneyi. Pansi pa mutu waukulu wakuti, “Top JNR Exec Quits To Be With Family,” (Nduna Yaikulu ya JNR Ileka Ntchito Kuti Ikakhala ndi Banja) Mainichi Daily News ya pa February 10, 1986, inasimba kuti: “Nduna yaikulu yapamwamba ya Japanese National Railways (JNR) inasankha kuleka ntchito m’malo mwa kupatukana ndi banja lake . . . Akutero Tamura, ‘Ntchito ya wotsogolera wamkulu ingatengedwe ndi wina aliyense. Koma ndiri tate yekha wa ana anga.’” Kodi mumatenga mathayo anu a ukholo mosamalitsa chotero?
Chifukwa Chimene Kuyesetsa Kwapadera Kuli Kofunika Tsopano
6. Kodi nchifukwa ninji chiri chovuta motero kulera ana moyenerera lerolino?
6 Mwinamwake palibe m’mbiri ya munthu pamene chinakhala chovuta kulera ana m’njira imene Mawu a Mulungu amalangizira, “m’maleredwe ndi m’chilangizo cha [Yehova].” (Aefeso 6:4) Chifukwa kaamba ka ichi chiri chakuti tikukhala “m’masiku otsiriza,” ndipo Satana ndi ziwanda zake akupangitsa tsoka lalikulu chifukwa iwo ali okwiya, podziŵa kuti ali kokha ndi kanthaŵi kochepa kowatsalira. (2 Timoteo 3:1-5; Chivumbulutso 12:7-12) Chotero, zoyesayesa za makolo m’kulera ana awo m’njira yaumulungu zikuzimidwa ndi “mpweya” wophiphiritsira pa umene Satana akusonyeza ulamuliro. “Mpweya” umenewo, kapena mzimu wa kudzikonda ndi kusamvera, uli wofalikira monga mpweya weniweni umene timapuma.—Aefeso 2:2.
7, 8. (a) Kodi nchiyani chimene wailesi ya kanema ingabweretse m’nyumba, ndipo komabe nchiyani chimene makolo ambiri amachita? (b) Kodi nchifukwa ninji kugwiritsira ntchito wailesi ya kanema monga mlezi wa mwana kuli kunyalanyaza komvetsa chisoni kwa thayo la ukholo?
7 Wailesi ya kanema, mwapadera, imabweretsa m’nyumba “mzimu wa kudziko” umenewu, “mpweya” waululu umenewu. (1 Akorinto 2:12) M’chenicheni chimene chimawonekera pa wailesi ya kanema kaŵirikaŵiri chimasonkhezeredwa molimba ndi mbali yamphamvu ya mkhalidwe wa chisembwere ndi kugonana kwa ofanana ziwalo m’munda wa zosangulutsa. (Aroma 1:24-32) Ana anu ali okhoterera mwapadera ku kulingalira kosakhala kwaumulungu ndi kunyansa kwa makhalidwe a chisembwere koperekedwa, mongadi mmene mpweya weniweni uliri ku kuipitsa. Koma nchiyani chimene makolo ambiri amachita?
8 Iwo amagwiritsira ntchito wailesi ya kanema monga mlezi wa mwana. “Osati tsopano, wokondedwa. Ndiri wotanganitsidwa. Pita ukapenyerere wailesi ya kanema,” iwo amauza ana awo. Wowulutsa mawu wotchuka wa pa wailesi ya kanema ananena kuti awa ali “mawu olankhulidwa mofala m’nyumba zambiri za ku America.” Ndipo komabe kutumiza ana kukapenyerera chirichonse chimene chingawoneke pa wailesi ya kanema kumafikira, m’chenicheni, ku kuwalekerera iwo. (Miyambo 29:15) Icho chimapanga mbali ya kunyalanyaza koipa kwa thayo la ukholo. Monga mmene wowulutsa mawu ameneyu anadziŵitsira ponena za kulera ana kuti: “Iri yowononga nthaŵi ndipo nkhani ya ukholoyi iri thayo lokulira ndipo silingapatsidwe kwa wina, ndithudi osati kwa wailesi ya kanema.”
9. Kodi ndi kuchokera ku kuipitsa kotani kumeme mwampadera ana amafuna chinjirizo?
9 Ngakhale kuli tero, chifukwa cha chitsenderezo cha nthaŵi m’zimene tikukhala, inu mungakhale woyedzamira, monga mmene analiri ophunzira, ku kuchotsa ana kotero kuti musamalire ku zimene zingalingaliridwe kukhala zinthu zofunika koposa. Koma kodi nchiyani chomwe chiri chofunika koposa kuposa ana anu enieniwo? Miyoyo yawo yauzimu iri pa ngozi! Inu mungakumbukire kuti pamene ngozi ya nyukliya pa Chernobyl inachitika mu Soviet Union mu 1986, ana anachotsedwa kuchokera ku gawo limenelo kuti achinjirizedwe kuchokera ku kuipitsa. Mofananamo, ngati muyenera kuchinjiriza thanzi lauzimu la ana anu, mufunikira kuwachinjiriza iwo kuchoka ku “mpweya” waululu wa dziko, womwe kaŵirikaŵiri umatulutsidwa kuchokera ku wailesi ya kanema.—Miyambo 13:20.
10. Ndi magwero ena ati a “mpweya” waululu amene ali ngozi kwa ana, ndipo ndi chitsanzo cha Baibulo chiti chomwe chimachitira chitsanzo ichi?
10 Pali magwero ena a “mpweya” waululu, ngakhale kuli tero, omwe angawononge mapindu a makhalidwe abwino ndipo angalimbitse maganizo achichepere. Mayanjano oipa ndi ana m’mudzi ndi ku sukulu angaphimbe zowonadi za Baibulo zozikidwa m’mitima yawo yofewayo. (1 Akorinto 15:33) Phunziro lingatengedwe kuchokera kwa mwana wamkazi wam’ng’ono wa Yakobo Dina, yemwe “akanka kukawona akazi akumeneko” ndipo, monga chotulukapo chake, anaipitsidwa ndi mmodzi wa amuna achichepere. (Genesis 34:1, 2) Ana amafunikira kulangizdwa bwino ndi kuphunzitsidwa kuti apewe misampha ya makhalidwe oipa a dziko lomwe liri loipitsidwa mokulira lerolino kuposa mmene linaliri panthaŵiyo.
Nchifukwa Ninji Kuphunzitsa Kuchokera ku Ubwana?
11. (a) Ndi liti pamene kuphunzitsa kwa ukholo kuyenera kuyamba? (b) Ndi zotulukapo zabwino zotani zimene zingayembekezeredwe?
11 Koma ndi liti pamene kuphunzitsa kwa ukholo kuyenera kuyamba? Baibulo limanena kuti Timoteo analandira maphunziro ake “kuyambira ku ubwana.” (2 Timoteo 3:15, NW) Mosangalatsa, breʹphos, liwu la Chigriki pano, kaŵirikaŵiri limagwiritsiridwa ntchito kaamba ka mwana wosabadwa, monga pa Luka 1:41, 44. Pamenepo khanda Yohane ananenedwa kukhala analumpha mkati mwa mimba ya amayi ake. Koma breʹphos akugwiritsiridwanso ntchito ponena za ana obadwa kumene a chiIsrayeli amene miyoyo yawo inawopsyezedwa m’Igupto nthaŵi imene Mose anabadwa. (Machitidwe 7:19, 20) M’nkhani ya Timoteo, liwulo mwachiwonekere likulozera kwa kantchowa chabe, kapena khanda, ndipo osati kokha kwa mwana wamng’ono. Timoteo analandira malangizo kuchokera m’zolembedwa zopatulike kuyambira kuutali umene chikumbukiro chake chikakhoza kufikira, kuchokera ku nthaŵi imene anali kokha khanda. Ndipo ndi zotulukapo zabwino chotani nanga! (Afilipi 2:19-22) Komabe, kodi makanda ongobadwa kumene ndithudi angapindule kuchokera ku kuphunzitsa koyambirira koteroko?
12. (a) Ndi liti pamene makanda angayambe kumwerekera zisindikizo ndi chidziwitso? (b) Ndi liti ndipo ndimotani mmeene makolo ayenera kuyambira kupereka malangizo auzimu kwa ana awo?
12 “Kumodzi kwa kukula kosangalatsa kwambiri m’munda wonse wa sayansi ya malingaliro kuli kumvetsetsa kwathu kwatsopano kwa kuthekera kokulira kwa kuphunzira ka khanda,” anasimba tero Dr. Edward Zigler, profesa wa pa Yale Yuniversite, mu 1984. M’chenicheni, maganizi ya Health inanena kuti: “Ana omwe adakali m’mimba angakhale okhoza kuwona, kumva, kulawa—ndi ‘kumva’ malingaliro, kufufuza kwatsopano kukulingalira tero.” Mwachiwonekere, makolo sangayambe mwamsanga kwambiri kuphunzitsa ana awo. (Deuteronomo 31:12) Iwo angayambe mwakuwasonyeza ana awo zithunzithunzi kuchokera m’mabukhu ndi kugawana nkhani ndi iwo. “Zaka zovuta kwambiri,” akutero Masaru Ibuka, mkonzi wa bukhu la Kindergarten Is Too Late, “ziri zaka kuyambira pa kubadwa kufikira ku zitatu.” Ichi chiri chifukwa chakuti maganizo achicheperewo ali mwapadera ndi kuthekera kwa kusintha, kumwerekera chidziŵitso mopepuka koposa, monga mmene chikusonyezedwera ndi kudziŵa chinenero chatsopano kofulumira kwa khanda. Profesa m’kuphunzira koyambirira kwa ubwana pa Yuniversite ya ku New York anafikira kunena kuti “makolo ayenera kuyamba kuphunzitsa ana kuŵerenga nthaŵi imene awabweretsa iwo kunyumba kuchokera ku chipatala”!
13. Nchiyani chimene chimachitira chitsanzo kuthekera kwa makanda kuphunzira?
13 Mayi wochokera ku Canada akulemba ponena za kuthekera kwa kuphunzira kwa mwana wake: “Tsiku lina ndinali kuŵerenga nkhani kuchokera mu Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kwa mwana wanga wamwamuna wa zaka zinayi ndi theka, Shaun. Pamene ndinapuma pa nsonga imodzi, ndinapeza ku kudabwitsidwa kwanga kuti iye anayamba kupitiriza nkhaniyo, liwu ndi liwu, monga mmene imawonekera mu Bukhu la Nkhani za Baibulo. . . . Ndinayesera ina ndipo kenaka inanso, ndipo iye anali ataloweza zonse. . . . Iye m’chenicheni waloweza, liwu ndi liwu, nkhani 33 zoyambirira, kuphatikizapo maina ovuta a malo ndi anthu.”a
14. (a) Ndi ndani omwe sali odabwitsidwa ndi zokwaniritsa za makanda? (b) Nchiyani chimene chiyenera kukhala chonulirapo cha makolo Achikristu? (c) Kodi ana ayenera kufunikira kukonzekeretsedwa kaamba ka chiyani, ndipo nchifukwa ninji?
14 Awo ozoloŵerana bwino ndi mphamvu yothekera ya kuphunzira ya makanda sali odabwitsidwa ndi nkhani zoterozo. “Dziko likanakhala lodzala ndi anzeru a akulu onga Einstein, Shakespeare, Beethoven ndi Leonardo da Vinci ngati tikanaphunzitsa makanda m’malo mwa ana,” akunena tero Dr. Glen Doman, mtsogoleri wa The Institutes for the Achievement of Human Potential. Ndithudi, chonulirapo cha makolo Achikristu, sichiri kutulutsa anzeru a akulu koma kufikira mitima ya ana awo kotero kuti anawo asadzapatuke kuchoka ku kutumikira Mulungu. (Miyambo 22:6) Zoyesayesa zoterozo zimafunikira kupangidwa pasadakhale mwanayo asanaloŵe sukulu, ndi cholinga cha kumukonzekeretsa iye kaamba ka ziyeso zimene adzakumana nazo kumeneko. Sukulu ya nasale kapena maprogramu a chisamaliro cha tsiku, mwachitsanzo, amawonetsa mapwando a tsiku la kubadwa ndi matchuthi omwe angakhale osangalatsa kwa ana. Chotero mwanayo afunikira kumvetsetsa chifukwa chimene atumiki a Yehova satengeramo mbali. Kupanda apo iye angakule ndi kudana ndi chipembedzo cha makolo ake.
Mmene Mungafikire Mtima wa Mwana
15, 16. Nchiyani chimene makolo angagwiritsire ntchito kuwathandiza iwo kufikira mtima wa mwana wawo, ndipo ndimotani mmene makonzedwe amenewa angagwiritsidwire ntchito mokhutiritsa?
15 Kuthandiza makolo kufikira mtima wa mwana wawo, zofalitsidwa zonga ngati kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuluyo zaperekedwa ndi Mboni za Yehova. Bukhuli limalankhula ponena za mapwando ndi mmene “angakhalire osangalatsa kwambiri” m’mutu wake “Anthu Amene Anasunga Masiku a Kubadwa.” Komabe mutuwo ukulongosola kuti mapwando aŵiri okha a masiku a kubadwa otchulidwa m’Baibulo anakondwereredwa ndi akunja, omwe sanali alambiri a Yehova, ndipo kuti pa phwando lirilonse ‘mutu wa winawake unadulidwa.’ (Marko 6:17-29; Genesis 40:20-22) Ndimotani mmene mungagwiritsire ntchito chidziŵitso chimenechi kufikira mtima wa mwana wanu?
16 Inu mungagwiritsire ntchito njira yophunzitsira yosangalatsa ya bukhu la Mphunzitsi Wamkuluyo mwakunena kuti: “Tsopano, ife tikudziŵa kuti chirichonse chimene chiri m’Baibulo chiri mmenemo kaamba ka chifukwa.” Kenaka funsani: “Chotero, nchiyani chimene munganene kuti Mulungu akutiuza ife ponena za mapwando a kusunga tsiku la kubadwa?” Mwana wanu mwakutero amathandizidwa kulingalira pa nkhaniyo ndi kufikira mapeto abwino. Pambali pa bukhu la Mphunzitsi Wamkuluyo, mabukhu ena aperekedwa kaamba ka kugwiritsira ntchito kwa makolo, kuphatikizapo Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndi mipambo ya “Moyo ndi Uminisitala za Yesu” zomwe zakhala zikuwoneka m’kope lirilonse la Nsanja ya Olonda kuyambira October 1985. Kodi mwakhala mukugwiritsira ntchito nkhanizi m’kuphunzitsa ana anu limodzinso ndi inu eni?
17. Ndi malingaliro okhoza kugwira ntchito otani amene aperekedwa pano kwa makolo?
17 Ndi mwana wanu, mufunikira kupita mobwerezabwereza mu nsonga zomwe zimakwaniritsa nkhani ndi mikhalidwe yomwe amayang’anizana nayo ku sukulu. Lolani mwana wanu kudziŵa kuti inu nonse aŵiri muli oŵerengera kwa Yehova. (Aroma 14:12) Wunikirani zinthu zabwino zimene Yehova amachita kaamba ka ife, mwakutero kusonkhezera mtima waung’ono wa mwana wanu kufuna kukondweretsa Yehova. (Machitidwe 14:17) Pangani magawo ophunzira kukhala nthaŵi yachimwemwe. Ana amakonda nkhani, chotero ndithudi gwirirani ntchito pa kuzika malangizo m’njira yophiphiritsira yomwe idzafikira mtima wa mwana wanu. Mabanja ambiri amaphonya mwaŵi wosangalatsa kaamba ka magawo oterowo mwakulephera kukhala ndi chakudya panthaŵi imodzi mokhazikika. Kodi mumadyera pamodzi monga banja? Ngati ayi, kodi mungawongolere mkhalidwewo? —Yerekezani ndi Machitidwe 2:42, 46, 47.
18, 19. (a) Ndimotani mmene makolo ayenera kundandalikira kuphunzitsa kwa ana awo, ndipo nchiyani chomwe sichingagomezeredwe mopambanitsa? (b) Ndi mbali ziti za chitsanzo chamakono cha kuphunzitsa kwa ukholo chimene chakusangalatsani, ndipo nchiyani chimene mukukhulupirira kuti chingatulukepo ngati kholo lagwiritsira ntchito izo?
18 Gawo lophunzira liyenera kusinthidwira ku msinku wa mwanayo. Chotero ndi khanda, limene nthaŵi yake yopereka chisamaliro iri ya malire, khalani ndi magawo angapo a afupi tsiku liri lonse. Kenaka, mopita patsogolo, atalikitseni iwo ndi kufutukula za mkati mwake. Kufunika kwa kukhala ndi nyengo zokhazikika kaamba ka kuphunzitsa ana anu sikungagogomezeredwe mopambanitsa. (Genesis 18:19; Deuteronomo 11:18-21) Tate wina, amene tsopano ali m’zaka zake za makumi asanu ndi aŵiri, anakhazikitsa chitsanzo chabwino m’kulera mwana wake wamwamuna, yemwe tsopano ali mkulu Wachikristu. Zaka zingapo zapitazo iye analongosola programu yake, akumanena kuti:
19 “Pamene mnyamata wathu anali chifupifupi chaka chimodzi ndinayamba kumuuza iye nkhani za Baibulo asanapite kogona, zolongosoledwa m’njira yokulitsidwa, yowoneka bwino kupanga chisonyezero chowonekera. Mwamsanga pemene iye anayamba kulankhula m’chaka chake chachiŵiri tinkagwada pambali pa kama yake ndipo ndinampangitsa iye kubwereza pambuyo panga, mawu ndi mawu, ‘Pemphero la Ambuye.’. . . Pamene iye anali ndi zaka zitatu ndinayamba kukhala ndi phunziro la Baibulo lokhazikika ndi iye . . . Iye akatsatira m’bukhu lake, mwapakamwa akumabwereza mawuwo pambuyo panga. Iye chotero anafikira kudziŵa kutchula mawu bwino lomwe ndipo anaphunzira kutchula momvekera bwino nagakhale mawu a akulu. . . . Kuti tithandize kupanga zowonadi za Baibulo kulowerera mozama mu mtima mwake, pamene anali ndi zaka zitatu tinayamba kumpangitsa iye kuloweza malemba a Baibulo opepuka. Panthaŵi imene analoŵa sukulu ya nasale anadziŵa chifupifupi malemba makumi atatu, ndipo September yapita pamene anayamba kalasi yoyamba iye anali ataloweza malemba makumi asanu ndi aŵiri. . . . Mnyamata wathu asanipite kukagona ndimampangitsa iye kubwereza ena a malemba ake. Mofananamo pamene iye awuka m’mawa iye kaŵirikaŵiri amanena malemba angapo a Baibulo monga mbali ya moni kaamba ka tsikulo.”
20. Nchiyani chomwe chiyenera kuphatikizidwa m’programu yophunzitsa, ndipo ndimotani mmene mwana angasangalalire ndi utumiki wa kunyumba ndi nyumba?
20 Programu yopita patsogolo yophunzitsa yoteroyo, kuphatikizapo chitsanzo choyenera cha ukholo ndi kugwiritsira ntchito kwa chilango chokhazikika, kudzapatsa mwana wanu chiyambi chabwino m’moyo kaamba ka chimene adzakhala woyamikira kwanthaŵi yonse. (Miyambo 22:15; 23:13, 14) Mbali yofunika koposa ya programuyi iyenera kukhala kuphunzitsa mu utumiki wa poyera kuyambira pa msinkhu wauchichepere. Chipangeni icho kukhala chokumana nacho chosangalatsa mwa kukonzekeretsa mwana wanu kukhala ndi kugawanamo kwatanthauzo. Tate wotchulidwa pamwambayo mowonjezereka anachitira ndemanga ponena za mwana wake wamwamuna: “Kuthekera kwake kwa kugwira malemba kumampangitsa iye kukhala wokhutiritsa mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba, popeza eninyumba ambiri amadabwitsidwa ndipo sangathe kukana chogawira cha magazini a Baibulo chimene iye amapereka. Iye wagawana mu utumiki Wachikristu umenewu kuyambira pamene anali ndi zaka zitatu zakubadwa, ndipo tsopano ali [pa msinkhu wa zaka 6] kaŵirikaŵiri wokhutiritsa kwambiri m’kugawira mabukhu a Baibulo ndi anthu kuposa mkazi wanga ndi ine.”—Galamukani!, January 22, 1965, masamba 3-4, Chingelezi.
21. (a) Kodi ndi mphatso yaikulu koposa yotani imene makolo angasiye kaamba ka ana awo? (b) Kodi ndi uphungu wotani umene waperekedwa kwa makolo, ndipo nchiyani chimene makolo onse okhala ndi ana ang’ono ayenera kukhala nacho?
21 Zowonadi, makolo Achikristu ali ndi cholowa chozizwitsa kwambiri, chidziŵitso cha Yehova, chofunikira kusiira ana awo ndipo limodzi nacho ziyembekezo za moyo wosatha, mtendere ndi chimwemwe m’dziko latsopano la ulemerero. (Miyambo 3:1-6, 13-18; 13:22) Pamwamba pa zina zonsezi, mu mtima wa wachichepere wanu mangirirani chidaliro m’kutsimikizirika kwa mtsogolo mokulira, limodzi ndi chikhumbo cha kutumikira Yehova. Pangani kulambira kowona kukhala chokumana nacho chachibadwa ndi chachimwemwe kaamba ka iwo. (1 Timoteo 1:11) Zikani chikhulupiriro mwa Yehova kuyambira ku ubwana. Ndipo musayesere, ayi, musayesere nkhomwe, kunyalanyaza magawo ophunzira okhazikika ndi iwo! Zipatseni izi malo anu oyamba apamwamba koposa, mopita patsogolo kumasanthulanso chidziŵitso chimene mwana wanu afunikira ndi mmene mungafikire bwino mitima yawo ndi icho. Muli otanganitsidwa ndipo pansi pa chididikizo; Satana ndi dziko lake amawona ku icho. Koma kumbukirani chitsanzo cha Yesu! Musakhale otanganitsidwa koposa kukhala ndi phunziro lokhazikika ndi ana anu!
[Mawu a M’munsi]
a Kale kwambiri iye asanyambe kuŵerenga, iye anali ataphunzira nkhani zimenezo mwakungomvetsera ku makaseti ojambulidwa a bukhulo.
Kodi Mukayankha Motani?
□ Ndi umboni wa Baibulo wotani umene umasonyeza kuti makolo ayenera kupereka malo oyambirira ku zosowa za ana awo?
□ Kodi nchifukwa ninji zoyesayesa zapadera ndi makolo tsopano zifunikira m’kuchinjiriza ana awo?
□ Nchifukwa ninji chiri chofunika koposa motero kuti ana aphunzitsidwe kuyambira ku ubwana
□ Kodi ndi ati omwe ali malingaliro ena ogwira ntchito kaamba ka makolo m’kufikira mtima wa mwana wawo?
□ Nchiyani chimene makolo Achikristu sayenera kunyalanyaza?
[Chithunzi patsamba 12]
Kuphunzitsa kwa ukholo sikungayambe mwamsanga kwambiri