Miyambo
29 Munthu amene amaumitsa khosi lake* pambuyo podzudzulidwa mobwerezabwereza+
Adzathyoledwa mwadzidzidzi ndipo sadzachira.+
3 Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa bambo ake,+
Koma woyenda ndi mahule amawononga chuma chake.+
6 Tchimo la munthu woipa limamutchera msampha,+
Koma munthu wolungama amafuula mokondwera ndipo amasangalala.+
7 Wolungama amafunitsitsa kuti anthu osauka aziweruzidwa mwachilungamo,+
Koma woipa safuna kuchita zimenezi.+
9 Munthu wanzeru akayamba kukangana ndi chitsiru,
Pamangokhala phokoso ndi kunyozana, ndipo munthu wanzeruyo sapindula chilichonse.+
10 Anthu okonda kukhetsa magazi amadana ndi munthu aliyense wosalakwa,+
Ndipo amafuna kuchotsa moyo wa anthu owongoka mtima.*
11 Munthu wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse,+
Koma wanzeru amakhala wodekha ndipo amalamulira mkwiyo wake.+
13 Munthu wosauka komanso munthu wopondereza ena ndi ofanana* pa chinthu chimodzi ichi:
Yehova amachititsa kuti maso a onsewa aziona kuwala.*
15 Chikwapu* komanso kudzudzula nʼzimene zimapereka nzeru,+
Koma mwana womulekerera amachititsa manyazi mayi ake.
18 Ngati anthu sakutsogoleredwa ndi Mulungu, amachita zinthu motayirira,+
Koma osangalala ndi amene amatsatira chilamulo.+
20 Kodi waona munthu amene amafulumira kulankhula asanaganize?+
Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu kuposa munthu ameneyu.+
21 Ngati munthu akusasatitsa kapolo wake kuyambira ali mwana,
Mʼtsogolo adzakhala wosayamika.
22 Munthu wosachedwa kukwiya amayambitsa mkangano.+
Aliyense amene sachedwa kupsa mtima amakhala ndi machimo ambiri.+
24 Amene amathandiza munthu wakuba amadzibweretsera mavuto.
Iye angamve kuitana kuti akapereke umboni,* koma osakanena chilichonse.+