Pitirizani Kuyenda Mopita Patsogolo M’njira ya Kachitidwe Yadongosolo
1 Mtumwi Paulo anali ndi chikondi chapadera kulinga ku mpingo wa mu Filipi, umene anathandizira kuupanga. Iye anali woyamikira kaamba ka zopereka zawo zakuthupi zosonyeza kukoma mtima ndipo anawatchula kukhala achitsanzo chabwino.—2 Akor. 8:1-6.
2 Kalata ya Paulo kwa Afilipi inasonkhezeredwa ndi chikondi chozama. Buku la Insight, Voliyumu 2, tsamba 631, limanena kuti: “M’kalata yonseyo iye akulimbikitsa mpingo wa Afilipi kupitiriza m’njira yawo yabwino—kumafunafuna kuzindikira kokulirapo ndi kugwiritsa motsimikiza Mawu a moyo, chikhulupiriro cholimbirapo, ndi chiyembakezo m’mphotho ilinkudza.” Iwo analabadira mwachimwemwe, akumalimbitsa chomangira chachikondi pakati pa iwo eni ndi mtumwiyo. Mawu a Paulo ali ndi tanthauzo lapadera kwa ife lerolino, akumatipatsa chifukwa chabwino cha kusinkhasinkha mosamalitsa pa chilangizo chakecho, makamaka zimene zanenedwa pa Afilipi 3:15-17.
3 Mkhalidwe Wokhwima wa Maganizo N’ngofunika: Pa Afilipi 3:15, Paulo analemba monga mwamuna wa zaka zambiri za chidziŵitso. Iye anazindikira kupita patsogolo kwauzimu kwa Afilipi, akumawathokoza kukhala Akristu okhwima a mkhalidwe wa maganizo woyenera. Malinga ngati mkhalidwe wawo wa maganizo unasonyeza kudzichepetsa ndi chiyamikiro zosonyezedwa ndi Yesu, iwo akapitiriza kukhala “osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chirema . . . , [akugwiritsa, NW] mawu a moyo.” (Afil. 2:15, 16) Pamene tiŵerenga mawu a Paulo, tiyenera kumva kuti iye akulankhula kwa ife. Chifukwa chake timakhumba mwakhama kukhala ndi mkhalidwe wa maganizo wofanana ndi umene Yesu anali nawo ndi kumasonyeza kuyamikira mathayo athu modzichepetsa. Tiyenera kumfikira Yehova m’pemphero mopitirizabe, tikumapempha chithandizo pankhani imeneyi ndi zinanso.—Afil. 4:6, 7.
4 Monga momwe Afilipi 3:16 akusonyezera, tonsefe tiyenera kuyesayesa kupita patsogolo. Liwu lakuti “kupita patsogolo” limatanthauza “kuyenda kutsogolo, kupanga kupita patsogolo.” Anthu opita patsogolo “amakondweretsedwa ndi maganizo atsopano, zotumbidwa zatsopano, kapena mipata yatsopano.” Paulo anafuna kuti Afilipiwo amvetsetse kuti Chikristu sichimaima malo amodzi ndipo awo ochichirikiza ayenera kupitabe patsogolo. Mzimu wawo wa kupita patsogolo ukasonyezedwa mwa kufunitsitsa kwawo kudzipenda okha, kuvomereza zifooko zawo, ndi kukalimira mipata ya kuchita zowonjezereka kapena kuwongolera mkhalidwe wa zimene ankachita. Lerolino gulu la Yehova la padziko lapansi likuyenda mopitabe patsogolo, likumafutukula ntchito zake nthaŵi zonse ndi kumvetsetsa kwake Mawu a Mulungu. Aliyense wa ife ayenera kuyendera limodzi nalo, akumatenga mwaŵi wa kugwiritsira ntchito makonzedwe ake onse ndi kukhala ndi phande lokwanira m’ntchito yake.
5 Kupita Patsogolo Kumafuna Njira ya Kachitidwe Yadongosolo: Paulo anapitiriza mwa kulimbikitsa abale ake ‘kuyendabe mwadongosolo m’njira ya kachitidwe imodzimodzi.’ (Afil. 3:16, NW) Kukhala adongosolo kumafuna kuti tiike anthu kapena zinthu m’malo ake oyenera kulinga kwa wina ndi mnzake ndi kukhala odzisungira bwino. Akristuwo mu Filipi anadzisungira m’malo awo oyenera, akumakhala pafupi ndi gulu la Yehova ndi wina ndi mnzake. Miyoyo yawo inalamuliridwa ndi lamulo la chikondi. (Yoh. 15:17; Afil. 2:1, 2) Paulo anawalimbikitsa kukhala ndi ‘mayendedwe oyenera uthenga wabwino.’ (Afil. 1:27) Kufunika kwa dongosolo ndi mkhalidwe wabwino kuli kofunikira kwambiri kwa Akristu lerolino.
6 Njira ya kachitidwe ndiyo kachitidwe ka chizoloŵezi ka mchitidwe wokhazikika. Motero ili yofanana kwambiri ndi njira ya chizoloŵezi yochitira zinthu. Kukhala ndi njira ya kachitidwe kukhoza kutithandiza chifukwa chakuti sitidzafunikira kuima kaye ndi kusinkhasinkha popanga zosankha za sitepe lathu lotsatira—tinakhazikitsa kale njira imene timatsatira mosonkhezeredwa ndi mphamvu ya chizoloŵezi.
7 Njira ya kachitidwe yadongosolo ya teokratiki ili ndi zizoloŵezi ndi machitidwe amene ali abwino, opindulitsa, aumulungu—ndi cholinga cha kudzilimbikitsa mwauzimu, kuthandiza ena, ndipo, ngati kuli kotheka, kuchita zowonjezereka mu utumiki wa Yehova. Chipambano cha kupeza zonulirapo zimenezi chimafuna kukhazikitsa ndi kusunga njira ya kachitidwe imene imaphatikizapo phunziro laumwini, kupezeka pamisonkhano mokhazikika, ndi kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira.
8 Zofunika Zophatikizidwa mu Njira ya Kachitidwe Yadongosolo: Chimodzi cha zofunika ndicho “chidziŵitso cholongosoka ndi kuzindikira kokwanira.” (Afil. 1:9, NW) Phunziro laumwini limazamitsa chikhulupiriro chathu, limakulitsa chiyamikiro chathu cha choonadi, ndipo limatisonkhezera ku ntchito zabwino. Komabe, zakhala zovuta kwa ena kuti akhale okhazikika m’zizoloŵezi za phunziro lawo. Chimodzi cha zifukwa zazikulu zoperekedwa ndicho kusoŵa nthaŵi.
9 Kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kuli ndi mapindu ambiri kwambiri. Uphungu wake ‘ngopindulitsa’ m’njira iliyonse. (2 Tim. 3:16, 17) Kodi tingapeze motani nthaŵi ya phunziro la Baibulo m’njira yathu ya kachitidwe ya tsiku ndi tsiku? Ena apeza kuti akhoza kuuka mofulumirapo ndi mphindi zingapo mmaŵa uliwonse, pamene maganizo awo ali ogalamuka. Ena amapeza kuti amachita bwinopo pamene aŵerenga kwa mphindi zingapo asanagone usiku. Akazi omwe amakhala panyumba usana angakhale okhoza kupatula nthaŵi pang’ono masana pamene ena asanabwere kuchokera kuntchito kapena kusukulu. Kuwonjezera pa kuŵerenga Baibulo kokhazikika, ena aphatikizapo kuŵerenga buku la Proclaimers pa njira yawo ya kachitidwe ya mlungu ndi mlungu ya phunziro.
10 Pamene tikhazikitsa zizoloŵezi zatsopano, pamakhala kuthekera kwakukulu kwakuti zidzawombana ndi zizoloŵezi zathu zakale. Mwinamwake kumbuyoku tinkalola zinthu zosafunika kwenikweni kutidyera nthaŵi. Kuleka njira imeneyi sikuli kwapafupi. Palibe aliyense amene adzakakamiza pa ife zizoloŵezi zochitira phunziro; ndiponso sitidzapemphedwa kupereka lipoti la mmene tikuchitira pambali imeneyi. Kukhazikika kwa zizoloŵezi za phunziro lathu kudzadalira kwakukulukulu pa kuyamikira kwathu “zinthu zofunika kwambiri” ndi kufunitsitsa kwathu kuwombola “nthaŵi yoyenera” kuti tipindule nazo.—Afil. 1:10, NW; Aef. 5:16, NW.
11 Misonkhano Yachikristu imachita mbali yaikulu m’kupita kwathu patsogolo kwauzimu, ikumapereka chilangizo ndi chilimbikitso chofunikira. Motero, kupezeka pamisonkhano kuli chofunika china cha njira yathu ya kachitidwe. Paulo anagogomezera kufunika kwa chimenechi. Iko sikuli chosankha chodalira pa zokonda za munthu.—Aheb. 10:24, 25.
12 Kodi tingasonyeze motani kukhala adongosolo polinganiza ndandanda yathu ya zochita ya mlungu ndi mlungu? Ena amalinganiza nthaŵi zakutizakuti kukhala zosamalira zinthu zaumwini ndiyeno kuyesa kukanikizira misonkhano m’mipata iliyonse yotsalapo, koma ziyenera kukhala mwa njira inayo. Misonkhano yathu ya mlungu ndi mlungu iyenera kupatsidwa chisamaliro choyamba, ndipo zochita zina zikumalinganizidwa pambuyo pake.
13 Kupezeka pamisonkhano mokhazikika kumafuna kulinganiza kwabwino ndi kugwirizana kwa banja. Pamasiku a mkati mwa mlungu ambiri a ife timakhala otanganitsidwa ndi zochita kwakuti kaŵirikaŵiri timakhala opanda nthaŵi yeniyeni. Zimenezi zimatanthauza kuti, ngati kuli kotheka, chakudya chamadzulo chiyenera kuikidwa panthaŵi yofulumira yoyenera kotero kuti banja likhale ndi nthaŵi yokwanira ya kudya, kukonzekera, ndi kufika pamsonkhano usanayambe. Mwa kutero, ziŵalo za banja zingagwirizane m’njira zosiyanasiyana.
14 Utumiki wakumunda wokhazikika uli wosapeŵeka ngati titi tipitirizebe kuyenda m’njira ya kachitidwe yadongosolo. Tonsefe timazindikira bwino lomwe thayo lathu lalikulu la kulalikira uthenga wa Ufumu. Chimenecho nchimene chimatipangitsa kukhala Mboni za Yehova. (Yes. 43:10) Popeza kuti ili ntchito yofulumira ndi yopindulitsa kwambiri imene ikuchitidwa lerolino, sitiyenera konse kuiona monga ngati mbali yaing’ono chabe ya njira yathu ya kachitidwe. Zili monga momwe Paulo analangizira kuti: “Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.”—Aheb. 13:15.
15 Pamene tilinganiza zochita zathu za mlungu uliwonse, nthaŵi zakutizakuti ziyenera kupatulidwa kaamba ka utumiki wakumunda. Mwachionekere mpingo umalinganiza misonkhano yokonzekera utumiki ingapo mlungu uliwonse, ndipo timangofunikira kusankha umene tingapezekepo. Kukakhala bwino kukalimira kukhala ndi phande m’mbali iliyonse ya utumiki, monga ngati kuchita ntchito ya kunyumba ndi nyumba ndi magazini ndi mabuku ena, kupanga maulendo obwereza, ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo. Tikhoza kulinganiza ngakhale pasadakhale kuchita umboni wamwamwaŵi mwa kunyamula mabuku ndi kukhala a maso kuona mipata yoyambira makambitsirano. Popeza kuti kaŵirikaŵiri timapita limodzi ndi ena, tiyenera kufunsira za ndandanda yawo kotero kuti tipange makonzedwe omwe adzayenerera tonse.
16 Njira yathu ya kachitidwe ya kulalikira iyenera kutsatiridwa mosasamala kanthu za mphwayi ya m’gawo. Timadziŵiratu kuti oŵerengeka okha ndiwo adzavomereza. (Mat. 13:15; 24:9) Ezekieli anatumidwa kukalalikira kwa anthu ‘opanduka, achipongwe, ndi ouma mtima.’ Yehova adalonjeza kuthandiza Ezekieli mwa ‘kulimbitsa mutu wake utsutsane nayo mitu yawo,’ ndiko, ‘kuulimbitsa kuposa mwala wolimbitsitsa.’ (Ezek. 2:3, 4; 3:7-9) Motero, njira ya kachitidwe yokhazikika imafuna kulimbikira.
17 Zitsanzo Zabwino Zoti Titsanzire: Ambirife timachita bwinopo mu utumiki wakumunda ngati pali wina wotsogolera. Paulo ndi anzake anapereka chitsanzo chabwino, ndipo anasonkhezera ena kumtsanzira. (Afil. 3:17) Njira yake ya kachitidwe inaphatikizapo mbali zonse zofunika kuti akhalebe wolimba mwauzimu.
18 Lerolinonso, tili odalitsidwa mwa kukhala ndi zitsanzo zabwino. Pa Ahebri 13:7, Paulo analimbikitsa kuti: “Kumbukirani atsogoleri anu, . . . ndipo poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe awo mutsanze chikhulupiriro chawo.” Ndithudi, Yesu ndiye Wotipatsa Chitsanzo, koma tikhoza kutsanzira chikhulupiriro chosonyezedwa ndi awo otsogolera. Mofanana ndi Paulo, akulu ayenera kuzindikira kufunika kwa kukhala zitsanzo zabwino kwa ena. Pamene kuli kwakuti mikhalidwe yawo yaumwini ingasiyane, aliyense ayenera kukhala wokhoza kusonyeza kuti akusunga njira ya kachitidwe yadongosolo m’kuika zinthu za Ufumu pamalo oyamba. Ngakhale kuti akulu ali ndi mathayo antchito ndi a banja, iwo ayenera kukhala ndi zizoloŵezi zokhazikika bwino za phunziro laumwini, kupezeka pamisonkhano, ndi kutsogolera mu utumiki wakumunda. Ngati akulu asonyeza umboni wakuti ‘akuweruza bwino nyumba zawo,’ onse mumpingo adzalimbikitsidwa kupitirizabe kuyenda m’njira ya kachitidwe yadongosolo.—1 Tim. 3:4, 5.
19 Zonulirapo za Chaka Chautumiki Chatsopano: Chiyambi cha chaka chautumiki chatsopano chili nthaŵi yoyenera kusinkhasinkha pa njira yathu ya kachitidwe. Kodi kupenda ntchito zathu za chaka chatha kumasonyezanji? Kodi tinali okhoza kusunga, kapena mwina kukulitsa, mlingo wa ntchito zathu? Mwinamwake tinali kuchita bwino kwenikweni m’phunziro lathu laumwini. Mwina tinapezeka pamisonkhano mokhazikika kapena tinawonjezera utumiki wathu wakumunda mwa kulembetsa monga apainiya othandiza. Mwinamwake tikhoza kutchula machitidwe akutiakuti a kukoma mtima Kwachikristu omwe tinachitira ena mumpingo wathu kapena m’banja lathu. Ngati zili motero, tingasangalale kuti tayenda m’njira imene imakondweretsa Mulungu, ndipo tili ndi chifukwa chabwino chakuti ‘tichulukire koposa momwemo.’—1 Ates. 4:1.
20 Bwanji ngati njira yathu ya kachitidwe inali yosakhazikika kwenikweni kapena ya apa ndi apo? Kodi tinayambukiridwa motani mwauzimu? Kodi kupita kwathu patsogolo kunadodometsedwa pa chifukwa chinachake? Kuwongolera kumayamba ndi pempho la chithandizo cha Yehova. (Afil. 4:6, 13) Kambitsiranani zosoŵa zanu ndi enawo m’banja, mukumapempha chithandizo chawo pakusintha mbali zina za njira yanu ya kachitidwe. Ngati zikukhalirani zovuta, pemphani akulu kuti akuthandizeni. Ngati tipanga kuyesayesa kwakhama ndi kulabadira chitsogozo cha Yehova, tingakhale otsimikiza kuti tidzapeŵa ‘kukhala aulesi kapena opanda zipatso.’—2 Pet. 1:5-8.
21 Kuyenda m’njira ya kachitidwe yolondola kumatsogolera ku madalitso amene amapangitsa zoyesayesa zanu kukhala zaphindu. Pamene mukutsimikiza mtima kuyendabe mopita patsogolo m’njira ya kachitidwe yolondola, “musakhale aulesi m’machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani [Yehova, NW].” (Aroma 12:11)—Kuti mupeze mafotokozedwe ambiri a nkhaniyi, onani Nsanja ya Olonda ya September 15, 1985, masamba 13-17.