Kodi Mumasonyeza Mzimu Wotani?
1 Paulo anamaliza kalata yake yopita ku mpingo wa ku Filipi ndi chilimbikitso chakuti: “Chisomo cha Ambuye Yesu Kristu chikhale ndi mzimu wanu.” (Afil. 4:23) Iye anawayamikira kaamba ka chikondwerero chawo chenicheni cha kulalikira mbiri yabwino limodzi ndi nkhaŵa yawo yachikondi kaamba ka ubwino wa wina ndi mnzake.—Afil. 1:3-5; 4:15, 16.
2 Tiyenera kukhala ndi chikhumbo cha kusonyeza mzimu umodzimodziwo mu mpingo wathu. Pamene onse asonyeza changu, kukoma mtima, ndi kuchereza, zimenezi zimakulitsa mzimu umene umaonekera kwa oona. Mzimu wabwino ndi wachikondi umadzetsa umodzi ndi kupita patsogolo kwauzimu. (1 Akor. 1:10) Mzimu wa kusakondwa umalefula ndi kuchititsa munthu kukhala wa mitima iŵiri.—Chiv. 3:15, 16.
3 Akulu Tsogolerani: Akulu ali ndi thayo la kusunga mzimu wabwino ndi wolimbikitsa pakati pawo ndi mumpingo mwawo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mpingo ungasonkhezeredwe ndi maganizo awo ndi khalidwe lawo. Timayamikira pokhala ndi akulu achangu mu utumiki wakumunda, amene amatipatsa moni ndi kumwetulira ndi liwu lokoma mtima, ndi amene ali olimbikitsa ndi omangirira mu uphungu wawo, kaya uperekedwa mwamseri kapena papulatifomu.—Aheb. 13:7.
4 Ndithudi, tonsefe tiyenera kuchita mbali yathu kuchititsa mpingo kukhala waubwenzi, wochereza, wachangu, ndi wa maganizo auzimu. Mmodzi ndi mmodzi, tingasonyeze kukoma mtima ndi chikondi poyanjana ndi ena. (1 Akor. 16:14) Sipayenera kukhala kulekanitsa msinkhu, fuko, maphunziro, kapena mkhalidwe wa chuma pakati pa ife. (Yerekezerani ndi Aefeso 2:21.) Chifukwa cha chiyembekezo chathu, tikhoza kusonyeza mzimu wa chisangalalo, kuchereza kooloŵa manja, ndi changu mu utumiki.—Aroma 12:13; Akol. 3:22, 23.
5 Tiyenera kuchititsa onse omwe amayanjana nafe, kuphatikizapo atsopano, kumva kuti ali olandiridwa ndi kuona chikondi ndi kudzipereka kwa ubalewo. Mwa utumiki wathu ndi mwa kusonyeza mikhalidwe yabwino Yachikristu, timapereka umboni wakuti mpingowo uli “mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” (1 Tim. 3:15) Timakhalanso ndi chisungiko chauzimu mwa “mtendere wa Mulungu” umene umatetezera mitima yathu ndi mphamvu ya maganizo. (Afil. 4:6, 7) Lekani kuti tonsefe tiyeseyesetu kusonyeza mzimu umene udzatipatsadi chisomo cha Yehova mwa Ambuye Yesu Kristu.—2 Tim. 4:22.