“Pitirizani Kusunga Amuna Oterowo Okondedwa”
“Muzindikire oterowo.”—1 AKORINTO 16:18.
1. Ndi amuna a mtundu wotani amene mtumwi Paulo anawasunga okondeka mwachindunji, ndipo nchiyani chimene iye analemba ponena za Mkristu mmodzi woteroyo?
MTUNDU wa amuna amene mtumwi Paulo anawasunga okondedwa mwachindunji anali awo omwe anali ofunitsitsa kuwononga mphamvu zawo mosasinkhasinkha kaamba ka Yehova ndi abale awo. Kwa wogwira naye ntchito mmodzi woteroyo, Paulo analemba kuti: “Mumlandire mwa Ambuye ndi chimwemwe chonse; [ndi kupitiriza kusunga amuna oterowo okondedwa, NW] anafikira pafupi imfa, akumawunikira moyo wake ku ngozi.”—Afilipi 2:29, 30.
2. Kodi ndi kwandani kumene timayenerera kulingalira kwapadera, ndipo nchifukwa ninji?
2 Lerolino, m’mipingo yoposa 55,000 ya Mboni za Yehova, muli amuna Achikristu abwino ambiri amene tifunikira kuyamikira mwachindunji chifukwa cha ntchito yawo yamphamvu pakati pa abale awo. Kusonyeza kuti tifunikira kusunga amuna oterowo kukhala okondeka, Paulo analongosola kuti: “Koma abale, tikupemphani, dziŵani iwo akugwira ntchito mwamphamvu mwa inu nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu; ndipo muwachitire ulemu wopasatu mwa chikondi chifukwa cha ntchito yawo. Khalani mumtendere mwa inu nokha.”—1 Atesalonika 5:12, 13.
3. (a) Nchiyani chimene chidzatithandiza kukhala a mtendere kwa wina ndi mnzake? (b) Ndi m’mikhalidwe yotani mmene akulu ayenera kukhazikitsa chitsanzo?
3 Chiyamikiro choyenera kaamba ka abale ndi alongo athu onse, ndipo makamaka kaamba ka akulu ogwira ntchito mwamphamvu, chiri mosakaikira nsonga yofunika m’kukhala kwathu mwa mtendere mkati mwa mipingo yathu. Mu ichi, monga m’mbali zonse za kukhala ndi moyo kwa Chikristu, akulu ayenera kukhala “chitsanzo ku gulu.” (1 Petro 5:2, 3) Ngakhale kuli tero, pamene kuli kwakuti akulu angayembekezere kuyamikiridwa moyenera ndi abale kaamba ka ntchito yawo yamphamvu, iwo ayeneranso kusonyeza chitsanzo m’kusonyeza kulingalirapo koyenera kaamba ka wina ndi mnzake.
“Kuchitira Wina ndi Mnzake Ulemu”
4, 5. (a) Nchiyani chomwe chimasonyeza kuti mtumwi Paulo anayamikira akulu ogwira ntchito mwamphamvu? (b) Kodi nchiyani chimene iye analemba kwa Akristu mu Roma, ndipo nchifukwa ninji mawu ake amagwira ntchito mwachindunji kwa akulu?
4 Mtumwi Paulo anakhazikitsa chitsanzo chabwino m’mbaliyi. Monga momwe tawonera m’nkhani yapitayo, iye anayang’ana kaamba ka zinthu zabwino mwa abale ndi alongo ake. Ndipo iye sanalimbikitse kokha Akristu kukonda ndi kulemekeza akulu ogwira ntchito mwamphamvu komanso anasonyeza chiyamikiro choyenera kaamba ka amenewa iyemwini. Iye mwachiwonekere anasunga amuna oterowo okondedwa.—Yerekezani ndi Afilipi 2:19-25, 29; Akolose 4:12, 13; Tito 1:4, 5.
5 M’kalata yake kwa Akristu mu Roma, Paulo analemba kuti: ‘M’chikondi chaubale khalani ndi chiyanjo chenicheni kaamba ka wina ndi mnzake. M’kusonyeza ulemu kwa wina ndi mnzake tsogolerani. Musakhale aulesi m’machitidwe anu. Khalani achangu mumzimu. Tumikirani Yehova.” (Aroma 12:10, 11, NW) Ndithudi, mawu amenewa amagwira ntchito choyambirira kwa akulu Achikristu. Iwo, pa Akristu onse, ayenera kutsogolera m’kusonyeza ulemu kwa wina ndi mnzake.
6. (a) Nchiyani chimene akulu ayenera kupewe kuchita, ? (b) Ndimotani mmene akulu angakulitsire chidaliro cha mpingo mu bungwe la akulu lonse?
6 Akulu ayenera kukhala osamala mwachindunji kusapanga ndemanga zokhumudwitsa ponena za ong’anira anzawo. Palibe mkulu mmodzi yemwe ali ndi mikhalidwe yonse ya Chikristu ku mlingo wokulira, popeza kuti onse ali opanda ungwiro. Ena amapambana m’mikhalidwe ina, koma ali ofooka mu ina. Ngati akulu ali ndi chikondi chaubale cholondola ndi chiyanjo chabwino kaamba ka wina ndi mnzake, iwo adzasenzetsana kufooka kwa wina ndi mnzake. M’kukambitsirana kwawo ndi abale, iwo adzaloza ku nsonga zamphamvu za akulu anzawo. Mwakutsogolera motero mk’kusonyeza ulemu kwa wina ndi mnzake, adzakulitsa chidaliro cha mpingo m’bungwe la akulu lonselo.
Kugwirira Ntchito Pamodzi monga Bungwe
7. Nchiyani chomwe chidzathandiza akulu kugwirira ntchito pamodzi m’chigwirizano, ndipo ndimotani mmene iwo adzasonyezera chimenechi?
7 Pambuyo palankhula za “mphatso mwa amuna” zimene Kristu anapanga ku mpingo wake padziko lapansi ndi chiyang’aniro cha kusintha abale ndi kaamba ka ntchito ya utumiki, mtumwi Paulo analemba kuti: “Tikule mu zinthu zonse kufikira iye ali mutu ndiye, Kristu.” (Aefeso 4:7-15) Kuzindikira kuti Kristu ali Mutu wokangalika wa mpingo, ndi kuti akulu afunikira kugonjera ku dzanja lake lamanja la ulamuliro, iri nsonga yomangirira mkati mwa bungwe lirilonse la akulu. (Aefeso 1:22; Akolose 1:18; Chivumbulutso 1:16, 20; 2:1) Iwo adzafunafuna chitsogozo chake mwa mzimu woyera, maprinsipulo a Baibulo, ndi chitsogozo choperekedwa ndi Bungwe Lolamulira la “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera.”—Mateyu 24:45-47; Machitidwe 15:2, 28; 16:4, 5.
8. Nchiyani chimene akulu onse ayenera kukumbukira, ndipo ndimotani mmene iwo adzasonyezera ulemu kwa wina ndi mnzake?
8 Akulu adzazindikira kuti Kristu, kupyolera mwa mzimu woyera, angatsogoze maganizo a mkulu aliyense m’bungwe la akululo kupereka prinsipulo la Baibulo lofunikira kuchita ndi mkhalidwe uliwonse kapena kupanga chigamulo chofunika. (Machitidwe 15:6-15) Palibe mkulu mmodzi aliyense yemwe ali ndi kukulira kwa mzimu mkati mwa bungwelo. Akulu adzasonyeza ulemu kwa wina ndi mnzake mwa kumvetsera mosamalitsa kwa aliyense m’chiŵerengero chawo yemwe abweretsa thandizo la prinsipulo la Baibulo kapena langizo lochokera ku Bungwe Lolamulira pa nkhani yomwe ikukambitsiridwa.
9. (a) Ndi mikhalidwe yauzimu yotani yomwe idzathandiza woyang’anira kupewa kusalingaliridwa ndi akulu anzake? (b) Ndimotani mmene mkulu angadzisonyezere iyemwini kukhala “wolingalira,” ndipo ndimotani mmene bungwe lolamulira la m’zana loyamba linakhazikitsira chitsanzo m’nkhaniyi?
9 Kudekha kwa Chikristu, kufatsa, ndi kudzichepetsa kudzachinjiriza mkulu aliyense ku kuyesera kulamulira pa abale ake ndi kuika malingaliro ake. (Miyambo 11:2; Akolose 3:12) Woyang’anira Wachikristu angakhale ndi mawonedwe amphamvu kwambiri ndi otsimikizirika pa nkhani ina. Koma ngati iye awona kuti akulu anzake ali ndi zifukwa za m’Malemba ndi za teokratiki kaamba ka kusiyanirana ndi iye, iye ‘adzadziyesa wodzichepetsa’ ndi kudzisonyeza iyemwini “wolingalira” mwa kugonjera ku kawonedwe ka ochulukira.a (Luka 9:48; 1 Timoteo 3:3) Iye adzatsatira chitsanzo chabwino chokhazikitsidwa ndi bungwe lolamulira la m’zana loyamba, amene, pambuyo pa kukambitsirana kwa m’Malemba, ndi pansi pa chitsogozo choperekedwa ndi Kristu kupyolera mwa mzimu woyera, anadza ku “mtima umodzi.”—Machitidwe 15:25.
10. (a) Nchiyani chimene chimatsimikizira kuti kuikidwa kwa bungwe la akulu mu mpingo uliwonse kuli makonzedwe ozikidwa m’Baibulo? (b) Ndimotani mmene bukhu la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu limalongosolera mapindu a kakonzedweka?
10 Kuikidwa kwa bungwe la akulu mu mpingo uliwonse kuti lipereke chitsogozo kwazikidwa pa chitsanzo chokhazikitsidwa ndi mpingo Wachikristu woyambirira. (Afilipi 1:1; 1 Timoteo 4:14; Tito 1:5; yerekezani ndi mawu a m’munsi pa liwu lakuti “elders” [akulu] pa Tito 1:5 mu The Jerusalem Bible.) Likumaika mofupikitsa nzeru ya kukonzedwaku, bukhu lakuti Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu (tsamba 37) limalongosola kuti: “Akulu ena adzakhala apadera kwambiri mu mkhalidwe umodzi kuposa mu wina, pamene enanso a bungwelo adzapambana m’mikhalidwe imeneyo mu imene ena angakhale ofooka. Pamenepo chiyambukiro chimakhala chakuti, mwakungolankhula, lonse lathunthu, bungwelo lidzakhala ndi mihalidwe yonse yabwino mkati mwake imene iri yofunika m’kuchita kuayng’anira koyenera mu mpingo wa Mulungu.”
Ulemu Wakuya Pakati pa Mabungwe a Akulu
11, 12. (a) Nchifukwa ninji bungwe la akulu lingakwaniritse zoposa zimene ziwalo zake zingachite aliyense payekha? (b) Ndimotani mmene Kristu Yesu ndi mtumwi Paulo anachitira ndi mabungwe a akulu oterowo, ndipo ndi uphungu wotani umene unaperekedwa?
11 Chotero, bungwe la akulu liri gawo la m’Malemba ku limene lonselo limaimira kuposa ochepera a mbali za ilo. Pamene akumana ndi kupemphera kamba ka chitsogozo cha Yehova kupyolera mwa Kristu ndi mzimu woyera, iwo angapange zigamulo zomwe sizikanakhoza kufikiridwa ngati akanafunsidwa mwaumwini. Pamene akulu akumana pamodzi, mikhalidwe yawo yosiyanasiyana imagwira ntchito ndi kutulutsa zotulukapo zomwe zimasonyeza chitsogozo cha Kristu pa nkhanizo.—Yerekezani ndi Mateyu 18:19, 20.
12 Kunena kuti Kristu anachita ndi mabungwe a akulu oterowo kukusonyezedwa ndi amuthenga omwe iye anatumiza ku “nyenyezi zisanu ndi ziŵiri,” kapena “angelo a mipingo isanu ndi iŵiri” mu Asia Minor. (Chivumbulutso 1:11, 20) Woyamba wa mauthenga amenewo unatumizidwa ku mpingo wa mu Efeso kupyolera mwa ‘mngelo’ wake, kapena bungwe la oyang’anira odzozedwa. Zaka zina 40 kumayambiriro, mtumwi Paulo analola bungwe la akulu nmu Efeso kupita ku Melita kaamba ka msonkhano wapadera ndi iye. Iye anawakumbutsa iwo kupereka chisamaliro kwa iwo eni ndi kuweta mpingo.—Machitidwe 20:17, 28.
13. Nchifukwa ninji akulu ayenera kupereka chisamaliro ku mzimu umene iwo amasonyeza mkati mwa bungwe lawo la akulu la kumaloko ndi mu unansi wawo wa gulu ndi mabungwe ena a akulu?
13 Mabungwe a akulu ayenera kupereka chisamaliro chachindunji ku kusunga mzimu wabwino, weniweni pakati pa iwo eni ndi mkati mwa mpingo wawo. (Machitidwe 20:30) Monga mmene Mkristu aliyense amasonyezera mzimu winawake, mofananamo mabungwe a akulu ndi mipingo yonse ingakulitse mzimu wachindunji. (Afilipi 4:23; 2 Timoteo 4:22; Filemoni 25) Zimachitika nthaŵi zina kuti akulu omwe amalemekezana wina ndi mnzake mkati mwa mpingo wawo weniweniwo amasonyeza kusoweka kwa kugwirizana ndi bungwe lina la akulu. M’mizinda ina kumene mipingo yosiyanasiyana imakumana mu holo imodzi, kusamvana nthaŵi zina kumabuka pakati pa mabungwe a akulu pa ndandanda ya kusonkhana, malire a gawo, kaikidwe ka magetsi a Nyumba ya Ufumu, ndi zina zotero. Maprinsipulo ofananawo a kuleza mtima, kufatsa, kudzichepetsa, ndi kulingalira omwe amalamulira akulu mkati mwa bungwe lirilonse ayenera kulamulira unansi pakati pa mabungwe a akulu. Mtumwi Paulo analangiza kuti: “Muchite zonse ku kumangilira.”—1 Akorinto 14:26.
Ulemu Woyenera kaamba ka Oyang’anira Oyendayenda
14. Ndi mbali zina ziti za akulu zomwe zimayenerera kusungidwa zokondeka, ndipo nchifukwa ninji?
14 Makonzedwe ena ozikidwa mu Baibulo omwe akugwira ntchito pakati pa mipingo ya Mboni za Yehova ali kuchezeredwa kwawo mokhazikika ndi akulu oyendayenda, otchedwa oyang’anira adera kapena achigawo. (Machitidwe 15:36; 16:4, 5) Awa, mwapadera, ali “akulu akuweruza bwino.” Mosasiyana ndi akulu ena, iwo “ayenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa mawu ndi m’chiphunzitso.”—1 Timoteo 5:17.
15. Ndi uphungu wotani umene mtumwi Yohane anapereka ponena za alengezi oyendayenda?
15 M’kalata yake yachitatu mtumwi Yohane anasuliza Diotrefe chifukwa anakana “kulandira abale [mwaulemu, NW].” (Versi 10) Abale amenewa anali Akristu oyendayenda omwe anayendayenda “chifukwa cha dzina la [Yehova].” (Versi 7) Iwo mwachiwonekere anatumizidwa monga alengezi kukalalikira mbiri yabwino ndi kumangirira mipingo m’mizinda yomwe anachezera. Yohane analangiza kuti alaliki oyendayenda ogwira ntchito mwamphamvu amenewa akayenera ‘kutumizidwa pa ulendo wawo woyenera Mulungu.’ (Versi 6) Mtumwiyo anawonjezera kuti: “Chifukwa chake, ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale othandizana nacho chowonadi.” (Versi 8) Iwo anafunikira kulandiridwa mwaulemu.
16. Ndimotani mmene Akristu onse lerolino angatsatirire chitsanzo cha Gayo mu “ntchito yokhulupirika” imene iye anachita kaamba ka alengezi a m’zana loyamba, ndipo nchifukwa ninji ichi chiri choyenera?
16 Mofananamo lerolino, oyang’anira oyendayenda otumizidwa ndi Bungwe Lolamulira kukalalikira mbiri yabwino ndi kuthandiza mipingo afunikira kulandiridwa mofatsa ndi ulemu. Abale amenewa ndi akazi awo (ngati ali okwatira monga mmene ambiri a iwo aliri) akhala ofunitsitsa kuleka kukhala m’nyumba imodzi. Iwo amayendayenda kuchokera ku malo ena kunka ku malo ena, kaŵirikaŵiri akumadalira pa kuchereza kwa abale kaamba ka chakudya chawo ndi kama logonapo. Kwa Gayo, yemwe mwachikondi anatenga alengezi oyendayenda m’zana loyamba C.E., Yohane analemba kuti: “Wokondedwa, uchita chokhulupirika nacho chirichonse, uwachitira abale ndi alendo omwe.” (3 Yohane 5) Mofananamo lerolino, awo omwe amayendayenda ‘m’malo mwa dzina la Yehova’ amayenera kusungidwa okondedwa ndi kusonyezedwa chikondi ndi ulemu.
17. Ndimotani mmene akulu a mu mpingo ayenera kusonyezera ulemu woyenera kaamba ka oimira ochezera a Bungwe Lolamulira?
17 Akulu, mwachindunji, ayenera kusonyeza ulemu woyenera kaamba ka oimira ochezera amenewa a Bungwe Lolamulira. Iwo amatumizidwa ku mipingo chifukwa cha mikhalidwe yawo yauzimu ndi zokumana nazo zawo, zomwe nthaŵi zambiri ziri zochulukira kuposa zija za akulu a kumaloko ambiri. Ena a oyang’anira oyendayenda amenewa angakhale achichepere mu zaka kuposa akulu ena a m’mipingo yomwe amachezera. Koma chimenecho sichiri chifukwa chokwanira cha kuwamanira ulemu woyenera . Iwo angadzimve kukhala ndi chifuno cha kusavomereza chiyamikiro cha akulu chofulumira cha mbale kukhala mtumiki wotumikira kapena mkulu, akumakumubukira chenjezo la Paulo kwa Timoteo. (1 Timoteo 5:22) Pamene kuli kwakuti woyang’anira woyendayenda ayenera kupereka kulingalira koyenera ku kukangana koperekedwa kutsogolo ndi akulu a kumaloko, akulu ayenera kukhala ofunitsitsa kumvetsera kwa iye ndi kupindula kuchokera ku zokumana nazo zake zokulira. Inde, ayenera “kusunga amuna oterowo okondedwa.”—Afilipi 2:29, NW.
“Zindikirani Amuna Oterowo”
18, 19. (a) Ndimotani mmene Paulo analongosolera chiyamikiro chake kaamba ka antchito anzake? (b) Ndi chitsanzo chotani chimene chimasonyeza kuti Paulo sanasunge za ku khosi molimbana ndi abale ake?
18 M’kalata yake yoyamba kwa Akorinto, Paulo analemba kuti: “Koma ndikupemphani inu, abale: mudziŵa banja la Stefana kuti ali chipatso chowundukula cha Akaya ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima. Kuti inunso muvomereze otere ndi yense wakuchita nawo ndi kugwiritsa ntchito. Koma ndikondwera pa kudza kwawo kwa Stefana ndi Fortunato ndi Akayiko, chifukwa iwo anandikwaniritsa chotsalira chanu. Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu. Chifukwa chake muzindikire otere.”—1 Akorinto 16:15-18.
19 Ndi mkhalidwe wabwino, woolowa manja chotani nanga umene Paulo anali nawo kulinga kwa abale ake, ena a amene sanadziŵidwe mofala. Koma Paulo anawakonda iwo chifukwa chakuti anali “ogwirizana” ndi “ogwira ntchito” mwamphamvu m’kuyesayesa kwawo kutumikira oyera. Paulo anakhazikitsanso chitsanzo chabwino cha kulola zakale kupita. Ngakhale kuti Yohane Marko anamugwiritsa mwala iye mkati mwa ulendo wake woyamba wa umishonale, Paulo pambuyo pake anamuyamikira iye motentha ku mpingo wa mu Kolose. (Machitidwe 13:13; 15:37, 38; Akolose 4:10) Pamene anaikidwa m’ndende mu Roma, Paulo anapempha kukhalapo kwa Marko chifukwa chakuti, monga mmene iye ananenera, “[Marko] ayenera kunditumikira.” (2 Timoteo 4:11) Palibe kubwezera kwa cholakwa pamenepo!
20. Ndimotani mmene Akristu mwachisawawa, ndi akulu mwachindunji, angasonyezere kuti amayamikira oyang’anira okhulupirika ndi kuti iwo “amasunga amuna oterewa okondeka”?
20 Lerolino pakati pa anthu a Mulungu, pali oyang’anira odzipereka ambiri amene, monga Stefana, akutumikira abale awo. Kukhala otsimikiza, iwo ali ndi zolakwa zawo ndi zolephera. Ngakhale ndi tero, iwo ali “ogwirizana” ndi “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera” ndi Bungwe lake Lolamulira, ndi “kugwira ntchito” mwamphamvu mu ntchito yolalikira ndi kuthandiza abale awo. Tiyenera ‘kugonjera ife eni ku anthu a mtundu woterowo,’ kuwayamikira kaamba ka kuthereka kwawo, osafunafuna zophophonya zawo. Akulu ayenera kutenga chitsogozo m’kusonyeza chiyamikiro chofunika ndi ulemu kaamba ka akulu anzawo. Akulu afunikira kugwirizana wina ndi mnzake mumzimu wachikondi ndi chigwirizano. Onse adzazindikira mtengo wa abale okhulupirika oterowo ndi “kupitiriza kusunga amuna oterowo okondedwa.”—Afilipi 2:29.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu a m’munsi mu New World Translation Reference Bible amasonyeza kuti liwu lakuti “kulingalira” pa 1 Timoteo 3:3 limatembenuza liwu la Chigriki limene m’chenicheni limatanthauza “kugonjera.”
Nsonga kaamba ka Kubwereramo
◻ Ndi mtundu wotani wa amuna umene Paulo anawasunga okondeka mwapadera, ndipo ndani yemwe ayenerera kulingalira kwathu kwapadera lerolino?
◻ Ndimotani mmene akulu angasonyezere kuti amalemekezana wina ndi mnzake?
◻ Nchifukwa ninji bungwe la akulu lingakwaniritse zoposa zimene ziwalo zake zingachite aliyense payekha?
◻ Ndi m’mbali ziti mmene bungwe la akulu lingasonyeze kuti limalemekeza bungwe lina la akulu?
◻ Ndi mbali za oyang’anira ziti zimene zimayenerera kusungidwa zokondeka mwapadera, ndipo ndimotani mmene ulemu woyenerera umenewu ungasonyezedwere?
[Chithunzi patsamba 15]
Akulu ayenera kusonyeza chiyamikiro choyenera kaamba ka wina ndi mnzake
[Chithunzi patsamba 18]
Sonyezani chikondi ndi ulemu kaamba ka oyang’anira oyendayenda