Machitidwe a Atumwi
15 Ndiyeno amuna ena ochokera ku Yudeya anayamba kuphunzitsa abale kuti: “Mukapanda kudulidwa mogwirizana ndi mwambo wa Mose,+ simungapulumuke.” 2 Koma Paulo ndi Baranaba sanagwirizane nazo ndipo anatsutsana nawo. Choncho iwo anasankha Paulo, Baranaba komanso anthu ena, kuti apite kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu+ kukawauza za nkhaniyi.
3 Mpingo utawaperekeza, anthu amenewa anapitiriza ulendo wawo kudzera ku Foinike ndi ku Samariya. Kumeneko ankafotokoza mwatsatanetsatane zoti anthu a mitundu ina ayamba kulambira Mulungu, ndipo abale onse anasangalala kwambiri ndi zimenezi. 4 Atafika ku Yerusalemu analandiridwa ndi manja awiri ndi mpingo, atumwi komanso akulu. Ndipo anafotokoza zinthu zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwowo. 5 Koma okhulupirira ena, amene kale anali mʼgulu lampatuko la Afarisi, anaimirira mʼmipando yawo nʼkunena kuti: “Mʼpofunika kuwadula komanso kuwalamula kuti azisunga Chilamulo cha Mose.”+
6 Choncho atumwi ndi akulu anasonkhana kuti akambirane za nkhani imeneyi. 7 Atatsutsana kwambiri za nkhaniyi, Petulo anaimirira nʼkuwauza kuti: “Abale anga, mukudziwa bwino kuti mʼmasiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu, kuti kudzera pakamwa panga, anthu a mitundu ina amve mawu a uthenga wabwino nʼkukhulupirira.+ 8 Ndipo Mulungu, amene amadziwa zamumtima,+ anachitira umboni powapatsa mzimu woyera+ ngati mmene anachitiranso kwa ife. 9 Iye sanasiyanitse mʼpangʼono pomwe pakati pa ife ndi iwo.+ Koma anayeretsa mitima yawo chifukwa cha chikhulupiriro chawo.+ 10 Ndiye nʼchifukwa chiyani inu mukumuyesa Mulungu posenzetsa ophunzira goli+ limene makolo athu ngakhalenso ifeyo sitinathe kulisenza?+ 11 Koma tsopano tikukhulupirira kuti ife tidzapulumuka chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu,+ mofanananso ndi anthu amenewa.”+
12 Zitatero gulu lonselo linakhala chete, ndipo linayamba kumvetsera pamene Baranaba ndi Paulo ankafotokoza zizindikiro ndi zodabwitsa zambiri zimene Mulungu anachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mwa iwo. 13 Atamaliza kulankhula, Yakobo anayankha kuti: “Abale anga, ndimvetsereni. 14 Sumiyoni+ wafotokoza bwino mmene Mulungu anacheukira anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti pakati pawo atengepo anthu odziwika ndi dzina lake.+ 15 Ndipo zimenezi zikugwirizana ndi zimene aneneri analemba zakuti: 16 ‘Zimenezi zikadzatha ndidzabwerera nʼkumanganso tenti* ya Davide imene inagwa. Ndidzamanganso malo ogumuka a nyumbayo nʼkuikonzanso. 17 Ndidzachita zimenezi kuti anthu otsalawo afunefune Yehova* ndi mtima wonse. Amufunefune pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu, anthu otchedwa ndi dzina langa, watero Yehova* amene akuchita zinthu zimenezi,+ 18 zomwe anatsimikiza kalekale kuti adzazichita.’+ 19 Choncho chigamulo* changa nʼchakuti, anthu a mitundu ina amene ayamba kulambira Mulungu, tisawavutitse.+ 20 Koma tiyeni tiwalembere kuti apewe zinthu zoipitsidwa ndi mafano,+ chiwerewere,*+ zopotola* ndi magazi.+ 21 Chifukwa kuyambira kalekale, anthu akhala akulalikira mumzinda ndi mzinda mawu ochokera mʼmabuku a Mose, popeza mabuku amenewa amawerengedwa mokweza mʼmasunagoge sabata lililonse.”+
22 Kenako atumwi ndi akulu pamodzi ndi mpingo wonse, anagwirizana zosankha amuna pakati pawo, kuti awatumize ku Antiokeya limodzi ndi Paulo ndi Baranaba. Choncho anasankha Yudasi wotchedwa Barasaba ndi Sila,+ omwe ankatsogolera abale. 23 Ndiyeno analemba kalata nʼkuwapatsira yonena kuti:
“Ife abale anu atumwi pamodzi ndi akulu, tikulembera inu abale athu ochokera mʼmitundu ina, amene muli ku Antiokeya,+ ku Siriya ndi ku Kilikiya: Landirani moni! 24 Tamva kuti ena ochokera pakati pathu akhala akukuvutitsani polankhula zinthu zokusokonezani,+ ngakhale kuti ife sitinawapatse malangizo aliwonse. 25 Choncho tonse tagwirizana kuti tisankhe amuna nʼkuwatumiza pamodzi ndi abale athu okondedwa, Baranaba ndi Paulo. 26 Anthu amenewa apereka miyoyo yawo chifukwa cha dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 27 Tikutumiza Yudasi ndi Sila, kuti iwonso adzakufotokozereni zinthu zomwezi ndi mawu apakamwa.+ 28 Chifukwa mzimu woyera+ komanso ifeyo taona kuti ndi bwino kuti tisakusenzetseni mtolo wolemera, kupatula zinthu zofunika zokhazi zomwe ndi 29 kupitiriza kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano,+ magazi,+ zopotola*+ ndi chiwerewere.*+ Mukamapewa zinthu zimenezi mosamala kwambiri, zinthu zidzakuyenderani bwino. Tikukufunirani zabwino zonse!”*
30 Amuna amenewa atanyamuka, anapita ku Antiokeya. Kumeneko anasonkhanitsa gulu lonse la anthu nʼkuwapatsa kalatayo. 31 Ataiwerenga, anasangalala chifukwa cha mawu olimbikitsawo. 32 Popeza Yudasi ndi Sila analinso aneneri, anawakambira abalewo nkhani zambiri ndipo anawalimbikitsa.+ 33 Atakhala kumeneko kwakanthawi, abalewo anawaperekeza ndipo anabwerera mwamtendere kwa amene anawatuma. 34* —— 35 Koma Paulo ndi Baranaba anatsala ku Antiokeya. Iwo pamodzi ndi anthu enanso ambiri ankaphunzitsa komanso kulengeza uthenga wabwino wa mawu a Yehova.*
36 Patapita masiku, Paulo anauza Baranaba kuti: “Tiyeni tibwerere kumizinda yonse kumene tinalalikira mawu a Yehova* kuti tikachezere abale ndiponso tikawaone kuti ali bwanji.”+ 37 Baranaba ankafunitsitsa kuti atenge Yohane, wotchedwanso Maliko.+ 38 Koma Paulo anaona kuti si bwino kumutenga chifukwa ulendo wina Yohane anawasiya ku Pamfuliya ndipo sanapite nawo ku ntchitoyi.+ 39 Zitatero anakangana koopsa mpaka anasiyana. Baranaba+ anatenga Maliko ndipo anayenda ulendo wapamadzi kupita ku Kupuro. 40 Koma Paulo anasankha Sila, ndipo abale atamupempherera Pauloyo kuti Yehova* amusonyeze kukoma mtima kwakukulu, ananyamuka.+ 41 Iye anadzera ku Siriya ndi ku Kilikiya ndipo ankalimbikitsa mipingo.