Phunzirani Kumvera Mwakulandira Chilango
TAYEREKEZERANI kuti mwaima patanthwe pamwamba pa phiri lalitali mukudzimva wokondwa kwambiri. Umenewo uli ufulu wosangalatsa chotani nanga!
Komabe ufulu wanu kwenikweni uli ndi polekezera. Lamulo lachilengedwe la mphamvu yokoka limaika malire pakayendedwe kanu konse; kuphonya pang’ono kungadzetse tsoka. Kumbali ina, nkosangalatsa chotani nanga kudziŵa kuti lamulo limodzimodzilo lamphamvu yokoka limakutetezerani kusatengeka mukuyandamira mumlengalenga. Chotero lamulolo mwachiwonekere liripo kaamba ka ubwino wanu. Kuvomereza malire amene limaika pakayendedwe kanu pamwamba pa phiri lalitalilo nkopindulitsa, kopulumutsa moyo ndithu.
Inde, panthaŵi zina malamulo ndi kuwamvera kwathu zingaike malire pa ufulu wathu, koma kodi zimenezi zimachititsa kumvera kukhala kosafunikira?
Mmene Mulungu Amawonera Kumvera
Pokhala “Mlengi,” Yehova ndiye “chitsime cha moyo.” Kaamba ka chifukwa chimenechi zolengedwa zake zonse ziyenera kumvera iye. Posonyeza kaimidwe kamaganizo koyenerera, wamasalmo analemba kuti: “Tiyeni, tipembedze tiŵerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga: Pakuti iye ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za m’dzanja mwake.”—Mlaliki 12:1; Salmo 36:9; 95:6, 7.
Kuyambira pachiyambi, Yehova wafuna kumvera kwa zolengedwa zake. Kupitiriza kukhalapo kwa Adamu ndi Hava kunadalira pakumvera. (Genesis 2:16, 17) Mofananamo angelo anayembekezeredwa kumvera, ngakhale kuti iwo ali mumpangidwe wa moyo woposa wa anthu. Chifukwa chakuti zina za zolengedwa zauzimu zimenezi zinakhala ‘zosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m’masiku a Nowa,’ zinalangidwa mwa kuponyedwa ‘kumaenje a mdima, zisungike zikaweruzidwe.’—1 Petro 3:19, 20; 2 Petro 2:4.
Kunena zowona, Mulungu amawona kumvera monga chiyeneretso chopezera chiyanjo chake. Timaŵerenga kuti: “Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mawu a Yehova? Tawonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.”—1 Samuel 15:22.
Chiyenera Kuphunziridwa—Chifukwa Chake Ndipo Motani
Kumvera kumapezetsa kaimidwe kolungama pamaso pa Mulungu, chotero nkofunika chotani nanga kwa ife kukuphunzira! Mofanana ndi kuphunzira chinenero chachilendo, chizoloŵezi cha kumvera chingaphunziridwe pamene tikali ana. Nchifukwa chake Baibulo limagogomezera kuphunzitsa ana kuyambira ukhanda wawo.—Yoswa 8:35.
Anthu ena amakono amatsutsa lingaliro la Baibulo, akumanena kuti kufuna kuti ana akhale omvera kumakhala kutsendereza maganizo awo. Iwo amanenetsa kuti ana ayenera kuloledwa kukulitsa malingaliro awo aumwini ndi miyezo yokhalira ndi moyo popanda kudodometsa kwa achikulire.
Koma m’ma 1960 pamene makolo ambiri anali ndi lingaliro limeneli, Wilhelm Hansen, mphunzitsi, mkonzi, ndi pulofesa wa zamaganizo, sanavomereze zimenezo. Iye analemba kuti: “M’zaka zoyambirira zakukula kwa mwana, panthaŵi imene unansi wake kwa makolo ake udakali wodalira pa iwo kotheratu, ‘choipa’ kwa iye chimakhala chimene makolo amaletsa ndipo ‘chabwino’ nchimene makolo amavomereza. Chifukwa chake, kumvera kokha kumatsogolera mwanayo m’kudzisungira kwabwino ndi kusonyeza makhalidwe ofunika amene ndiwo maziko a moyo wamakhalidwe abwino.”—Yerekezerani ndi Miyambo 22:15.
Mawu a Mulungu amagogomezera kufunika kwa kuphunzira kumvera. Timaŵerenga kuti: “Ndidziŵa, AMBUYE inu, kuti sikuli kwa munthu kusankha njira zake; ndiponso sikuli kwa munthu kulinganiza njira ya moyo wake.” (Yeremiya 10:23, The New English Bible) Mbiri njodzala ndi zochitika zimene anthu alinganiza njira ya moyo wawo malinga ndi miyezo yawoyawo ndipo aloŵa m’mavuto owopsa kaamba ka kutero. Kodi nchifukwa ninji zimenezi zimachitika kaŵirikaŵiri? Chifukwa chakuti anthu alibe chidziŵitso, nzeru, ndi luntha la kulinganiza njira ya moyo wawo mwa iwo okha. Zoipirapo, iwo ali ndi chibadwa chakupanga zosankha zolakwika. Mwamsanga pambuyo pa Chigumula, Yehova anati ponena za munthu: “Ndingaliro ya mtima wa munthu iri yoipa kuyambira pa unyamata wake.”—Genesis 8:21.
Chotero, palibe aliyense amene amabadwa ndi chikhoterero chakumvera Yehova. Tiyenera kuchikhomereza mwa ana athu ndi kupitiriza kuchiphunzira m’moyo wathu wonse. Aliyense wa ife afunikira kukulitsa mkhalidwe wa mtima wa Mfumu Davide, amene analemba kuti: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’chowonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; Pakuti inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.”—Salmo 25:4, 5.
Phunzitsani Kumvera mwa Kukhala Womvera
Amayi ŵa Yesu ndi atate ake omlera anadziŵa bwino lomwe mikhalidwe yokhudza kubadwa kwa Yesu. Chotero iwo anazindikira kuti iye anali kudzachita mbali yofunika m’kukwaniritsidwa kwa zifuno za Yehova. (Yerekezerani ndi Luka 1:35, 46, 47.) Kwa iwo mawu akutiwo “Tawonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova” anali ndi tanthauzo lapadera. (Salmo 127:3) Iwo anazindikira mokwanira thayo lawo lalikululo, motero analinso ofulumira kumvera malangizo aumulungu, onga ngati pamene anauzidwa kuthaŵira ku Igupto kapena kupita ku Galileya pambuyo pake.—Mateyu 2:1-23.
Makolo a Yesu anazindikiranso thayo lawo lokhudza chilango. Zowona, m’kukhalapo kwake asanakhale munthu, Yesu anali womvera nthaŵi zonse. Koma pamene anali padziko lapansi, anaphunzira kukhala womvera pansi pamikhalidwe yatsopano kotheratu. Choyamba, anayenera kumvera makolo opanda ungwiro chifukwa chakuti ngakhale mwana wangwiro amafunikira chilango mwanjira ya malangizo ndi chiphunzitso. Makolo ake anapereka zimenezi. Kumbali ina, chilango cha nthyole chinali chosafunikira. Yesu anali womvera nthaŵi zonse; sanafunikira kuuzidwa kaŵiri. Timaŵerenga kuti: “Kenako anapita kunyumba limodzi nawo [makolo ake] ku Nazarete ndipo anali womvera kwa iwo.”—Luka 2:51, Phillips.
Yosefe ndi Mariya anadziŵanso njira yophunzitsira Yesu mwakupereka chitsanzo chabwino. Mwachitsanzo, timaŵerenga kuti “atate wake ndi amake akamuka chaka ndi chaka ku Yerusalemu ku Paskha.” (Luka 2:41) Mwakupanga makonzedwe akupita limodzi ndi banja lake, Yosefe anasonyeza kuti anali wofunitsitsa kusamalira umoyo wawo wauzimu ndi kuti anatenga kulambira Yehova mwamphamvu. Anali chitsanzo chabwino chotani nanga! Mofananamo, mwakumvera kwawo m’nkhani za kulambira, makolo angaphunzitse ana awo kumvera lerolino.
Chifukwa cha chilango cholungama choperekedwa ndi Yosefe ndi Mariya, “Yesu anakulabe m’nzeru ndi mumsinkhu, ndi m’chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.” Ndichitsanzo chabwino chotani nanga choyenera kutsanziridwa ndi makolo Achikristu lerolino!—Luka 2:52.
“Mverani . . . m’Zonse”
“Ana inu, mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.” (Akolose 3:20) Yesu anamvera makolo ake m’zonse chifukwa chakuti kumvera kwawo Yehova sikunawalole kukakamiza Yesu—kapena abale ndi alongo ake kwa amayi—kuchita zosiyana ndi chifuniro cha Yehova.
Mofananamo, makolo ambiri lerolino akuphunzitsa ana awo mwachipambano kukhala omvera m’zonse. Tamvetserani atate atatu, amene, pokhala anapyola nthaŵi yawo yolera ana, tsopano akutumikira panthambi ya Watch Tower Society.
Theo akusimba mmene iye ndi mkazi wake analerera ana awo asanu. Iye akuti: “Nkofunika kulola ana kudziŵa kuyambira paubwana wawo kuti nafenso achikulire timalakwa. Mwachisoni, timalakwa mobwerezabwereza ndipo nthaŵi zonse timapempha chikhululukiro ndi chithandizo kwa Atate wathu wakumwamba. Mwadala tinalola ana athu kuwona kuti monga momwe iwo analikulimbanira ndi nkhaŵa za ubwana, nafenso tinali kulimbana ndi nkhaŵa za uchikulire.”
Kuti mwana aphunzire kumvera, pamafunikira unansi wachikondi pakati pa iye ndi makolo ake. Hermann akunena kuti ponena za mkazi wake: “Iye sanali amayi wa anyamatawo basi komanso bwenzi lawo. Iwo anazindikira zimenezi, chotero kunali kosavuta kwa iwo kumvera.” Ndiyeno akuwonjezera uphungu wothandiza wosonyeza mmene unansi wa makolo ndi ana ungakulitsidwire, iye akuti: “Mwadala tinakhala zaka zingapo osagwiritsira ntchito makina otsukira mbale, kotero kuti mbalezo zinatsukidwa ndi kupukutidwa ndi manja. Tinagaŵira ana athu aamuna ntchito yopukuta mbalezo, akumatero mosinthana. Inali nthaŵi yabwino koposa ya kukambitsirana izi ndi izi.”
Unansi wachikondi pakati pa makolo ndi ana uli chitsanzo cha unansi umene Mkristu ayenera kukhala nawo ndi Yehova. Rudolf akufotokoza mmene iye ndi mkazi wake anachitira kuthandiza ana awo aamuna aŵiri kukulitsa unansi woterowo: “Maziko athu anali phunziro labanja lokhazikika. Tinagaŵira anawo nkhani zoyenerera zosiyanasiyana kuti azifufuze. Ndiponso tinaŵerengera limodzi Baibulo ndiyeno kukambitsirana nkhanizo. Ana athu anawona kuti Yehova amayembekezeranso makolo kumvera, osati ana okha.”
Makolo Achikristu amazindikira kuti lemba louziridwa lakuti “Zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo” limawaphatikiza iwo ndi ana awo omwe. Choncho pamene ana ali ndi thayo la kumvera makolo awo m’zonse, makolonso ayenera kukhala omvera m’zonse zimene Yehova afuna kwa iwo. Kuwonjezera pakulimbitsa unansi wa makolo ndi ana, makolo ndi ana ayenera kufunitsitsa kulimbitsa unansi wawo ndi Mulungu.—Miyambo 6:23.
Wonani Kumvera Kukhala Koyenera
Tiyenera kuthokoza chotani nanga kuti Mawu a Mulungu amapereka uphungu wotero wogwira ntchito wa kulera ana! (Wonani bokosi.) Ana amene amaphunzira kumvera kuchokera kwa makolo amene amaŵalanga molungama alidi magwero a chimwemwe cha gulu lonse Lachikristu la abale.
Pokhala kuti kumvera Mulungu kumatanthauza moyo, tiyenera kupeŵa lingaliro lakuchotsapo ziletso zimene malamulo a Mulungu amaika paufulu wathu waumwini—ngakhale mwakanthaŵi. Mwachitsanzo, tayerekezerani kuti tachotsapo lamulo lachilengedwe la mphamvu yokoka. Ha, tingakondwere chotani nanga ndi kuuluka mumlengalenga kuchokera pamwamba pa phiri popanda chododometsa ufulu wathu chichirichonse! Koma kodi chingachitike nchiyani ngati mphamvuyo yabwererapo? Kalanga ine, kugwa kwathu kungakhale kwatsoka chotani nanga!
Kuphunzira kumvera mwa kulandira chilango kumawonjezera kukula kwa umunthu wolinganizika ndipo kumatithandiza kudziŵa malire athu. Kumatithandiza kupeŵa kukhala okakamiza ndi kusalingalira zoyenerera ndi zosoŵa za ena. Kumatithandiza kupeŵa kukaikakaika. Kunena mwachidule, kumabweretsa chimwemwe.
Chotero kaya ndinu wachikulire kapena mwana, phunzirani kumvera mwakulandira chilango kotero kuti ‘kukhale bwino ndi inu’ ndiponso kuti ‘mukhale nthaŵi yaikulu padziko.’ (Aefeso 6:1-3) Kodi ndani angafune kuika pachiswe chiyembekezo chake cha kukhala ndi moyo kosatha mwa kulephera kuphunzira kumvera chifukwa chakusalandira chilango?—Yohane 11:26.
[Bokosi patsamba 29]
MAKOLO, PHUNZITSANI KUMVERA MWAKULANGA MOLUNGAMA
1. Langani malinga ndi malamulo ndi malangizo Amalemba.
2. Langani osati mwakungokakamiza kumvera koma mwakufotokoza chifukwa chake kumvera kuli kwa nzeru.—Mateyu 11:19b.
3. Langani mosakwiya osatinso molalata.—Aefeso 4:31, 32.
4. Langani mosapyola paunansi wabwino ndi wachikondi.—Akolose 3:21; 1 Atesalonika 2:7, 8; Ahebri 12:5-8.
5. Langani ana kuyambira ukhanda wawo.—2 Timoteo 3:14, 15.
6. Langani mobwerezabwereza ndi moyenerera.—Deuteronomo 6:6-9; 1 Atesalonika 2:11, 12.
7. Dzilangeni inu mwini choyamba ndipo motero phunzitsani mwakupereka chitsanzo.—Yohane 13:15; yerekezerani ndi Mateyu 23:2, 3.
8. Perekani chilango mukumadalira Yehova kotheratu, kupempha chithandizo chake m’pemphero.—Oweruza 13:8-10.
[Chithunzi patsamba 28]
“Zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo”