‘Mutumikire Ambuye Kristu Mwaukapolo’
M’MBIRI yonse, anthu mamiliyoni ambiri asenza mtolo waukapolo. Mwachitsanzo, zaka zikwi zambiri zapitazo, oyang’anira achiigupto anawasautsa kwambiri Aisrayeli. Monga mmene Baibulo likunenera, “anawaikira Aisrayeli olamulira akapolo kuti awalemetse ndi akatundu olemera,” makamaka poumba njerwa.—Eksodo 1:11, The Jerusalem Bible.
M’maiko ambiri lerolino, sikuti anthu amachita ukapolo weniweni, koma ambiri amagwira ntchito nthaŵi yaitali m’mikhalidwe yovuta—nthaŵi zina yoipa. Asenza mtolo wolemera umene ungatchedwe ukapolo wazachuma.
Komabe, pali mtundu wina wa ukapolo womwe si wolemetsa iyayi. Mtumwi Paulo analangiza okhulupirira anzake kuti: ‘Mutumikire Ambuye Kristu mwaukapolo.’ (Akolose 3:24) Amene amasankha kukhala akapolo a Kristu katundu wawo wolemera amapepuka. Yesu mwiniyo anati: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”—Mateyu 11:28-30.
Kusenza goli la Kristu sikumammasula munthu pa udindo wake wosamalira banja lake mwakuthupi. (1 Timoteo 5:8) Komabe, kumammasuladi pa misampha yambiri yofunafuna zinthu zakuthupi. M’malo mopanga chuma chakuthupi kukhala cholinga chawo chachikulu pamoyo, Akristu amakhutira ndi zimene ali nazo.—1 Timoteo 6:6-10; yerekezerani ndi 1 Akorinto 7:31.
Akristu amapezanso mpumulo pamene akukwaniritsa ntchito yawo yolalikira ‘uthenga wabwino’ wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Zimenezi zimawapatsa chimwemwe chenicheni ndi chikhutiro!
Tiyenera kuyamikira kuti ‘tikutumikira Ambuye Kristu mwaukapolo.’
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.