Kodi Nkuvaliranji Kudzichepetsa?
MKONZI wa ku Amereka, Edgar Allan Poe anangomaliza kuŵerengera mabwenzi ake nthano yake yatsopano. Iwo moseka anati iye anagwiritsira ntchito dzina la ngwazi mobwerezabwereza kopambanitsa. Kodi Poe anachita motani? Bwenzi lina linakumbukira kuti: “Mzimu wake wonyada sunathe kupirira chidzudzulo chapoyera choterocho, chotero mokwiya, mabwenzi ake asanakhoze kumletsa, anaponyera pepala lirilonse m’moto wonyeketsa.” Nthano “yosangalatsa kwabasi, yosiyana kotheratu ndi mkwiyo wake . . . wanthaŵi zonse,” inawonongeka. Kudzichepetsa kukanaipulumutsa.
Ngakhale kuti kunyada kumapangitsa anthu kuchita zinthu zopusa, kuli kowanda m’dziko lonse. Koma atumiki a Yehova ayenera kukhala osiyana. Ayenera kuvala chovala chokonzedwa bwino cha kudzichepetsa.
Kodi Kudzichepetsa Nchiyani?
Mtumwi Paulo analoza ku chovala Chachikristu cha kudzichepetsa pamene analembera okhulupirira anzake m’mzinda wakale wa Kolose. Iye anafulumiza kuti: ‘Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima.’—Akolose 3:12.
Inde, kudzichepetsa ndiko “kufatsa kwa maganizo.” Ndiko “kudzichepetsa kwa maganizo; kusoŵa kunyada; kufatsa.” Munthu wodzichepetsa ali wa “mzimu wodekha; wosanyada.” Iye ali “waulemu wakuya kapena wodzisungira.” (The World Book Dictionary, Volyumu I, tsamba 1030) Kudzichepetsa simantha kapena kufooka. Kwenikweni, kunyada kumasonyeza kufooka, pamene kuli kwakuti kusonyeza kudzichepetsa nthaŵi zambiri kumalira kulimba mtima ndi nyonga.
Mu Malemba liwu Lachihebri lomasuliridwa ‘dzichepetse’ m’lingaliro lenileni limatanthauza kuti “dzipondereze.” Chifukwa chake, wolemba Miyambo wanzeru anapereka uphungu wakuti: ‘Mwananga, ngati . . . wakodwa ndi mawu a m’kamwa mwako, . . . dzipulumutse; popeza waloŵa m’dzanja la mnzako, pita nudzichepetse [dzipondereze], numdandaulire mnzako.’ (Miyambo 6:1-3) Ndiko kuti, kankhirani pambali kunyada, vomerani kulakwa kwanu, ongolerani nkhaniyo.
Kuyenera Kukhala Kowona
Sianthu onse amene amawonekera kukhala ofatsa amene ali ndi kudzichepetsa kowona. Anthu ena owonekera kukhala ofatsa m’chenicheni akhoza kukhala onyada ndipo adzachita chirichonse kuti apeze zimene afuna. Ndiyeno pali aja amene amagwiritsira ntchito chofunda cha kudzichepetsa kwachinyengo kuti akondweretse ena. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anakumana ndi ena omwe anasonyeza “kudzichepetsa konyengezera,” ndipo anasonyeza kuti yense wakuchita chimenechi anali kwenikweni “wotukumuka popanda chifukwa chenicheni ndi mkhalidwe wake wakuthupi wa maganizo.” Munthu woteroyo analingalira molakwika kuti kukhala ndi chiyanjo cha Mulungu kunadalira pakuti kaya anadya, kumwa, kapena kukhudza zinthu zinazake kapena kusunga masiku achipembedzo kapena kusatero. Zowonadi, iye angakhale anawonekera kukhala wopembedza ndi wofatsa, koma kudzichepetsa kwake kwachinyengo kunali kopanda pake. (Akolose 2:18, 23, NW) Ndithudi, kunampangitsa kulingalira kuti mphotho ya moyo inaperekedwa kwa aja omwe anakana zinthu zakuthupi. Kunapangitsanso mtundu wamachenjera wakukondetsa zinthu zakuthupi chifukwa chakuti ziletso zakusanguluka zinaikidwa kwenikweni pazinthu zakuthupi zimene munthuyo anadzinenera kuti anazinyansa.
Kumbali ina, kudzichepetsa kowona kumamletsa munthu kusonyeza kudzitama m’kavalidwe, kapesedwe, ndi njira yamoyo. (1 Yohane 2:15-17) Munthu wovala chovala cha kudzichepetsa samakokera chidwi kwa iye yekha mosayenerera kapena ku maluso ake. Mmalomwake, kudzichepetsa kumamthandiza kuchita ndi ena mumkhalidwe wolingalirana ndi kudziwona monga momwe Mulungu amamuwonera. Kodi zimenezo ziri tero motani?
Lingaliro la Yehova
Pamene mneneri Samueli anati adzoze mfumu yatsopano ya mtundu wa Israyeli, analingalira kuti Eliyabu, mwana wamwamuna wa Jese, anasankhidwa ndi Yehova. Koma Mulungu anamuuza Samueli kuti: ‘Usayang’ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza ine ndinamkana iye; pakuti Yehova sawona monga awona munthu; pakuti munthu ayang’ana chowoneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.’ Ana a Jese asanu ndi aŵiri anakanidwa. Mulungu anasankha Davide, yemwe anatsimikizira kukhala mwamuna wokhulupirika ndi wodzichepetsa.—1 Samueli 13:14; 16:4-13.
Chovala cha kudzichepetsa chimatitetezera kusakhala onyada, odzikuza—ndi osavomerezedwa ndi Mulungu. Iye ‘akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.’ (Yakobo 4:6) Lingaliro lake lasonyezedwa m’mawu aŵa a wamasalmo: ‘Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo; koma wodzikuza amdziŵira kutali.’ (Salmo 138:6; 1 Petro 5:5, 6) Zimene Mulungu amafuna kwa atumiki ake nzowonekera bwino m’funso iri, lofunsidwa pa Mika 6:8: ‘Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?’
Kumasonyezedwa ndi Mulungu ndi Kristu
Nkosadabwitsa kuti Yehova amatiyembekezera kusonyeza kudzichepetsa! Ndiumodzi wa mikhalidwe yake. Mulungu atampulumutsa kwa adani ake, Davide anaimba kuti: ‘Mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu [Yehova]: . . . Ndipo chifatso chanu chandikuza ine.’ (Salmo 18:35; 2 Samueli 22:1, 36) Ngakhale kuti Yehova akhala kutali m’miyamba, ‘adzichepetsa apenye zam’mwamba ndi zapadziko lapansi. Amene autsa wosauka kumchotsa kufumbi, nakweza waumphaŵi kumchotsa kudzala. Kuti amkhalitse pamodzi ndi akulu.’ (Salmo 113:5-8) Mulungu amasonyeza kudzichepetsa mwakusonyeza chifundo kwa anthu ochimwa. Kuchita kwake ndi anthu ochimwa ndi kupereka Mwana wake monga nsembe kaamba ka machimo ndizo zisonyezero za kudzichepetsa kwake, chikondi, ndi mikhalidwe ina.—Aroma 5:8; 8:20, 21.
Yesu Kristu, yemwe anali ‘wofatsa ndi wodzichepetsa mtima,’ anakhazikitsa chitsanzo chachikulu koposa chaumunthu cha kudzichepetsa. (Mateyu 11:29) Iye anauza ophunzira ake kuti: ‘Ndipo amene aliyense akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.’ (Mateyu 23:12) Kumeneko sikunali chabe luso lakulankhula. Madzulo Yesu asanafe, anasambitsa mapazi a atumwi ake, akuchita utumiki wochitidwa mwamwambo ndi akapolo. (Yohane 13:2-5, 12-17) Yesu anatumikira Mulungu modzichepetsa asanabwere ku dziko lapansi ndipo wasonyeza kudzichepetsa chiyambire kuukitsidwira kwake kumwamba kumalo okwezeka. Chotero Paulo anachenjeza okhulupirira anzake ‘kuyesa anzawo oŵaposa iwo eni’ ndi kukhala ndi mkhalidwe wakudzichepetsa wa Yesu Kristu.—Afilipi 2:3, 5-11.
Popeza kuti Mulungu ndi Kristu amasonyeza kudzichepetsa, awo ofuna chiyanjo chaumulungu ayenera kusonyeza mkhalidwe umenewu. Ngati tikhala odzikuza nthaŵi zina, kukakhala kwanzeru kudzichepetsa ndi kupempha chikhululukiro cha Mulungu. (Yerekezerani ndi 2 Mbiri 32:24-26.) Ndipo mmalo mokhala ndi malingaliro odzikuza ponena za ife eni, tifunikira kugwiritsira ntchito uphungu wa Paulo wakuti: ‘Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nawo odzichepetsa.’ (Aroma 12:16) Komabe, kodi ndimotani mmene kudzichepetsa kungatipindulitsire ife ndi ena?
Mapindu a Kudzichepetsa
Phindu limodzi la kudzichepetsa nlakuti kumatiletsa kudzitama. Motero sitimakwiitsa ena ndipo timapeŵa kuchititsidwa manyazi enife ngati anthuwo sachititsidwa chidwi ndi zipambano zathu. Tiyenera kudzitamandira mwa Yehova, osati mwa ife eni.—1 Akorinto 1:31.
Kudzichepetsa kumatithandiza kupeza chitsogozo chaumulungu. Yehova anatumiza mngelo ndi masomphenya kwa Danieli chifukwa chakuti mneneriyo anadzichepetsa pamaso pa Mulungu pamene ankafunafuna chitsogozo ndi kuzindikira. (Danieli 10:12) Pamene Ezara anali pafupi kutsogoza anthu a Yehova kuchoka m’Babulo ali ndi golidi ndi siliva wambiri wokakongoletsera kachisi m’Yerusalemu, analengeza kusala kudya kotero kuti iwo akhoze kudzichepetsa pamaso pa Mulungu. Kodi chotulukapo chinali chotani? Yehova anaŵatetezera ku chiukiro cha adani mkati mwa ulendo woopsa. (Ezara 8:1-14, 21-32) Mofanana ndi Danieli ndi Ezara, tiyeni tisonyezetu kudzichepetsa ndi kufunafuna chitsogozo cha Yehova mmalo moyesayesa kukwaniritsa ntchito zopatsidwa ndi Mulungu mwa nzeru ndi nyonga za ife eni.
Ngati tavala chovala cha kudzichepetsa, tidzalemekeza ena. Mwachitsanzo, ana odzichepetsa amalemekeza ndi kumvera makolo awo. Akristu ofatsa nawonso amalemekeza okhulupirira anzawo a m’maiko ena, fuko, ndi makulidwe, popeza kuti kudzichepetsa kumatipangitsa kukhala opanda tsankho.—Machitidwe 10:34, 35; 17:26.
Kudzichepetsa kumapititsa patsogolo chikondi ndi mtendere. Munthu wodzichepetsa samakangana ndi okhulupirira anzake poyesayesa kukhazikitsa zoyenerera zake zolingaliridwa. Paulo anangochita zinthu zimene zinali zomangirira ndipo sakavutitsa chikumbumtima cha mbale. (Aroma 14:19-21; 1 Akorinto 8:9-13; 10:23-33) Kudzichepetsa kumatithandizanso kupititsa patsogolo chikondi ndi mtendere mwakukhululukira ena machimo awo kwa ife. (Mateyu 6:12-15; 18:21, 22) Kumatisonkhezera kupita kwa munthu amene talakwirayo, kuvomera kulakwa kwathu, kupempha chikhululukiro chake, ndikuchita zimene tingathe kuwongolera choipa chirichonse chimene tingakhale tinachita. (Mateyu 5:23, 24; Luka 19:8) Ngati munthu wolakwiridwayo watifikira, kudzichepetsa kumatisonkhezera kuthetsa nkhaniyo mwamtendere mumzimu wa chikondi.—Mateyu 18:15; Luka 17:3.
Chipulumutso chimadalira pakusonyeza kudzichepetsa. Mwachitsanzo, ponena za Mulungu, kwanenedwa kuti: ‘Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa; koma maso anu ali pa odzikuza kuti muŵachepetse.’ (2 Samueli 22:28) Pamene Mfumu Yesu Kristu ‘ayenda m’njira ya chowonadi, chifatso, ndi chilungamo,’ adzapulumutsa odzichepetsa pamaso pake ndi pa Atate wake. (Salmo 45:4) Awo osonyeza kudzichepetsa akhoza kupeza mpumulo m’mawu aŵa: ‘Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.’—Zefaniya 2:3.
Kudzichepetsa ndi Gulu la Mulungu
Kudzichepetsa kumasonkhezera anthu a Mulungu kuzindikira gulu lake ndi kukhala momwemo monga osunga umphumphu. (Yerekezerani ndi Yohane 6:66-69.) Ngati sitinapatsidwe thayo lautumiki lomwe tinkayembekezera kulandira, kudzichepetsa kumatithandiza kugwirizana ndi awo okhala ndi mathayo mkati mwa mpingo. Ndipo kugwirizana kwathu kodzichepetsa kumakhazikitsa chitsanzo chabwino.
Kumbali ina, kudzichepetsa kumatitetezera kusasonyeza kudzikuza ponena za mathayo athu autumiki pakati pa anthu a Yehova. Kumatitsekereza kufunafuna ulemu kaamba ka ntchito imene tagaŵiridwa kuichita m’gulu la Mulungu. Ndiponso, ngati tikutumikira monga akulu, kudzichepetsa kudzatithandiza kuchita mwachifundo ndi gulu la Mulungu.—Machitidwe 20:28, 29; 1 Petro 3:8.
Kudzichepetsa ndi Chilango
Chovala cha kudzichepetsa chimatithandiza kulandira chilango. Anthu odzichepetsa sali ngati Uziya, Mfumu ya Yuda, amene mtima wake unakhala wodzikuza kwambiri kotero kuti analanda mathayo aunsembe. Iye ‘analakwira Yehova naloŵa m’kachisi kukafukiza pa guwa lansembe la chofukiza.’ Pamene Uziya anakwiira ansembe chifukwa chomuwongolera, anakanthidwa ndi khate. Ha, ndimtengo wotani nanga woulipira kaamba ka kusoŵa kudzichepetsa! (2 Mbiri 26:16-21; Miyambo 16:18) Musakhale ngati Uziya ndi kulola kudzikuza kukulepheretsani kulandira chilango kuchokera kwa Mulungu kupyolera mwa Mawu Ake ndi gulu.
Ponena za ichi Paulo anauza Akristu odzozedwa Achihebri kuti: ‘Mwana wanga, usayese chopepuka kulanga kwa [Yehova, NW], kapena usakomoke podzudzulidwa ndi iye; Pakuti amene [Yehova] amkonda amlanga, nakwapula mwana ali yense amlandira. . . . Chilango chirichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu choŵaŵa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloŵeretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.’ (Ahebri 12:5-11) Kumbukiraninso kuti, “zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.”—Miyambo 6:23.
Valanibe Kudzichepetsa
Nkofunika chotani nanga kuti Akristu nthaŵi zonse avale chovala cha kudzichepetsa! Chimatisonkhezera kulimbika monga olengeza Ufumu, modzichepetsa kuchitira umboni kunyumba ndi nyumba kufunafuna anthu “owongoka mtima kaamba ka moyo wosatha.” (Machitidwe 13:48, NW; 20:20) Ndithudi, kudzichepetsa kumatithandiza kupitirizabe kumvera Mulungu m’zinthu zonse, ngakhale kuti otsutsa odzikuza amada njira yathu yolungama.—Salmo 34:21.
Popeza kuti kudzichepetsa kumatisonkhezera ‘kukhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse,’ iye amawongola mayendedwe athu. (Miyambo 3:5, 6) Kwenikweni, tingayende ndi Mulungu ndi kusangalala ndi chivomerezo chake ndi dalitso kokha ngati tavala mkhalidwe wabwino umenewu. Monga momwe wophunzira Yakobo analembera kuti: ‘Dzichepetseni pamaso pa [Yehova, NW], ndipo adzakukwezani.’ (Yakobo 4:10) Chotero tiyeni tivaletu kudzichepetsa, chovala chokongolacho chokonzedwa ndi Yehova Mulungu.