Achinyamata, Yesetsani Kuti Kupita Kwanu Patsogolo Kuonekere
“Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Kangalika nazo, kuti kupita kwako patsogolo kuonekere kwa anthu onse.”—1 TIM. 4:15.
1. Kodi Yehova amafunira zotani achinyamata?
MFUMU yanzeru Solomo inalemba kuti: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako.” (Mlal. 11:9) Uthenga umenewu ndi wochokera kwa Yehova Mulungu ndipo iye amafuna kuti achinyamatanu muzisangalala. Ndipotu Yehova amafuna kuti mupitirize kusangalala nthawi yonse ya moyo wanu. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti achinyamata ambiri amalakwitsa pochita zinthu zambiri ndipo izi zimawabweretsera mavuto ambiri mtsogolo. Ngakhalenso Yobu anadandaula chifukwa cha mavuto amene anali ngati ‘cholowa cha mphulupulu za ubwana wake.’ (Yobu 13:26) Mkhristu wachinyamata akamakula amafunika kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu. Akapanda kusankha bwino amakumana ndi mavuto ambiri ndipo amanong’oneza bondo moyo wake wonse.—Mlal. 11:10.
2. Kodi achinyamata ayenera kutsatira malangizo a m’Baibulo ati kuti apewe kulakwitsa posankha zinthu?
2 Komatu achinyamata ayenera kusankha zinthu mwanzeru. Taganizirani malangizo amene Paulo anauza Akorinto. Iye ananena kuti: “Musakhale ana aang’ono pa luntha la kuzindikira . . . koma pa luntha la kuzindikira khalani aakulu msinkhu.” (1 Akor. 14:20) Kumvera malangizo akuti tikhale ndi luntha la kuzindikira komanso kuti tiziganiza ngati munthu wamkulu, kungathandize achinyamata kuti asalakwitse posankha zinthu.
3. Kodi mungatani kuti muziganiza ngati munthu wamkulu?
3 Achinyamata, dziwani kuti mufunika kuchita khama kuti muziganiza ngati munthu wamkulu. Paulo anauza Timoteyo kuti: “Usalole kuti munthu aliyense akuderere poona kuti ndiwe mnyamata. M’malo mwake, ukhale chitsanzo kwa okhulupirika m’kalankhulidwe, m’makhalidwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, ndi m’chiyero. . . . Pitiriza kudzipereka pa kuwerenga pamaso pa anthu, kuwadandaulira, ndi kuwaphunzitsa . . . Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Kangalika nazo, kuti kupita kwako patsogolo kuonekere kwa anthu onse.” (1 Tim. 4:12-15) Akhristu achinyamata ayenera kuyesetsa kuti kupita patsogolo kwawo kuonekere kwa anthu onse.
Kodi Kupita Patsogolo N’kutani?
4. Kodi kupita patsogolo mwauzimu kumatanthauza chiyani?
4 Kupita patsogolo kumatanthauza “kusintha n’kuyamba kuchita zinthu zabwino kwambiri.” Paulo anali kulimbikitsa Timoteyo kuti ayesetse kupita patsogolo pa nkhani ya zolankhula zake, khalidwe lake, kusonyeza chikondi, chikhulupiriro, chiyero ndiponso pochita utumiki wake. Iye anayenera kuyesetsa kupereka chitsanzo chabwino kwambiri pa moyo wake. Choncho anayenera kupitirizabe kuyesetsa kupita patsogolo mwauzimu.
5, 6. (a) Kodi kupita patsogolo kwa Timoteyo kunayamba liti kuonekera? (b) Kodi masiku ano achinyamata angam’tsanzire bwanji Timoteyo pa nkhani ya kupita patsogolo?
5 Mmene Paulo ankalemba malangizo amenewa, cha pakati pa 61 ndi 64 C.E., n’kuti Timoteyo ali kale mkulu wodziwa zinthu. Sikuti anali atangoyamba kumene kupita patsogolo mwauzimu. Tikutero chifukwa choti pofika m’ma 49 kapena 50 C.E., Timoteyo ayenera kuti anali ndi zaka zothamangira m’ma 20 kapena kuposa ndipo “abale a ku Lusitara ndi ku Ikoniyo anam’chitira umboni wabwino,” chifukwa anaona mmene iye ankapitira patsogolo mwauzimu. (Mac. 16:1-5) Pa nthawiyi, Paulo anam’tenga Timoteyo pa ulendo wake waumishonale. Ataona kwa miyezi ingapo mmene Timoteyo anali kupitira patsogolo, Paulo anam’tumiza ku Tesalonika kuti akatonthoze ndi kulimbikitsa Akhristu a mumzindawo. (Werengani 1 Atesalonika 3:1-3, 6.) N’zoonekeratu pamenepa kuti Timoteyo anayamba ali wamng’ono kuonetsa kuti akupita patsogolo.
6 Inu achinyamata mumpingo, yesetsani panopo kukhala ndi makhalidwe ofunikira kuti muonetse bwinobwino kuti mukupita patsogolo pa moyo wanu wachikhristu ndiponso pa luso lanu lophunzitsa choonadi cha m’Baibulo. Kumbukirani kuti kungoyambira ali ndi zaka 12, Yesu “anali kukulabe m’nzeru.” (Luka 2:52) Motero, tiyeni tione njira zitatu zimene mungaonetsere kuti mukupita patsogolo pa moyo wanu: (1) Mukamakumana ndi mavuto enaake, (2) Mukamakonzekera banja, ndipo (3) Mukamayesetsa kukhala “mtumiki wabwino.”—1 Tim. 4:6.
Muyenera “Kuganiza Bwino” Mukamakumana ndi Mavuto
7. Kodi achinyamata amamva bwanji akakumana ndi mavuto?
7 Mkhristu wina wa zaka 17, dzina lake Carol, anati: “Nthawi ina maganizo ankandichulukira kwambiri ndipo ndinkalefuka kwambiri moti thupi linkangoti zii, osafuna n’komwe kudzuka m’mamawa.”a N’chifukwa chiyani iyeyu ankamva choncho? Carol ali ndi zaka 10, makolo ake anasudzulana ndipo iye anayamba kukhala ndi mayi ake, omwe sankatsatira mfundo za m’Baibulo. N’kutheka kuti inunso muli pa mavuto amene mukuona kuti sangathe.
8. Kodi Timoteyo anakumana ndi mavuto otani?
8 Timoteyo nayenso ankakumana ndi mavuto pa nthawi imene ankapita patsogolo mwauzimu. Mwachitsanzo iye ‘ankadwaladwala’ m’mimba. (1 Tim. 5:23) Pamene Paulo anatumiza Timoteyo ku Korinto kukathandiza pa mavuto amene anthu ena oderera Atumwi anayambitsa, Paulo analimbikitsa mpingowo kuti ugwirizane ndi Timoteyo n’cholinga choti iye “asadzakhale ndi mantha” pakati pawo. (1 Akor. 4:17; 16:10, 11) N’kutheka kuti Timoteyo anali wamanyazi kapena wamantha.
9. Kodi kuganiza bwino kumatanthauza chiyani, nanga kumasiyana bwanji ndi mzimu wa mantha?
9 Pofuna kuthandiza Timoteyo, Paulo anam’kumbutsa kuti, “Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha, koma wamphamvu, wachikondi, ndi wa kuganiza bwino.” (2 Tim. 1:7) “Kuganiza bwino” kumatanthauza kutha kuganizira zinthu mwakuya komanso mwanzeru. Izi zimaphatikizapo kuona zinthu mmene zilili ndiponso kusakhumudwa msanga ngati zinthuzo sizinachitike mmene ife tinkafunira. Achinyamata ena amasonyeza kuti ali ndi mzimu wamantha. Iwo akakumana ndi mavuto amayesa kuwathawa mwina poonera TV nthawi yaitali, kumwa kwambiri mowa ndi mankhwala osokoneza bongo, kugona kwambiri, kukonda kupita m’mapwando kapena kuchita zachiwerewere. Baibulo limalangiza Akhristu kuti ayenera “kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, ndi kukhala a maganizo abwino ndi a chilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu m’dongosolo lino la zinthu.”—Tito 2:12.
10, 11. Kodi kuganiza bwino kumatithandiza bwanji kuti tikhale olimba mwauzimu?
10 Baibulo limalimbikitsa “anyamata kukhala oganiza bwino.” (Tito 2:6) Ngati mumamvera malangizo amenewa ndiye kuti mukakumana ndi mavuto muzipemphera kwa Mulungu ndi kudalira mphamvu yake. (Werengani 1 Petulo 4:7.) Mukatero mudzayamba kudalira kwambiri “mphamvu imene Mulungu amapereka.”—1 Pet. 4:11.
11 Zinthu ziwiri zimene zinathandiza Carol ndizo kuganiza bwino komanso kupemphera. Iye anati: “Zinali zovuta kukhala limodzi ndi mayi anga chifukwa choti anali ndi khalidwe loipa. Pa moyo wanga wonse, imeneyi ndi imodzi mwa nkhani zimene zandivutitsapo kwambiri. Koma pemphero linandithandiza kwambiri. Ndikudziwa kuti Yehova ali nane ndipo sindiopa chilichonse.” Dziwani kuti mavuto angathe kukuchititsani kuti mukhale munthu wabwino komanso wolimba mwauzimu. (Sal. 105:17-19; Maliro 3:27) Mulungu sadzakusiyani zivute zitani. Musakayike zoti iye ‘adzakuthangatani.’—Yes. 41:10.
Kukonzekera Ukwati Wabwino
12. N’chifukwa chiyani Mkhristu amene akuganiza zokwatira kapena kukwatiwa ayenera kutsatira mfundo ya pa Miyambo 20:25?
12 Achinyamata ena amakwatira kapena kukwatiwa msanga poganiza kuti akatero ndiye kuti mavuto amene amakumana nawo kunyumba, kusungulumwa kwawo komanso nkhawa zawo zonse zitheratu ndipo azikhala osangalala. Komatu malumbiro aukwati si nkhani yofunika kuitenga mwachibwanabwana. M’nthawi za m’Baibulo panali anthu ena amene ankawinda kapena kuti kulumbira kwa Mulungu asanaganizire bwino zimene akulonjezazo. (Werengani Miyambo 20:25.) Nthawi zina achinyamata saganizira bwinobwino zinthu zimene iwo adzafunike kuchita kuti ukwati wawo ukhale wabwino. Ndiyeno amadzazindikira mochedwa kuti pali zinthu zambiri zimene akufunika kuchita zimene mwina sankaziganizira n’komwe.
13. Kodi amene akufuna kuyamba chibwenzi ayenera kudzifunsa mafunso ati, nanga ndi malangizo othandiza ati amene alipo kale?
13 Motero musanayambe chibwenzi ndi munthu aliyense ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani ndikufuna kukwatira kapena kukwatiwa? Kodi ndi zinthu ziti zimene ndikuyembekezera m’banja? Kodi munthu ameneyu ndi woyeneradi kuti ndimange naye banja? Kodi ndine wokonzekadi kusamalira udindo wanga m’banja?’ Pofuna kukuthandizani kuti mudzifufuze moyenera, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wapereka malangizo osapita m’mbali pa nkhani imeneyi.b (Mat. 24:45-47) Muyenera kuona kuti amenewa ndi malangizo amene Yehova akukupatsani inuyo panokha. Ganizirani mofatsa mfundo zimenezi ndipo zigwiritsireni ntchito. Musakhale ngati “kavalo, kapena ngati bulu, wopanda nzeru.” (Sal. 32:8, 9) Muyenera kukhala wamkulu msinkhu pa nkhani yomvetsa udindo wam’banja. Ngati mukuona kuti ndinu wokonzeka kuyamba chibwenzi musaiwale kukhala “chitsanzo . . . m’chiyero.”—1 Tim. 4:12.
14. Kodi kukula mwauzimu kungakuthandizeni bwanji mukalowa m’banja?
14 Kukula mwauzimu kumathandizanso kwambiri munthu akalowa m’banja. Mkhristu wokhwima mwauzimu amayesetsa ‘kufika pa msinkhu woyenererana ndi kudzala ndi Khristu.’ (Aef. 4:11-14) Iye amachita khama kwambiri kukhala ndi makhalidwe amene Khristu anali nawo. “Khristu sanadzikondweretse yekha” ndipo iye ndi Chitsanzo chathu. (Aroma 15:3) Aliyense m’banja akamayesetsa kuchita zinthu zopindulitsa mnzake osati kumangofuna zopindulitsa iye yekha, m’banjamo aliyense amakhala mwamtendere ndiponso mosangalala. (1 Akor. 10:24) Mwamuna amayesetsa kusonyeza chikondi chololera kuvutikira ena ndipo mkazi amagonjera mwamuna wake ngati mmene Yesu amachitira ndi Mutu wake.—1 Akor. 11:3; Aef. 5:25.
“Kwaniritsa Utumiki Wako Bwino Lomwe”
15, 16. Kodi mungatani kuti kupita patsogolo kwanu kuonekere mu utumiki?
15 Ponena za ntchito yofunika ya Timoteyo, Paulo analemba kuti: “Pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu . . . ndikukulamula mwamphamvu kuti lalika mawu, chita nawo mwachangu.” Iye anatinso: “Gwira ntchito ya mlaliki, kwaniritsa utumiki wako bwino lomwe.” (2 Tim. 4:1, 2, 5) Kuti atsatire lamulo limeneli, Timoteyo anayenera kukhala “wokula bwino ndi mawu a chikhulupiriro.”—Werengani 1 Timoteyo 4:6.
16 Kodi mungatani kuti mukhale “wokula bwino ndi mawu a chikhulupiriro”? Paulo analemba kuti: “Pitiriza kudzipereka pa kuwerenga pamaso pa anthu, kuwadandaulira, ndi kuwaphunzitsa. Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Kangalika nazo.” (1 Tim. 4:13, 15) Kuti munthu apite patsogolo amafunika kuchita khama kwambiri pophunzira Baibulo payekha. Mawu akuti “kangalika” amasonyeza kuika maganizo onse pa chinthu chimene ukuchitacho. Kodi inuyo muli ndi zizolowezi zotani pa nkhani ya kuphunzira Baibulo? Kodi mumakangalika ndi “zinthu zozama za Mulungu”? (1 Akor. 2:10) Kapena kodi mumangochita zinthu mosaikirapo mtima? Kusinkhasinkha zinthu zimene mukuphunzira kungakuthandizeni.—Werengani Miyambo 2:1-5.
17, 18. (a) Kodi ndi luso liti limene muyenera kuyesetsa kukhala nalo? (b) Kodi kukhala ndi mtima umene Timoteyo anali nawo kungakuthandizeni bwanji mu utumiki?
17 Mpainiya wina wachinyamata, dzina lake Michelle, anati: “Kuti ndizilalikira mogwira mtima, ndili ndi ndandanda yophunzira Baibulo pandekha komanso sindijomba kumisonkhano. Izi zikundithandiza kuti ndizikula mwauzimu.” Kuchita upainiya kungakuthandizeni kukulitsa luso lanu logwiritsa ntchito Baibulo mukakhala mu utumiki komanso kuti mukule mwauzimu. Yesetsani kumawerenga bwino komanso kupereka ndemanga zogwira mtima pamisonkhano yachikhristu. Kuti musonyeze kuti mukupita patsogolo, muyenera kukonzekera bwino nkhani pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu n’kukamba motsatira mfundo zokhazo zimene zikupezeka pamene pachokera nkhani yanu.
18 ‘Munthu wogwira ntchito ya mlaliki’ amalalikira mogwira mtima pothandiza anthu ena kuti adzapulumuke. Kuti zimenezi zitheke m’pofunika kukhala ndi “luso la kuphunzitsa.” (2 Tim. 4:2) Mukamalowa mu utumiki ndi anthu amene ali ndi luso pa ntchito yolalikira mudzaphunzira luso lawo la kuphunzitsa ngati mmene Timoteyo anaphunzirira kwa Paulo. (1 Akor. 4:17) Ponena za anthu amene anawathandiza, Paulo anati anawapatsa uthenga komanso ‘moyo wake.’ Izi zikutanthauza kuti anagwiritsa ntchito moyo wake weniweniwo pofuna kuwathandiza chifukwa choti ankawakonda kwambiri. (1 Ates. 2:8) Kuti mutengere chitsanzo cha Paulo mu utumiki, muyenera kukhala ndi mtima umene Timoteyo anali nawo. Iye ankaganizira kwambiri anthu ena ndipo ‘ankatumikira monga kapolo popititsa patsogolo uthenga wabwino.’ (Werengani Afilipi 2:19-23.) Kodi inunso mumasonyeza mtima wololera kuvutikira ena mukakhala mu utumiki?
Kupita Patsogolo Kumabweretsa Chimwemwe Chenicheni
19, 20. Kodi kupita patsogolo mwauzimu kumabweretsa bwanji chimwemwe?
19 Kuti munthu apite patsogolo mwauzimu amafunika kuchita khama kwambiri. Koma mwakuyesetsa kunola luso lanu lophunzitsa, mungathe kudzafika pokhala ndi mwayi ‘wolemeretsa ambiri’ mwauzimu, ndipo iwo adzakhala ‘kolona wanu wa chisangalalo.’ (2 Akor. 6:10; 1 Ates. 2:19) Fred, yemwe ndi mtumiki wa nthawi zonse, anati: “Mosiyana ndi kale lonse, panopo ntchito yanga yaikulu ndi kuthandiza anthu ena. Ndaona kuti kupatsa kumabweretsadi chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.”
20 Ponena za chimwemwe chimene anapeza chifukwa chokula mwauzimu, mpainiya wina wachitsikana, dzina lake Daphne, anati: “Nditayamba kuphunzira zambiri za Yehova, ndinayamba kumukonda kwambiri. Ukamayesetsa kusangalatsa Yehova ndi mtima wako wonse, umamva bwino kwambiri.” Ngakhale kuti si nthawi zonse pamene anthu angathe kuona kuti munthu akupita patsogolo mwauzimu, Yehova nthawi zonse amaona ndipo amasangalala kwambiri ndi zimenezi. (Aheb. 4:13) Ndithudi, Akhristu achinyamata dziwani kuti mungathe kutamanda Atate wanu wakumwamba. Pitirizani kukondweretsa mtima wake poyesetsa ndi mtima wanu wonse kuti kupita patsogolo kwanu kuonekere.—Miy. 27:11.
[Mawu a M’munsi]
a Tasintha mayina ena.
b Onani buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri pa mutu wakuti “Kodi Munthu Ameneyu ndi Woyenera Kuti Ndimange Naye Banja?” Nsanja ya Olonda ya May 15, 2001, pa mutu wakuti “Malangizo a Mulungu Othandiza Posankha Wokwatirana Naye.”
Kodi Mwaphunzira Chiyani?
• Kodi kukula mwauzimu kumatanthauza chiyani?
• Kodi mungatani kuti kupita patsogolo kwanu kuonekere . . .
mukamakumana ndi mavuto?
mukamakonzekera ukwati?
mukakhala mu utumiki?
[Chithunzi patsamba 15]
Kupemphera kungakuthandizeni kuthana ndi mavuto
[Chithunzi patsamba 16]
Kodi ofalitsa achinyamata angatani kuti akhale aluso pophunzitsa?