Fulumizanani ku Chikondano ndi Ntchito Zabwino—MotanI?
“Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, . . . tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.”—AHEBRI 10:24, 25.
1, 2. (a) Kodi nchifukwa ninji kunali kofunika kuti Akristu oyambirira apeze chitonthozo ndi chilimbikitso pa kusonkhana kwawo pamodzi? (b) Kodi ndi uphungu wotani wa Paulo umene unasonyeza za kufunika kwa kusonkhana pamodzi?
ANASONKHANA chobisala, ataunjikana m’nyumba yotsekedwa. Kunjako, kunali ngozi yokhayokha. Mtsogoleri wawo, Yesu, anali atangophedwa kumene poyera, ndipo anali atachenjeza otsatira ake kuti akachitiridwa moipa mofanana naye. (Yohane 15:20; 20:19) Koma pamene anali kulankhula monong’ona ponena za Yesu wawo wokondedwa, kukhala pamodziko mwina kunawachititsa kumva ngati osungika pang’ono.
2 Pamene zaka zinapyola, Akristu anayang’anizana ndi mayesero osiyanasiyana ndi mazunzo. Mofanana ndi ophunzira oyambirira amenewo, iwo anapeza chitonthozo ndi chilimbikitso posonkhana pamodzi. Motero, mtumwi Paulo analemba pa Ahebri 10:24, 25: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.”
3. Kodi nchifukwa ninji munganene kuti Ahebri 10:24, 25 si lamulo chabe lakuti Akristu azisonkhana pamodzi?
3 Mawu amenewo si lamulo chabe la kupitiriza kusonkhana pamodzi. Amapereka muyezo wouziridwa waumulungu wa misonkhano yonse Yachikristu—ndipo ndithudi, wa chochitika chilichonse pamene Akristu asonkhana pamodzi. Lerolino kuposa ndi kale lonse, pamene tikuona bwino lomwe kuyandikira kwa tsiku la Yehova, zitsenderezo ndi ngozi za dongosolo ili loipa zimachititsa misonkhano yathu kukhaladi ngati malo othaŵirako, magwero a nyonga ndi chilimbikitso cha onse. Kodi tingachitenji kuti zimenezi zikhale motero? Chabwino, tiyeni tipende mawu a Paulo mosamalitsa, tikumafunsa mafunso aakulu atatu: Kodi ‘kuganizirana wina ndi mnzake’ kumatanthauzanji? Kodi ‘kufulumizana ku chikondano ndi ntchito zabwino’ kumatanthauzanji? Lomaliza, kodi ‘tingadandaulirane’ motani m’nthaŵi zino zovuta?
‘Ganiziranani Wina ndi Mnzake’
4. Kodi ‘kuganizirana wina ndi mnzake’ kumatanthauzanji?
4 Pamene Paulo analimbikitsa Akristu ‘kuganizirana wina ndi mnzake’ anagwiritsira ntchito verebu Yachigiriki ka·ta·no·eʹo, liwu losonyeza mlingo waukulu wakuti “kuzindikira.” Theological Dictionary of the New Testament imati limatanthauza “kulunjikitsa maganizo onse a munthuwe pa chinthu china.” Malinga ndi W. E. Vine, lingatanthauzenso “kumvetsetsa bwino, kulingalira mosamalitsa.” Chotero pamene Akristu ‘aganizirana wina ndi mnzake,’ iwo samangozindikira mwapamwamba chabe koma amagwiritsira ntchito kuganiza kwawo konse ndi kuyesa kuona mwakuya.—Yerekezerani ndi Ahebri 3:1.
5. Kodi ndi mbali zina zotani za munthu zimene zingakhale zobisika, ndipo nchifukwa ninji tiyenera kuganizira zimenezi?
5 Tifunikira kukumbukira kuti mwa munthu muli zambiri kuposa zimene kaonekedwe kake kakunja, ntchito yake, kapena umunthu wake ungasonyeze. (1 Samueli 16:7) Kaŵirikaŵiri mkhalidwe wofatsa wakunja umabisa malingaliro ovutika kapena mkhalidwe wanthabwala. Ndiyenonso, makulidwe amasiyana kwambiri. Ena akumana ndi mavuto owopsa m’miyoyo yawo; ena pakali pano akupirira ndi mikhalidwe imene mungaone kukhala yovuta kuilingalira. Kaŵirikaŵiri zimachitika kuti kuipidwa kwathu ndi chizoloŵezi china cha mbale kapena mlongo wina chimatha pamene tidziŵa zambiri ponena za makulidwe kapena mikhalidwe ya munthuyo.—Miyambo 19:11.
6. Kodi ndi njira zina zotani zimene tingadziŵanirane bwino, ndipo ndi zotulukapo zabwino zotani zimene zingakhalepo?
6 Ndithudi, zimenezi sizimatanthauza kuti tiloŵerere mosapemphedwa m’nkhani ya munthu mwini. (1 Atesalonika 4:11) Chikhalirechobe, tingasonyezedi chikondwerero chaumwini mwa wina ndi mnzake. Zimenezi zimaloŵetsamo zoposa kungopatsana moni pa Nyumba Yaufumu. Bwanji osapatula munthu wina amene mungafune kudziŵana naye bwino ndi kucheza naye mphindi zingapo misonkhano isanayambe kapena pambuyo pake? Chabwinonso kwambiri ndicho, ‘kuchereza alendo’ mwa kuitana bwenzi limodzi kapena mabwenzi aŵiri kunyumba kwanu kudzadya nawo chakudya wamba. (Aroma 12:13) Sonyezani chikondwerero. Mvetserani. Kungofunsa za mmene munthuyo anafikira pakudziŵa ndi kukonda Yehova kungavumbule zambiri. Komabe, inu mungadziŵe zambiri mwa kugwirira ntchito pamodzi mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Kuganizirana wina ndi mnzake m’njira zotero kudzatithandiza kukulitsa kumverana chisoni kwenikweni, kapena kuchitirana chifundo.—Afilipi 2:4; 1 Petro 3:8.
‘Fulumizanani’
7. (a) Kodi ndimotani mmene kuphunzitsa kwa Yesu kunakhudzira mtima anthu? (b) Kodi nchiyani chimene chinapangitsa kuphunzitsa kwake kukhala kwamphamvu kwambiri?
7 Pamene tiganizirana wina ndi mnzake, timakhala okonzekera bwinopo kufulumizana, kusonkhezerana kuchitapo kanthu. Makamaka akulu Achikristu amachita mbali yaikulu pankhaniyi. Ponena za nthaŵi ina pamene Yesu ananena mawu poyera, timaŵerenga kuti: “Makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake.” (Mateyu 7:28) Panthaŵi inanso ngakhale asilikali ena amene anatumidwa kukammanga anabwerera akumanena kuti: “Nthaŵi yonse palibe munthu analankhula chotero.” (Yohane 7:46) Kodi nchiyani chimene chinapangitsa kuphunzitsa kwa Yesu kukhala kwamphamvu chotero? Zisonyezero za kutengeka maganizo? Ayi; Yesu analankhula mwaulemu. Komabe, nthaŵi zonse anali ndi chonulirapo cha kufika mitima ya omvetsera ake. Chifukwa chakuti anaganizira anthu, anadziŵa mmenedi akanawasonkhezerera. Anagwiritsira ntchito mafanizo omveka bwino, ndi ofeŵa amene anasonyeza zinthu zozoloŵereka za moyo wa tsiku ndi tsiku. (Mateyu 13:34) Mofananamo, awo amene amapereka nkhani pa misonkhano yathu ayenera kutsanzira Yesu mwa kupereka nkhani zogwira mtima, zotentha zimene zimasonkhezera. Mofanana ndi Yesu, ife tingayeseyese kupeza mafanizo amene amayenerera omvetsera athu ndi kufika mitima yawo.
8. Kodi Yesu anafulumiza motani ndi chitsanzo, ndipo kodi ndimotani mmene tingamtsanzirire pankhaniyi?
8 Potumikira Mulungu wathu, tonsefe tingafulumizane mwa kupereka chitsanzo. Yesu anafulumizadi omvetsera ake. Anakonda ntchito ya utumiki Wachikristu ndipo analemekeza utumiki. Iye anati unali ngati chakudya chake. (Yohane 4:34; Aroma 11:13) Changu chotero chingakhale choyambukira. Kodi nanunso mungachititse chisangalalo chanu cha mu utumiki kuonekera? Uzani ena za zokumana nazo zanu zabwino mumpingo, pamene mukupeŵa mosamala kachitidwe ka kudzitamandira. Pamene mupempha ena kukagwira nanu ntchito, onani ngati mungawathandize kupeza chisangalalo chenicheni cha kulankhula ndi ena za Yehova, Mlengi wathu Wamkulu.—Miyambo 25:25.
9. (a) Kodi njira zina nzotani za kufulumiza ena zimene tiyenera kuzipeŵa, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi nchiyani chimene chiyenera kutisonkhezera kudzipereka mu utumiki wa Yehova?
9 Komabe, samalani kusafulumiza ena m’njira yolakwa. Mwachitsanzo, mwina popanda cholinga chimenecho tingawachititse kumva kukhala aliwongo ponena za kusachita zambiri. Tingawachititse kukhala ndi manyazi popanda cholinga chimenecho mwa kuwayerekezera ndi ena amene mwachionekere ali okangalika, kapena mwina tingaike miyezo yeniyeni ndi kufooketsa awo amene sakuikwaniritsa. Iliyonse ya njira zimenezi ingasonkhezere ena kuchitapo kanthu kwakanthaŵi, komatu Paulo sanalembe kuti, ‘Fulumizanani ku kupatsana liwongo ndi ntchito zabwino.’ Ayi, tiyenera kufulumizana ku chikondano, pamenepo ntchito zabwino zidzatsatira chifukwa cha chisonkhezero chabwino. Palibe aliyense amene ayenera kusonkhezeredwa makamaka chifukwa cha kuganizira zimene ena mumpingo adzaganiza ponena za iye ngati sakwaniritsa kwenikweni zimene ayenera kuchita.—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 9:6, 7.
10. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukumbukira kuti sitili ambuye pa chikhulupiriro cha ena?
10 Kufulumizana sikumatanthauza kulamulirana. Ngakhale kuti anapatsidwa ulamuliro ndi Mulungu, mtumwi Paulo modzichepetsa anakumbutsa mpingo wa Akorinto: “Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu.” (2 Akorinto 1:24) Ife monga iye ngati tizindikira kuti kusankhira ena zimene ayenera kuchita mu utumiki wa Yehova sikuli thayo lathu, kapena kulamulira zikumbumtima zawo m’zosankha zawo zina za munthu mwini, tidzapeŵa kukhala ‘wopambanitsa pa kulungama,’ opanda chimwemwe, olimbirira, oipidwa, kapena olamulira. (Mlaliki 7:16) Mikhalidwe yotero simachititsa kufulumizana; imatsendereza.
11. Kodi nchiyani chimene chinasonkhezera anthu kupereka zopereka m’masiku a kumangidwa kwa chihema cha Israyeli, ndipo kodi zimenezo zingakhale choncho motani m’tsiku lathu?
11 Tikufuna kuti zoyesayesa zonse mu utumiki wa Yehova zichitidwe mu mzimu wofanana monga mu Israyeli wakale pamene zopereka zomangira chihema zinafunika. Eksodo 35:21 amaŵerengedwa kuti: “Ndipo anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wamfunitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha kuntchito.” Iwo sanasonkhezeredwe mongodzionetsera chabe koma anasonkhezereka kuchokera mkati, kuchokera mu mtima. Kwenikweni, panopo Chihebri chimaŵerengedwa kuti “aliyense amene mtima wake unamnyamutsa” anapereka mphatsozo. (Kanyenye ngwathu.) Ndiponso, tiyeni tiyeseyese kunyamutsana mitima panthaŵi iliyonse pamene tili pamodzi. Mzimu wa Yehova udzakwaniritsa mbali yotsalayo.
‘Dandauliranani’
12. (a) Kodi ndi ati amene ali matanthauzo ena a liwu Lachigiriki lotembenuzidwa kuti ‘dandaulira’? (b) Kodi ndimotani mmene mabwenzi a Yobu analepherera kumlimbikitsa? (c) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa kuweruzana?
12 Pamene Paulo analemba kuti tiyenera ‘kudandaulirana,’ anagwiritsira ntchito liwu Lachigiriki lakuti pa·ra·ka·leʹo, limene lingatanthauzenso ‘kulimbitsa, kutonthoza.’ M’matembenuzidwe a Septuagint Yachigiriki liwu limodzimodzili linagwiritsiridwa ntchito pa Yobu 29:25, pamene Yobu anafotokozedwa monga munthu amene amatonthoza olira maliro. Komabe, pamene Yobu mwiniyo anali m’mayesero aakulu, sanalandire chilimbikitso chotero. “Otonthoza” ake atatu anali otanganitsidwa ndi kumuimba mlandu ndi kumlangiza kwakuti analephera kumumvetsetsa kapena kumchitira chisoni. Kwenikweni, m’kulankhula kwawo konse, sanatchule Yobu ndi dzina ngakhale kamodzi kokha. (Siyanitsani ndi Yobu 33:1, 31.) Mwachionekere anamuona kukhala vuto m’malo mwa kumuona monga munthu. Mposadabwitsa kuti Yobu motaya mtima anati kwa iwo: “Moyo wanu ukadakhala m’malo mwa moyo wanga”! (Yobu 16:4) Chimodzimodzinso lerolino, ngati mukufuna kulimbikitsa wina, mchitireni chifundo! Musaweruze. Monga momwe Aroma 14:4 amanenera, “ndani iwe wakuweruza mnyamata wa mwini wake? Iye aimirira kapena kugwa kwa mbuye wake wa mwini yekha. Ndipo adzaimiritsidwa; pakuti [Yehova, NW] ali wamphamvu kumuimiritsa.”
13, 14. (a) Kodi ndi mfundo yoona yotani imene tifunikira kukhutiritsa nayo abale ndi alongo athu kuti tiwatonthoze? (b) Kodi Danieli analimbitsidwa motani ndi mngelo?
13 Liwu la mtundu wa pa·ra·ka·leʹo ndi dzina lake logwirizanitsidwa nalo limatembenuzidwa kuti “chitonthozo” pa 2 Atesalonika 2:16, 17: “Ndipo Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa [chitonthozo, NW] chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo, [atonthoze, NW] mitima yanu, nakhazikitse inu mu ntchito yonse ndi mawu onse abwino.” Onani kuti Paulo akugwirizanitsa lingaliro la kuchititsa mtima wathu kutonthozedwa ndi mfundo yoona yakuti Yehova amatikonda. Chotero tingalimbikitsane ndi kutonthozana mwa kutsimikizira mfundo yofunika yoona imeneyo.
14 Panthaŵi ina mneneri Danieli anavutika maganizo kwambiri ataona masomphenya owopsa kwakuti anati: “Kukoma kwanga kunasandulika chivundi mwa ine, wosakhalanso ndi mphamvu ine.” Yehova anatumiza mngelo amene anakumbutsa Danieli nthaŵi zingapo kuti iye anali “wokondedwatu” pamaso pa Mulungu. Chotulukapo chake? Danieli anauza mngeloyo: “Mwandilimbikitsa.”—Danieli 10:8, 11, 19.
15. Kodi akulu ndi oyang’anira oyendayenda ayenera kupereka chiyamikiro ndi chiwongolero choyenerera motani?
15 Nayi tsopano njira ina yolimbikitsira ena. Ayamikireni! Kuloŵa mu mzimu wa kusuliza ndi wankhalwe nkosavuta kwambiri. Zoonadi, pali nthaŵi zina pamene kuwongolera kungakhale kofunika, makamaka kochitidwa ndi akulu ndi oyang’anira oyendayenda. Koma kungakhale bwino ngati angakumbukiridwe chifukwa cha chilimbikitso chawo chachikondi m’malo mwa kukhala ndi mkhalidwe wofuna kupezera chifukwa.
16. (a) Polimbikitsa ochita tondovi, kodi nchifukwa ninji kaŵirikaŵiri kuli kosakwanira kungowalimbikitsa kuchita zambiri mu utumiki wa Yehova? (b) Kodi Yehova anathandiza motani Eliya pamene anali wochita tondovi?
16 Awo amene makamaka ali ochita tondovi amafuna chilimbikitso, ndipo Yehova amafuna ifeyo monga Akristu anzawo kukhala opereka chithandizo—makamaka ngati tili akulu. (Miyambo 21:13) Kodi tingachitenji? Yankho lake silingakhale losavuta kwambiri monga ngati kungowauza kuchita zambiri mu utumiki wa Yehova. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti zimenezo zingapereke lingaliro lakuti kuchita tondovi kwawo nkochititsidwa ndi kusachita kwawo zokwanira. Kaŵirikaŵiri sizili choncho. Panthaŵi ina mneneri Eliya anachita tondovi kwakukulu kwakuti anafuna kufa; komabe zimenezi zinachitika panthaŵiyo pamene anali wotanganitsidwa kwambiri mu utumiki wake wa Yehova. Kodi Yehova anachita naye motani? Anatumiza mngelo kukampatsa thandizo labwino. Eliya anaululira Yehova za kukhosi, akumanena kuti analingalira kuti anali wopanda pake mofanana ndi makolo ake amene anamwalira, kuti ntchito yake inachitidwa mwachabe, ndi kuti anali yekhayekha. Yehova anamvetsera ndi kumtonthoza ndi zisonyezero zochititsa mantha za mphamvu Yake ndipo anamtsimikiziritsa kuti sanali yekha konse ndi kuti ntchito imene anali atayamba idzamalizidwa. Yehova analonjezanso kupatsa Eliya bwenzi loti aliphunzitse limene potsirizira pake lidzamloŵa m’malo.—1 Mafumu 19:1-21.
17. Kodi mkulu angalimbikitse motani munthu amene amadzisuliza mopambanitsa?
17 Ha, nzolimbikitsa chotani nanga! Nafenso tilimbikitsetu awo amene ali pakati pathu amene ali ovutika mtima. Yesayesani kuwamvetsetsa mwa kumvetsera! (Yakobo 1:19) Perekani chitonthozo cha m’Malemba chogwirizana ndi zosoŵa zawo. (Miyambo 25:11; 1 Atesalonika 5:14) Kuti alimbikitse awo amene amadzisuliza kwambiri, akulu angapereke umboni wa m’Malemba mokoma mtima wakuti Yehova amawakonda ndipo amawaŵerengera.a Kukambitsirana za dipo kungakhale njira ina yamphamvu yolimbikitsira awo amene amadziona kukhala opanda pake. Munthu amene ali ndi chisoni chifukwa cha tchimo lina lakale angafunikire kusonyezedwa kuti dipo lamuyeretsa ngati walapadi ndi kutembenuka pa mchitidwe uliwonse wotero.—Yesaya 1:18.
18. Kodi chiphunzitso cha dipo chiyenera kugwiritsiridwa ntchito motani polimbikitsa munthu amene wachitiridwa tchimo ndi wina, monga ngati mwa kugwiriridwa chigololo?
18 Ndithudi, mkulu adzasinkhasinkha za munthuyo kotero kuti agwiritsire ntchito bwino chiphunzitsocho. Talingalirani za chitsanzochi: Nsembe ya dipo ya Kristu inaphiphiritsiridwa ndi nsembe zanyama za Chilamulo cha Mose, zimene zinafunidwa kutetezera machimo onse. (Levitiko 4:27, 28) Komabe, panalibe lamulo lakuti wogwiriridwa chigololo anafunikira kupereka nsembe ya tchimo yotero. Chilamulocho chinati iwo ‘asamamchitira kanthu’ kumlanga. (Deuteronomo 22:25-27) Chotero, ngati mlongo lerolino waukiridwa ndi kugwiriridwa chigololo, ndipo zamchititsa kudziona kukhala wodetsedwa ndi wopanda pake, kodi kukakhala koyenera kugogomezera kufunikira kwa dipo la kuyeretsera tchimo limenelo? Ayi ndithudi. Iyeyo sanachimwe pa kuukiridwako. Wogwirira chigololoyo ndiye anachimwa ndipo afunikira kuyeretsedwa. Komabe, chikondi chosonyezedwa ndi Yehova ndi Kristu pa kupereka dipo chingagwiritsiridwe ntchito monga umboni wakuti iyeyo sanadetsedwe pamaso pa Mulungu ndi tchimo la munthu wina koma kuti iye ali wamtengo wapatali kwa Yehova ndipo amakondedwabe naye.—Yerekezerani ndi Marko 7:18-23; 1 Yohane 4:16.
19. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuyembekezera kuti kuyanjana kwathu konse ndi abale ndi alongo kudzakhala kolimbikitsa, komano kodi tiyenera kutsimikiziranji?
19 Inde, uliwonse umene ungakhale mkhalidwe wa munthu m’moyo, mosasamala kanthu za mikhalidwe iliyonse yopweteka imene ingaipitse mbiri yake yakale, ayenera kukhala wokhoza kupeza chilimbikitso mumpingo wa anthu a Yehova. Ndipo iye adzatero ngati ife aliyense payekha tiyesayesa kuganizirana wina ndi mnzake, kufulumizana, ndi kudandaulirana nthaŵi iliyonse pamene tisonkhana. Komabe, pokhala tili opanda ungwiro, nthaŵi zina tonsefe timalephera kuchita motero. Mwachisoni, timagwiritsana mwala ndipo ngakhale kuŵaŵitsana mitima panthaŵi ndi nthaŵi. Yesani kusasumika maganizo pa zofooka za ena pankhaniyi. Ngati musumika maganizo pa zophophonya, mudzadziika pangozi ya kukhala wosuliza kwambiri mpingo ndipo mwina mungagwere mu msampha weniweniwo umene Paulo anafunitsitsa kutithandiza kuupeŵa, ndiko kuti, kuleka kusonkhana kwathu pamodzi. Zimenezo zisachitiketu! Pamene dongosolo ili lakale likufikira kukhala langozi ndi lotsendereza kwambiri, tiyeni tikhale otsimikizira kuchita zimene tingathe kupangitsa mayanjano athu pamisonkhano kukhala omangirira—poona tsiku la Yehova likuyandikira!
[Mawu a M’munsi]
a Mkulu angasankhe kuŵerenga nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi anthu otero—mwachitsanzo, nkhani yakuti “Kodi Mudzapindula ndi Chisomo?” ndi “Kupambana Nkhondo Yolimbana ndi Kuchita Tondovi.”—Nsanja ya Olonda ya February 15 ndi March 1, 1990.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti misonkhano ndi mayanjano athu akhale olimbikitsa m’masiku ano otsiriza?
◻ Kodi kuganizirana kumatanthauzanji?
◻ Kodi kufulumizana kumatanthauzanji?
◻ Kodi nchiyani chimene chimaloŵetsedwa m’kudandaulirana?
◻ Kodi ochita tondovi angadandauliridwe motani?
[Chithunzi patsamba 16]
Kuchereza alendo kumatithandiza kudziŵana bwino
[Chithunzi patsamba 18]
Pamene Eliya anali wochita tondovi, Yehova mokoma mtima anamtonthoza