Danieli
10 Mʼchaka chachitatu cha ulamuliro wa Mfumu Koresi+ ya Perisiya, Mulungu anamuululira nkhani inayake Danieli, amene ankadziwikanso ndi dzina lakuti Belitesazara.+ Nkhani imene anauzidwayo inali yoona ndipo inali yokhudza nkhondo yaikulu. Danieli anamvetsa nkhani imeneyi ndipo anathandizidwa kumvetsa zinthu zimene anaonazo.
2 Masiku amenewo, ineyo Danieli, ndinakhala ndikulira+ kwa milungu itatu yathunthu. 3 Sindinadye chakudya chokoma, sindinadye nyama kapena kumwa vinyo ndipo sindinadzole mafuta aliwonse kwa milungu itatu yathunthu. 4 Pa tsiku la 24 la mwezi woyamba, ndili mʼmbali mwa mtsinje waukulu, mtsinje wa Tigirisi,*+ 5 ndinaona munthu atavala nsalu+ ndipo mʼchiuno mwake anali atamangamo lamba wa golide wa ku Ufazi. 6 Thupi lake linkanyezimira ngati mwala wa kulusolito,+ nkhope yake inkawala ngati mphezi, maso ake ankaoneka ngati miyuni yamoto, manja ake komanso mapazi ake ankaoneka ngati kopa*+ wonyezimira, ndipo mawu ake ankamveka ngati mawu a gulu lalikulu la anthu. 7 Ine ndekha Danieli, ndi amene ndinaona masomphenyawo+ koma amuna amene ndinali nawo sanawaone. Komabe iwo anayamba kunjenjemera kwambiri ndipo anathawa nʼkukabisala.
8 Choncho ndinatsala ndekha ndipo nditaona masomphenya odabwitsawa, mphamvu zonse zinandithera. Nkhope yanga imene inkaoneka yolemekezeka inasintha kwambiri, moti ndinalibenso mphamvu.+ 9 Kenako ndinamva munthu uja akulankhula. Koma nditamva kuti akulankhula, ndinagona pansi chafufumimba nʼkugona tulo tofa nato.+ 10 Ndiyeno ndinamva dzanja likundikhudza+ ndipo linandigwedeza kuti ndidzuke. Nditadzuka ndinagwada nʼkugwira pansi ndi manja anga. 11 Kenako iye anandiuza kuti:
“Iwe Danieli, munthu wokondedwa* kwambiri,+ mvetsera mwatcheru mawu amene ndikufuna kukuuza. Tsopano imirira chifukwa ine ndatumidwa kwa iwe.”
Atandiuza zimenezi, ndinaimirira koma ndikunjenjemera.
12 Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Iwe Danieli, usachite mantha.+ Mawu ako akhala akumveka kuyambira tsiku loyamba pamene unatsegula mtima wako kuti umvetse tanthauzo la zinthu zimenezi, ndiponso pamene unadzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, ndipo ine ndabwera chifukwa cha mawu akowo.+ 13 Koma kalonga+ wa ufumu wa Perisiya ananditsekereza kwa masiku 21. Ndiyeno Mikayeli,*+ mmodzi wa akalonga aakulu,* anabwera kudzandithandiza. Pa nthawi imeneyo ndinakhalabe pomwepo pafupi ndi mafumu a Perisiya. 14 Ine ndabwera kudzakuthandiza kuti umvetse zimene zidzachitikire anthu a mtundu wako mʼmasiku otsiriza,+ chifukwa masomphenyawa ndi okhudza zimene zidzachitike mʼtsogolo.”+
15 Atandiuza mawu amenewa, ndinayangʼana pansi ndipo sindinathenso kulankhula. 16 Ndiyeno winawake wooneka ngati munthu anandiyandikira nʼkukhudza milomo yanga.+ Atatero, ndinayamba kulankhula ndipo ndinauza amene anali ataimirira patsogolo panga uja kuti: “Mbuyanga, ine ndikunjenjemera chifukwa cha zimene ndaona mʼmasomphenyawa ndipo mphamvu zandithera.+ 17 Choncho ine mtumiki wanu ndingathe bwanji kulankhula nanu mbuyanga?+ Panopa ndilibe mphamvu ndipo ndikupuma movutikira.”+
18 Ndiyeno wooneka ngati munthu uja anandikhudzanso nʼkundipatsa mphamvu.+ 19 Kenako anandiuza kuti: “Iwe munthu wokondedwa kwambiri,*+ usachite mantha.+ Mtendere ukhale nawe.+ Limba mtima, ndithu limba mtima.” Akulankhula nane, ndinalimbikitsidwa ndipo ndinanena kuti: “Lankhulani mbuyanga chifukwa inu mwandilimbikitsa.”
20 Ndiyeno anandiuza kuti: “Kodi ukudziwa chifukwa chake ndabwera kwa iwe? Tsopano ndibwerera kuti ndikamenyane ndi kalonga wa Perisiya.+ Ndikachoka, kalonga wa Girisi abwera. 21 Komabe ndikuuza zinthu zimene zinalembedwa mʼbuku la choonadi. Palibe aliyense amene akundithandiza kwambiri pa zinthu zimenezi kupatulapo Mikayeli,+ amene ndi kalonga wanu.”+