Tidane Nacho Choipa
YEHOVA ndi Mulungu woyera. M’nthaŵi zakale anali “Woyera wa Israyeli,” ndipo pokhala wotero analamula kuti Israyeli akhalenso woyera, wosadetsedwa. (Salmo 89:18) Anauza anthu ake osankhidwa kuti: “Chifukwa chake mukhale oyera, popeza ine ndine woyera.” (Levitiko 11: 45) Aliyense amene anafuna ‘kukwera m’phiri la Yehova’ anafunikira kukhala “woyera m’manja ndi woona m’mtima.” (Salmo 24:3, 4) Zimenezo zinatanthauza zoposa kungopeŵa chabe machitidwe auchimo. Zinatanthauza ‘kudana nacho choipa.’—Miyambo 8:13.
Mwachikondi, Yehova anakhazikitsa malamulo atsatanetsatane kotero kuti mtundu wa Israyeli ukanatha kuzindikira ndi kupeŵa cholakwa. (Aroma 7:7, 12) Malamulo ameneŵa anaphatikizapo zitsogozo zamphamvu za makhalidwe abwino. Chigololo, mathanyula, kugonana pachibale, ndi kugona nyama zonsezo zinasonyezedwa kukhala zodetsa zauzimu. (Levitiko 18:23; 20:10-17) Awo amene anali ndi liwongo la machitidwe oipa ameneŵa anali kusadzidwa pa mtundu wa Israyeli.
Pamene mpingo wa Akristu odzozedwa unakhala “Israyeli wa Mulungu,” miyezo yamakhalidwe yofananayo inaperekedwa kwa iwo. (Agalatiya 6:16) Akristunso anayenera ‘kudana nacho choipa.’ (Aroma 12:9) Mawu a Yehova kwa Aisrayeli anagwiranso ntchito kwa iwo: “Muzikhala oyera mtima, pakuti ine ndine woyera mtima.” (1 Petro 1:15, 16) Machitachita odetsa oterowo monga dama, chigololo, mathanyula, kugona nyama, ndi kugonana pachibale sizinayenera kudzaipitsa mpingo wachikristuwo. Aja amene anakana kuleka kuchita zinthu zoterozo sanali kudzaphatikizidwa mu Ufumu wa Mulungu. (Aroma 1:26, 27; 2:22; 1 Akorinto 6:9, 10; Ahebri 13:4) ‘M’masiku otsiriza’ ano, miyezo yofananayo imagwira ntchito kwa “nkhosa zina.” (2 Timoteo 3:1; Yohane 10:16) Monga chotulukapo chake, Akristu odzozedwa ndi nkhosa zina amapanga mtundu wa anthu oyera ndi abwino, okhoza kutenga dzina la Mulungu wawo monga Mboni za Yehova.—Yesaya 43:10.
Kusunga Mpingo Woyera
Mosemphana ndi zimenezo, dziko limalekerera mitundu yonse ya makhalidwe oipa. Ngakhale kuti Akristu oona ngosiyana, sayenera kuiŵala kuti ambiri amene tsopano akutumikira Yehova nthaŵi ina anali kudziko. Pali ambiri amene, asanadziŵe Mulungu wathu woyera, analibe chifukwa cholekera kukhutiritsa zolingalira ndi zikhumbo zawo zathupi lochimwa, akumakunkhulika mu “kusefukira komwe kwa chitayiko.” (1 Petro 4:4) Mtumwi Paulo, pambuyo pofotokoza machitachita onyansa a anthu oipa amitundu, anati: “Ena a inu munali otere.” Ngakhalebe anatero, anapitiriza kuti: “Koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.”—1 Akorinto 6:11.
Amenewotu ndi mawu otonthoza! Chilichonse chimene munthu anachita poyambirira m’moyo, amadzasintha pamene uthenga wabwino waulemerero wa Kristu ukhudza mtima wake. Amasonyeza chikhulupiriro ndi kudzipatulira kwa Yehova Mulungu. Kuyambira pamenepo kumka mtsogolo amakhala ndi moyo woyera mwa makhalidwe, wosambitsidwa pamaso pa Mulungu. (Ahebri 9:14) Machimo amene anachita mmbuyomu amakhululukidwa, ndipo angathe “kutambalitsira za mtsogolo.”a—Afilipi 3:13, 14; Aroma 4:7, 8.
Yehova anakhululukira Davide wolapayo pa mbanda ndi chigololo chake, ndipo anakhululukiranso Manase wolapayo pakulambira kwake mafano konyansa ndi kukhetsa kwake mwazi wochuluka. (2 Samueli 12:9, 13; 2 Mbiri 33:2-6, 10-13) Tingayamikiredi kuti ali wokonzekera kutikhululukira nafenso ngati tilapa ndi kumfikira moona mtima ndi modzichepetsa. Komabe, mosasamala kanthu kuti Yehova anakhululukira Davide ndi Manase, amuna aŵiri ameneŵa—ndi Aisrayeli onse—anafunikira kukumana ndi zotulukapo za machitidwe awo auchimo. (2 Samueli 12:11, 12; Yeremiya 15:3-5) M’njira yofananayo, ngakhale kuti Yehova amakhululukira ochimwa nalapa, pangakhalabe zotulukapo za machitidwe awo zimene sizingapeŵedwe.
Zotulukapo Zosapeŵeka
Mwachitsanzo, munthu wa moyo wachiwerewere amene anatenga AIDS angalandire choonadi ndi kutembenuka mpaka pa sitepe la kudzipatulira ndi ubatizo. Tsopano ali Mkristu woyera mwauzimu wokhala ndi unansi ndi Mulungu ndipo chiyembekezo chodabwitsa chamtsogolo; komabe adakali ndi AIDS. Potsirizira pake iye angafe nayo nthendayo, chotulukapo chachisoni koma chosapeŵeka cha khalidwe lake lakale. Kwa Akristu ena ziyambukiro za makhalidwe oipitsitsa akale zingapitirizebe m’njira zina. Kwa zaka zambiri pambuyo pa ubatizo wawo, mwinamwake kwamoyo wawo wonse m’dongosolo lino la zinthu, angafunikire kulimbana ndi zilakolako zathupi lawo kuti abwerere ku njira yamoyo wawo wakale wachisembwere. Ndi chithandizo cha mzimu wa Yehova, ambiri amapambana podziletsa. Koma amafunikira kumenya nkhondo yosalekeza.—Agalatiya 5:16, 17.
Oterowo sakuchimwa malinga ngati amalamulira zilakolako zawo. Koma ngati ali amuna, mwa nzeru angasankhe ‘kusakalimira’ mathayo mumpingo pamene adakalimbanabe ndi zilakolako zamphamvu zathupi. (1 Timoteo 3:1) Chifukwa nchiyani? Chifukwa amadziŵa chidaliro chimene mpingo uli nacho mwa akulu. (Yesaya 32:1, 2; Ahebri 13:17) Amazindikira kuti akulu amafikiridwa ndi nkhani zambiri zachinsinsi ndipo amafunikira kusamalira nkhani zowopsa. Sikungakhale chikondi, nzeru, kapena kuganiza bwino kuti wina amene ali pankhondo yolimbana ndi zikhumbo zonyansa zathupi akalimire malo a thayo ngati amenewo.—Miyambo 14:16; Yohane 15:12, 13; Aroma 12:1.
Kwa munthu amene anali wogona ana asanabatizidwe, pangakhale chotulukapo china. Pamene aphunzira choonadi, amalapa ndi kutembenuka, osabweretsa tchimo lake lankhalwelo mumpingo. Pambuyo pake angapite patsogolo, kuzilakiratu zilakolako zake zoipa zija, ndipo ngakhale kufuna ‘kukalimira’ malo athayo mumpingo. Komabe, bwanji ngati anthu m’chitaganya akumdziŵabe kuti anali wogona ana? Kodi angakhalebe “wopanda chirema,. . . wochitiridwa umboni wabwino ndi anthu akunja,. . . wopanda chinenezo”? (1 Timoteo 3:1-7, NW; Tito 1:7) Kutalitali. Chotero, sangayenerere mathayo a mpingo.
Pamene Mkristu Wodzipatulira Achimwa
Yehova amazindikira kuti ndife ofooka ndi kuti ngakhale pambuyo pa ubatizo tingagwere m’tchimo. Mtumwi Yohane analembera Akristu a m’tsiku lake kuti: “Izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama; ndipo Iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.” (1 Yohane 2:1, 2) Indedi, pa maziko a nsembe ya Yesu, Yehova adzakhululukira Akristu obatizidwa amene akugwera m’tchimo—ngati iwo alapadi moona mtima ndi kusiya njira yawo yolakwa.
Chitsanzo cha chimenechi chinaoneka mumpingo wa ku Korinto m’zaka za zana loyamba. Mtumwi Paulo anamva za nkhani ya dama lapachibale mumpingo wanthete umenewo, ndipo analangiza kuti munthu amene anachita zimenezoyo achotsedwe. Pambuyo pake, wochimwayo analapa, ndipo Paulo analamula mpingo kuti umbwezeretse. (1 Akorinto 5:1, 13; 2 Akorinto 2:5-9) Motero, mwa mphamvu yochiritsa ya kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova, ndi mtengo waukulu wansembe ya dipo ya Yesu, munthuyo anayeretsedwa pa tchimo lake. Zinthu zofananazo zingachitike lero. Komanso, ngakhale ngati munthu wobatizidwa amene wachita tchimo alapa ndi kukhululukidwa ndi Yehova, pangakhalebe zotulukapo zopitirizabe zatchimo lake.—Miyambo 10:16, 17; Agalatiya 6:7.
Mwachitsanzo, ngati mtsikana wodzipatulira wachita dama, angamve chisoni kwambiri ndi kachitidwe kakeko ndipo potsirizira pake nkubwezeretsedwa ku thanzi lauzimu mwa chithandizo champingo. Koma bwanji ngati ali ndi pathupi chifukwa cha chisembwere chake? Pamenepo moyo wake wonse mosapeŵeka wasintha ndi zimene anachita. Mwamuna amene anachita chigololo angalape ndi kusachotsedwa. Koma mnzake wa muukwati wopanda liwongoyo ali ndi zifukwa za m’Malemba zomsudzulira, ndipo angasankhe kutero. (Mateyu 19:9) Ngati mkaziyo amsudzula, mwamunayo, ngakhale wakhululukidwa ndi Yehova, adzakhala ndi zotulukapo zopweteka za tchimo lakelo kwa moyo wake wonse.—1 Yohane 1:9.
Bwanji nanga za mwamuna amene mwadyera asudzula mkazi wake kuti akakwatire mkazi wina? Angathe kulapa potsirizira pake ndi kubwezeretsedwa mumpingo. M’kupita kwa zaka angapite patsogolo ndi ‘kupitirira kutsata ukulu msinkhu.’ (Ahebri 6:1) Koma malinga ngati mkazi wake woyamba akhalabe wosakwatiwa, mwamunayo sangayenerere kutumikira pa malo a thayo mumpingo. Saali “mwamuna wa mkazi mmodzi” chifukwa analibe maziko a m’Malemba osudzulira mkazi wake woyamba.—1 Timoteo 3:2, 12.
Kodi zimenezi si zifukwa zamphamvu zoti Mkristu akulitse kunyansidwa kwake ndi chimene chili choipa?
Bwanji Za Wogona Ana?
Bwanji ngati Mkristu wachikulire wobatizidwa agona mwana? Kodi wochimwayo ndi woipa kwambiri kwakuti Yehova sangamkhululukire konse? Ayi sichoncho. Yesu anatero kuti ‘kuchitira mwano mzimu woyera’ ndiko kunali kosakhululukidwa. Ndipo Paulo anati palibenso nsembe ya machimo kwa iye amene abwerezabwereza tchimo mwadala mosasamala kanthu za kudziŵa kwake choonadi. (Luka 12:10; Ahebri 10:26, 27) Koma palibe paliponse pamene Baibulo limanena kuti Mkristu wachikulire amene agona mwana—kaya wachibale kapena wina—sangakhululukidwe. Ndithudi, machimo ake angayeretsedwe ngati alapa moona kuchokera mumtima ndi kusintha mayendedwe ake, koma angafunikire kulimbanabe ndi zilakolako za thupi zolakwa zimene anakulitsa. (Aefeso 1:7) Ndipo pangakhale zotulukapo zimene sangathe kupeŵa.
Zikumadalira pa lamulo la m’dziko limene amakhala, wogona ana angafunikire kuloŵa ndende kapena kupatsidwa zilango zina za Boma. Mpingo sumtetezera pazimenezi. Ndiponso, munthuyo wasonyeza chifooko chachikulu chimene tsopano chiyenera kulingaliridwa mwamphamvu. Ngati aoneka kuti walapa, adzalimbikitsidwa kupita patsogolo mwauzimu, kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda, ngakhale kutenga mbali mu Sukulu Yautumiki Wateokrase ndi mbali zosakhala zophunzitsa pa Msonkhano Wautumiki. Komabe, izi sizikutanthauza kuti angayenerere kutumikira pa malo a thayo mumpingo. Kodi zifukwa za m’Malemba ndi zotani pankhaniyi?
Choyamba, mkulu ayenera kukhala “wodziletsa.” (Tito 1:8, NW) Zoona, palibe aliyense wa ife ali nako kudziletsa kotheratu. (Aroma 7:21-25) Koma Mkristu wachikulire wodzipatulira amene agwera m’tchimo la kugona mwana amasonyeza chifooko cha thupi chachilendo. Zochitika zasonyeza kuti wachikulire woteroyo angagwirirenso ana ena. Ndithudi, sikuti aliyense wogona ana amabwerezanso tchimolo, koma ambiri amatero. Ndipo mpingo sungathe kupenda mitima koti nkudziŵa amene angabwerezenso kapena amene sangabwerezenso kugona ana. (Yeremiya 17:9) Chotero, uphungu wa Paulo kwa Timoteo ukugwira ntchito ndi chigogomezero champhamvu kwa achikulire amene anagonapo ana: “Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni.” (1 Timoteo 5:22) Kaamba kofuna kutetezera ana athu, munthu wodziŵika kuti anali wogona ana sangayenerere malo a thayo mu mpingo. Ndiponso sangakhale mpainiya, kapena kutumikira m’mbali ina iliyonse yautumiki wanthaŵi zonse.—Yerekezerani ndi pulinsipulo la pa Eksodo 21:28, 29.
Ena angafunse kuti, ‘Kodi ena sanachite machimo amitundu ina ndipo mwachionekere nkulapa, kenaka nkudzabwerezanso machimowo pambuyo pake?’ Inde, zimenezo zachitikadi, koma pali mbali zina zoyenera kuzilingalira. Mwachitsanzo, ngati wachikulire akopa mwauchiwerewere wachikulire wina, wachikulireyo ayenera kukhala wokhoza kukana zonyengerera za winayo. Ana ngosavuta kuwanyenga, kuwasokoneza, kapena kuwawopseza. Baibulo limanena za kupanda nzeru kwa mwana. (Miyambo 22:15; 1 Akorinto 13:11) Yesu anagwiritsira ntchito ana monga chitsanzo cha kudzichepetsa koona mtima. (Mateyu 18:4; Luka 18:16, 17) Kuona mtima kwa mwana kumaphatikizapo kupandiratu chidziŵitso. Ana ambiri ngomasuka, ofunitsitsa kukondweretsa wina, choncho ngosavuta kunyengezedwa ndi wachikulire wopseterera amene iwo amadziŵa ndi kumdalira. Chifukwa cha chimenecho, mpingo uli ndi thayo pamaso pa Yehova la kutetezera ana.
Ana olangizidwa bwino amaphunzira kumvera ndi kulemekeza makolo awo, akulu, ndi achikulire ena. (Aefeso 6:1, 2; 1 Timoteo 5:1, 2; Ahebri 13:7) Kungakhale kuyaluka koopsa ngati mmodzi wa olemekezeka ameneŵa angagwiritsire ntchito molakwa chidaliro choona mtima cha mwana wosadziŵa kanthuyo ndi kumnyengeza kapena kumuumiriza kuti agonjere kugonedwa naye. Awo amene anagonedwapo mwa njira imeneyi kaŵirikaŵiri amavutika kwa zaka zambiri kuti aiŵale nsautso yamaganizo imene inatsatirapo. Chotero, wogona ana woteroyo mpingo umampatsa chilango chachikulu ndi ziletso. Si malo ake monga munthu wolemekezeka amene ayenera kukhala chodetsa nkhaŵa, m’malo mwake, ndi chiyero chopanda banga cha mpingo.—1 Akorinto 5:6; 2 Petro 3:14.
Ngati wogona ana alapa moona mtima, adzaona nzeru yogwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo. Ngati aphunziradi kudana nacho choipa, adzanyansidwa ndi zimene anachita ndi kulimbikira kupeŵa kubwerezanso tchimo lakelo. (Miyambo 8:13; Aroma 12:9) Ndiponso, ayeneradi kuyamikira Yehova pachikondi Chake chachikulu, kuti munthu wochimwa wolapa monga iye, angalambirebe Mulungu wathu woyera ndi kuyembekeza kudzapezeka pakati pa “oongoka mtima” amene adzakhala padziko lapansi kosatha.—Miyambo 2:21.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Mafunso Ochokera Kwa Oŵerenga m’kope la Nsanja ya Olonda ya May 1, 1996.
[Mawu Otsindika patsamba 28]
Pamene kuli kwakuti Yehova amakhululukira ochimwa olapa, pangakhalebe zotulukapo za machitidwe awo zimene sizingapeŵedwe