Thayo Lobala Ana mu Nthaŵi Ino ya Mapeto
“Akuweruza bwino ana awo.”—1 TIMOTEO 3:12.
1. Nchiyani chimene chiri chikhumbo chachibadwa cha akazi ambiri, ndipo ndimotani mmene ichi chimasonyezedwera kumayambiriro m’moyo?
CHIMWEMWE cha ukholo chiri chosakanidwa. Luso lachibadwa la umayi liri lachilengedwe, ngakhale kuti liri lamphamvu mwa akazi ena kusiyana ndi ena. M’maiko ambiri a Kumadzulo, anyamata achichepere ali osangalatsidwa kwambiri m’kuseŵera ndi zoseŵeretsa zachitsulo, pamene kuli kwakuti atsikana achichepere mwachisawawa amakonda tizidoli, timene opanga zoseŵeretsa amakalamira kuzipanga kukhala monga zenizeni monga mmene kungathekere. Atsikana ambiri amakhala ndi moyo kokha kudikira tsiku limene iwo adzakhala okhoza kuyangata, osati chidoli, koma mwana wawo wawo wamoyo, wotentha, womalankhula.
Chimwemwe ndi Mathayo
2. Ndimotani mmene makolo ayenera kulingalira mwana wobadwa chatsopano, ndipo nchiyani chimene iwo ayenera kukonzekera kuchita?
2 Thayo lobala ana limafunikira makolo kulingalira mwana wobadwa chatsopanoyo osati chinthu choseŵeretsa koma monga chinthu cholengedwa kaamba ka chimene moyo wake ndi mtsogolo mwake iwo ali oŵerengera kwa Mlengi. Pamene iwo abweretsa mwana m’dziko, makolo ayenera kukonzekera kutenga thayo lalikulu ndi kulinganiza zinthu mofananamo. Iwo akuyamba pa programu ya zaka 20 zakudyetsa, kuveka, chisamaliro chaumoyo, ndi maphunziro, yokhala ndi chotulukapo chake chosanenedweratu.
3. Nchifukwa ninji Miyambo 23:24, 25 ingagwiritsiridwe ntchito kwa makolo ambiri Achikristu?
3 Mwachimwemwe, makolo ambiri Achikristu alera ana omwe akhala okhulupirika, atumiki odzipereka a Yehova. Ena awona ana awo akukula ndi kulowa mu utumiki wa nthaŵi zonse monga ngati apainiya, amishonale, kapena ziwalo za banja la Beteli. Za makolo oterowo mowonadi chinganenedwe kuti: “Atate wa wolungama adzasekeradi; wobala mwana wanzeru adzakondwera naye. Atate wako ndi amako akondwere, amako wakukubala asekere.”—Miyambo 23:24, 25.
Kuwawidwa Mtima kwa Makolo
4, 5. (a) Nchiyani chimene chimafunidwa mwa Malemba ndi akulu ndi atumiki otumikira omwe ali ndi ana? (b) Ndimotani mmene ana ena atanthauzira “matsoka” kwa atate awo?
4 Koma ichi nthaŵi zonse sichimakhala tero, ngakhale kwa akulu amene ali ndi ana. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndipo kuyenera woyang’anira akhale wopanda chirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, . . . woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wa kukhala nawo ana ake omvera iye ndi kulemekezeka konse; (koma ngati munthu sadziŵa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji mpingo wa Mulungu?)” Paulo akuwonjezera kuti: “Atumiki otumikira akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana awo, ndi iwo a m’nyumba yawo ya iwo okha.”—1 Timoteo 3:2-5, 12, NW.
5 Ndithudi, akulu Achikristu ndi atumiki otumikira sangakhale ndi thayo ngati ana awo, pamene akula, akana kupitiriza kutumikira Yehova. Koma iwo ali ndi thayo kaamba ka ana awo a ang’ono ndi ana achikulire omwe adakali m’nyumba yawo. Akulu ndi atumiki otumikira ataya mwaŵi wabwino kwambiri wa utumiki chifukwa cha kukhala onyalanyaza kapena kulephera mwamphamvu kukwaniritsa zifuno za m’Malemba za “kuweruza bwino ana awo ndi iwo a m’nyumba yawo ya iwo okha.” Kwa oterowo, ndiponso kwa ena ambiri, ana awo awabweretsera iwo kupsyinjika kokulira kuposa chimwemwe. Ndi mobwerezabwereza chotani nanga mmene mwambiwo watsimikizira kukhala wowona: “Mwana wopusa ndiye tsoka la atate wake”!—Miyambo 19:13.
Utate wa Thayo
6. Ndi funso lotani limene amuna Achikristu ayenera kudzifunsa?
6 Amuna onse Achikristu, kaya iwo ali ndi mathayo a mpingo kapena ayi, ayeneranso kulingalira chotulukapo chimene kusamalira ana achichepere kungakhale nako pa uzimu wa akazi awo. Ngati mkazi sali wamphamvu mwauzimu, ndimotani mmene khanda, kapena unyinji wa makanda, ungayambukirire phunziro lake laumwini ndi mwaŵi wa kugawanamo mu ntchito yolalikira?
7. Nchiyani chimene chachitika kwa akazi Achikristu ena, ndipo nchiyani chimene kaŵirikaŵiri chimakhala choyambitsa mkhalidwewu?
7 Kodi amuna nthaŵi zonse amazindikira kuti kusamalira khanda kapena mwana wachichepere kaŵirikaŵiri kumaletsa akazi awo kupeza phindu lokulira kuchokera ku Phunziro la Bukhu la Pampingo, misonkhano ya ku Nyumba ya Ufumu, misonkhano yadera, ndi misonkhano ya chigawo? Mkhalidwe woterowo ungatenge miyezi ingapo, ndipo ngakhale zaka, pamene khanda litsatira khanda linzake. Chiri m’chilengedwe cha zinthucho kuti cholemetsa, m’chochitikachi, chimagwera mokulira pa mayi, osati pa atate. Chawonedwa nthaŵi zina kuti pamene kuli kwakuti amuna ena Achikristu amapita patsogolo mwauzimu, ngakhale ku nsonga ya kufikira pa kugawiridwa mwaŵi mu mpingo, akazi awo amakhala ofooka mwauzimu. Nchifukwa ninji? Kaŵirikaŵiri chiri chifukwa chakuti ana awo achichepere amaletsa akazi awo kusumika malingaliro pa misonkhano, kuchita phunziro la Baibulo lozama, kapena kutengamo mbali yaikulu mu ntchito ya umboni. Kodi utate ungatchedwe kukhala wathayo ngati ulola mikhalidwe yotereroyo kuchitika?
8. Ndimotani mmene atate ambiri amagawanirana thayo la kuyang’anira ana, ndi phindu lotani kwa akazi awo?
8 Mwamwaŵi, ichi sichiri tero nthaŵi zonse. Atate ambiri Achikristu amachita mmene angathere kuthandiza ndi thayo la kuyang’anira ana. Iwo amatenga gawo lawo lotheratu m’kuwona kuti ana awo akukhala chete mkati mwa misonkhano ya mpingo. Ngati khanda lawo liyamba kulira, kapena mwana wawo ayamba kuvutitsa, iwo m’mbali yawo adzamutenga kupita kunja kaamba ka chilango choyenera. Nchifukwa ninji amayi nthaŵi zonse ayenera kukhala amene angaziphonya mbali m’misonkhano? Kunyumba, amuna olingalira amathandiza akazi awo ndi ntchito za panyumba ndi m’kugoneka ana kuti mwamuna ndi mkazi angakhale pansi kusumika maganizo mwabata pa zinthu zauzimu.
9. Nchiyani chimene chimatsimikizira kuti ana sali nthaŵi zonse chokhumudwitsa?
9 Pamene zinthu zalinganizidwa moyenerera mu mpingo, amayi achichepere okhala ndi makanda angagawanemo mu utumiki wa upainiya wothandizira. Ena ali ngakhale apainiya okhazikika. Chotero ana nthaŵi zonse siali chokhumudwitsa. Makolo ambiri Achikristu amasonyeza mzimu wabwino waupainiya.
Opanda Mwana Koma Achimwemwe
10. Nchiyani chimene okwatirana ena alingalira, ndipo ndimotani mmene iwo adalitsidwira?
10 Okwatirana ena achichepere asankha kukhala opanda ana. Ngakhale kuti akazi anali ndi kudzimva kwachibadwa kwa mphamvu kwa kufuna kukhala mayi monga kuja kwa akazi ena, iwo anasankhapo, m’chigwirizano ndi amuna awo, kapena kukhala ndi ana ndi cholinga chofuna kudzipereka iwo eni kukutumikira Yehova nthaŵi zonse. Ambiri a iwo atumikira monga apainiya kapena amishonale. Iwo tsopano angayang’ane m’mbuyo pa zaka zambiri ndi chiyamikiro. Motsimikizirika, iwo abala osati ana akuthupi. Koma iwo akhoza kubala ophunzira atsopano omwe apitiriza mokhulupirika kulambira Yehova. ‘Ana enieni m’chikhulupiriro’ amenewa sadzaiwala nkomwe yemwe anali chiŵiya cha kuwabweretsera iwo “mawu a chowonadi.”—1 Timoteo 1:2; Aefeso 1:13; yerekezani ndi 1 Akorinto 4:14, 17; 1 Yohane 2:1.
11. (a) Ndi kuti kumene okwatirana ambiri opanda ana akutumikira Yehova, ndipo nchifukwa ninji iwo samadandaula? (b) Ndi lemba liti limene lingagwiritsiridwe ntchito kwa okwatirana onse omwe akhala opanda ana “chifukwa cha Ufumu”?
11 Okwatirana ambiri kuzungulira padziko lonse omwe anyalanyaza chimwemwe cha kukhala kholo akhala okhoza kutumikira Yehova mu ntchito yadera, ntchito ya chigawo, kapena pa Beteli. Iwo mofananamo ayang’ana m’mbuyo ndi chikhutiritso pa miyoyo yawo yowonongedwa m’kutumikira Yehova ndi abale awo mu mwaŵi wapadera umenewu. Iwo sadzimvera chisoni. Pamene kuli kwakuti iwo analibe chimwemwe cha kubweretsa ana m’dziko, iwo achita mbali yofunika kwambiri m’kupititsa patsogolo zikondwerero za Ufumu mu mbali zawo zosiyanasiyana za ntchito. Kwa okwatirana amenewa amene akhala opanda ana “chifukwa cha ufumu,” lembali liri logwira ntchito limene limanena kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.”—Mateyu 19:12; Ahebri 6:10.
Nkhani ya Umwini
12. (a) Nchifukwa ninji kubala ana kuli mwaŵi wapadera? (b) Kodi ndi mkati mwa nyengo ziti mmene kubala ana kunali ntchito yopatsidwa ndi Mulungu?
12 Monga mmene tawonera pachiyambi pa kukambitsiranaku, kubala ana iri mphatso yochokera kwa Mulungu. (Masalmo 127:3) Iwo uli mwaŵi wapadera umene zolengedwa zauzimu za Yehova sizimatengamo mbali. (Mateyu 22:30) Panakhala nthaŵi pamene kubala ana kunapanga mbali ya ntchito imene Yehova anagawira kwa atumiki ake padziko lapansi. Umu ndi mmene zinaliri ndi Adamu ndi Hava. (Genesis 1:28) Chinalinso chowona ndi opulumuka a Chigumula. (Genesis 9:1) Yehova anafuna kuti ana Aisrayeli ayenera kukhala ochuluka kupyolera mwa kubala ana.—Genesis 46:1-3; Eksodo 1:7, 20; Deuteronomo 1:10.
13, 14. (a) Nchiyani chimene chinganenedwe ponena za kubala ana lerolino, ndipo kodi ndi chisulizo chotani chimene chingakhale chosayenera? (b) Pamene kubala ana mu nthaŵi ino ya mapeto kuli nkhani yaumwini, ndi uphungu wotani umene ukuperekedwa?
13 Lerolino, kubala ana sikuli mwachindunji mbali ya ntchito imene Yehova wapereka kwa anthu ake. Mosasamala kanthu za chimenecho, iko kudakalibe mwaŵi umene iye wapereka kwa anthu okwatirana ngati iwo akhumba icho. Chotero, okwatirana Achikristu omwe asankha kuyamba banja sayenera kusulizidwa ndiponso okwatirana omwe asankhapo kusakhala ndi ana sayenera kusulizidwa.
14 Chotero nkhani ya kubala ana mu nthaŵi ino ya mapeto iri yaumwini imene okwatirana aliwonse ayenera kugamulapo kwa iwo eni. Komabe, popeza “nthaŵi yotsala yafupikitsidwa,” okwatirana angachite bwino kuwona mosamalitsa ndipo mwapemphero ubwino ndi kuipa kwakubala ana m’nthaŵi zino. (1 Akorinto 7:29) Awo amene angasankhe kukhala ndi ana ayenera kukhala ozindikira kotheratu osati kokha chimwemwe chimene kubala ana kungabweretse komanso mathayo olowetsedwa ndi mavuto omwe angabuke kaamba ka iwoeni ndi ana awo amene angabweretse m’dziko.
Pamene Sanakonzekeredwe
15, 16. (a) Ndi kawonedwe kotani kamene kayenera kupewedwa pamene mimba yosayembekezeredwa iwoneka, ndipo nchifukwa ninji? (b) Ndimotani mmene mwana aliyense ayenera kuwonedwera, kuphatikizapo mathayo otani?
15 Ena amanena kuti: ‘Zimenezo nzabwino kwambiri, koma bwanji ngati mwana abwera mosayembekezeredwa?’ Ichi chachitika kwa okwatirana ambiri omwe anazindikira kotheratu nsonga yakuti iyi si nthaŵi yabwino ya kubweretsa ana m’dziko. Ena a iwo akhala mu utumiki wa nthaŵi zonse kwa zaka zingapo. Ndimotani mmene iwo ayenera kuwonera kufika kwa mlendo wosayembekezeredwa?
16 Apa ndi pamene ukholo wathayo umagwira ntchito. Zowona, mimba ingakhale yosayembekezeredwa, koma khanda limene limabwera silingalingaliridwe kukhala losafunidwa ndi makolo Achikristu. Mosasamala kanthu kuti ndi masinthidwe otani amene kufika kwake kungabweretse m’miyoyo yawo, iwo motsimikizirika safunikira kudzimva okwiitsidwa kulinga ku ilo. Ndiko nkomwe, iwo anali ndi thayo pa kuyambidwa kwake. Tsopano popeza kuti iye wafika, iwo ayenera kulandira kusintha kwa mkhalidwe wawo, akumadziŵa kuti, m’njira imodzi kapena inzake, “nthaŵi ndi zochitika zosawonedweratu zimagwera” anthu onse. (Mlaliki 9:11) Mofunitsitsa kapena ayi, iwo atenga mbali mu ntchito yolenga imene Yehova Mulungu ali Mkonzi wake. Iwo ayenera kulandira mwana wawo monga chikhulupiriro chopatulika ndipo mwachikondi kutenga mathayo awo monga “makolo m’chigwirizano ndi Ambuye.”—Aefeso 6:1.
“Chitani Zonse M’dzina la Ambuye”
17. Ndi uphungu wotani umene mtumwi Paulo anapereka kwa Akolose, ndipo ndimotani mmene uphungu umenewo ungatsatiridwire lerolino?
17 Nthaŵi yochepa asanapereke uphungu pa nkhani za banja, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndipo chirichonse mukachichita m’mawu kapena mu ntchito, chitani zonse m’dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa iye.” (Akolose 3:17-21) Mosasamala kanthu kuti ndi mkhalidwe wotani umene Mkristu angadzipeze iyemwini, ayenera kukhala woyamikira kwa Yehova ndi kutenga mwaŵi wa mkhalidwe wake “kuchita chirichonse m’dzina la Ambuye.”
18, 19. (a) Ndimotani mmene Akristu osakwatira ndi okwatirana opanda ana “angachitire zonse m’dzina la Ambuye”? (b) Ndimotani mmene makolo Achikristu ayenera kuwonera ana awo, ndipo ndi chonulirapo chotani chimene ayenera kukhazikitsa kaamba ka iwo eni?
18 Mkristu yemwe wasankha kukhala wosakwatira adzagwiritsira ntchito ufulu wake, osati kaamba ka kudzimwerekeretsa kwauwmini, koma kugwira ntchito “ndi mtima wonse monga kwa Yehova,” ngati nkotheka mu mtundu wina wa utumiki wa nthaŵi zonse. (Akolose 3:23; 1 Akorinto 7:32) Mofananamo, okwatirana omwe asankha kusakhala ndi ana ‘sadzachititsa nalo dziko’ mwadyera koma adzapereka ku utumiki wa Ufumu malo a akulu othekera m’miyoyo yawo.—1 Akorinto 7:29-31.
19 Ponena za Akristu omwe ali ndi ana, iwo ayenera kulandira ukholo wawo m’njira yokhala ndi thayo. M’malo moyang’ana pa ana awo monga choletsa kutumikira Yehova, iwo ayenera kuwalingalira iwo monga gawo lapadera. Nchiyani chimene ichi chidzasonyeza? Chabwino, pamene Mkristu wodzipereka akumana ndi winawake yemwe akusonyeza chikondwerero m’chowonadi, iye amayambitsa phunziro la Baibulo lapanyumba lokhazikika ndi ameneyo. Pamene wayambitsa phunzirolo, Mboniyo imakhala yaluntha, kubwererako mlungu ndi mlungu ndi cholinga chofuna kuthandiza wokondwererayo kupanga kupita patsogolo kwauzimu. Palibe china chirichonse chosiyanako chimene chimafunikira m’nkhani ya ana Achikristu. Phunziro la Baibulo lokhazikika, lolingaliridwa bwino, loyambidwa mwamsanga monga mmene kungathekere ndipo likumachitidwa pamaziko okhazikika, limafunikira kuthandiza wachichepere kukula mwauzimu ndi kuphunzira kukonda Mlengi wake. (2 Timoteo 3:14, 15) Kuwonjezerapo, makolo ayenera kukhala osamalitsa kusonyeza chitsanzo chabwino cha khalidwe la Chikristu panyumba, monga mmene amachitira m’Nyumba ya Ufumu. Ndipo ngati kuli kotheka iwo adzatenga thayo la kuphunzitsa ana awo mu utumiki wa m’munda. M’njira imeneyi, m’kuwonjezera ku kulalikira kwa achikulire ena, makolo adzafunafuna, ndi thandizo la Yehova, “kupanga ophunzira” a ana awo awo.—Mateyu 28:19.
Ana Mkati mwa “Chisautso Chachikulu”
20. (a) Nchiyani chimene chiri kutsogolo kwathu, ndipo ndi za mavuto otani amene Yesu anapereka chenjezo? (b) Kodi ndi kugwirizana kotani kumene mawu a Yesu ali nako pa kulera ana mu nthaŵi ya mapeto?
20 Kutsogolo kwathu kuli “chisautso chachikulu chonga sipadakhale chotero kuyambira chiyambi chadziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.” (Mateyu 24:21, NW) Idzakhala nthaŵi yovuta kwa achikulire ndi ana mofanana. Mu ulosi wake pa mapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu, Yesu ananeneratu kuti chowonadi cha Chikristu chidzagawanitsa banja. Iye ananena kuti: “Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuti amuphe, ndi atate mwana wake; ndi ana adzawombana ndi akuwabala, nadzawaphetsa.” (Marko 13:12) Mwachiwonekere, kulera ana mu nthaŵi ya mapeto nthaŵi zonse sikudzakhala chimwemwe chenicheni. Iko kungabweretse kusweka mtima, kukhumudwitsidwa, ndipo ngakhale tsoka, monga mmene mawu a Yesu ogwidwa mawu pamwambapo akusonyezera.
21. (a) Pamene mukulingalira za mtsogolo motsimikizirika, nchifukwa ninji makolo sayenera kukhala odera nkhaŵa mopambanitsa? (b) Kodi nchiyani chimene chingakhale chiyembekezo chawo, kaamba ka iwoeni ndi ana awo?
21 Koma pamene tikukhala achindunji ponena za mavuto amene ali kutsogolo, awo amene ali ndi ana achichepere sayenera kukhala odera nkhaŵa mopambanitsa ponena za mtsogolo. Ngati iwo akhala okhulupirika ndi kuchita monga mmene angathere kulera ana awo “m’maleredwe ndi chilangizo cha Yehova,” iwo angakhale otsimikiziridwa kuti ana awo omvera adzalingaliridwa mwachiyanjo. (Aefeso 6:4, NW; yerekezani ndi 1 Akorinto 7:14.) Monga mbali ya “khamu lalikulu,” iwo ndi ana awo achichepere angayembekezere kupulumuka “chisautso chachikulu.” Ngati ana oterowo akula kukhala atumiki okhulupirika a Yehova, iwo adzakhala oyamikira kosatha kwa iye kuti iwo anali makolo okhala ndi thayo.—Chivumbulutso 7:9, 14; Miyambo 4:1, 3, 10.
Mafunso Akubwereramo
◻ Ndi programu ya nthaŵi yaitali yotani imene kubadwa kwa mwana kumaphatikiza?
◻ Nchifukwa ninji akulu ena ndi atumiki otumikira ataya mathayo awo?
◻ Ndi nsonga zotani zimene mwamuna Wachikristu ayenera kulingalira m’chigwirizano ndi kukhala ndi pakati kwa mkazi wake?
◻ Nchiyani chimene chimatsimikizira kuti okwatirana Achikristu angakhale opanda ana ndipo achimwemwe?
◻ Ndimotani mmene kubadwa kwa mwana kuyenera kulingaliridwira ndi makolo, ndipo nchifukwa ninji iwo safunikira kudera nkhaŵa kopambanitsa ponena za mtsogolo?
[Chithunzi patsamba 24]
Atate angatengemo mbali mu thayo la kusunga ana kukhala chete mkati mwa misonkhano