Miyambo
4 Ana anga, mverani malangizo* a bambo anu.+
Mvetserani kuti mupeze luso lomvetsa zinthu,
2 Chifukwa ndidzakupatsani malangizo abwino.
4 Bambo anga ankandiphunzitsa kuti: “Mtima wako ugwire mwamphamvu mawu anga.+
Uzisunga malamulo anga kuti upitirize kukhala ndi moyo.+
5 Upeze nzeru, upezenso luso lomvetsa zinthu.+
Usaiwale ndipo usapatuke pa zimene ndimakuuza.
6 Nzeruzo usazisiye ndipo zidzakuteteza.
Uzikonde ndipo zidzakuteteza.
7 Nzeru ndi chinthu chofunika kwambiri,+ choncho upeze nzeru,
Ndipo pa zinthu zonse zimene upeze, upezenso luso lomvetsa zinthu.+
8 Uzilemekeze kwambiri ndipo zidzakukweza.+
Zidzakulemekeza chifukwa chakuti wazikumbatira.+
9 Zidzaika nkhata yamaluwa yokongola kumutu kwako.
Zidzakuveka chisoti chachifumu chokongola.”
12 Ukamayenda, mapazi ako sadzapanikizika.
Ndipo ngati ukuthamanga sudzapunthwa.
13 Gwira mwamphamvu malangizo ndipo usawasiye.+
Uwasunge bwino chifukwa iwo ndi moyo wako.+
16 Chifukwa iwo sangagone mpaka atachita zoipa.
Tulo sitiwabwerera mpaka atachititsa kuti wina agwe.
17 Amadya chakudya chimene achipeza chifukwa chochita zoipa,
Ndipo amamwa vinyo amene amupeza chifukwa chochita chiwawa.
18 Koma njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kwa mʼmawa
Kumene kumawonjezereka mpaka kunja kutawala kwambiri.+
19 Njira ya oipa ili ngati mdima.
Iwo sadziwa chimene chimawapunthwitsa.
21 Zisachoke pamaso pako.
Uzisunge mkati mwa mtima wako.+
22 Chifukwa amene amazipeza adzakhala ndi moyo+
Ndipo thupi lawo lonse lidzakhala lathanzi.
23 Uteteze mtima wako kuposa zinthu zonse zimene umaziteteza,+
Chifukwa mumtimamo ndi mmene muli akasupe a moyo.
27 Usakhotere kudzanja lamanja kapena lamanzere.+
Phazi lako lipatuke pa zinthu zoipa.