Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’makalata Opita kwa Atesalonika ndi Timoteyo
KUYAMBIRA nthawi imene mtumwi Paulo anakhazikitsa mpingo watsopano ku Tesalonika, mpingowo unatsutsidwa kwambiri. Choncho Timoteyo atabweretsa uthenga wabwino kuchokera ku mpingo wa ku Tesalonika, Paulo analembera kalata mpingowo kuti auyamikire ndi kuulimbikitsa. Kalata imeneyi inalembedwa cha m’ma 50 C.E. ndipo inali kalata yoyamba ya Paulo youziridwa. Nthawi imeneyi n’kuti Timoteyo ali ndi zaka pafupifupi 20. Patapita nthawi pang’ono, Paulo analemberanso a Khristu a ku Tesalonika kalata ina yachiwiri. M’kalatayi, Paulo anakonza maganizo olakwika amene ena anali nawo ndipo analimbikitsa abale kuti apitirize kukhala olimba m’chikhulupiriro.
Patapita zaka 10, Paulo analembera kalata Timoteyo. Panthawiyi n’kuti Paulo ali ku Makedoniya ndipo Timoteyo ali ku Efeso. M’kalatayi Paulo analimbikitsa Timoteyo kukhalabe ku Efeso kuti athandize abale kukhalabe olimba mwauzimu ngakhale kuti mu mpingomo munali aphunzitsi onyenga. Mzinda wa Roma utayaka moto mu 64 C.E., Akhristu anayamba kuzunzidwa kwambiri ndipo panthawi imeneyi Paulo analembera Timoteyo kalata yachiwiri. Imeneyi inali kalata yomaliza imene Paulo analemba. Masiku ano, malangizo a m’makalata anayi a Paulo amenewa angatilimbikitsenso.—Aheb. 4:12.
‘KHALANI MASO’
Paulo anayamikira Akhristu a ku Tesalonika chifukwa cha ‘ntchito zawo za chikhulupiriro, za chikondi, ndiponso kupirira kwawo.’ Iye anawauza kuti iwo ndi ‘chiyembekezo, chimwemwe komanso kolona’ wake.—1 Ates. 1:3; 2:19.
Atauza Akhristu a ku Tesalonika kuti azilimbikitsana ndi chiyembekezo cha chiukiriro, Paulo anati: “Tsiku la Yehova lidzabwera ndendende ngati mbala usiku.” Iye anawalimbikitsanso ‘kukhala maso’ ndi kusunga maganizo awo.—1 Ates. 4:16-18; 5:2, 6.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
4:15-17—Kodi ndani ‘amatengedwa m’mitambo kukakumana ndi Ambuye mu mlengalenga,’ ndipo zimenezi zimachitika bwanji? Amenewa ndi Akhristu odzozedwa amene ali ndi moyo m’nthawi ya kukhalapo kwa Khristu mu mphamvu zake za Ufumu. Iwo ‘amakumana ndi Ambuye’ Yesu m’miyamba yosaoneka. Koma kuti zimenezi zichitike, amafunika kufa kaye kenako n’kuukitsidwa monga zolengedwa zauzimu. (Aroma 6:3-5; 1 Akor. 15:35, 44) Popeza kukhalapo kwa Khristu kunayamba kale, Akhristu odzozedwa amene amafa masiku ano, ‘amatengedwa’ kapena kuti amaukitsidwa nthawi yomweyo.—1 Akor. 15:51, 52.
5:23—Kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamene anapemphera kuti ‘mzimu, moyo, ndi thupi la abale, zisungidwe’? Paulo amanena za mzimu, moyo ndi thupi la mpingo wachikhristu lopangidwa ndi anthu osiyanasiyana kuphatikizapo Akhristu odzozedwa ndi mzimu a ku Tesalonika. M’malo mongopemphera kuti mpingo usungidwe, iye anapemphera kuti “mzimu” wa mpingowo usungidwe. Anapempheranso kuti mpingo ukhale ndi “moyo” kapena kuti upitirire kukhalapo komanso anapempherera “thupi,” lomwe limaimira gulu la Akhristu odzozedwa. (1 Akor. 12:12, 13) Choncho pemphero limeneli limasonyeza kuti Paulo ankakonda kwambiri mpingowo.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:3, 7; 2:13; 4:1-12; 5:15. Kuti uphungu wathu ukhale wogwira mtima, tiyenera kuyamikira ndi kulimbikitsa munthu amene tikumulangizayo.
4:1, 9, 10. Anthu olambira Yehova ayenera kupitiriza kupita patsogolo mwauzimu.
5:1-3, 8, 20, 21. Pamene tsiku la Yehova likuyandikira, tiyeni “tisunge maganizo athu ndi kuvala chodzitetezera cha pachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi. Tivalenso chiyembekezo cha chipulumutso monga chisoti.” Komanso tifunika kutsatira kwambiri zimene Mawu a Mulungu aulosi, Baibulo, amanena.
“CHIRIMIKANI”
Anthu ena mu mpingo posintha zimene Paulo ananena m’kalata yake yoyamba, ankanena kuti “kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Khristu” kwayandikira. Powathandiza kusiya maganizo amenewa, Paulo ananena za zinthu zimene ‘zidzayambe kufika.’—2 Ates. 2:1-3.
Paulo anawalangiza kuti: “Chirimikani ndipo gwiranibe zolimba miyambo imene munaphunzitsidwa.” Iye anawauzanso kuti ‘apewe m’bale aliyense woyenda mosalongosoka.’—2 Ates. 2:15; 3:6.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
2:3, 8—Kodi “munthu wosamvera malamulo” ndi ndani, ndipo adzam’thetsa bwanji? “Munthu” ameneyu ndi gulu la atsogoleri achipembedzo. Ndipo Yesu Khristu, yemwe ndi “Mawu,” kapena kuti wom’lankhulira wamkulu wa Mulungu, ndiye wapatsidwa udindo wolengeza kwa anthu oipa chiweruzo cha Mulungu ndi kulamula kuti awonongedwe. (Yoh. 1:1) Choncho, tinganene kuti Yesu ndiye adzathetse munthu wosamvera malamulo “ndi mzimu [mphamvu yogwira ntchito] wa m’kamwa mwake.”
2:13, 14—Kodi Akhristu odzozedwa ‘anasankhidwa motani kuchokera pachiyambi kuti adzapulumuke’? Gulu la odzozedwa linasankhidwiratu nthawi imene Yehova anakonza zoti mbewu ya mkazi idzalalire mutu wa Satana. (Gen. 3:15) Yehova ananeneratunso zinthu zimene amafunika kukwaniritsa, ntchito imene adzagwire ndi mayesero amene adzakumane nawo. Choncho iye anawaitana ku “chipulumutso chimenechi.”
Zimene Tikuphunzirapo:
1:6-9. Powononga anthu oipa, Yehova sawononga anthu abwino.
3:8-12. Kuyandikira kwa tsiku la Yehova kusalepheretse munthu kugwira ntchito kuti apezere banja lake zinthu zofunika komanso kuti azithandize potumikira Mulungu. Kusafuna kugwira ntchito kungapangitse munthu kukhala waulesi ndiponso ‘wolowerera nkhani za ena.’—1 Pet. 4:15.
“SUNGA BWINO CHIMENE UNAIKIZIDWA”
Paulo analangiza Timoteyo kuti ‘apitirize kumenya nkhondo yabwino. Akhale ndi chikhulupiriro, ndiponso chikumbumtima chabwino.’ Mtumwiyu anatchula zinthu zimene amuna afunika kukwaniritsa kuti aikidwe pa udindo mu mpingo. Paulo analangizanso Timoteyo kuti ‘apewe nkhani zonama zimene zimaipitsa zoyera.’—1 Tim. 1:18, 19; 3:1-10, 12, 13; 4:7.
Paulo analemba kuti: “Usadzudzule mwamuna wachikulire mokalipa.” Iye analangizanso Timoteyo kuti: “Sunga bwino chimene unaikizidwa. Pewa nkhani zopanda pake zimene zimaipitsa zoyera. Upewenso mitsutso pa zimene ena monama amati ndiko ‘kudziwa zinthu.’”—1 Tim. 5:1; 6:20.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:18; 4:14—Kodi ndi “maulosi” otani amene ananenedwa okhudza Timoteyo? Payenera kuti panali maulosi ena okhudza ntchito zimene Timoteyo adzachite mu mpingo wachikhristu, amene Paulo analemba mouziridwa ali ku Lusitara paulendo wake wachiwiri wa umishonale. (Mac. 16:1, 2) Chifukwa cha “maulosi” amenewa, akulu a mu mpingo ‘anaika manja’ pa Timoteyo, kuti agwire ntchito yapadera.
2:15—Kodi mkazi ‘amatetezeka bwanji mwakubereka ana’? Kubereka ana, kuwasamalira, ndi kusamala pakhomo, zimapangitsa mkazi kukhala ‘wotetezeka’ osati womangokhala ndiponso ‘wodyera ena miseche ndi kulowerera nkhani za eni.’—1 Tim. 5:11-15.
3:16—Kodi chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwa Mulungu n’chiyani? Zoti anthu angamvere ulamuliro wa Yehova m’zinthu zonse, chinali chinsinsi kwa nthawi yaitali. Yesu anasonyeza kuti zimenezi n’zotheka pokhalabe wokhulupirika kwa Mulungu mpaka imfa yake.
6:15, 16—Kodi mawu amenewa akunena za Yehova Mulungu kapena za Yesu Khristu? Mawu amenewa akunena za amene adzaonekere, yemwe ndi Yesu Khristu. (1 Tim. 6:14) Mosiyana ndi anthu amene amalamulira monga mafumu ndi ambuye, Yesu ndi “Wamphamvu yekhayu,” ndipo iye yekha ndi amene ali ndi moyo wosakhoza kufa. (Dan. 7:14; Aroma 6:9) Kuchokera nthawi imene anapita kumwamba, palibe munthu aliyense padziko lapansi amene “angamuone.”
Zimene Tikuphunzirapo:
4:15. Kaya takhala Akhristu posachedwapa kapena tinakhala kale, tiyenera kuyesetsa kupita patsogolo ndiponso kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova.
6:2. Ngati timagwira ntchito kwa wokhulupirira mnzathu, tisam’pezerere. Koma tizilimbikira ntchito kuposa mmene tingachitire kwa munthu amene si wokhulupirira mnzathu.
“LALIKA MAWU, CHITA NAWO MWACHANGU”
Pofuna kuti Timoteyo akonzekere mavuto amene adzakumane nawo, Paulo anamulembera kuti: “Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha, koma wamphamvu, wachikondi, ndi wa kuganiza bwino.” Timoteyo analangizidwa kuti: “Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu, koma ayenera kukhala wodekha kwa onse. Ayeneranso kukhala woyenerera kuphunzitsa.”—2 Tim. 1:7; 2:24.
Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti: “Pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira utakhutira nazo.” Ziphunzitso za ampatuko zinali zitafala, choncho mtumwiyu analimbikitsa woyang’anira wachinyamatayu kuti: “Lalika mawu, chita nawo mwachangu . . . dzudzula, tsutsa, dandaulira.”—2 Tim. 3:14; 4:2.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:13—Kodi “chitsanzo cha mawu opindulitsa” n’chiyani? “Mawu opindulitsa” ndi “mawu a Ambuye wathu Yesu Khristu” omwe ndi ziphunzitso zoona zachikhristu. (1 Tim. 6:3) Zimene Yesu anaphunzitsa komanso zimene ankachita zinali zogwirizana ndi Mawu a Mulungu. Choncho “mawu opindulitsa” angatanthauzenso ziphunzitso zonse za m’Baibulo. Ziphunzitso zimenezi zingatithandize kudziwa zimene Yehova amafuna kuti tizichita. Timatsatira chitsanzo chimenechi mwa kugwiritsa ntchito zimene timaphunzira m’Baibulo.
4:13—Kodi “zikopa” zimenezi n’chiyani? Mawu akuti “zikopa” akunena za zinthu zimene ankalembapo, zopangidwa ndi zikopa. Choncho, n’kutheka kuti Paulo ankafuna mipukutu ya Malemba Achiheberi kuti aziwerenga ali ku ndende ku Roma. Ina mwa mipukutuyi iyenera kuti inali yopangidwa ndi gumbwa ndipo ina inali ya zikopa.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:5; 3:15. Chinthu chachikulu chimene chinachititsa Timoteyo kukhulupirira Khristu Yesu, kapena kuti chimene chinamulimbikitsa kuchita zonse zimene anachita, chinali Malemba amene anaphunzitsidwa kunyumba ali wamng’ono. N’zofunika kwambiri kuti makolo aziganizira mofatsa mmene akukwaniritsira udindo wawo kwa Mulungu komanso kwa ana awo.
1:16-18. Okhulupirira anzathu akamayesedwa, akamazunzidwa kapena akaikidwa m’ndende, tiziwapempherera komanso kuchita zonse zimene tingathe kuti tiwathandize.—Miy. 3:27; 1 Ates. 5:25.
2:22. Akhristu, makamaka achinyamata, asamataye nthawi yambiri ndi kuchita masewera olimbitsa thupi, kumvera nyimbo, kuyendayenda, kucheza kwambiri, kapenanso kuchita zinthu zina zotere, kuti azikhala ndi nthawi yokwanira yochita zinthu zauzimu.
[Chithunzi patsamba 31]
Kodi ndi kalata iti imene mtumwi Paulo anamalizira kulemba?