Kalata Yachiwiri Yopita kwa Atesalonika
2 Komabe abale, pa nkhani yokhudza kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Khristu+ komanso kusonkhanitsidwa kwathu kwa iye,+ tikukupemphani kuti 2 musalole kuti wina aliyense asinthe maganizo anu omwe ndi olondola. Musasokonezeke ngati wina atanena kuti tsiku la Yehova*+ lafika, ngakhale atanena kuti uthengawo ndi wochokera kwa Mulungu,+ kapena atanena kuti anawerenga mʼkalata imene anthu ena akunena kuti ife ndi amene tinalemba.
3 Musalole kuti aliyense akusocheretseni* mwa njira iliyonse chifukwa tsikulo lisanafike, choyamba mpatuko+ ukuyenera kuchitika ndiponso munthu wosamvera malamulo,+ amene ndi mwana wa chiwonongeko,+ akuyenera kuonekera. 4 Iye amatsutsa komanso kudzikweza pamwamba pa aliyense wotchulidwa kuti mulungu kapena chilichonse chimene chimalambiridwa,* moti amakhala pansi mʼkachisi wa Mulungu nʼkumadzionetsa poyera kuti iye ndi mulungu. 5 Kodi simukukumbukira kuti pamene ndinali nanu ndinkakuuzani zimenezi?
6 Ndipo inu mukudziwa chimene chikuchititsa kuti panopa asaonekere, kuti adzaonekere pa nthawi yake yoyenera. 7 Zoona, kuipa kwa munthu ameneyu, komwe ndi kwachinsinsi, kwayamba kale kugwira ntchito.+ Koma kuipa kumeneku kupitiriza kukhala chinsinsi mpaka amene akumulepheretsa atachoka. 8 Kenako, wosamvera malamuloyo adzaonekera poyera. Ambuye Yesu adzathetsa wosamvera malamuloyu ndi mzimu wamʼkamwa mwake+ ndipo adzamuwonongeratu pa nthawi imene kukhalapo kwa Yesuyo kudzaonekere.+ 9 Koma kukhalapo kwa wosamvera malamuloyo kukutheka ndi mphamvu za Satana.+ Iye akuchita ntchito iliyonse yamphamvu, zizindikiro zabodza, zodabwitsa+ 10 komanso akugwiritsa ntchito njira iliyonse yachinyengo+ kuti apusitse amene akupita kukawonongedwa. Izi zidzakhala chilango kwa iwo chifukwa sanalandire komanso kukonda choonadi kuti adzapulumuke. 11 Nʼchifukwa chake Mulungu walola kuti iwo apusitsidwe ndi ziphunzitso zabodza nʼcholinga choti azikhulupirira bodza,+ 12 kuti onsewo adzaweruzidwe chifukwa sanakhulupirire choonadi koma ankasangalala ndi zosalungama.
13 Komabe, tiyenera kumathokoza Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale amene Yehova* amakukondani, chifukwa Mulungu anakusankhani kuchokera pachiyambi+ kuti mudzapulumuke. Anachita zimenezi pokuyeretsani+ ndi mzimu wake komanso chifukwa munakhulupirira choonadi. 14 Anakuitanani ku chipulumutso chimenechi kudzera mu uthenga wabwino umene tikulengeza, kuti mudzapeze ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 15 Choncho abale, khalani olimba+ ndipo gwirani mwamphamvu miyambo imene munaphunzitsidwa,+ kaya kudzera mu uthenga wapakamwa kapena mʼkalata yochokera kwa ife. 16 Komanso Ambuye wathu Yesu Khristu ndiponso Mulungu Atate wathu, amene anatikonda+ ndipo salephera kutilimbikitsa komanso anatipatsa chiyembekezo chabwino,+ kudzera mwa kukoma mtima kwakukulu, 17 alimbikitse mitima yanu ndi kukulimbikitsani kuti nthawi zonse muzichita komanso kulankhula zinthu zabwino.