Olimba Ngati Nangula Chifukwa cha Chiyembekezo, Osonkhezeredwa ndi Chikondi
“Zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.”—1 AKORINTO 13:13.
1. Kodi mtumwi Paulo akutichenjeza za chiyani?
MTUMWI Paulo akutichenjeza kuti chikhulupiriro chathu chingasweke ngati chombo. Akunena za “kukhala nacho chikhulupiriro ndi chikumbumtima chokoma, chimene ena adachikankha, chikhulupiriro chawo chidatayika [“chinasweka ngati chombo,” NW].” (1 Timoteo 1:19) M’zaka za zana loyamba C.E., zombo zoyenda panyanja zinali zopanga ndi matabwa. Pokhapokha ngati zombozo zinapangidwa mwaluso ndi matabwa olimba m’pamene zinali kutha kuyenda panyanja.
2. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuchimanga bwino chombo cha chikhulupiriro chathu, ndipo tifunikira kuchitanji?
2 Chimene tingachitche kuti chombo cha chikhulupiriro chathu chiyenera kuyandamabe panyanja yowinduka ya anthu. (Yesaya 57:20; Chivumbulutso 17:15) Choncho, chiyenera kumangidwa bwino, ndipo zimenezi zimadalira ife tomwe. Pamene “nyanja” za Ayuda ndi Aroma zinakwiyira kwambiri Akristu oyambirira, Yuda analemba kuti: “Okondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mu Mzimu Woyera, mudzisunge nokha m’chikondi cha Mulungu, ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Kristu, kufikira moyo wosatha.” (Yuda 20, 21) Popeza kuti Yuda ananenanso za kulimbana ‘chifukwa cha chikhulupiriro chopatsidwa kwa oyera mtima,’ mawu akuti “chikhulupiriro choyeretsetsa” angakhale akutanthauza ziphunzitso zonse zachikristu, kuphatikizapo uthenga wabwino wa chipulumutso. (Yuda 3) Kristu ndiye maziko a chikhulupiriro chimenecho. Tifunikira kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kuti tigwiritse chikhulupiriro choona chachikristu.
Kupirira Namondwe wa Mbiri Yoopsa ya Magulu Ampatuko
3. Kodi ena akugwiritsa ntchito bwanji “mbiri yoopsa ya magulu ampatuko”?
3 Zaka zaposachedwapa, takhala tikumva nkhani zoopsa za anthu odzipha muunyinji, kupha anzawo, ndi kuukira kwa zigaŵenga ndipo ochita zimenezi ndi a m’timagulu tampatuko. N’chifukwa chakedi anthu ambiri, ngakhale atsogoleri andale oona mtima, amayesayesa kuteteza anthu osalakwa, makamaka ana aang’ono, kuwateteza ku magulu oopsa ampatuko oterewa. Popeza kuti mosakayikira “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano” ndiye akuchititsa maupandu oopsa amenewa, iye wabutsa mbiri yoopsa ya magulu ampatuko, ndipo akuigwiritsa ntchito kuukira anthu a Yehova. (2 Akorinto 4:4; Chivumbulutso 12:12) Ena apezerapo mwayi pamenepa ndipo akusonkhezera anthu kutsutsa ntchito yathu. M’mayiko ena, ayamba kampeni imene cholinga chake choonekeratu ndicho kuteteza anthu ku “magulu oopsa ampatuko” koma akulakwitsa mwa kutchulanso Mboni za Yehova, ndiye akumatineneza mwa kupinda mawu. Zimenezi zachititsa umboni wa kukhomo ndi khomo kukhala wovuta kwambiri m’mayiko ena a ku Ulaya, ndipo zachititsa anthu ena amene anali kuphunzira nafe Baibulo kuleka kuphunzira. Kenako zimenezi zalefula abale athu ena.
4. Kodi n’chifukwa chiyani chitsutso sichiyenera kutilefula?
4 Komabe, m’malo moti chitsutso chitilefule, chiyenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu chakuti tikutsata Chikristu choona. (Mateyu 5:11, 12) Akristu oyambirira ananenezedwa kuti anali kagulu koukira boma, ndipo anali ‘kuneneredwa ponseponse.’ (Machitidwe 24:5; 28:22) Koma mtumwi Petro analimbikitsa okhulupirira anzake, pamene anawalembera kuti: “Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu: koma popeza mulawana ndi Kristu zowawa zake, kondwerani; kutinso pa vumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu.” (1 Petro 4:12, 13) Winanso wa m’bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba analemba mofananamo kuti: “Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, mmene mukugwa m’mayesero amitundumitundu; pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro. Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasoŵa kanthu konse.” (Yakobo 1:2-4) Monga momwe mphepo zamphamvu panyanja zimayesera kulimba kwa chombo, momwemonso namondwe wa chitsutso amavumbula mbali zosalimba za chombo chathu cha chikhulupiriro.
Nsautso Imachita Chipiriro
5. Kodi tingatsimikize bwanji kuti chikhulupiriro chathu n’cholimba posautsidwa?
5 Akristu angadziŵe kuti ali ndi chipiriro ndi kuti chikhulupiriro chawo n’cholimba pokhapokha atakumana ndi anamondwe a nsautso. Chipiriro chathu ‘chingakhale nayo ntchito yake yangwiro’ panyanja yowinduka pokhapokha ‘titakhala angwiro ndi opanda chilema, osasoŵa kanthu konse,’ kuphatikizapo chikhulupiriro cholimba. Paulo analemba kuti: “M’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m’kupirira kwambiri, m’zisautso, m’zikakamizo, m’zopsinja.”—2 Akorinto 6:4.
6. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera ‘kukondwera m’zisautso,’ ndipo zimenezi zimalimbitsa motani chiyembekezo chathu?
6 Mphepo zamphamvu za nsautso zimene tingakumane nazo nthaŵi zina tiyenera kuziona monga mipata yosonyezera kuti chombo cha chikhulupiriro chathu n’cholimba ndi chokhazikika. Paulo analembera Akristu a ku Roma kuti: “Tikondwera m’zisautso; podziŵa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizoloŵezi [“mkhalidwe woyanjidwa,” NW]; ndi chizoloŵezi [“mkhalidwe woyanjidwawo,” NW] chichita chiyembekezo: ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi.” (Aroma 5:3-5) Kulimba poyesedwa kumatipezetsa chiyanjo cha Yehova. Ndiyeno zimenezi zimalimbitsa chiyembekezo chathu.
Chifukwa Chake Ena Amasweka Ngati Chombo
7. (a) Monga mmene mawu a Paulo akusonyezera, kodi ena anasweka bwanji ngati chombo mwauzimu? (b) Kodi ena apambuka bwanji pa choonadi lero?
7 Pamene Paulo anachenjeza za ‘kusweka ngati chombo,’ anali kunena za ena amene ‘adakankha’ chikumbumtima chawo chabwino nataya chikhulupiriro chawo. (1 Timoteo 1:19) Ena a iwo anali Humenayo ndi Alesandro, amene anakhala ampatuko, napambuka pa choonadi nalankhula zamwano. (1 Timoteo 1:20; 2 Timoteo 2:17, 18) Lero, ampatuko, amene amapambuka pa choonadi, amamenya ndi mawu “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kumene kuli ngati kuluma dzanja limene kale linali kuwadyetsa mwauzimu. Ena amafanana ndi “kapolo woipa,” amene mumtima mwake amati “Mbuye wanga wachedwa.” (Mateyu 24:44-49; 2 Timoteo 4:14, 15) Amatsutsa zoti dongosolo la zinthu loipali latsala pang’ono kutha kwinaku amaneneza gulu la kapolo limene lili maso mwauzimu chifukwa chakuti likufulumiza anthu a Yehova kukhala atcheru komanso achangu. (Yesaya 1:3) Anthu ampatuko ngati amenewo amatha ‘kupasula chikhulupiriro cha ena,’ kuwaswa mwauzimu ngati chombo.—2 Timoteo 2:18.
8. Kodi n’chiyani chimene chachititsa ena kuswa kapena kumiza chombo chawo cha chikhulupiriro?
8 Akristu ena odzipatulira aswa chombo cha chikhulupiriro chawo mwa kukankhira pambali chikumbumtima chawo ndi kuloŵerera zokondweretsa za dzikoli ndi chisembwere chake. (2 Petro 2:20-22) Enanso amamiza chombo cha chikhulupiriro chawo chifukwa chakuti malo opulumukira a dongosolo latsopano la zinthu sanayambebe kuonekera kumtunda. Popeza satha kuŵerengera nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa maulosi ndipo amaiŵala “tsiku la Yehova,” amasiya kulambira koona. (2 Petro 3:10-13; 1 Petro 1:9) Posapita nthaŵi amangopeza kuti ali m’madzi amatope owinduka a dongosolo lino la zinthu. (Yesaya 17:12, 13; 57:20) Ena amene asiya kusonkhana ndi mpingo wachikristu amakhulupirirabe kuti ndiwo uli ndi chipembedzo choona. Komabe, amaoneka kuti satha kuleza mtima ndipo alibe chipiriro chofunika kuti akhoze kudikira dziko latsopano limene Yehova Mulungu walonjeza. Moyo wa m’Paradaiso wawachedwera kwambiri.
9. Kodi Akristu ena odzipatulira koma oŵerengeka akuchitanji, ndipo mfundo zimenezi ziyenera kutifikitsa polingalira za chiyani?
9 Akristu ena odzipatulira a m’mayiko ena akuchita ngati afunya mathanga a chombo cha chikhulupiriro chawo. Chombocho chidakayandamabe, koma m’malo mothamanga ndi chikhulupiriro chonse, akungoyenda ngati si ulendo wofuna changu. Ena atamva chiyembekezo cha “Paradaiso posachedwapa,” anachita khama kwambiri kuti adzaloŵemo—anakangalika kwambiri pantchito yolalikira ndi kupezeka nthaŵi zonse pamisonkhano ya mpingo, yadera, ndi yachigawo. Koma tsopano poganiza kuti chiyembekezo chawo chikutenga nthaŵi yaitali chisanakwaniritsidwe, safunanso kuchita khama ngati kale lija. Amaonetsa zimenezo mwa kufooka pantchito yolalikira, kusasonkhana mokhazikika, ndipo amakonda kuphonya mapologalamu ena a msonkhano wadera kapena wachigawo. Ena akumawonongera nthaŵi yambiri pa zosangalatsa ndi kupeza chuma. Mfundo zimenezi zikutifikitsa polingalira za chimene chiyenera kutisonkhezera kwambiri pamoyo wathu malinga ndi kudzipatulira kwathu kwa Yehova. Kodi changu chathu mu utumiki wake chiyenera kukhala chifukwa chakuti tili ndi chiyembekezo cha “Paradaiso posachedwapa”?
Chiyembekezo Chili Ngati Nangula
10, 11. Kodi chiyembekezo chathu Paulo anachiyerekeza ndi chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani chili chitsanzo choyenera?
10 Paulo ananena kuti Yehova analonjeza kuti madalitso akadzera mwa Abrahamu. Ndiyeno mtumwiyo anafotokoza kuti: “Mulungu, . . . analoŵa pakati ndi lumbiro; kuti mwa zinthu ziŵiri zosasinthika, [mawu ake ndi lumbiro lake] m’mene Mulungu sakhoza kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathaŵira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu; chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso.” (Ahebri 6:17-19; Genesis 22:16-18) Chiyembekezo cha Akristu odzozedwa n’cha moyo wosakhoza kufa kumwamba. Lero, unyinji wa atumiki a Yehova ali ndi chiyembekezo chosangalatsa cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. (Luka 23:43) Popanda chiyembekezo chimenecho, munthu sangakhale ndi chikhulupiriro.
11 Nangula ndi chida china cholimba choteteza chombo komanso chofunika kwambiri kuti chombocho chikhale malo amodzi chisatengeke ndi mphepo. Palibe aliyense woyendetsa chombo amene amayamba ulendo kuchoka padoko alibe nangula. Popeza kuti Paulo anapezeka kangapo m’ngozi ya kusweka kwa chombo, anadziŵa kuti moyo wa amalinyero umadalira anangula a chombo chawo. (Machitidwe 27:29, 39, 40; 2 Akorinto 11:25) M’zaka za zana loyamba, chombo chinalibe injini yothandiza mmalinyero kuwongolera chombocho mmene anafunira. Zombo zankhondo zokha n’zimene zinali zochita kupalasa, koma zombo zina wamba zinali kudalira mphepo kuzikankha. Ngati chombo chinali pangozi yokankhidwira kumatanthwe, chokha chimene mmalinyero anali kutha kuchita chinali kuponya nangula m’madzi mpaka nyanja itakhala bata, akudalira kuti nangulayo adzalumabe pansi osazuka. Ndiye chifukwa chake Paulo anayerekeza kuti chiyembekezo cha Mkristu chili ngati “nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso.” (Ahebri 6:19) Pamene anamondwe a chitsutso atiomba kapena takumana ndi ziyeso zina, chiyembekezo chathu chodabwitsa chili ngati nangula amene amatilimbitsa anthu amoyo, kuti chombo chathu cha chikhulupiriro chisatengeketengeke kumka ku mchenga woopsa wa kukayikira kapena ku miyala yangozi ya mpatuko.—Ahebri 2:1; Yuda 8-13.
12. Kodi tingapeŵe bwanji kulekana ndi Yehova?
12 Paulo anachenjeza Akristu achihebri kuti: “Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo.” (Ahebri 3:12) M’mawu achigiriki, tanthauzo lenileni la “kulekana” ndi “kudzipatula,” ndiko kuti, kuchita mpatuko. Koma tingapeŵe kusweka koipa ngati kumeneko. Chikhulupiriro ndi chiyembekezo zingatithandize kumamatira kwa Yehova ngakhale panthaŵi ya anamondwe oopsa a ziyeso. (Deuteronomo 4:4; 30:19, 20) Chikhulupiriro chathu sichidzakhala ngati chombo chotengekatengeka ndi mphepo za chiphunzitso cha mpatuko. (Aefeso 4:13, 14) Ndipo titakhala ndi chiyembekezo monga nangula, tidzatha kudutsa anamondwe m’moyo monga atumiki a Yehova.
Timasonkhezeredwa ndi Chikondi ndi Mzimu Woyera
13, 14. (a) Kodi n’chifukwa chiyani nangula wa chiyembekezo chathu saali wokwanira payekha? (b) Kodi mphamvu yotisonkhezera kuchitira Yehova utumiki wopatulika iyenera kukhala chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?
13 Mkristu sangapite patsogolo mpaka kuloŵa m’dongosolo latsopano ngati amangotumikira Yehova n’cholinga chokhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Pamene kuli kwakuti ali ndi nangula wa chiyembekezo chake monga chom’limbikitsa m’moyo, amafunikiranso kuti pa chiyembekezo chake ndi chikhulupiriro chake awonjezepo mphamvu yosonkhezera ya chikondi. Paulo anagogomeza mfundo imeneyi pamene analemba kuti: “Zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.”—1 Akorinto 13:13.
14 Chikondi chochokera pansi pa mtima ndicho chiyenera kukhala mphamvu yotisonkhezera kuchitira Yehova utumiki wopatulika, poyamikira chikondi chake chachikulu chimene ali nacho pa ife. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi. Umo chidaoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anam’tuma Mwana wake wobadwa yekha, aloŵe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye. Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.” (1 Yohane 4:8, 9, 19) Pofuna kuyamikira Yehova, cholinga chathu chachikulu chisakhale kufuna kupulumuka basi, koma kufuna kuona dzina lake loyera likuyeretsedwa ndi kuonanso kutsimikizidwa kwa uchifumu wake wolungama.
15. Kodi chikondi chathu pa Yehova chikugwirizana motani ndi nkhani ya uchifumu wake?
15 Yehova amafuna kuti tizim’tumikira chifukwa chom’konda iyeyo, osati chifukwa tikufuna kukhala m’Paradaiso basi. Insaikulopediya yofotokoza za Baibulo, yotchedwa Insight on the Scripturesa imati: “Yehova amakondwera kuona kuti uchifumu wake komanso chichirikizo chimene zolengedwa zake zimapereka maziko ake kwenikweni ndi chikondi. Amafuna anthu okhawo amene amakonda uchifumu wake chifukwa chakuti mikhalidwe yake n’njabwino kwambiri ndiponso chifukwa chakuti uchifumuwo n’ngwolungama, anthu amene amafuna uchifumu wake wokhawo, osatinso wina. (1 Akor. 2:9) Anthuwo amasankha kulamuliridwa ndi uchifumu wake m’malo mofuna kudziimira paokha—chifukwa chakuti amam’mdziŵa iye komanso amadziŵa za chikondi chake, chilungamo, ndi nzeru, zimenenso amadziŵa kuti ziposeratu zawo. (Sal. 84:10, 11)”—Voliyumu 2, tsamba 275.
16. Kodi chikondi chathu pa Yesu chimatisonkhezera motani pamoyo wathu?
16 Monga Akristu, timakondanso Yesu chifukwanso iye anatikonda. Paulo anati: “Chikondi cha Kristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa; ndipo adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa Iye amene adawafera iwo, nauka.” (2 Akorinto 5:14, 15) Kristu ndiye maziko okha amene pamangidwa moyo wathu wauzimu, chikhulupiriro chathu ndi chiyembekezo chathu. Kukonda kwathu Kristu Yesu kumalimbitsa chiyembekezo chathu ndi kukhazikitsa chikhulupiriro chathu, makamaka panthaŵi ya ziyeso zonga namondwe.—1 Akorinto 3:11; Akolose 1:23; 2:6, 7.
17. Kodi mphamvu yogwira ntchito imene Yehova amatipatsa n’chiyani, ndipo kufunika kwake kwasonyezedwa bwanji pa Machitidwe 1:8 ndi pa Aefeso 3:16?
17 Pamene kuli kwakuti chikondi chathu pa Mulungu ndi Mwana wake ndicho mphamvu yaikulu yotisonkhezera pamoyo wathu monga Akristu, Yehova amatipatsanso kanthu kena kamene kamatisonkhezera, kutilimbitsa, ndi kutipatsa nyonga yochitira utumiki wake. Tikunena mphamvu yake yogwira ntchito, kapena mzimu woyera. Mawu achihebri ndi achigiriki otembenuzidwa kuti “mzimu” kwenikweni amatanthauza mpweya umene ukuyenda mwamphamvu, monga mphepo. Zombo za panyanja zonga zimene Paulo anali kukwera zinali kukankhidwa ndi mphamvu yosaoneka ya mphepo kuti zikafike kumene zinali kupita. Mofananamo, timafunikira chikondi ndi mphamvu yosaoneka ya Mulungu yogwira ntchito kuti chombo cha chikhulupiriro chathu chizitipititsabe kutsogolo mu utumiki wa Yehova.—Machitidwe 1:8; Aefeso 3:16.
Tiyeni Mpaka Titafika Kumene Tikupita!
18. Kodi n’chiyani chidzatithandiza kupirira ziyeso zilizonse za chikhulupiriro chathu m’tsogolo?
18 Chikhulupiriro chathu ndi chikondi chathu zingayesedwe kwambiri tisanafike m’dongosolo latsopano la zinthu. Koma Yehova watipatsa nangula ‘wokhazikika ndi wolimbanso’—chiyembekezo chathu chodabwitsa. (Ahebri 6:19; Aroma 15:4, 13) Ngati tikukanthidwa ndi zitsutso ndi ziyeso, tingapirirebe ngati tili olimba zedi ngati nangula chifukwa cha chiyembekezo chathu. Namondwe woyamba atangotha, koma winanso asanayambe, tiyeni titsimikize kulimbitsa chiyembekezo chathu ndi kulimbitsanso chikhulupiriro chathu.
19. Kodi tingamawongolerebe motani chombo cha chikhulupiriro chathu mpaka titafika kumalo opulumukira m’dziko latsopano la Mulungu?
19 Paulo asanatchule za “nangula wa moyo,” anati: “Tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga ku chiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro; kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikuloŵa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.” (Ahebri 6:11, 12) Posonkhezeredwa ndi chikondi chathu pa Yehova ndi Mwana wake, komanso mwa mphamvu ya mzimu woyera, tiyeni tiziwongolerabe chombo cha chikhulupiriro chathu mpaka titafika kumalo opulumukira m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kubwereramo
◻ Ponena za chikhulupiriro chathu, kodi Paulo anatipatsa chenjezo lotani?
◻ Kodi ena asweka motani ngati chombo mwauzimu, ndipo enanso akuchepetsa motani liŵiro lawo?
◻ Kodi ndi mkhalidwe uti waumulungu umene ufunika kuwonjezedwa pa chikhulupiriro chathu?
◻ Kodi chidzatithandiza kufika kumalo opulumukira m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza n’chiyani?
[Chithunzi patsamba 16]
Chombo cha chikhulupiriro chathu chiyenera kumangidwa bwino kuti chipirire anamondwe m’moyo
[Chithunzi patsamba 17]
Chikhulupiriro chathu chingasweke ngati chombo
[Chithunzi patsamba 18]
Chiyembekezo ndicho nangula wa moyo wathu monga Akristu