Kodi ndi Mulungu Uti Amene Muyenera Kulambira?
CHOYAMBA, kodi ndani amene ali Mulungu mmodzi yekhayo woyenera kulambiridwa? Baibulo limayankha molunjika kwenikweni. Bukhu la Chibvumbulutso likulengeza kuti: ‘Muyenera inu, Yehova, Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.’ (Chibvumbulutso 4:11) Inde, Yehova, Mlengiyo, ndiye Mulungu yekha amene amafunikira kulambira kwathu. Chifukwa ninji? Tidzabwerera ku funso limenelo posachedwapa. Koma choyamba, tiyeni tilankhule za milungu ina imene imalambiridwa ndi anthu.
Chomwe Chiri Kumbuyo kwa Milungu Yonse Yonama
Ngakhale kuti anthu amatumikira milungu yambiri, chowonadi nchakuti kulambira konse koperekedwa kwa milungu yonse m’maiko onse—kupatulapo kulambira koperekedwa kwa Yehova, Mlengiyo—kumatumikira chifuno cha mulungu mmodzi yekha. Mwanjira yotani? Ŵerengani mawu a mtumwi Paulo kwa Akristu a ku Korinto. Mumzinda umenewo milungu yambiri inkalambiridwa, kuyambira pa Aphrodite wachiŵereŵere mpaka Aesculapius, mulungu wawo wochiritsa. Komabe, Paulo anasonyeza kuti pali magwero oipa amodzi okha kumbuyo kwa milungu imeneyi. Iye analemba kuti: “Zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda; [osati kwa Mulungu, NW].” (1 Akorinto 10:20) Inde, Akorinto achikunjawo ankalambira ziŵanda.
Ziŵanda zinakhalako mwakupanduka. Choyamba ndipo chachikulu koposa cha zonse chinali cholengedwa chaungelo chimene chinanyenga Hava kuswa lamulo la Mulungu kalelo m’munda wa Edene. (Genesis 3:1-6; Yohane 8:44) Chitatero, cholengedwachi chinapanduka motsutsana ndi ufumu wa Mlengi. Pambuyo pake, iye anadzatchedwa Satana, kutanthauza “Wotsutsa.” Pambuyo pake, zolengedwa zina zauzimu zinagwirizana naye m’kupandukako. Nazonso zinakhala ziŵanda, ndipo Satana akuzindikiritsidwa kukhala ‘mkulu wa ziŵanda.’ (Mateyu 12:24, 26) M’bukhu la Chibvumbulutso, ziŵanda zimenezi zikutchedwa “angelo” a Satana. (Chibvumbulutso 12:7) Choncho kulambira ziŵanda nkofanana ndi kulambira Satana.
Satana ali ndi chisonkhezero chachikulu. Mtumwi Yohane ananena kuti “dziko lonse lapansi” ligona m’mphamvu yake, ndipo Paulo anamutcha “mulungu wa nthawi yino ya pansi pano.” (1 Yohane 5:19; 2 Akorinto 4:4) Chotero, kulambira mulungu wina kupatulapo Yehova kulidi kulambira Satana. Kumatumikira kotheratu zifuno za Satana chifukwa chakuti chonulirapo chake ndicho kunyenga ana a Adamu ndi Hava kupandukira Yehova. Popeza kuti Satana ‘akunyenga dziko lonse,’ mwachiwonekere iye wapambana m’zochitika zambiri. (Chibvumbulutso 12:9) Koma osati m’zonse. Padakali mamiliyoni ambiri amene akukalamira kulambira Yehova. Chifukwa ninji?
Zipatso za Kulambira Kolakwa
Choyamba, iwo amadziŵa kuti kulambira milungu ina osati Yehova kumawatengera zinthu zambiri kuposa zimene amafuna kulipira. Zofukulidwa m’mabwinja mu Carthage wakale Kumpoto kwa Afirika zinavumbula manda a ana. M’mandamo mudali mafupa a achichepere omwe adaperekedwa nsembe kwa mulungu Wachifoinike, Baala. Nsembe za ana ndizo zinali mtengo woopsa umene anthu a ku Carthage amenewo anapereka chifukwa cholambira Baala. Chikatolika cha nyengo zapakati chinafunanso mtengo pamene chinapangitsa kuvutika kosaneneka m’Nkhondo Zamitanda zokhetsa mwazi ndi Zilango zankhalwe. Kulambira milungu ya Inca isanafike nthaŵi ya Columbia wa ku Amereka kunaloŵetsamo mwambo wakupha anthu zikwi zambiri.
M’nthaŵi zamakono kwenikweni, mitundu yosiyanasiyana ya kulambira yaloŵetsedwamo m’kupha kwa unyinji mu India, ndipo yathandizira kuchititsa mavuto aakulu a ndale zadziko ku Middle East ndi Kumpoto kwa Ireland. Umbuli, kukhulupirira malaulo, ndi mantha ziyeneranso kundandalitsidwa kukhala mbali ya mtengo umene munthu akulipira kaamba ka kulambira kwake milungu yambiri.
Kodi Nchifukwa Ninji Muyenera Kutumikira Yehova Mulungu?
Kumbali ina, kulambira Yehova kumabweretsa mapindu okhaokha. Choyamba, ndi “Iye amene ali ndi moyo ku nthawi za nthawi, amene analenga m’mwamba ndi zinthu ziri momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu ziri momwemo, ndi nyanja ndi zinthu ziri momwemo.” (Chibvumbulutso 10:6) Chotero, tiyenera kumlambira iye chifukwa chakuti ndiye Mlengi wathu.
Kuwonjezera apa, tiyenera kulambira Yehova Mulungu chifukwa chakuti mikhalidwe yake imatikopa kumlambira iye. Mtumwi Yohane ananena kuti ‘Mulungu ndiye chikondi.’ (1 Yohane 4:8) Mwamuna wokhulupirika Yobu ananena kuti ‘[Mulungu] ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikulu.’ (Yobu 9:4) Mose anaimba motere za iye: ‘Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; iye ndiye wolungama ndi wolunjika.’ (Deuteronomo 32:4) Kodi ndani angakaikekaike kutumikira Mulungu woteroyo?
Kuwonjezerapo, Baibulo limati: ‘Chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.’ (1 Timoteo 4:8) Zimenezi nzowona chotani nanga! Yehova amafunira anthu zimene ziri zabwino. Iye anapereka dziko lapansi monga mudzi wokongola wa zolengedwa zake, ndipo anapereka zinthu zambiri kotero kuti moyo ukhale wosangalatsa. Mosasamala kanthu za kupanduka kwa munthu, Mulungu wapitirizabe kuchilikiza moyo padziko lapansili, kupereka zosoŵa zonse zakuthupi za anthu pamene ‘amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.’—Mateyu 5:45.
Koma “lonjezano la ku moyo uno” limanka patali. Kutumikira Mulungu nkokhutiritsa ndi kokwaniritsa. Ndiko kumene tinapangidwira kuchita. Ndipo Mulungu amathandiza awo amene amamtumikira mokhulupirika kuti akhale ndichipambano m’moyo. Kupyolera m’Baibulo, iye amapereka chitsogozo kwa mbeta, okwatirana, ana—anthu amikhalidwe yonse. Iye amapereka nzeru zodalirika, zogwira ntchito kutithandiza m’mikhalidwe yonse kotero kuti tingathetse mavuto amoyo monga anthu opanda ungwiro m’dziko lokhala pansi pa chisonkhezero cha Satana. Ngati timalambira Mulungu m’njira imene imamkondweretsa, tingasangalale ndi ‘mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse.’—Afilipi 4:7.
Lodziŵikanso, liri “lonjezano . . . la moyo ulinkudza.” Yesu anauza Nikodemo Mfarisiyo kuti: ‘Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.’ (Yohane 3:16) Moyo wosatha! Kodi ndi mulungu uti kupatulapo Yehova amene angalonjeze chinthu choterocho ndiyeno nkukwaniritsa lonjezo lake? Mkhalidwe womalizira wa anthu olandira mphatso yaikulu imeneyo ukulongosoledwa m’Chibvumbulutso motere: ‘[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.’ (Chibvumbulutso 21:4, 5) Ndithudi, ziyembekezo za moyo ulinkudza ziyenera kutipangitsa kufuna kutumikira Yehova!
Pamenepo, kodi ndi Mulungu uti amene tiyenera kulambira? Yehova yekha, Mlengiyo. Pa milungu yonse, kwa iye kokha mawu awa amagwira ntchito: ‘Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zowona, Mfumu inu ya nthaŵi zosatha. Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Yehova? Chifukwa inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.’ (Chibvumbulutso 15:3, 4) Awo amene amavomereza ku chenjezo ili la wamasalmo nganzeru chotani nanga: “Tiyeni, tipembedze tiwerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga”!—Salmo 95:6.
[Chithunzi patsamba 6]
Milungu ina imene Satana wapangitsa anthu kuilambira
[Chithunzi patsamba 7]
Ziyembekezo za moyo ulinkudza ziyenera kutipangitsa kufuna kutumikira Yehova